Settings
Surah Competition [At-Takathur] in Chewa
أَلۡهَىٰكُمُ ٱلتَّكَاثُرُ ﴿1﴾
Kwakutangwanitsani kusonkhanitsa (chuma chambiri ndi ana).[477]
حَتَّىٰ زُرۡتُمُ ٱلۡمَقَابِرَ ﴿2﴾
Mpakana mwapita kumanda (mwamwalira ndikukalowa m’manda).
كَلَّا سَوۡفَ تَعۡلَمُونَ ﴿3﴾
Sichoncho! Mudziwa posachedwapa.[478]
ثُمَّ كَلَّا سَوۡفَ تَعۡلَمُونَ ﴿4﴾
Ndiponso sichoncho! Mudziwa posachedwapa.
كَلَّا لَوۡ تَعۡلَمُونَ عِلۡمَ ٱلۡیَقِینِ ﴿5﴾
Sichoncho! mukadakhala mukudziwa, kudziwa kwachitsimikizo (sibwenzi mukutangwanika ndi za mdziko).
لَتَرَوُنَّ ٱلۡجَحِیمَ ﴿6﴾
Ndithudi mudzauona Moto.
ثُمَّ لَتَرَوُنَّهَا عَیۡنَ ٱلۡیَقِینِ ﴿7﴾
Kenako mudzauona ndithu ndi diso lachitsimikizo.
ثُمَّ لَتُسۡـَٔلُنَّ یَوۡمَىِٕذٍ عَنِ ٱلنَّعِیمِ ﴿8﴾
Tsono patsikulo ndithudi mudzafunsidwa za mtendere (omwe munapatsidwa).[479]
English
Chinese
Spanish
Portuguese
Russian
Japanese
French
German
Italian
Hindi
Korean
Indonesian
Bengali
Albanian
Bosnian
Dutch
Malayalam
Romanian