Main pages

الۤمۤ ﴿1﴾

Alif-Lâm-Mîm.[1]

ذَ ٰ⁠لِكَ ٱلۡكِتَـٰبُ لَا رَیۡبَۛ فِیهِۛ هُدࣰى لِّلۡمُتَّقِینَ ﴿2﴾

Ili ndi Buku lopanda chipeneko mkati mwake, ndichiongoko cha (anthu) oopa Allah.

ٱلَّذِینَ یُؤۡمِنُونَ بِٱلۡغَیۡبِ وَیُقِیمُونَ ٱلصَّلَوٰةَ وَمِمَّا رَزَقۡنَـٰهُمۡ یُنفِقُونَ ﴿3﴾

Omwe amakhulupirira zosaoneka ndi maso (monga Munda wamtendere, Moto, Angelo ndi zina zotere zomwe Allah ndi Mtumiki (s.a.w) adazifotokoza, amapemphera Swala moyenera, ndiponso amapereka m’zimene tawapatsa.

وَٱلَّذِینَ یُؤۡمِنُونَ بِمَاۤ أُنزِلَ إِلَیۡكَ وَمَاۤ أُنزِلَ مِن قَبۡلِكَ وَبِٱلۡـَٔاخِرَةِ هُمۡ یُوقِنُونَ ﴿4﴾

Ndi amene akukhulupirira zomwe zidavumbulutsidwa kwa iwe, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kale iwe usadadze, nakhulupiriranso motsimikiza kuti lilipo tsiku lachimaliziro.

أُو۟لَـٰۤىِٕكَ عَلَىٰ هُدࣰى مِّن رَّبِّهِمۡۖ وَأُو۟لَـٰۤىِٕكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ ﴿5﴾

Iwowo (omwe ali ndi chikhalidwe chotere), ali pachiongoko chochokera kwa Mbuye wawo (Allah), ndipo iwowo ndi omwe ali opambana (pokapeza ulemelero wapamwamba ku Minda ya mtendere).

إِنَّ ٱلَّذِینَ كَفَرُوا۟ سَوَاۤءٌ عَلَیۡهِمۡ ءَأَنذَرۡتَهُمۡ أَمۡ لَمۡ تُنذِرۡهُمۡ لَا یُؤۡمِنُونَ ﴿6﴾

Ndithu amene sadakhulupirire, nchimodzimodzi kwa iwo uwachenjeze kapena usawachenjeze sangakhulupirire.

خَتَمَ ٱللَّهُ عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ وَعَلَىٰ سَمۡعِهِمۡۖ وَعَلَىٰۤ أَبۡصَـٰرِهِمۡ غِشَـٰوَةࣱۖ وَلَهُمۡ عَذَابٌ عَظِیمࣱ ﴿7﴾

(Ali ngati kuti) Allah wawadinda chidindo chotseka mitima yawo ndi makutu awo (kotero kuti kuunika kwa chikhulupiliro sikungalowemo), ndipo m’maso mwawo muli chophimba (sangathe kuona zozizwitsa za Allah); choncho iwo adzalandira chilango chachikulu.

وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن یَقُولُ ءَامَنَّا بِٱللَّهِ وَبِٱلۡیَوۡمِ ٱلۡـَٔاخِرِ وَمَا هُم بِمُؤۡمِنِینَ ﴿8﴾

Pakati pa anthu alipo (anthu achinyengo) amene akunena: “Takhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro,” pomwe iwo sali okhulupirira.

یُخَـٰدِعُونَ ٱللَّهَ وَٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ وَمَا یَخۡدَعُونَ إِلَّاۤ أَنفُسَهُمۡ وَمَا یَشۡعُرُونَ ﴿9﴾

Akufuna kunyenga Allah ndi amene akhulupirira, ndipo sanyenga aliyense koma okha, ndipo iwo sazindikira (kuti akudzinyenga okha).

فِی قُلُوبِهِم مَّرَضࣱ فَزَادَهُمُ ٱللَّهُ مَرَضࣰاۖ وَلَهُمۡ عَذَابٌ أَلِیمُۢ بِمَا كَانُوا۟ یَكۡذِبُونَ ﴿10﴾

M’mitima mwawo muli matenda; ndipo Allah wawaonjezera matenda. Choncho iwo adzalandira chilango chopweteka chifukwa cha bodza lawo.

وَإِذَا قِیلَ لَهُمۡ لَا تُفۡسِدُوا۟ فِی ٱلۡأَرۡضِ قَالُوۤا۟ إِنَّمَا نَحۡنُ مُصۡلِحُونَ ﴿11﴾

Ndipo akauzidwa kuti: “Musaononge padziko,” amayankha kuti: “Ife ndife okonza.”

أَلَاۤ إِنَّهُمۡ هُمُ ٱلۡمُفۡسِدُونَ وَلَـٰكِن لَّا یَشۡعُرُونَ ﴿12﴾

Dziwani kuti, ndithudi, iwo ndiwo ali oononga (pa dziko); koma sakuzindikira.

وَإِذَا قِیلَ لَهُمۡ ءَامِنُوا۟ كَمَاۤ ءَامَنَ ٱلنَّاسُ قَالُوۤا۟ أَنُؤۡمِنُ كَمَاۤ ءَامَنَ ٱلسُّفَهَاۤءُۗ أَلَاۤ إِنَّهُمۡ هُمُ ٱلسُّفَهَاۤءُ وَلَـٰكِن لَّا یَعۡلَمُونَ ﴿13﴾

Ndipo akauzidwa kuti, “Khulupirirani monga momwe anthu ena akhulupirira,” amayankha kuti: “Kodi tikhulupirire monga momwe zakhulupirira zitsiru?” Dziwani kuti, ndithudi, iwo ndi omwe ali zitsiru, koma sakudziwa.

وَإِذَا لَقُوا۟ ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ قَالُوۤا۟ ءَامَنَّا وَإِذَا خَلَوۡا۟ إِلَىٰ شَیَـٰطِینِهِمۡ قَالُوۤا۟ إِنَّا مَعَكُمۡ إِنَّمَا نَحۡنُ مُسۡتَهۡزِءُونَ ﴿14﴾

Ndipo akakumana ndi amene akhulupirira, amanena: “Takhulupirira.” Koma akakhala pa okha ndi asatana awo, amati: “Ndithudi ife tili pamodzi nanu. Timangowachita chipongwe basi.”

ٱللَّهُ یَسۡتَهۡزِئُ بِهِمۡ وَیَمُدُّهُمۡ فِی طُغۡیَـٰنِهِمۡ یَعۡمَهُونَ ﴿15﴾

Allah adzawalipira chipongwe chawocho, ndipo akuwalekelera akungoyumbayumba (kugwira njakata) m’kusokera kwawo.

أُو۟لَـٰۤىِٕكَ ٱلَّذِینَ ٱشۡتَرَوُا۟ ٱلضَّلَـٰلَةَ بِٱلۡهُدَىٰ فَمَا رَبِحَت تِّجَـٰرَتُهُمۡ وَمَا كَانُوا۟ مُهۡتَدِینَ ﴿16﴾

Oterewo ndiomwe asinthanitsa chiongoko ndi kusokera, koma malonda awo sadawapindulire chilichonse, tero sadali oongoka.

مَثَلُهُمۡ كَمَثَلِ ٱلَّذِی ٱسۡتَوۡقَدَ نَارࣰا فَلَمَّاۤ أَضَاۤءَتۡ مَا حَوۡلَهُۥ ذَهَبَ ٱللَّهُ بِنُورِهِمۡ وَتَرَكَهُمۡ فِی ظُلُمَـٰتࣲ لَّا یُبۡصِرُونَ ﴿17﴾

Fanizo lawo lili ngati (munthu wa paulendo wafungatiridwa ndi mdima) yemwe wayatsa moto; ndipo pamene udaunika zomwe zidali m’mphepete mwake, Allah nkuwachotsera kuunika kwawoko nawasiya mu mdima osatha kuona.

صُمُّۢ بُكۡمٌ عُمۡیࣱ فَهُمۡ لَا یَرۡجِعُونَ ﴿18﴾

(Nakhala ngati) agonthi, abubu, akhungu; ndipo sangabwelerenso (ku chiwongoko).

أَوۡ كَصَیِّبࣲ مِّنَ ٱلسَّمَاۤءِ فِیهِ ظُلُمَـٰتࣱ وَرَعۡدࣱ وَبَرۡقࣱ یَجۡعَلُونَ أَصَـٰبِعَهُمۡ فِیۤ ءَاذَانِهِم مِّنَ ٱلصَّوَ ٰ⁠عِقِ حَذَرَ ٱلۡمَوۡتِۚ وَٱللَّهُ مُحِیطُۢ بِٱلۡكَـٰفِرِینَ ﴿19﴾

Kapena (fanizo lawonso) lili ngati chimvula chochokera ku mitambo m’kati mwake muukhala mdima, mphenzi ndi kung’anima, naika zala zawo m’makutu mwawo chifukwa chamkokomo ndikuopa imfa (pomwe kutero sikungawathandize chilichonse). Ndipo Allah akudziwa bwinobwino za osakhulupirira.

یَكَادُ ٱلۡبَرۡقُ یَخۡطَفُ أَبۡصَـٰرَهُمۡۖ كُلَّمَاۤ أَضَاۤءَ لَهُم مَّشَوۡا۟ فِیهِ وَإِذَاۤ أَظۡلَمَ عَلَیۡهِمۡ قَامُوا۟ۚ وَلَوۡ شَاۤءَ ٱللَّهُ لَذَهَبَ بِسَمۡعِهِمۡ وَأَبۡصَـٰرِهِمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَیۡءࣲ قَدِیرࣱ ﴿20﴾

Kung’anima kukuyandikira kutsomphola maso awo; nthawi iliyonse kukawaunikira, nkuyenda m’menemo (mkuunikamo). Koma kukawachitira mdima, nkuyima. ndipo Allah akadafuna akadawachotsera kumva kwawo ndi kuona kwawo. Ndithudi, Allah Ngokhoza chilichonse.

یَـٰۤأَیُّهَا ٱلنَّاسُ ٱعۡبُدُوا۟ رَبَّكُمُ ٱلَّذِی خَلَقَكُمۡ وَٱلَّذِینَ مِن قَبۡلِكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تَتَّقُونَ ﴿21﴾

E inu anthu! pembedzani Mbuye wanu Yemwe adakulengani inu ndi omwe adalipo kale, kuti mukhale oopa (Allah).

ٱلَّذِی جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ فِرَ ٰ⁠شࣰا وَٱلسَّمَاۤءَ بِنَاۤءࣰ وَأَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَاۤءِ مَاۤءࣰ فَأَخۡرَجَ بِهِۦ مِنَ ٱلثَّمَرَ ٰ⁠تِ رِزۡقࣰا لَّكُمۡۖ فَلَا تَجۡعَلُوا۟ لِلَّهِ أَندَادࣰا وَأَنتُمۡ تَعۡلَمُونَ ﴿22﴾

(Allah) Yemwe adakupangirani nthaka kukhala ngati mphasa, ndi thambo kukhala ngati denga; ndipo adatsitsa madzi kuchokera ku mitambo natulutsa ndi madziwo zipatso zosiyanasiyana kuti zikhale chakudya chanu. Choncho Allah musampangire anzake uku inu mukudziwa (kuti alibe wothandizana naye).

وَإِن كُنتُمۡ فِی رَیۡبࣲ مِّمَّا نَزَّلۡنَا عَلَىٰ عَبۡدِنَا فَأۡتُوا۟ بِسُورَةࣲ مِّن مِّثۡلِهِۦ وَٱدۡعُوا۟ شُهَدَاۤءَكُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ إِن كُنتُمۡ صَـٰدِقِینَ ﴿23﴾

Ndipo ngati muli m’chikaiko ndi zomwe tamvumbulutsira kapolo wathu (kuti sizinachokere kwa Ife,) tabweretsani sura imodzi yolingana ndi Quraniyi (m’kayankhulidwe ka nzeru ndi kayalidwe ka malamulo ake). Ndipo itanani athandizi anu (kuti akuthandizeni) osakhala Allah; ngati inu mukunena zoona (kuti Qur’an njopekedwa).

فَإِن لَّمۡ تَفۡعَلُوا۟ وَلَن تَفۡعَلُوا۟ فَٱتَّقُوا۟ ٱلنَّارَ ٱلَّتِی وَقُودُهَا ٱلنَّاسُ وَٱلۡحِجَارَةُۖ أُعِدَّتۡ لِلۡكَـٰفِرِینَ ﴿24﴾

Choncho ngati simutha (kubweretsa sura imodzi yonga ya m’Qurani) ndiye kuti simudzatha. Choncho opani Moto omwe nkhuni zake ndi anthu ndi miyala umene wakonzedwera kwa osakhulupirira.

وَبَشِّرِ ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ وَعَمِلُوا۟ ٱلصَّـٰلِحَـٰتِ أَنَّ لَهُمۡ جَنَّـٰتࣲ تَجۡرِی مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَـٰرُۖ كُلَّمَا رُزِقُوا۟ مِنۡهَا مِن ثَمَرَةࣲ رِّزۡقࣰا قَالُوا۟ هَـٰذَا ٱلَّذِی رُزِقۡنَا مِن قَبۡلُۖ وَأُتُوا۟ بِهِۦ مُتَشَـٰبِهࣰاۖ وَلَهُمۡ فِیهَاۤ أَزۡوَ ٰ⁠جࣱ مُّطَهَّرَةࣱۖ وَهُمۡ فِیهَا خَـٰلِدُونَ ﴿25﴾

Ndipo auze nkhani yabwino amene akhulupirira nachita ntchito zabwino (molungama) kuti ndithu adzalandira minda ya mtendere momwe mitsinje ikuyenda pansi pake (ndi patsogolo pake). Nthawi iliyonse kumeneko akapatsidwa zipatso ngati chakudya, adzakhala akunena: “Izi ndizomwe tidapatsidwa kale,” (chifukwa chakuti) adzapatsidwa zipatso zofanana (m’maonekedwe ake ndi zimene adapatsidwapo kale. Koma makomedwe ake ngosiyana). Ndiponso akalandira m’menemo akazi oyeretsedwa (kuuve wamtundu uliwonse); ndipo iwo adzakhala m’menemo nthawi yaitali.

