Settings
Surah The declining day [Al-Asr] in Chewa
Surah The declining day [Al-Asr] Ayah 3 Location Makkah Number 103
وَٱلۡعَصۡرِ ﴿1﴾
Ndikuilumbilira nthawi.[480]
إِنَّ ٱلۡإِنسَـٰنَ لَفِی خُسۡرٍ ﴿2﴾
Ndithu munthu aliyense ndi wotaika (chifukwa chakugonjetsedwa ndi zilakolako zake).
إِلَّا ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ وَعَمِلُوا۟ ٱلصَّـٰلِحَـٰتِ وَتَوَاصَوۡا۟ بِٱلۡحَقِّ وَتَوَاصَوۡا۟ بِٱلصَّبۡرِ ﴿3﴾
Kupatula amene akhulupirira (mwa Allah) ndi kumachita zabwino, ndikumalangizana kutsatira choona ndiponso ndi kumalangizana za kupirira (potsatira malamulo a Allah ndi zina za mdziko).[481]