Settings
Surah The Elephant [Al-fil] in Chewa
Surah The Elephant [Al-fil] Ayah 5 Location Makkah Number 105
أَلَمۡ تَرَ كَیۡفَ فَعَلَ رَبُّكَ بِأَصۡحَـٰبِ ٱلۡفِیلِ ﴿1﴾
Kodi sudaone momwe Mbuye wako adawachitira eni njovu?[485]
أَلَمۡ یَجۡعَلۡ كَیۡدَهُمۡ فِی تَضۡلِیلࣲ ﴿2﴾
Kodi sadachichite chiwembu chawo kukhala chosokera (chopanda phindu?)
وَأَرۡسَلَ عَلَیۡهِمۡ طَیۡرًا أَبَابِیلَ ﴿3﴾
Ndipo adawatumizira magulumagulu a mbalame otsatizana. (ndipo adawazungulira mbali zonse).
تَرۡمِیهِم بِحِجَارَةࣲ مِّن سِجِّیلࣲ ﴿4﴾
Zimawagenda ndi miyala ya moto.
فَجَعَلَهُمۡ كَعَصۡفࣲ مَّأۡكُولِۭ ﴿5﴾
Choncho adawachita ngati m’mera wodyedwa (ndi nyama ndi kulavulidwa).