۞ إِنَّ ٱللَّهَ لَا یَسۡتَحۡیِۦۤ أَن یَضۡرِبَ مَثَلࣰا مَّا بَعُوضَةࣰ فَمَا فَوۡقَهَاۚ فَأَمَّا ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ فَیَعۡلَمُونَ أَنَّهُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّهِمۡۖ وَأَمَّا ٱلَّذِینَ كَفَرُوا۟ فَیَقُولُونَ مَاذَاۤ أَرَادَ ٱللَّهُ بِهَـٰذَا مَثَلࣰاۘ یُضِلُّ بِهِۦ كَثِیرࣰا وَیَهۡدِی بِهِۦ كَثِیرࣰاۚ وَمَا یُضِلُّ بِهِۦۤ إِلَّا ٱلۡفَـٰسِقِینَ ﴿26﴾

Ndithu Allah sachita manyazi kupereka fanizo la udzudzu ndi choposerapo (pa udzudzuwo). Koma amene akhulupirira akuzindikira kuti (fanizolo) ndiloona ndi lochokera kwa Mbuye wawo. Koma amene sadakhulupirire, akunena: “Kodi Allah akufunanji pa fanizo lotereli?” (Allah) amawalekelera ambiri kusokera ndi fanizo lotere, komanso amawaongola ambiri ndi fanizonso lotere. Komatu sawalekelera kusokera nalo kupatula okhawo opandukira chilamulo (Chake).

ٱلَّذِینَ یَنقُضُونَ عَهۡدَ ٱللَّهِ مِنۢ بَعۡدِ مِیثَـٰقِهِۦ وَیَقۡطَعُونَ مَاۤ أَمَرَ ٱللَّهُ بِهِۦۤ أَن یُوصَلَ وَیُفۡسِدُونَ فِی ٱلۡأَرۡضِۚ أُو۟لَـٰۤىِٕكَ هُمُ ٱلۡخَـٰسِرُونَ ﴿27﴾

Omwe akuswa chipangano cha Allah pambuyo pochimanga (kuti adzachikwaniritsa; ndi kutsatira malamulo a Allah), ndiponso amadula (chibale) chomwe Allah adalamula kuti chilumikizidwe, naononga pa dziko (poyambitsa nkhondo ndi ziwawa); iwo ndiamene ali otayika.

كَیۡفَ تَكۡفُرُونَ بِٱللَّهِ وَكُنتُمۡ أَمۡوَ ٰ⁠تࣰا فَأَحۡیَـٰكُمۡۖ ثُمَّ یُمِیتُكُمۡ ثُمَّ یُحۡیِیكُمۡ ثُمَّ إِلَیۡهِ تُرۡجَعُونَ ﴿28﴾

Kodi mungamkane chotani Allah chikhalirecho inu mudali akufa ndipo adakupatsani moyo (nakuikani pa dziko lapansi)? Kenako adzakupatsani imfa (ikakwana nthawi yanu yofera). Kenako adzakuukitsani (ndikukutulutsani m’manda). Ndipo kenako mudzabwezedwa kwa Iye (kuti mukaweruzidwe pa zomwe mudali kuchita).

هُوَ ٱلَّذِی خَلَقَ لَكُم مَّا فِی ٱلۡأَرۡضِ جَمِیعࣰا ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰۤ إِلَى ٱلسَّمَاۤءِ فَسَوَّىٰهُنَّ سَبۡعَ سَمَـٰوَ ٰ⁠تࣲۚ وَهُوَ بِكُلِّ شَیۡءٍ عَلِیمࣱ ﴿29﴾

Iye ndi Yemwe adakulengerani zonse za m’dziko lapansi, kenako adalunjika ku thambo nakonza thambo zisanu ndi ziwiri. Iye Ngodziwa chinthu chilichonse.[2]

وَإِذۡ قَالَ رَبُّكَ لِلۡمَلَـٰۤىِٕكَةِ إِنِّی جَاعِلࣱ فِی ٱلۡأَرۡضِ خَلِیفَةࣰۖ قَالُوۤا۟ أَتَجۡعَلُ فِیهَا مَن یُفۡسِدُ فِیهَا وَیَسۡفِكُ ٱلدِّمَاۤءَ وَنَحۡنُ نُسَبِّحُ بِحَمۡدِكَ وَنُقَدِّسُ لَكَۖ قَالَ إِنِّیۤ أَعۡلَمُ مَا لَا تَعۡلَمُونَ ﴿30﴾

Akumbutse (anthu ako nkhani iyi) panthawi yomwe Mbuye wako anati kwa Angelo: “Ine ndikufuna kuika m’dziko lapansi wondiimilira.” (Angelo) adati: “Kodi muika m’menemo amene azidzaonongamo ndi kukhetsa mwazi, pomwe ife tikukulemekezani ndi kukutamandani mokuyeretsani?” (Allah) adati: “Ndithudi, Ine ndikudziwa zimene simukuzidziwa.”

وَعَلَّمَ ءَادَمَ ٱلۡأَسۡمَاۤءَ كُلَّهَا ثُمَّ عَرَضَهُمۡ عَلَى ٱلۡمَلَـٰۤىِٕكَةِ فَقَالَ أَنۢبِـُٔونِی بِأَسۡمَاۤءِ هَـٰۤؤُلَاۤءِ إِن كُنتُمۡ صَـٰدِقِینَ ﴿31﴾

Ndipo (Allah) adaphunzitsa Adam mayina a (zinthu) zonse; nazibweretsa (zinthuzo) pamaso pa Angelo, naati (kwa Angelo): “Ndiuzeni mayina a zinthu izi ngati mukunena zoona (kuti inu ndinu ozindikira zinthu).”

قَالُوا۟ سُبۡحَـٰنَكَ لَا عِلۡمَ لَنَاۤ إِلَّا مَا عَلَّمۡتَنَاۤۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡعَلِیمُ ٱلۡحَكِیمُ ﴿32﴾

(Angelo) adati: “Kuyeretsedwa Nkwanu! Ife tilibe kuzindikira kupatula chimene mwatiphunzitsa. Ndithudi, Inu Ngodziwa kwambiri, Anzeru zakuya.”

قَالَ یَـٰۤـَٔادَمُ أَنۢبِئۡهُم بِأَسۡمَاۤىِٕهِمۡۖ فَلَمَّاۤ أَنۢبَأَهُم بِأَسۡمَاۤىِٕهِمۡ قَالَ أَلَمۡ أَقُل لَّكُمۡ إِنِّیۤ أَعۡلَمُ غَیۡبَ ٱلسَّمَـٰوَ ٰ⁠تِ وَٱلۡأَرۡضِ وَأَعۡلَمُ مَا تُبۡدُونَ وَمَا كُنتُمۡ تَكۡتُمُونَ ﴿33﴾

(Allah) adanena: “E iwe Adam!: Auze mayina ake (azinthuzo).” Ndipo pamene adawauza mayina ake, (Iye) adati: “Kodi Sindinakuuzeni kuti Ine ndikudziwa zobisika zakumwamba ndi pansi, ndiponso ndikudziwa zimene mukuonetsera poyera ndi zimene mukubisa?”

وَإِذۡ قُلۡنَا لِلۡمَلَـٰۤىِٕكَةِ ٱسۡجُدُوا۟ لِـَٔادَمَ فَسَجَدُوۤا۟ إِلَّاۤ إِبۡلِیسَ أَبَىٰ وَٱسۡتَكۡبَرَ وَكَانَ مِنَ ٱلۡكَـٰفِرِینَ ﴿34﴾

Ndipo (akumbutse anthu ako nkhani iyi) parnene tidawauza Angelo: “Mgwadireni Adam.” Onse adamugwadira kupatula Iblisi (Satana); anakana nadzitukumula. Tero adali m’modzi mwa osakhulupirira.

وَقُلۡنَا یَـٰۤـَٔادَمُ ٱسۡكُنۡ أَنتَ وَزَوۡجُكَ ٱلۡجَنَّةَ وَكُلَا مِنۡهَا رَغَدًا حَیۡثُ شِئۡتُمَا وَلَا تَقۡرَبَا هَـٰذِهِ ٱلشَّجَرَةَ فَتَكُونَا مِنَ ٱلظَّـٰلِمِینَ ﴿35﴾

Ndipo tidati: “E iwe Adam! Khala iwe ndi mkazi wako m’mundamo (mu Edeni); idyani m’menemo motakasuka paliponse pamene mwafuna; koma musauyandikire Mtengo uwu kuopera kuti mungakhale mwa odzichitira okha zoipa.”

فَأَزَلَّهُمَا ٱلشَّیۡطَـٰنُ عَنۡهَا فَأَخۡرَجَهُمَا مِمَّا كَانَا فِیهِۖ وَقُلۡنَا ٱهۡبِطُوا۟ بَعۡضُكُمۡ لِبَعۡضٍ عَدُوࣱّۖ وَلَكُمۡ فِی ٱلۡأَرۡضِ مُسۡتَقَرࣱّ وَمَتَـٰعٌ إِلَىٰ حِینࣲ ﴿36﴾

Koma Satana (Iblisi yemwe uja) adawalakwitsa onse awiriwo (nanyoza lamulo la Allah ndikudya mtengo woletsedwawo), nawatulutsa (mu Mtendere) momwe adaalimo. Ndipo tidawauza: “Tsikani (mukakhale pa dziko lapansi) pakati panu pali chidani. Tsopano pokhala panu ndi pa dziko lapansi, ndipo mukapeza chisangalalo pamenepo kwakanthawi.”

فَتَلَقَّىٰۤ ءَادَمُ مِن رَّبِّهِۦ كَلِمَـٰتࣲ فَتَابَ عَلَیۡهِۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلتَّوَّابُ ٱلرَّحِیمُ ﴿37﴾

Ndipo Adam adalandira mawu kuchokera kwa Mbuye wake, (napempha chikhululuko cha Allah kupyolera m’mawuwo), ndipo (Mbuye wake) adavomera kulapa kwake. Ndithudi, Iyeyo Ngolandira kwambiri kulapa, Wachisoni chosatha.

قُلۡنَا ٱهۡبِطُوا۟ مِنۡهَا جَمِیعࣰاۖ فَإِمَّا یَأۡتِیَنَّكُم مِّنِّی هُدࣰى فَمَن تَبِعَ هُدَایَ فَلَا خَوۡفٌ عَلَیۡهِمۡ وَلَا هُمۡ یَحۡزَنُونَ ﴿38﴾

Tidati: “Tsikani m’menemo nonsenu. Ngati chitakufikani chiongoko chochokera kwa Ine, choncho amene adzatsate chiongoko Changacho, pa iwo sipadzakhala mantha. Ndiponso iwo sadzadandaula.”

وَٱلَّذِینَ كَفَرُوا۟ وَكَذَّبُوا۟ بِـَٔایَـٰتِنَاۤ أُو۟لَـٰۤىِٕكَ أَصۡحَـٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِیهَا خَـٰلِدُونَ ﴿39﴾

“Koma amene sanakhulupirire natsutsa mawu athu, iwowo ndiwo anthu a ku Moto. M’menemo akakhalamo nthawi yaitali.”

یَـٰبَنِیۤ إِسۡرَ ٰ⁠ۤءِیلَ ٱذۡكُرُوا۟ نِعۡمَتِیَ ٱلَّتِیۤ أَنۡعَمۡتُ عَلَیۡكُمۡ وَأَوۡفُوا۟ بِعَهۡدِیۤ أُوفِ بِعَهۡدِكُمۡ وَإِیَّـٰیَ فَٱرۡهَبُونِ ﴿40﴾

E inu ana a Israyeli! kumbukirani chisomo Changa chomwe ndidakudalitsani nacho, ndipo kwaniritsani pangano Langa Nanenso ndikwaniritsi pangano lanu. Ndipo Ine Ndekha ndiopeni.

وَءَامِنُوا۟ بِمَاۤ أَنزَلۡتُ مُصَدِّقࣰا لِّمَا مَعَكُمۡ وَلَا تَكُونُوۤا۟ أَوَّلَ كَافِرِۭ بِهِۦۖ وَلَا تَشۡتَرُوا۟ بِـَٔایَـٰتِی ثَمَنࣰا قَلِیلࣰا وَإِیَّـٰیَ فَٱتَّقُونِ ﴿41﴾

Ndipo khulupirirani zimene ndavumbulutsa, zomwe zikuchitira umboni zimene muli nazo, ndipo musakhale oyamba kuzikana; ndipo musagulitse mawu Anga ndi (zinthu za) mtengo wochepa. Ndipo Ine Ndekha ndiopeni.

وَلَا تَلۡبِسُوا۟ ٱلۡحَقَّ بِٱلۡبَـٰطِلِ وَتَكۡتُمُوا۟ ٱلۡحَقَّ وَأَنتُمۡ تَعۡلَمُونَ ﴿42﴾

Ndipo musasakanize choona ndi chonama; ndi kubisa choona uku mukudziwa.

