Settings
Surah The Traducer [Al-Humaza] in Chewa
وَيْلٌۭ لِّكُلِّ هُمَزَةٍۢ لُّمَزَةٍ ﴿1﴾
Kuonongeka koopsa kudzampeza aliyense wojeda ndi wonyoza anthu polozera (ndi maso kapena kuyankhula ndi lirime).[482]
ٱلَّذِى جَمَعَ مَالًۭا وَعَدَّدَهُۥ ﴿2﴾
Yemwe wasonkhanitsa chuma ndikumachiwerengera.[483]
يَحْسَبُ أَنَّ مَالَهُۥٓ أَخْلَدَهُۥ ﴿3﴾
Akuganiza kuti chuma chakecho chimkhazika (pa dziko) nthawi yaitali (ndikumteteza ku zimene sakuzifuna).
كَلَّا ۖ لَيُنۢبَذَنَّ فِى ٱلْحُطَمَةِ ﴿4﴾
Sichoncho! (Asiye maganizo amenewo) ndithudi, akaponyedwa ku Moto woononga (chifukwa cha kuipa kwa zochita zake).
وَمَآ أَدْرَىٰكَ مَا ٱلْحُطَمَةُ ﴿5﴾
Ndi chiyani chingakudziwitse za Moto woonongawu?
نَارُ ٱللَّهِ ٱلْمُوقَدَةُ ﴿6﴾
Umenewu ndi Moto wa Allah woyaka (nthawi zonse, woononga chilichonse choponyedwa mmenemo).
ٱلَّتِى تَطَّلِعُ عَلَى ٱلْأَفْـِٔدَةِ ﴿7﴾
Umene umakwera mpaka ku mtima.[484]
إِنَّهَا عَلَيْهِم مُّؤْصَدَةٌۭ ﴿8﴾
Ndithu motowo ukawazinga (ndi kuwatsekera makomo).
فِى عَمَدٍۢ مُّمَدَّدَةٍۭ ﴿9﴾
Munsanamira za zitalizitali (kotero kuti sakatha kugwedezeka mmenemo kapena kupulumuka).