وَأَقِیمُوا۟ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُوا۟ ٱلزَّكَوٰةَ وَٱرۡكَعُوا۟ مَعَ ٱلرَّ ٰ⁠كِعِینَ ﴿43﴾

Ndipo pempherani Swala moyenera ndikupereka chopereka (Zakaat), ndipo weramani pamodzi ndi owerama.

۞ أَتَأۡمُرُونَ ٱلنَّاسَ بِٱلۡبِرِّ وَتَنسَوۡنَ أَنفُسَكُمۡ وَأَنتُمۡ تَتۡلُونَ ٱلۡكِتَـٰبَۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ ﴿44﴾

Kodi mukulamula anthu kuchita zabwino ndi kudziiwala inu eni pomwe inu mukuwerenga Buku? Kodi simuzindikira?

وَٱسۡتَعِینُوا۟ بِٱلصَّبۡرِ وَٱلصَّلَوٰةِۚ وَإِنَّهَا لَكَبِیرَةٌ إِلَّا عَلَى ٱلۡخَـٰشِعِینَ ﴿45﴾

Ndipo dzithandizeni (pa zinthu zanu) popirira ndi popemphera Swala. Ndithudi, Swala yo ndiyolemera kupatula kwa odzichepetsa (kwa Allah).

ٱلَّذِینَ یَظُنُّونَ أَنَّهُم مُّلَـٰقُوا۟ رَبِّهِمۡ وَأَنَّهُمۡ إِلَیۡهِ رَ ٰ⁠جِعُونَ ﴿46﴾

Omwe akutsimikiza kuti adzakumana ndi Mbuye wawo, ndi kuti adzabwerera kwa Iye.

یَـٰبَنِیۤ إِسۡرَ ٰ⁠ۤءِیلَ ٱذۡكُرُوا۟ نِعۡمَتِیَ ٱلَّتِیۤ أَنۡعَمۡتُ عَلَیۡكُمۡ وَأَنِّی فَضَّلۡتُكُمۡ عَلَى ٱلۡعَـٰلَمِینَ ﴿47﴾

E inu ana a Israyeli! Kumbukirani chisomo Changa chomwe ndidakudalitsani nacho. Ndithudi, Ine ndinakuchitirani ubwino kuposa zolengedwa zonse (pa nthawiyo).

وَٱتَّقُوا۟ یَوۡمࣰا لَّا تَجۡزِی نَفۡسٌ عَن نَّفۡسࣲ شَیۡـࣰٔا وَلَا یُقۡبَلُ مِنۡهَا شَفَـٰعَةࣱ وَلَا یُؤۡخَذُ مِنۡهَا عَدۡلࣱ وَلَا هُمۡ یُنصَرُونَ ﴿48﴾

Choncho opani tsiku lomwe munthu aliyense sadzathandiza mnzake ndi chilichonse, ndipo sikudzavomerezedwa kwa iye (munthuyo) dandaulo lililonse, ndiponso silidzalandiridwa dipo kwa iye; ndipo iwo sadzapulumutsidwa.

وَإِذۡ نَجَّیۡنَـٰكُم مِّنۡ ءَالِ فِرۡعَوۡنَ یَسُومُونَكُمۡ سُوۤءَ ٱلۡعَذَابِ یُذَبِّحُونَ أَبۡنَاۤءَكُمۡ وَیَسۡتَحۡیُونَ نِسَاۤءَكُمۡۚ وَفِی ذَ ٰ⁠لِكُم بَلَاۤءࣱ مِّن رَّبِّكُمۡ عَظِیمࣱ ﴿49﴾

Ndipo (kumbukirani) pamene tidakupulumutsani kwa anthu a Farawo, omwe amakuzunzani ndi chilango choipa; adali kuzinga (kupha) ana anu achimuna ndikuwasiya moyo achikazi. Ndipo m’zimenezo mudali mayeso aakulu ochokera kwa Mbuye wanu.

وَإِذۡ فَرَقۡنَا بِكُمُ ٱلۡبَحۡرَ فَأَنجَیۡنَـٰكُمۡ وَأَغۡرَقۡنَاۤ ءَالَ فِرۡعَوۡنَ وَأَنتُمۡ تَنظُرُونَ ﴿50﴾

Ndipo (kumbukiraninso) pamene tidailekanitsa nyanja chifukwa cha inu (kuti muoloke pa mchenga wouma), potero tidakupulumutsani ndi kuwamiza anthu a Farawo (pamodzi ndi iye mwini) uku inu mukuona; (chomwe chidali chizizwa choonekera).

وَإِذۡ وَ ٰ⁠عَدۡنَا مُوسَىٰۤ أَرۡبَعِینَ لَیۡلَةࣰ ثُمَّ ٱتَّخَذۡتُمُ ٱلۡعِجۡلَ مِنۢ بَعۡدِهِۦ وَأَنتُمۡ ظَـٰلِمُونَ ﴿51﴾

(Kumbukiraninso) pamene tidamulonjeza Mûsa masiku makumi anayi (kuti tidzampatsa buku la Taurat patapita masiku makumi anayi pambuyo pa kupulumuka kwanu ndi kuonongeka kwa Farawo); kenako inu mudapembedza thole (mwana wa ng’ombe) pambuyo pake, (iye kulibe, atapita ku chipangano cha Mbuye wake). Ndipo inu muli ochita zoipa.

ثُمَّ عَفَوۡنَا عَنكُم مِّنۢ بَعۡدِ ذَ ٰ⁠لِكَ لَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ ﴿52﴾

Kenako tidakukhululukirani pambuyo pa zimenezo, kuti muthokoze (mtendere wa Allah).

وَإِذۡ ءَاتَیۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَـٰبَ وَٱلۡفُرۡقَانَ لَعَلَّكُمۡ تَهۡتَدُونَ ﴿53﴾

Ndipo (kumbukiraninso) pamene Mûsa tidampatsa buku lolekanitsa choonadi ndi chonama kuti inu muongoke (polilingalira ndi kutsatira malamulo ake).

وَإِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِۦ یَـٰقَوۡمِ إِنَّكُمۡ ظَلَمۡتُمۡ أَنفُسَكُم بِٱتِّخَاذِكُمُ ٱلۡعِجۡلَ فَتُوبُوۤا۟ إِلَىٰ بَارِىِٕكُمۡ فَٱقۡتُلُوۤا۟ أَنفُسَكُمۡ ذَ ٰ⁠لِكُمۡ خَیۡرࣱ لَّكُمۡ عِندَ بَارِىِٕكُمۡ فَتَابَ عَلَیۡكُمۡۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلتَّوَّابُ ٱلرَّحِیمُ ﴿54﴾

Ndipo (kumbukiraninso) pamene Mûsa adanena kwa anthu ake kuti “E inu anthu anga! Ndithudi, inu mwadzichitira nokha zoipa pompembedza thole (mwana wa ng’ombe). Choncho lapani kwa Mlengi wanu, ndipo iphanani nokha (amene ali abwino aphe oipa). Kutero ndi bwino kwa inu pamaso pa Mlengi wanu.” Choncho (Allah) wavomera kulapa kwanu. Ndithudi, Iye Ngovomera kulapa mochuluka, Wachisoni chosatha.

وَإِذۡ قُلۡتُمۡ یَـٰمُوسَىٰ لَن نُّؤۡمِنَ لَكَ حَتَّىٰ نَرَى ٱللَّهَ جَهۡرَةࣰ فَأَخَذَتۡكُمُ ٱلصَّـٰعِقَةُ وَأَنتُمۡ تَنظُرُونَ ﴿55﴾

Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene Mudati: “E iwe Mûsa!; Sitingakukhulupirire iwe mpaka timuone Allah masomphenya.” Ndipo nkokomo wa moto udakugwirani uku inu mukuona.

ثُمَّ بَعَثۡنَـٰكُم مِّنۢ بَعۡدِ مَوۡتِكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ ﴿56﴾

Kenako tidakuukitsani ku imfa pambuyo pakufa kwanu, kuti muyamike.

وَظَلَّلۡنَا عَلَیۡكُمُ ٱلۡغَمَامَ وَأَنزَلۡنَا عَلَیۡكُمُ ٱلۡمَنَّ وَٱلسَّلۡوَىٰۖ كُلُوا۟ مِن طَیِّبَـٰتِ مَا رَزَقۡنَـٰكُمۡۚ وَمَا ظَلَمُونَا وَلَـٰكِن كَانُوۤا۟ أَنفُسَهُمۡ یَظۡلِمُونَ ﴿57﴾

Ndipo tidakuphimbani ndi mthunzi wa mitambo (pamene mudali kuoloka chipululu cha mchenga), ndipo tidakutsitsirani Mana (zakumwa zotsekemera ngati uchi) ndi Salwa (zinziri), ndi kukuuzani: “Idyani zinthu zabwino izi zimene takupatsani.” Komatu sadatichitire Ife choipa koma adali kudzichitira okha zoipa.

وَإِذۡ قُلۡنَا ٱدۡخُلُوا۟ هَـٰذِهِ ٱلۡقَرۡیَةَ فَكُلُوا۟ مِنۡهَا حَیۡثُ شِئۡتُمۡ رَغَدࣰا وَٱدۡخُلُوا۟ ٱلۡبَابَ سُجَّدࣰا وَقُولُوا۟ حِطَّةࣱ نَّغۡفِرۡ لَكُمۡ خَطَـٰیَـٰكُمۡۚ وَسَنَزِیدُ ٱلۡمُحۡسِنِینَ ﴿58﴾

Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene tidati: “Lowani m’mudzi uwu, ndikudya m’menemo motakasuka paliponse pamene mwafuna; ndipo lowerani pachipata chake uku mutawerama (kusonyeza kuthokoza Allah) ndipo nenani: “E Mbuye wathu! Tikhululukireni machimo athu.” “Tikukhululukirani machimo anu ndipo tiwaonjezera (mphoto yaikulu) ochita zabwino.”

فَبَدَّلَ ٱلَّذِینَ ظَلَمُوا۟ قَوۡلًا غَیۡرَ ٱلَّذِی قِیلَ لَهُمۡ فَأَنزَلۡنَا عَلَى ٱلَّذِینَ ظَلَمُوا۟ رِجۡزࣰا مِّنَ ٱلسَّمَاۤءِ بِمَا كَانُوا۟ یَفۡسُقُونَ ﴿59﴾

Koma anthu oipa adasintha (lamulo la Allah, nanena) mawu ena osati amene adawuzidwa. Tero, anthu oipawo tidawatsitsira mliri wochokera kumwamba, chifukwa chakutuluka kwawo m’chilamulo cha Allah.

۞ وَإِذِ ٱسۡتَسۡقَىٰ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِۦ فَقُلۡنَا ٱضۡرِب بِّعَصَاكَ ٱلۡحَجَرَۖ فَٱنفَجَرَتۡ مِنۡهُ ٱثۡنَتَا عَشۡرَةَ عَیۡنࣰاۖ قَدۡ عَلِمَ كُلُّ أُنَاسࣲ مَّشۡرَبَهُمۡۖ كُلُوا۟ وَٱشۡرَبُوا۟ مِن رِّزۡقِ ٱللَّهِ وَلَا تَعۡثَوۡا۟ فِی ٱلۡأَرۡضِ مُفۡسِدِینَ ﴿60﴾

Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene Mûsa adapemphera anthu ake madzi kwa Allah (atagwidwa ndi ludzu loopsa m’chipululu), tidati: “Menya mwala ndi ndodo yakoyo.” (Atamenya), anatulukadi m’menemo akasupe khumi ndi awiri. Potero fuko lililonse lidadziwa malo awo omwera. (Izi zidachitika kuti asakangane). Choncho idyani, ndiponso imwani mu zopatsa za Allah (popanda inu kuzivutikira), ndipo musasimbwe pa dziko uku mukuononga.

وَإِذۡ قُلۡتُمۡ یَـٰمُوسَىٰ لَن نَّصۡبِرَ عَلَىٰ طَعَامࣲ وَ ٰ⁠حِدࣲ فَٱدۡعُ لَنَا رَبَّكَ یُخۡرِجۡ لَنَا مِمَّا تُنۢبِتُ ٱلۡأَرۡضُ مِنۢ بَقۡلِهَا وَقِثَّاۤىِٕهَا وَفُومِهَا وَعَدَسِهَا وَبَصَلِهَاۖ قَالَ أَتَسۡتَبۡدِلُونَ ٱلَّذِی هُوَ أَدۡنَىٰ بِٱلَّذِی هُوَ خَیۡرٌۚ ٱهۡبِطُوا۟ مِصۡرࣰا فَإِنَّ لَكُم مَّا سَأَلۡتُمۡۗ وَضُرِبَتۡ عَلَیۡهِمُ ٱلذِّلَّةُ وَٱلۡمَسۡكَنَةُ وَبَاۤءُو بِغَضَبࣲ مِّنَ ٱللَّهِۗ ذَ ٰ⁠لِكَ بِأَنَّهُمۡ كَانُوا۟ یَكۡفُرُونَ بِـَٔایَـٰتِ ٱللَّهِ وَیَقۡتُلُونَ ٱلنَّبِیِّـۧنَ بِغَیۡرِ ٱلۡحَقِّۗ ذَ ٰ⁠لِكَ بِمَا عَصَوا۟ وَّكَانُوا۟ یَعۡتَدُونَ ﴿61﴾

Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene mudati: “E iwe Mûsa! Sitingathe kupirira ndi chakudya chamtundu umodzi (chomwe ndi Mana ndi Salwa); choncho tipemphere kwa Mbuye wako kuti atitulutsire (atipatse) ife zimene nthaka imameretsa, monga masamba, nkhaka, adyo, nyemba za mtundu wa chana ndi anyezi.” Iye adati: “Kodi mukufuna kusinthitsa chonyozeka ndi chabwino? Pitani m’midzi, ndipo kumeneko mukapeza zimene mwapemphazi.” Potero adapatsidwa kunyozeka ndi kusauka; nabwerera ndi mkwiyo wa Allah. Zimenezo n’chifukwa chakuti iwo sadali okhulupirira zisonyezo za Allah, ndikuti adali kupha aneneri a Allah popanda chifukwa. Zidali tero chifukwa cha kunyoza kwawo, ndipo adali olumpha malire.

إِنَّ ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ وَٱلَّذِینَ هَادُوا۟ وَٱلنَّصَـٰرَىٰ وَٱلصَّـٰبِـِٔینَ مَنۡ ءَامَنَ بِٱللَّهِ وَٱلۡیَوۡمِ ٱلۡـَٔاخِرِ وَعَمِلَ صَـٰلِحࣰا فَلَهُمۡ أَجۡرُهُمۡ عِندَ رَبِّهِمۡ وَلَا خَوۡفٌ عَلَیۡهِمۡ وَلَا هُمۡ یَحۡزَنُونَ ﴿62﴾

Ndithu amene akhulupirira (aneneri akale), ndi Ayuda, ndi Akhirisitu ndi Asabayi[3]; aliyense wa iwo amene akhulupirire Allah (tsopano, monga momwe akunenera Mneneri Muhammad (s.a.w) nakhulupiriranso za tsiku lachimaliziro, uku akuchita ntchito zabwino, akalandira mphoto yawo kwa Mbuye wawo. Pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso sadzadandaula.

وَإِذۡ أَخَذۡنَا مِیثَـٰقَكُمۡ وَرَفَعۡنَا فَوۡقَكُمُ ٱلطُّورَ خُذُوا۟ مَاۤ ءَاتَیۡنَـٰكُم بِقُوَّةࣲ وَٱذۡكُرُوا۟ مَا فِیهِ لَعَلَّكُمۡ تَتَّقُونَ ﴿63﴾

Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi, inu Ayuda) pamene tidalandira chipangano chanu (kuti mudzagwiritsa ntchito zomwe zili m’buku la Taurat), ndipo tidakweza pamwamba panu phiri (la Sinai; tidati kwa inu): “Gwirani mwamphamvu chimene takupatsani, ndipo kumbukirani zili m’menemo (pozigwiritsa ntchito. Ndiponso musazinyozere) kuti mukhale oopa Allah.”

ثُمَّ تَوَلَّیۡتُم مِّنۢ بَعۡدِ ذَ ٰ⁠لِكَۖ فَلَوۡلَا فَضۡلُ ٱللَّهِ عَلَیۡكُمۡ وَرَحۡمَتُهُۥ لَكُنتُم مِّنَ ٱلۡخَـٰسِرِینَ ﴿64﴾

Koma pambuyo pazimenezo mudatembenuka ndikunyoza. Pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo chake pa inu, mukadakhala mwa otayika (oonongeka pa dziko lapansi).

وَلَقَدۡ عَلِمۡتُمُ ٱلَّذِینَ ٱعۡتَدَوۡا۟ مِنكُمۡ فِی ٱلسَّبۡتِ فَقُلۡنَا لَهُمۡ كُونُوا۟ قِرَدَةً خَـٰسِـِٔینَ ﴿65﴾

Ndithudi mudawadziwa (anthu) amene adapyola malire mwa inu pakuswa kupatulika kwa tsiku la Sabata (m’mene tidawalangira chifukwa chosodza nsomba pa tsiku loletsedwa). Ndipo tidati kwa iwo: “Khalani anyani onyozeka.”

فَجَعَلۡنَـٰهَا نَكَـٰلࣰا لِّمَا بَیۡنَ یَدَیۡهَا وَمَا خَلۡفَهَا وَمَوۡعِظَةࣰ لِّلۡمُتَّقِینَ ﴿66﴾

Ndipo tidakuchita kukhala anyaniko, chilango chochenjeza amene adalipo pa nthawiyo ndi akudza pambuyo pawo, ndiponso phunziro kwa oopa Allah.

وَإِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِۦۤ إِنَّ ٱللَّهَ یَأۡمُرُكُمۡ أَن تَذۡبَحُوا۟ بَقَرَةࣰۖ قَالُوۤا۟ أَتَتَّخِذُنَا هُزُوࣰاۖ قَالَ أَعُوذُ بِٱللَّهِ أَنۡ أَكُونَ مِنَ ٱلۡجَـٰهِلِینَ ﴿67﴾

(Kumbukiraninso nkhani iyi, inu Ayuda) pamene Mûsa adauza anthu ake: “Ndithudi, Allah akukulamulani kuti muzinge ng’ombe.” Iwo adati: “Kodi ukutichitira zachipongwe?” Iye adati: “(Sichoncho), ndikudzitchinjiriza ndi Allah kukhala mwa anthu aumbuli.”

قَالُوا۟ ٱدۡعُ لَنَا رَبَّكَ یُبَیِّن لَّنَا مَا هِیَۚ قَالَ إِنَّهُۥ یَقُولُ إِنَّهَا بَقَرَةࣱ لَّا فَارِضࣱ وَلَا بِكۡرٌ عَوَانُۢ بَیۡنَ ذَ ٰ⁠لِكَۖ فَٱفۡعَلُوا۟ مَا تُؤۡمَرُونَ ﴿68﴾

Iwo adati: “Tipemphere kwa Mbuye wako kuti atifotokozere bwino za ng’ombeyo.” Iye adati: “Ndithudi Iye akunena kuti ng’ombeyo simkota kapena mthanthi, koma yapakatikati pa zimenezi. Tero chitani zimene mukulamulidwa.”

قَالُوا۟ ٱدۡعُ لَنَا رَبَّكَ یُبَیِّن لَّنَا مَا لَوۡنُهَاۚ قَالَ إِنَّهُۥ یَقُولُ إِنَّهَا بَقَرَةࣱ صَفۡرَاۤءُ فَاقِعࣱ لَّوۡنُهَا تَسُرُّ ٱلنَّـٰظِرِینَ ﴿69﴾

Iwo adatinso: “Tipemphere kwa Mbuye wako kuti atilongosolere maonekedwe ake.” (Mûsa) adati: “Iye akuti ng’ombeyo ikhale yachikasu kwambiri, yowakondweretsa oiwona.”

قَالُوا۟ ٱدۡعُ لَنَا رَبَّكَ یُبَیِّن لَّنَا مَا هِیَ إِنَّ ٱلۡبَقَرَ تَشَـٰبَهَ عَلَیۡنَا وَإِنَّاۤ إِن شَاۤءَ ٱللَّهُ لَمُهۡتَدُونَ ﴿70﴾

Iwo adatinso: “Tipemphere kwa Mbuye wako kuti atilongosolere mmene kakhalidwe kake kalili. Ndithudi, ng’ombe zimene wafotokozazo n’zofanana kwa ife. Ndipo ndithudi, Allah akafuna tikhala oongoka.”

قَالَ إِنَّهُۥ یَقُولُ إِنَّهَا بَقَرَةࣱ لَّا ذَلُولࣱ تُثِیرُ ٱلۡأَرۡضَ وَلَا تَسۡقِی ٱلۡحَرۡثَ مُسَلَّمَةࣱ لَّا شِیَةَ فِیهَاۚ قَالُوا۟ ٱلۡـَٔـٰنَ جِئۡتَ بِٱلۡحَقِّۚ فَذَبَحُوهَا وَمَا كَادُوا۟ یَفۡعَلُونَ ﴿71﴾

Adati: “Ndithudi Iye akuti, imeneyo ndi n’gombe yosaigwiritsa ntchito yolima m’nthaka, ndiponso yosathilira mbewu; yabwinobwino yopanda banga.” Iwo adati: “Tsopano wabweretsa (mawu a) choonadi.” Choncho adaizinga, koma padatsala pang’ono kuti asachite (lamulolo).

وَإِذۡ قَتَلۡتُمۡ نَفۡسࣰا فَٱدَّ ٰ⁠رَ ٰٔۡ ⁠تُمۡ فِیهَاۖ وَٱللَّهُ مُخۡرِجࣱ مَّا كُنتُمۡ تَكۡتُمُونَ ﴿72﴾

Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene mudapha munthu, kenako mudakangana ndi kukankhirana za munthuyo, (ena ankati uje ndiye wapha, pomwe ena ankati koma uje ndiye wapha). Ndipo Allah atulutsira poyera zimene mudali kubisa.

فَقُلۡنَا ٱضۡرِبُوهُ بِبَعۡضِهَاۚ كَذَ ٰ⁠لِكَ یُحۡیِ ٱللَّهُ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَیُرِیكُمۡ ءَایَـٰتِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ ﴿73﴾

Choncho tidati: “Mmenyeni (wakufayo) ndi gawo la nyamayo. (Potero auka ndikunena za amene adamupha).” Momwemo Allah adzawaukitsa akufa (m’manda monga adamuukitsira wakufayo pamaso panu), ndipo akukusonyezani zizindikiro Zake kuti mukhale ndi nzeru.

ثُمَّ قَسَتۡ قُلُوبُكُم مِّنۢ بَعۡدِ ذَ ٰ⁠لِكَ فَهِیَ كَٱلۡحِجَارَةِ أَوۡ أَشَدُّ قَسۡوَةࣰۚ وَإِنَّ مِنَ ٱلۡحِجَارَةِ لَمَا یَتَفَجَّرُ مِنۡهُ ٱلۡأَنۡهَـٰرُۚ وَإِنَّ مِنۡهَا لَمَا یَشَّقَّقُ فَیَخۡرُجُ مِنۡهُ ٱلۡمَاۤءُۚ وَإِنَّ مِنۡهَا لَمَا یَهۡبِطُ مِنۡ خَشۡیَةِ ٱللَّهِۗ وَمَا ٱللَّهُ بِغَـٰفِلٍ عَمَّا تَعۡمَلُونَ ﴿74﴾

Koma mitima yanu idauma pa mbuyo pa zimenezo; (nkukhala gwa!) ngati mwala kapena kuposerapo. Ndithudi pali miyala ina yomwe ikutuluka mkati mwake mitsinje; ndipo pali ina imene imang’ambika nkutuluka madzi mkati mwake; ndipo pali ina imene imagudubuzika chifukwa cha kuopa Allah. (Koma inu Ayuda simulalikika ngakhale mpang’ono pomwe). Ndipo Allah sali wonyalanyaza zimene mukuchita.

۞ أَفَتَطۡمَعُونَ أَن یُؤۡمِنُوا۟ لَكُمۡ وَقَدۡ كَانَ فَرِیقࣱ مِّنۡهُمۡ یَسۡمَعُونَ كَلَـٰمَ ٱللَّهِ ثُمَّ یُحَرِّفُونَهُۥ مِنۢ بَعۡدِ مَا عَقَلُوهُ وَهُمۡ یَعۡلَمُونَ ﴿75﴾

۞ Kodi (inu Asilamu) mukuyembekezera kuti angakukhulupirireni (Ayudawo) pomwe ena a iwo ankamvera mawu a Allah, kenako nkuwasintha pambuyo powazindikira bwinobwino, uku akudziwa?

وَإِذَا لَقُوا۟ ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ قَالُوۤا۟ ءَامَنَّا وَإِذَا خَلَا بَعۡضُهُمۡ إِلَىٰ بَعۡضࣲ قَالُوۤا۟ أَتُحَدِّثُونَهُم بِمَا فَتَحَ ٱللَّهُ عَلَیۡكُمۡ لِیُحَاۤجُّوكُم بِهِۦ عِندَ رَبِّكُمۡۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ ﴿76﴾

Ndipo akakumana ndi amene akhulupirira, amanena: Takhulupirira (kuti uyu, Muhammad (s.a.w) ndi mneneri woona, ndipo watchulidwa m’mabuku athu).” Koma akakhala kwaokha kuseli, amati: “Mukuwauza iwo (Asilamu) zimene Allah anakufotokozerani (m’buku la Taurat) kuti adzakhale ndi mtsutso pa inu kwa Mbuye wanu? Kodi mulibe nzeru?

أَوَلَا یَعۡلَمُونَ أَنَّ ٱللَّهَ یَعۡلَمُ مَا یُسِرُّونَ وَمَا یُعۡلِنُونَ ﴿77﴾

“Kodi sadziwa kuti Allah akudziwa zomwe akubisa ndi zomwe akuonetsera poyera? (Kwa Allah palibe chobisika).

وَمِنۡهُمۡ أُمِّیُّونَ لَا یَعۡلَمُونَ ٱلۡكِتَـٰبَ إِلَّاۤ أَمَانِیَّ وَإِنۡ هُمۡ إِلَّا یَظُنُّونَ ﴿78﴾

Ndipo mwa iwo (Ayudawo) zilipo mbuli zosadziwa kuwerenga buku (la Allah), koma ziyembekezero zabodza basi, ndipo iwo alibe china koma kungoganizira.

فَوَیۡلࣱ لِّلَّذِینَ یَكۡتُبُونَ ٱلۡكِتَـٰبَ بِأَیۡدِیهِمۡ ثُمَّ یَقُولُونَ هَـٰذَا مِنۡ عِندِ ٱللَّهِ لِیَشۡتَرُوا۟ بِهِۦ ثَمَنࣰا قَلِیلࣰاۖ فَوَیۡلࣱ لَّهُم مِّمَّا كَتَبَتۡ أَیۡدِیهِمۡ وَوَیۡلࣱ لَّهُم مِّمَّا یَكۡسِبُونَ ﴿79﴾

Chilango cha ukali chili pa amene akulemba buku ndi manja awo, kenako nanena: “Ili lachokera kwa Allah,” (akunena bodzalo) kuti apeze zinthu za mtengo wochepa (za m’dziko lapansi); choncho kuonongeka kuli pa iwo chifukwa cha zomwe manja awo alemba, ndiponso kuonongeka n’kwawo chifukwa cha zomwe akupeza.

وَقَالُوا۟ لَن تَمَسَّنَا ٱلنَّارُ إِلَّاۤ أَیَّامࣰا مَّعۡدُودَةࣰۚ قُلۡ أَتَّخَذۡتُمۡ عِندَ ٱللَّهِ عَهۡدࣰا فَلَن یُخۡلِفَ ٱللَّهُ عَهۡدَهُۥۤۖ أَمۡ تَقُولُونَ عَلَى ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ ﴿80﴾

Ndipo akunena: “Sudzatikhudza Moto kupatula masiku owerengeka basi.”Auze: “Kodi mudapangana naye Allah, kuti potero sadzaswa lonjezo Lake, kapena mukungomunenera Allah zimene simukuzidziwa?”

بَلَىٰۚ مَن كَسَبَ سَیِّئَةࣰ وَأَحَـٰطَتۡ بِهِۦ خَطِیۤـَٔتُهُۥ فَأُو۟لَـٰۤىِٕكَ أَصۡحَـٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِیهَا خَـٰلِدُونَ ﴿81﴾

Sichoncho! Koma amene wachita choipa, nam’zungulira machimo akeo, otero ndi anthu a ku Moto. M’menemo adzakhala nthawi yaitali.

وَٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ وَعَمِلُوا۟ ٱلصَّـٰلِحَـٰتِ أُو۟لَـٰۤىِٕكَ أَصۡحَـٰبُ ٱلۡجَنَّةِۖ هُمۡ فِیهَا خَـٰلِدُونَ ﴿82﴾

Ndipo amene akhulupirira nachita zabwino, iwowo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere. M’menemo adzakhala nthawi yaitali.

وَإِذۡ أَخَذۡنَا مِیثَـٰقَ بَنِیۤ إِسۡرَ ٰ⁠ۤءِیلَ لَا تَعۡبُدُونَ إِلَّا ٱللَّهَ وَبِٱلۡوَ ٰ⁠لِدَیۡنِ إِحۡسَانࣰا وَذِی ٱلۡقُرۡبَىٰ وَٱلۡیَتَـٰمَىٰ وَٱلۡمَسَـٰكِینِ وَقُولُوا۟ لِلنَّاسِ حُسۡنࣰا وَأَقِیمُوا۟ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُوا۟ ٱلزَّكَوٰةَ ثُمَّ تَوَلَّیۡتُمۡ إِلَّا قَلِیلࣰا مِّنكُمۡ وَأَنتُم مُّعۡرِضُونَ ﴿83﴾

Ndipo (akumbutse nkhani iyinso) pamene tidalandira pangano lamphamvu la ana a Israyeli kuti: Musapembedze aliyense koma Allah; ndipo muwachitire zabwino makolo anu ndi achibale anu, ndi amasiye, ndi masikini (osoŵedwa); ndipo nenani kwa anthu mwaubwino; ndipo pempherani Swala moyenera ndi kupereka Zakaat, kenako mudatembenuka monyozera kupatula ochepa mwa inu, ndipo inu ndinu onyozera.

وَإِذۡ أَخَذۡنَا مِیثَـٰقَكُمۡ لَا تَسۡفِكُونَ دِمَاۤءَكُمۡ وَلَا تُخۡرِجُونَ أَنفُسَكُم مِّن دِیَـٰرِكُمۡ ثُمَّ أَقۡرَرۡتُمۡ وَأَنتُمۡ تَشۡهَدُونَ ﴿84﴾

Ndipo kumbukirani pamene tidalandira pangano lanu kuti simukhetsa mwazi wanu, ndikutinso simudzatulutsana nokha m’nyumba zanu, ndipo inu munavomereza zimenezi, ndipo inu mukuikira umboni zimenezi (koma simudatsate malamulowo).

ثُمَّ أَنتُمۡ هَـٰۤؤُلَاۤءِ تَقۡتُلُونَ أَنفُسَكُمۡ وَتُخۡرِجُونَ فَرِیقࣰا مِّنكُم مِّن دِیَـٰرِهِمۡ تَظَـٰهَرُونَ عَلَیۡهِم بِٱلۡإِثۡمِ وَٱلۡعُدۡوَ ٰ⁠نِ وَإِن یَأۡتُوكُمۡ أُسَـٰرَىٰ تُفَـٰدُوهُمۡ وَهُوَ مُحَرَّمٌ عَلَیۡكُمۡ إِخۡرَاجُهُمۡۚ أَفَتُؤۡمِنُونَ بِبَعۡضِ ٱلۡكِتَـٰبِ وَتَكۡفُرُونَ بِبَعۡضࣲۚ فَمَا جَزَاۤءُ مَن یَفۡعَلُ ذَ ٰ⁠لِكَ مِنكُمۡ إِلَّا خِزۡیࣱ فِی ٱلۡحَیَوٰةِ ٱلدُّنۡیَاۖ وَیَوۡمَ ٱلۡقِیَـٰمَةِ یُرَدُّونَ إِلَىٰۤ أَشَدِّ ٱلۡعَذَابِۗ وَمَا ٱللَّهُ بِغَـٰفِلٍ عَمَّا تَعۡمَلُونَ ﴿85﴾

Tsono inu nomwe ndi amene mukuphana ndikuwatulutsa ena a inu m’nyumba zawo; mukuthandiza adani anu powachitira (abale anu masautso) mwauchimo ndi molumpha malire. Koma akakudzerani akaidi ogwidwa ku nkhondo, mukuwaombola, pomwe nkoletsedwa kwa inu kuwatulutsa. Kodi mukukhulupirira mbali ina ya buku, mbali ina nkuikana? Choncho palibe mphoto kwa ochita izi mwa inu koma kuyaluka pamoyo wa pa dziko lapansi; ndipo tsiku la chiweruziro adzalowetsedwa ku chilango chokhwima kwambiri. Ndipo Allah sali wonyalanyaza zimene mukuchita[4].

أُو۟لَـٰۤىِٕكَ ٱلَّذِینَ ٱشۡتَرَوُا۟ ٱلۡحَیَوٰةَ ٱلدُّنۡیَا بِٱلۡـَٔاخِرَةِۖ فَلَا یُخَفَّفُ عَنۡهُمُ ٱلۡعَذَابُ وَلَا هُمۡ یُنصَرُونَ ﴿86﴾

Iwowo ndi amene asinthanitsa moyo wa dziko lapansi ndi moyo ulinkudza choncho sadzawachepetsera chilango, ndiponso sadzapulumutsidwa.

وَلَقَدۡ ءَاتَیۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَـٰبَ وَقَفَّیۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِۦ بِٱلرُّسُلِۖ وَءَاتَیۡنَا عِیسَى ٱبۡنَ مَرۡیَمَ ٱلۡبَیِّنَـٰتِ وَأَیَّدۡنَـٰهُ بِرُوحِ ٱلۡقُدُسِۗ أَفَكُلَّمَا جَاۤءَكُمۡ رَسُولُۢ بِمَا لَا تَهۡوَىٰۤ أَنفُسُكُمُ ٱسۡتَكۡبَرۡتُمۡ فَفَرِیقࣰا كَذَّبۡتُمۡ وَفَرِیقࣰا تَقۡتُلُونَ ﴿87﴾

Ndithudi Mûsa tidampatsa buku (la Taurat) ndipo tidatsatiza pambuyo pake atumiki (ena). Ndipo Isa (Yesu) mwana wa Mariya tidampatsa zizizwa zoonekera, ndi kumulimbikitsa ndi Mzimu Woyera (Gabrieli). Nthawi iliyonse akakudzerani mtumiki ndi chomwe mitima yanu siikonda, mumadzikweza. Ena mudawatsutsa ndipo ena mudawapha.

وَقَالُوا۟ قُلُوبُنَا غُلۡفُۢۚ بَل لَّعَنَهُمُ ٱللَّهُ بِكُفۡرِهِمۡ فَقَلِیلࣰا مَّا یُؤۡمِنُونَ ﴿88﴾

(Iwo) adati: “Mitima yathu yakutidwa, (potero tikulephera kumvetsa ulaliki wako, iwe Muhammad (s.a.w).’’ Iwo ngabodza pa zimene akunenazi. Koma Allah wawatembelera chifukwa cha kusakhulupirira kwawo). Tero n’zochepa zimene akuzikhulupirira.

وَلَمَّا جَاۤءَهُمۡ كِتَـٰبࣱ مِّنۡ عِندِ ٱللَّهِ مُصَدِّقࣱ لِّمَا مَعَهُمۡ وَكَانُوا۟ مِن قَبۡلُ یَسۡتَفۡتِحُونَ عَلَى ٱلَّذِینَ كَفَرُوا۟ فَلَمَّا جَاۤءَهُم مَّا عَرَفُوا۟ كَفَرُوا۟ بِهِۦۚ فَلَعۡنَةُ ٱللَّهِ عَلَى ٱلۡكَـٰفِرِینَ ﴿89﴾

Ndipo pamene buku lidawadzera (m’nyengo ya mtumiki Muhammad {s.a.w}) lochokera kwa Allah, loikira umboni zomwe zili pamodzi ndi iwo (adalikana), pomwe kale (lisadadze bukulo) adali kupempha chithandizo (kupyolera kwa mtumiki wolonjezedwa) chogonjetsera amene sadakhulupirire. Koma pamene chidawadzera chimene adachidziwa, (Qur’an) adachikana. Choncho matembelero a Allah ali pa osakhulupirira.

بِئۡسَمَا ٱشۡتَرَوۡا۟ بِهِۦۤ أَنفُسَهُمۡ أَن یَكۡفُرُوا۟ بِمَاۤ أَنزَلَ ٱللَّهُ بَغۡیًا أَن یُنَزِّلَ ٱللَّهُ مِن فَضۡلِهِۦ عَلَىٰ مَن یَشَاۤءُ مِنۡ عِبَادِهِۦۖ فَبَاۤءُو بِغَضَبٍ عَلَىٰ غَضَبࣲۚ وَلِلۡكَـٰفِرِینَ عَذَابࣱ مُّهِینࣱ ﴿90﴾

N’choipa zedi chimene asinthanitsira (chisangalalo cha tsiku lachimaliziro cha) mitima yawo pa kukana kwao zimene Allah adavumbulutsa, chifukwa cha njiru basi kuti Allah watsitsira chifundo chake amene wamfuna mwa akapolo Ake (amene sali Myuda). Potero adabwerera ndi mkwiyo wa Allah kuonjezera pa mkwiyo wakale. Ndipo osakhulupirira adzakhala ndi chilango chosambula.

وَإِذَا قِیلَ لَهُمۡ ءَامِنُوا۟ بِمَاۤ أَنزَلَ ٱللَّهُ قَالُوا۟ نُؤۡمِنُ بِمَاۤ أُنزِلَ عَلَیۡنَا وَیَكۡفُرُونَ بِمَا وَرَاۤءَهُۥ وَهُوَ ٱلۡحَقُّ مُصَدِّقࣰا لِّمَا مَعَهُمۡۗ قُلۡ فَلِمَ تَقۡتُلُونَ أَنۢبِیَاۤءَ ٱللَّهِ مِن قَبۡلُ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِینَ ﴿91﴾

Ndipo akauzidwa (Ayuda): “Khulupirirani zimene Allah wavumbulutsa (kwa mtumiki Muhammad {s.a.w}).” Amanena: “Tikukhulupirira zimene zidavumbulitsidwa kwa ife,” ndipo amazikana zomwe sizili zimenezo ngakhale izo zili zoona, zomwe zikutsimikizira pa zimene ali nazo pamodzi. Nena: “Nanga bwanji mudapha aneneri a Allah kalelo ngati muli okhulupiriradi?”

۞ وَلَقَدۡ جَاۤءَكُم مُّوسَىٰ بِٱلۡبَیِّنَـٰتِ ثُمَّ ٱتَّخَذۡتُمُ ٱلۡعِجۡلَ مِنۢ بَعۡدِهِۦ وَأَنتُمۡ ظَـٰلِمُونَ ﴿92﴾

Ndipo adakudzerani Mûsa ndi zisonyezo zoonekera, koma pambuyo pake mudapembedza thole (mwana wa ng’ombe), ndipo potero mudali anthu ochita zoipa kwabasi.

وَإِذۡ أَخَذۡنَا مِیثَـٰقَكُمۡ وَرَفَعۡنَا فَوۡقَكُمُ ٱلطُّورَ خُذُوا۟ مَاۤ ءَاتَیۡنَـٰكُم بِقُوَّةࣲ وَٱسۡمَعُوا۟ۖ قَالُوا۟ سَمِعۡنَا وَعَصَیۡنَا وَأُشۡرِبُوا۟ فِی قُلُوبِهِمُ ٱلۡعِجۡلَ بِكُفۡرِهِمۡۚ قُلۡ بِئۡسَمَا یَأۡمُرُكُم بِهِۦۤ إِیمَـٰنُكُمۡ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِینَ ﴿93﴾

Ndipo (kumbukirani nkhani iyi, inu ana a Israyeli) pamene tidalandira kwa inu pangano lamphamvu, ndipo tidakukwezerani phiri pamwamba panu (uku tikuti): “Gwiritsani mwamphamvu (malamulo) amene takupatsani, ndipo mverani.” (Iwo) adati: “Tamva (mawu anu), koma tanyozera.” Ndipo adamwetsedwa m’mitima mwawo kukonda kupembedza thole (mwana wang’ombe) chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Nena: “N’choipa zedi chimene chikhulupiliro chanu chikukulamulirani ngati inu mulidi okhulupirira.”

قُلۡ إِن كَانَتۡ لَكُمُ ٱلدَّارُ ٱلۡـَٔاخِرَةُ عِندَ ٱللَّهِ خَالِصَةࣰ مِّن دُونِ ٱلنَّاسِ فَتَمَنَّوُا۟ ٱلۡمَوۡتَ إِن كُنتُمۡ صَـٰدِقِینَ ﴿94﴾

Auze (Ayudawo): “Ngati nyumba yomaliza kwa Allah njanu nokha, osati anthu ena (monga momwe mukunenera), ilakalakeni imfa ngati mukunenadi zoona.”

وَلَن یَتَمَنَّوۡهُ أَبَدَۢا بِمَا قَدَّمَتۡ أَیۡدِیهِمۡۚ وَٱللَّهُ عَلِیمُۢ بِٱلظَّـٰلِمِینَ ﴿95﴾

Koma sadzailakalaka (imfa) ngakhale pang’ono, chifukwa cha zomwe manja awo adatsogoza (chifukwa cha machimo omwe adadzichitira). Ndipo Allah akudziwa bwino za anthu oipa.

وَلَتَجِدَنَّهُمۡ أَحۡرَصَ ٱلنَّاسِ عَلَىٰ حَیَوٰةࣲ وَمِنَ ٱلَّذِینَ أَشۡرَكُوا۟ۚ یَوَدُّ أَحَدُهُمۡ لَوۡ یُعَمَّرُ أَلۡفَ سَنَةࣲ وَمَا هُوَ بِمُزَحۡزِحِهِۦ مِنَ ٱلۡعَذَابِ أَن یُعَمَّرَۗ وَٱللَّهُ بَصِیرُۢ بِمَا یَعۡمَلُونَ ﴿96﴾

Ndipo muwapeza (Ayuda) kuti ngokondetsetsa kukhala ndi moyo wautali kuposa anthu ena, kuposanso anthu amene akuphatikiza (Allah ndi mafano). Aliyense wa iwo amafuna atapatsidwa moyo wokwana zaka chikwi chimodzi. Pomwe kupatsidwa kwake moyo wautali sikungamuike kutali ndi chilango. Ndipo Allah akuona zonse zimene akuchita.

قُلۡ مَن كَانَ عَدُوࣰّا لِّجِبۡرِیلَ فَإِنَّهُۥ نَزَّلَهُۥ عَلَىٰ قَلۡبِكَ بِإِذۡنِ ٱللَّهِ مُصَدِّقࣰا لِّمَا بَیۡنَ یَدَیۡهِ وَهُدࣰى وَبُشۡرَىٰ لِلۡمُؤۡمِنِینَ ﴿97﴾

Nena: “Amene akhale mdani wa Gaburieli (chifukwa chobweretsa chivumbulutso kwa Muhammad {s.a.w}, iyeyo ndi mdani wa Allah). Ndithudi, iye waivumbulutsa Qur’an mumtima mwako mwachilolezo cha Allah. Kudzatsimikidzira zomwe zidali patsogolo pake, ndiponso ndi chiongoko ndi nkhani yabwino kwa okhulupirira.

مَن كَانَ عَدُوࣰّا لِّلَّهِ وَمَلَـٰۤىِٕكَتِهِۦ وَرُسُلِهِۦ وَجِبۡرِیلَ وَمِیكَىٰلَ فَإِنَّ ٱللَّهَ عَدُوࣱّ لِّلۡكَـٰفِرِینَ ﴿98﴾

Amene ali mdani wa Allah, angelo Ake, atumiki Ake, Gaburieli ndi Mikayeli, ndithu Allah ndi mdani wa osakhulupirira.

وَلَقَدۡ أَنزَلۡنَاۤ إِلَیۡكَ ءَایَـٰتِۭ بَیِّنَـٰتࣲۖ وَمَا یَكۡفُرُ بِهَاۤ إِلَّا ٱلۡفَـٰسِقُونَ ﴿99﴾

Ndithu tavumbulutsa kwa iwe zisonyezo zoonekera. Ndipo palibe wozikana koma okhawo opandukira chilamulo cha Allah.

أَوَكُلَّمَا عَـٰهَدُوا۟ عَهۡدࣰا نَّبَذَهُۥ فَرِیقࣱ مِّنۡهُمۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا یُؤۡمِنُونَ ﴿100﴾

Kodi sizili tero kuti panthawi iliyonse akupangana pangano lamphamvu, ena aiwo akulitaya? Koma ambiri aiwo sakhulupirira.

وَلَمَّا جَاۤءَهُمۡ رَسُولࣱ مِّنۡ عِندِ ٱللَّهِ مُصَدِّقࣱ لِّمَا مَعَهُمۡ نَبَذَ فَرِیقࣱ مِّنَ ٱلَّذِینَ أُوتُوا۟ ٱلۡكِتَـٰبَ كِتَـٰبَ ٱللَّهِ وَرَاۤءَ ظُهُورِهِمۡ كَأَنَّهُمۡ لَا یَعۡلَمُونَ ﴿101﴾

Ndipo pamene (Ayuda) adawadzera Mtumiki wochokera kwa Allah uku akutsimikidzira chomwe iwo ali nacho, gulu lina mwa omwe adapatsidwa buku adataya buku la Allah kumbuyo kwa misana yawo ngati kuti sakulidziwa.

وَٱتَّبَعُوا۟ مَا تَتۡلُوا۟ ٱلشَّیَـٰطِینُ عَلَىٰ مُلۡكِ سُلَیۡمَـٰنَۖ وَمَا كَفَرَ سُلَیۡمَـٰنُ وَلَـٰكِنَّ ٱلشَّیَـٰطِینَ كَفَرُوا۟ یُعَلِّمُونَ ٱلنَّاسَ ٱلسِّحۡرَ وَمَاۤ أُنزِلَ عَلَى ٱلۡمَلَكَیۡنِ بِبَابِلَ هَـٰرُوتَ وَمَـٰرُوتَۚ وَمَا یُعَلِّمَانِ مِنۡ أَحَدٍ حَتَّىٰ یَقُولَاۤ إِنَّمَا نَحۡنُ فِتۡنَةࣱ فَلَا تَكۡفُرۡۖ فَیَتَعَلَّمُونَ مِنۡهُمَا مَا یُفَرِّقُونَ بِهِۦ بَیۡنَ ٱلۡمَرۡءِ وَزَوۡجِهِۦۚ وَمَا هُم بِضَاۤرِّینَ بِهِۦ مِنۡ أَحَدٍ إِلَّا بِإِذۡنِ ٱللَّهِۚ وَیَتَعَلَّمُونَ مَا یَضُرُّهُمۡ وَلَا یَنفَعُهُمۡۚ وَلَقَدۡ عَلِمُوا۟ لَمَنِ ٱشۡتَرَىٰهُ مَا لَهُۥ فِی ٱلۡـَٔاخِرَةِ مِنۡ خَلَـٰقࣲۚ وَلَبِئۡسَ مَا شَرَوۡا۟ بِهِۦۤ أَنفُسَهُمۡۚ لَوۡ كَانُوا۟ یَعۡلَمُونَ ﴿102﴾

Ndipo adatsatira njira za afiti zomwe asatana adali kuwafotokozera m’nthawi ya ufumu wa Sulaiman. Ndipo Sulaiman sadamkane Allah (sadali mfiti), koma asatana ndi amene adamkana, naphunzitsa anthu ufiti (umene adaudziwa kuyambira kale); natsatiranso (njira za ufiti) zimene zinatsitsidwa kwa Angelo awiri Haruta ndi Maruta (ku midzi ya) ku Babulo. Koma Angelowo sadaphunzitse aliyense pokhapokha atamuuza kuti: “Ife ndife mayeso (ofuna kuona kugonjera kwanu malamulo a Allah); choncho musamkane (Allah).” Komabe ankaphunzira kwa iwo njira zolekanitsira pakati pa munthu ndi mkazi wake, (ndi zina zotero). Ndipo sadavutitse aliyense ndi zimenezo koma mwachilolezo cha Allah. Ndipo akuphunzira zomwe zingawavutitse pomwe sizingawathandize. Ndithudi, akudziwa kuti yemwe wausankha (ufitiwo) sadzakhala ndi gawo lililonse (la zinthu zabwino) tsiku lachimaliziro. Ndithudi, nchoipitsitsa chimene adzisankhira okha akadakhala akudziwa.

وَلَوۡ أَنَّهُمۡ ءَامَنُوا۟ وَٱتَّقَوۡا۟ لَمَثُوبَةࣱ مِّنۡ عِندِ ٱللَّهِ خَیۡرࣱۚ لَّوۡ كَانُوا۟ یَعۡلَمُونَ ﴿103﴾

Ndipo iwo akadakhulupirira nadzitchinjiriza (ku zoletsedwa), ndithudi, mphoto yochokera kwa Allah ikadakhala yabwino kwa iwo, akadadziwa.

یَـٰۤأَیُّهَا ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ لَا تَقُولُوا۟ رَ ٰ⁠عِنَا وَقُولُوا۟ ٱنظُرۡنَا وَٱسۡمَعُوا۟ۗ وَلِلۡكَـٰفِرِینَ عَذَابٌ أَلِیمࣱ ﴿104﴾

E inu amene mwakhulupirira! Musam’nenere (Mneneri liwu lakuti) “raina” (ndicholinga chomunenera kuti iye ndi mbutuma), koma mnenereni (liwu lakuti) “utiyang’anire,” ndipo mverani malamulo. Kwa osakhulupirira kuli chilango chopweteka.

مَّا یَوَدُّ ٱلَّذِینَ كَفَرُوا۟ مِنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَـٰبِ وَلَا ٱلۡمُشۡرِكِینَ أَن یُنَزَّلَ عَلَیۡكُم مِّنۡ خَیۡرࣲ مِّن رَّبِّكُمۡۚ وَٱللَّهُ یَخۡتَصُّ بِرَحۡمَتِهِۦ مَن یَشَاۤءُۚ وَٱللَّهُ ذُو ٱلۡفَضۡلِ ٱلۡعَظِیمِ ﴿105﴾

Amene sadakhulupirire mwa anthu a mabuku (Ayuda ndi Akhirisitu) ndi omphatikiza Allah (Arabu), safuna kuti chabwino chilichonse chochokera kwa Mbuye wanu chitsitsidwe kwa inu (Asilamu). Koma Allah amamsankhira chifundo Chake amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino ochuluka.

۞ مَا نَنسَخۡ مِنۡ ءَایَةٍ أَوۡ نُنسِهَا نَأۡتِ بِخَیۡرࣲ مِّنۡهَاۤ أَوۡ مِثۡلِهَاۤۗ أَلَمۡ تَعۡلَمۡ أَنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَیۡءࣲ قَدِیرٌ ﴿106﴾

Ayah (ndime) iliyonse yomwe tikuifafaniza kapena kuiiwalitsa (mu mtima wako) tikubweretsa yabwino kuposa iyo, kapena yofanana nayo. Kodi sukudziwa kuti Allah Ngokhoza chinthu chilichonse?

أَلَمۡ تَعۡلَمۡ أَنَّ ٱللَّهَ لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَـٰوَ ٰ⁠تِ وَٱلۡأَرۡضِۗ وَمَا لَكُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ مِن وَلِیࣲّ وَلَا نَصِیرٍ ﴿107﴾

Kodi siudziwa kuti ufumu wakumwamba ndi pansi ngwa Allah? Ndipo inu kupatula Iye Allah mulibe mtetezi ngakhale mthandizi.

أَمۡ تُرِیدُونَ أَن تَسۡـَٔلُوا۟ رَسُولَكُمۡ كَمَا سُىِٕلَ مُوسَىٰ مِن قَبۡلُۗ وَمَن یَتَبَدَّلِ ٱلۡكُفۡرَ بِٱلۡإِیمَـٰنِ فَقَدۡ ضَلَّ سَوَاۤءَ ٱلسَّبِیلِ ﴿108﴾

Kodi mukufuna kumfunsa Mtumiki wanu (inu Asilamu) monga momwe Mûsa adafunsidwira kale (mafunso achipongwe)? Ndipo amene angasinthitse chikhulupiliro ndi kusakhulupirira, ndithudi wasokera njira yolingana (yopanda majiga).

وَدَّ كَثِیرࣱ مِّنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَـٰبِ لَوۡ یَرُدُّونَكُم مِّنۢ بَعۡدِ إِیمَـٰنِكُمۡ كُفَّارًا حَسَدࣰا مِّنۡ عِندِ أَنفُسِهِم مِّنۢ بَعۡدِ مَا تَبَیَّنَ لَهُمُ ٱلۡحَقُّۖ فَٱعۡفُوا۟ وَٱصۡفَحُوا۟ حَتَّىٰ یَأۡتِیَ ٱللَّهُ بِأَمۡرِهِۦۤۗ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَیۡءࣲ قَدِیرࣱ ﴿109﴾

Ambiri mwa amene anapatsidwa mabuku, akufuna kukubwezani (kukutembenuzani) kuti mukhale osakhulupirira pambuyo pa chikhulupiliro chanu, chifukwa chadumbo lomwe lili m’mitima mwawo (lomwe lawapeza) pambuyo powaonekera choonadi poyera. Choncho akhululukireni ndi kuwasiya kufikira Allah adzabweretse lamulo Lake[5]; ndithudi Allah Ngokhoza chilichonse.

وَأَقِیمُوا۟ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُوا۟ ٱلزَّكَوٰةَۚ وَمَا تُقَدِّمُوا۟ لِأَنفُسِكُم مِّنۡ خَیۡرࣲ تَجِدُوهُ عِندَ ٱللَّهِۗ إِنَّ ٱللَّهَ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِیرࣱ ﴿110﴾

Ndipo pempherani Swala moyenera ndiponso perekani Zakaat. Ndipo chilichonse chabwino chimene mukudzitsogozera mukachipeza kwa Allah. Ndithudi, Allah akuona zonse zimene mukuchita.

وَقَالُوا۟ لَن یَدۡخُلَ ٱلۡجَنَّةَ إِلَّا مَن كَانَ هُودًا أَوۡ نَصَـٰرَىٰۗ تِلۡكَ أَمَانِیُّهُمۡۗ قُلۡ هَاتُوا۟ بُرۡهَـٰنَكُمۡ إِن كُنتُمۡ صَـٰدِقِینَ ﴿111﴾

Eti akunena: “Palibe amene adzalowe ku Munda wamtendere koma amene ali Myuda Kapena Mkhirisitu.” Zimenezo nzokhumba zawo chabe. Nena: “Bweretsani umboni wanu ngati mukunena zoona.”

بَلَىٰۚ مَنۡ أَسۡلَمَ وَجۡهَهُۥ لِلَّهِ وَهُوَ مُحۡسِنࣱ فَلَهُۥۤ أَجۡرُهُۥ عِندَ رَبِّهِۦ وَلَا خَوۡفٌ عَلَیۡهِمۡ وَلَا هُمۡ یَحۡزَنُونَ ﴿112﴾

Ayi, koma amene nkhope yake yagonjera kwa Allah uku akuchita zabwino (kwa anthu anzawo) iye ndi amene adzapeza mphoto yake kwa Mbuye wake. Ndipo pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso iwo sadzadandaula.

وَقَالَتِ ٱلۡیَهُودُ لَیۡسَتِ ٱلنَّصَـٰرَىٰ عَلَىٰ شَیۡءࣲ وَقَالَتِ ٱلنَّصَـٰرَىٰ لَیۡسَتِ ٱلۡیَهُودُ عَلَىٰ شَیۡءࣲ وَهُمۡ یَتۡلُونَ ٱلۡكِتَـٰبَۗ كَذَ ٰ⁠لِكَ قَالَ ٱلَّذِینَ لَا یَعۡلَمُونَ مِثۡلَ قَوۡلِهِمۡۚ فَٱللَّهُ یَحۡكُمُ بَیۡنَهُمۡ یَوۡمَ ٱلۡقِیَـٰمَةِ فِیمَا كَانُوا۟ فِیهِ یَخۡتَلِفُونَ ﴿113﴾

Ndipo Ayuda akumanena: “Akhrisitu alibe chilichonse (chotsamira pa chipembedzo chawo);” naonso Akhrisitu akumanena: “Ayuda alibe chilichonse (chotsamira pa chipembedzo chawo),” pomwe onsewa akuwerenga buku (lomwe adawavumbulutsira popanda kutsatira zili m’bukulo). Momwemonso akunena amene sali odziwa (Arabu opembedza mafano) monga zonena zawo (Ayuda). Allah adzaweruza pakati pawo tsiku la chimaliziro pa zomwe adali kusiyana.

وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن مَّنَعَ مَسَـٰجِدَ ٱللَّهِ أَن یُذۡكَرَ فِیهَا ٱسۡمُهُۥ وَسَعَىٰ فِی خَرَابِهَاۤۚ أُو۟لَـٰۤىِٕكَ مَا كَانَ لَهُمۡ أَن یَدۡخُلُوهَاۤ إِلَّا خَاۤىِٕفِینَۚ لَهُمۡ فِی ٱلدُّنۡیَا خِزۡیࣱ وَلَهُمۡ فِی ٱلۡـَٔاخِرَةِ عَذَابٌ عَظِیمࣱ ﴿114﴾

Kodi alipo woipitsitsa woposa amene akutsekereza (anthu kulowa) m’misikiti ya Allah kuti lisatchulidwe m’menemo dzina Lake nalimbika kuiononga (misikitiyo)? - Kotero kuti sikunali koyenera kwa iwo kulowa mmenemo koma mwa mantha. Kuyaluka kwa pa dziko lapansi nkwawo ndipo tsiku lachimaliziro iwo adzapeza chilango chachikulu.

وَلِلَّهِ ٱلۡمَشۡرِقُ وَٱلۡمَغۡرِبُۚ فَأَیۡنَمَا تُوَلُّوا۟ فَثَمَّ وَجۡهُ ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ وَ ٰ⁠سِعٌ عَلِیمࣱ ﴿115﴾

Ndipo kuvuma ndi kuzambwe nkwa Allah; ndipo pamalo paliponse pamene mwatembenukira, (pomwe Allah wakulamulirani kuti mutembenukire), pamenepo mupezapo chiyanjo cha Allah. Ndithudi Allah Ngokwanira ponseponse, Wodziwa chilichonse.

وَقَالُوا۟ ٱتَّخَذَ ٱللَّهُ وَلَدࣰاۗ سُبۡحَـٰنَهُۥۖ بَل لَّهُۥ مَا فِی ٱلسَّمَـٰوَ ٰ⁠تِ وَٱلۡأَرۡضِۖ كُلࣱّ لَّهُۥ قَـٰنِتُونَ ﴿116﴾

Ndipo (osakhulupirira) akumanena: “Allah wadzipangira mwana.” (Allah) wapatukana ndi zimenezo. Koma (zolengedwa) zonse za kumwamba ndi pansi Nzake. Zonse zikumumvera Iye.

بَدِیعُ ٱلسَّمَـٰوَ ٰ⁠تِ وَٱلۡأَرۡضِۖ وَإِذَا قَضَىٰۤ أَمۡرࣰا فَإِنَّمَا یَقُولُ لَهُۥ كُن فَیَكُونُ ﴿117﴾

(Iye ndi) Mlengi wa thambo ndi nthaka popanda chofanizira. Ndipo akafuna chinthu kuti chichitike amangoti: “Chitika,” ndipo chimachitikadi.

وَقَالَ ٱلَّذِینَ لَا یَعۡلَمُونَ لَوۡلَا یُكَلِّمُنَا ٱللَّهُ أَوۡ تَأۡتِینَاۤ ءَایَةࣱۗ كَذَ ٰ⁠لِكَ قَالَ ٱلَّذِینَ مِن قَبۡلِهِم مِّثۡلَ قَوۡلِهِمۡۘ تَشَـٰبَهَتۡ قُلُوبُهُمۡۗ قَدۡ بَیَّنَّا ٱلۡـَٔایَـٰتِ لِقَوۡمࣲ یُوقِنُونَ ﴿118﴾

Ndipo aja osadziwa akunena: “Bwanji Allah sakutiyankhula ife? Kapena kutibwerera chizindikiro (chizizwa)?” Mofanana ndi zoyankhula zawozo adanenanso amene adalipo kale. Mitima yawo yalingana. Ndithu Ife tazifotokoza zizindikiro momveka kwa anthu otsimikiza (m’chikhulupiliro).

إِنَّاۤ أَرۡسَلۡنَـٰكَ بِٱلۡحَقِّ بَشِیرࣰا وَنَذِیرࣰاۖ وَلَا تُسۡـَٔلُ عَنۡ أَصۡحَـٰبِ ٱلۡجَحِیمِ ﴿119﴾

Ndithudi, Ife takutumiza (iwe Mtumiki {s.a.w}) ndi choonadi kuti ukhale wouza nkhani zabwino ndi wochenjeza. Ndipo siudzafunsidwa za anthu a ku Moto.

وَلَن تَرۡضَىٰ عَنكَ ٱلۡیَهُودُ وَلَا ٱلنَّصَـٰرَىٰ حَتَّىٰ تَتَّبِعَ مِلَّتَهُمۡۗ قُلۡ إِنَّ هُدَى ٱللَّهِ هُوَ ٱلۡهُدَىٰۗ وَلَىِٕنِ ٱتَّبَعۡتَ أَهۡوَاۤءَهُم بَعۡدَ ٱلَّذِی جَاۤءَكَ مِنَ ٱلۡعِلۡمِ مَا لَكَ مِنَ ٱللَّهِ مِن وَلِیࣲّ وَلَا نَصِیرٍ ﴿120﴾

Ndipo Ayuda ndi Akhrisitu sangakondwere nawe pokhapokha utatsatira chipembedzo chawo. Nena: “Ndithudi, chiongoko cha Allah ndichomwe chili chiongoko chenicheni.” Ngati utsata zilakolako zawo pambuyo pa zomwe zakudzera, monga kuzindikira (kwenikweni), sudzapeza mtetezi aliyense ngakhale mthandizi kwa Allah.

ٱلَّذِینَ ءَاتَیۡنَـٰهُمُ ٱلۡكِتَـٰبَ یَتۡلُونَهُۥ حَقَّ تِلَاوَتِهِۦۤ أُو۟لَـٰۤىِٕكَ یُؤۡمِنُونَ بِهِۦۗ وَمَن یَكۡفُرۡ بِهِۦ فَأُو۟لَـٰۤىِٕكَ هُمُ ٱلۡخَـٰسِرُونَ ﴿121﴾

Anthu omwe tidawapatsa buku naliwerenga kuwerenga koyenera (kopanda kusintha mawu ake ndi matanthauzo ake), iwo ndi amene akulikhulupirira (bukuli la Qur’an). Koma amene angalikane iwowa ndi omwe ali oonongeka.

یَـٰبَنِیۤ إِسۡرَ ٰ⁠ۤءِیلَ ٱذۡكُرُوا۟ نِعۡمَتِیَ ٱلَّتِیۤ أَنۡعَمۡتُ عَلَیۡكُمۡ وَأَنِّی فَضَّلۡتُكُمۡ عَلَى ٱلۡعَـٰلَمِینَ ﴿122﴾

E inu ana a Israyeli! Kumbukirani chisomo changa chomwe ndidakudalitsani nacho. Ndithudi, ndidakuchitirani zabwino kuposa zolengedwa zonse (panthawi imeneyo).

وَٱتَّقُوا۟ یَوۡمࣰا لَّا تَجۡزِی نَفۡسٌ عَن نَّفۡسࣲ شَیۡـࣰٔا وَلَا یُقۡبَلُ مِنۡهَا عَدۡلࣱ وَلَا تَنفَعُهَا شَفَـٰعَةࣱ وَلَا هُمۡ یُنصَرُونَ ﴿123﴾

Ndipo opani tsiku lomwe munthu aliyense sadzathandiza munthu mnzake ndi chilichonse, ndipo dipo silidzalandiridwa, ngakhale dandaulo lililonse silidzamthandiza, ndiponso iwo sadzapulumutsidwa.

۞ وَإِذِ ٱبۡتَلَىٰۤ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمَ رَبُّهُۥ بِكَلِمَـٰتࣲ فَأَتَمَّهُنَّۖ قَالَ إِنِّی جَاعِلُكَ لِلنَّاسِ إِمَامࣰاۖ قَالَ وَمِن ذُرِّیَّتِیۖ قَالَ لَا یَنَالُ عَهۡدِی ٱلظَّـٰلِمِینَ ﴿124﴾

Ndipo kumbukirani pamene Ibrahim Mbuye wake (Allah) adamuyesa iye mayeso ndi malamulo ambiri; ndipo iye adakwaniritsa. Adamuuza: “Ndithudi, Ine ndichita iwe kukhala mtsogoleri wa anthu.” (Ibrahim adayankha kuti): “Kodi ndi ana anga omwe?” Adati: “(Inde; koma) lonjezo langa silingawafike ochita zoipa.”

وَإِذۡ جَعَلۡنَا ٱلۡبَیۡتَ مَثَابَةࣰ لِّلنَّاسِ وَأَمۡنࣰا وَٱتَّخِذُوا۟ مِن مَّقَامِ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمَ مُصَلࣰّىۖ وَعَهِدۡنَاۤ إِلَىٰۤ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمَ وَإِسۡمَـٰعِیلَ أَن طَهِّرَا بَیۡتِیَ لِلطَّاۤىِٕفِینَ وَٱلۡعَـٰكِفِینَ وَٱلرُّكَّعِ ٱلسُّجُودِ ﴿125﴾

Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene tidapanga nyumba (ya Al-Kaaba) kuti pakhale pamalo pobwererapo anthu (poyendera anthu) ndikukhalanso malo achitetezo. Ndipo pachiteni kukhala popemphelera Swala pamalo pomwe Ibrahim adali kuimilira (pomamga nyumbayo). Ndipo tidalamula Ibrahim ndi Ismail kuti: “Ayeretsereni nyumba Yanga oizungulira (pochita twawaf) ndi amene akuchita m’bindikiro, owerama ndi kulambira (kuswali mmememo).

وَإِذۡ قَالَ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمُ رَبِّ ٱجۡعَلۡ هَـٰذَا بَلَدًا ءَامِنࣰا وَٱرۡزُقۡ أَهۡلَهُۥ مِنَ ٱلثَّمَرَ ٰ⁠تِ مَنۡ ءَامَنَ مِنۡهُم بِٱللَّهِ وَٱلۡیَوۡمِ ٱلۡـَٔاخِرِۚ قَالَ وَمَن كَفَرَ فَأُمَتِّعُهُۥ قَلِیلࣰا ثُمَّ أَضۡطَرُّهُۥۤ إِلَىٰ عَذَابِ ٱلنَّارِۖ وَبِئۡسَ ٱلۡمَصِیرُ ﴿126﴾

Ndipo (kumbukirani nkhani iyi) pamene Ibrahim adanena: “E Mbuye wanga! Uchiteni mzinda uwu (wa Makka) kukhala wa chitetezo, ndipo zipatseni nzika zake zipatso, amene akukhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro mwa iwo. Allah adati: “Nayenso wosakhulupirira ndinkondweretsa pang’ono; kenako ndidzamkankhira ku chilango cha Moto. Taonani kunyansa malo obwerera.

وَإِذۡ یَرۡفَعُ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمُ ٱلۡقَوَاعِدَ مِنَ ٱلۡبَیۡتِ وَإِسۡمَـٰعِیلُ رَبَّنَا تَقَبَّلۡ مِنَّاۤۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلسَّمِیعُ ٱلۡعَلِیمُ ﴿127﴾

Ndipo (kumbukiraninso) pamene Ibrahim ndi Ismail ankakhazikitsa maziko a nyumba (uku akupempha kwa Allah): “E Mbuye wathu! Tilandireni (ntchito yathuyi), ndithudi, Inu ndinu Akumva; Odziwa.”

رَبَّنَا وَٱجۡعَلۡنَا مُسۡلِمَیۡنِ لَكَ وَمِن ذُرِّیَّتِنَاۤ أُمَّةࣰ مُّسۡلِمَةࣰ لَّكَ وَأَرِنَا مَنَاسِكَنَا وَتُبۡ عَلَیۡنَاۤۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلتَّوَّابُ ٱلرَّحِیمُ ﴿128﴾

“E Mbuye wathu! Tichiteni Kukhalala Asilamu (ogonjera Inu), pamodzinso ndi ana athu muwachite kukhala fuko la Chisilamu (logonjera Inu). Ndipo tidziwitseni (njira) za mapemphero athu; ndipo landirani kulapa kwathu, ndithudi, Inu Ndinu Wolandira kulapa mochuluka; Wachisoni chosatha.”

رَبَّنَا وَٱبۡعَثۡ فِیهِمۡ رَسُولࣰا مِّنۡهُمۡ یَتۡلُوا۟ عَلَیۡهِمۡ ءَایَـٰتِكَ وَیُعَلِّمُهُمُ ٱلۡكِتَـٰبَ وَٱلۡحِكۡمَةَ وَیُزَكِّیهِمۡۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡعَزِیزُ ٱلۡحَكِیمُ ﴿129﴾

“E Mbuye wathu! Atumizireni mtumiki wochokera mwa iwo, kuti awawerengere Ayah (ndime) zanu ndikuwaphunzitsa buku (Lanu) ndi nzeru ndikuti awayeretse. Ndithudi Inu Ndinu Amphamvu zoposa, Anzeru zakuya.”

وَمَن یَرۡغَبُ عَن مِّلَّةِ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمَ إِلَّا مَن سَفِهَ نَفۡسَهُۥۚ وَلَقَدِ ٱصۡطَفَیۡنَـٰهُ فِی ٱلدُّنۡیَاۖ وَإِنَّهُۥ فِی ٱلۡـَٔاخِرَةِ لَمِنَ ٱلصَّـٰلِحِینَ ﴿130﴾

Kodi ndani anganyozere chipembedzo cha Ibrahim posakhala yemwe mtima wake uli wopusa? Ndithudi, tidamsankha (Ibrahim) pa dziko lapansi; ndipo iye tsiku lachimaliziro adzakhala m’modzi wa anthu abwino.”

إِذۡ قَالَ لَهُۥ رَبُّهُۥۤ أَسۡلِمۡۖ قَالَ أَسۡلَمۡتُ لِرَبِّ ٱلۡعَـٰلَمِینَ ﴿131﴾

(Kumbukiraninso) pamene Mbuye wake adamuuza kuti: “Khala Msilamu (gonjera).” (Iye) adati: “Ndili Msilamu (ndagonjera) kwa Mbuye wa zolengedwa zonse.”

وَوَصَّىٰ بِهَاۤ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمُ بَنِیهِ وَیَعۡقُوبُ یَـٰبَنِیَّ إِنَّ ٱللَّهَ ٱصۡطَفَىٰ لَكُمُ ٱلدِّینَ فَلَا تَمُوتُنَّ إِلَّا وَأَنتُم مُّسۡلِمُونَ ﴿132﴾

Ndipo Ibrahim adalangizanso ana ake za zimenezi, chonchonso Ya’qub (adalangizanso ana ake kuti): “E inu ana anga! Ndithudi, Allah wakusankhirani chipembedzo; choncho musafe pokhapokha muli Asilamu (ogonjera Mulungu).”

أَمۡ كُنتُمۡ شُهَدَاۤءَ إِذۡ حَضَرَ یَعۡقُوبَ ٱلۡمَوۡتُ إِذۡ قَالَ لِبَنِیهِ مَا تَعۡبُدُونَ مِنۢ بَعۡدِیۖ قَالُوا۟ نَعۡبُدُ إِلَـٰهَكَ وَإِلَـٰهَ ءَابَاۤىِٕكَ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمَ وَإِسۡمَـٰعِیلَ وَإِسۡحَـٰقَ إِلَـٰهࣰا وَ ٰ⁠حِدࣰا وَنَحۡنُ لَهُۥ مُسۡلِمُونَ ﴿133﴾

Kapena inu (Ayuda ndi Akhrisitu) mudalipo pamene Ya’qub idamdzera imfa, pamene adati kwa ana ake: “Kodi pambuyo panga mudzapembedza yani?” Iwo adayankha nati: “Tidzapembedza Mulungu wako, Mulungu wa makolo ako; Ibrahim, Ismail ndi Ishâq; Mulungu mmodzi basi. Ndipo ife kwa Iye tili Asilamu (ogonjera).”

تِلۡكَ أُمَّةࣱ قَدۡ خَلَتۡۖ لَهَا مَا كَسَبَتۡ وَلَكُم مَّا كَسَبۡتُمۡۖ وَلَا تُسۡـَٔلُونَ عَمَّا كَانُوا۟ یَعۡمَلُونَ ﴿134﴾

Umenewo ndi mbadwo wa anthu umene udamka kale. Udzapeza zimene udachita, ndipo inunso mudzapeza zimene mudachita. Ndipo inu simudzafunsidwa zimene iwo ankachita.

وَقَالُوا۟ كُونُوا۟ هُودًا أَوۡ نَصَـٰرَىٰ تَهۡتَدُوا۟ۗ قُلۡ بَلۡ مِلَّةَ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمَ حَنِیفࣰاۖ وَمَا كَانَ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِینَ ﴿135﴾

Ndipo (Ayuda ndi Akhrisitu) adati (kwa Asilamu): “Khalani Ayuda kapena Akhrisitu mukhala oongoka.” Nena: “Koma (tikutsata) chipembedzo cha Ibrahim yemwe adaleka zipembedzo zopotoka, ndipo sadali mwa ophatikiza (Allah ndi mafano).”

قُولُوۤا۟ ءَامَنَّا بِٱللَّهِ وَمَاۤ أُنزِلَ إِلَیۡنَا وَمَاۤ أُنزِلَ إِلَىٰۤ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمَ وَإِسۡمَـٰعِیلَ وَإِسۡحَـٰقَ وَیَعۡقُوبَ وَٱلۡأَسۡبَاطِ وَمَاۤ أُوتِیَ مُوسَىٰ وَعِیسَىٰ وَمَاۤ أُوتِیَ ٱلنَّبِیُّونَ مِن رَّبِّهِمۡ لَا نُفَرِّقُ بَیۡنَ أَحَدࣲ مِّنۡهُمۡ وَنَحۡنُ لَهُۥ مُسۡلِمُونَ ﴿136﴾

Nenani (inu Asilamu kuwauza Ayuda ndi Akhrisitu); “Takhulupirira Allah ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa ife, ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa Ibrahim, Ismail, Ishâq, Ya’qub ndi zidzukulu (zake) ndi zimene adapatsidwa Mûsa, Isa (Yesu), ndiponso zimene adapatsidwa aneneri (ena) kuchokera kwa Mbuye wawo. Sitilekanitsa pakati pa mmodzi wa iwo (koma onse tikuwakhulupirira). Ndipo ife kwa Iye tili Asilamu (ogonjera).”

فَإِنۡ ءَامَنُوا۟ بِمِثۡلِ مَاۤ ءَامَنتُم بِهِۦ فَقَدِ ٱهۡتَدَوا۟ۖ وَّإِن تَوَلَّوۡا۟ فَإِنَّمَا هُمۡ فِی شِقَاقࣲۖ فَسَیَكۡفِیكَهُمُ ٱللَّهُۚ وَهُوَ ٱلسَّمِیعُ ٱلۡعَلِیمُ ﴿137﴾

Choncho ngati akhulupirira (Ayuda ndi Akhrisitu) monga mmene mwakhulupirira inu, ndiye kuti awongoka. Koma ngati akutembenuka (posakhulupirira) ndiye kuti iwo ali m’kutsutsana. Choncho Allah akuteteza ku zoipa zawo, ndipo Iye Ngwakumva; Wodziwa.

صِبۡغَةَ ٱللَّهِ وَمَنۡ أَحۡسَنُ مِنَ ٱللَّهِ صِبۡغَةࣰۖ وَنَحۡنُ لَهُۥ عَـٰبِدُونَ ﴿138﴾

(Tsatirani) chiongoko cha Allah (Chisilamu). Kodi ndi ndani amene ali ndi chiongoko chabwino kuposa Allah? Ndipo ife Iye Yekha timupembedza.

قُلۡ أَتُحَاۤجُّونَنَا فِی ٱللَّهِ وَهُوَ رَبُّنَا وَرَبُّكُمۡ وَلَنَاۤ أَعۡمَـٰلُنَا وَلَكُمۡ أَعۡمَـٰلُكُمۡ وَنَحۡنُ لَهُۥ مُخۡلِصُونَ ﴿139﴾

Nena (iwe Muhammad {s.a.w} kwa Ayuda ndi Akhrisitu): “Ha! Mukutsutsana nafe za Allah (ponena kuti bwanji wapereka uneneri kumbali ya ife), pomwe Iye ndi Mbuye wathu ndiponso Mbuye wanu? (Pamene mudali olungama adakupatsani uneneri, ndipo pamene mudakhota adakulandani natipatsa ife). Ife tili ndi zochita zathu; inunso muli ndi zochita zanu, ndipo ife tikudzipereka kwathunthu kwa Iye (Allah).”

أَمۡ تَقُولُونَ إِنَّ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمَ وَإِسۡمَـٰعِیلَ وَإِسۡحَـٰقَ وَیَعۡقُوبَ وَٱلۡأَسۡبَاطَ كَانُوا۟ هُودًا أَوۡ نَصَـٰرَىٰۗ قُلۡ ءَأَنتُمۡ أَعۡلَمُ أَمِ ٱللَّهُۗ وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن كَتَمَ شَهَـٰدَةً عِندَهُۥ مِنَ ٱللَّهِۗ وَمَا ٱللَّهُ بِغَـٰفِلٍ عَمَّا تَعۡمَلُونَ ﴿140﴾

Kapena (inu Ayuda) mukunena kuti Ibrahim, Ismail Ishâq, Yaqub ndi zidzukulu anali Ayuda kapena Akhrisitu? Nena: “Kodi inu ndi odziwa kwambiri kapena Allah?” Kodi ndani woipitsitsa koposa yemwe wabisa umboni omwe ali nao ochokera kwa Allah! Komatu Allah sali wonyalanyaza pa zimene mukuchita.

تِلۡكَ أُمَّةࣱ قَدۡ خَلَتۡۖ لَهَا مَا كَسَبَتۡ وَلَكُم مَّا كَسَبۡتُمۡۖ وَلَا تُسۡـَٔلُونَ عَمَّا كَانُوا۟ یَعۡمَلُونَ ﴿141﴾

Umenewo ndi mbadwo wa anthu umene udamka kale. Udzapeza zimene udachita, ndipo inunso mudzapeza zimene mudachita. Ndipo inu simudzafunsidwa zimene iwo ankachita.

۞ سَیَقُولُ ٱلسُّفَهَاۤءُ مِنَ ٱلنَّاسِ مَا وَلَّىٰهُمۡ عَن قِبۡلَتِهِمُ ٱلَّتِی كَانُوا۟ عَلَیۡهَاۚ قُل لِّلَّهِ ٱلۡمَشۡرِقُ وَٱلۡمَغۡرِبُۚ یَهۡدِی مَن یَشَاۤءُ إِلَىٰ صِرَ ٰ⁠طࣲ مُّسۡتَقِیمࣲ ﴿142﴾

۞ Posachedwapa mbutuma za anthu zikhala zikunena: “Nchiyani chimene chawatembenuza ku chibula (mbali yoyang’ana popemphera) chawo chomwe akhala akulunjika nkhope zawo.” Nena: “Kuvuma ndi kuzambwe ndi kwa Allah amamuongolera amene wamfuna kunjira yolunjika.”

وَكَذَ ٰ⁠لِكَ جَعَلۡنَـٰكُمۡ أُمَّةࣰ وَسَطࣰا لِّتَكُونُوا۟ شُهَدَاۤءَ عَلَى ٱلنَّاسِ وَیَكُونَ ٱلرَّسُولُ عَلَیۡكُمۡ شَهِیدࣰاۗ وَمَا جَعَلۡنَا ٱلۡقِبۡلَةَ ٱلَّتِی كُنتَ عَلَیۡهَاۤ إِلَّا لِنَعۡلَمَ مَن یَتَّبِعُ ٱلرَّسُولَ مِمَّن یَنقَلِبُ عَلَىٰ عَقِبَیۡهِۚ وَإِن كَانَتۡ لَكَبِیرَةً إِلَّا عَلَى ٱلَّذِینَ هَدَى ٱللَّهُۗ وَمَا كَانَ ٱللَّهُ لِیُضِیعَ إِیمَـٰنَكُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ بِٱلنَّاسِ لَرَءُوفࣱ رَّحِیمࣱ ﴿143﴾

Choncho takusankhani (inu Asilamu) kukhala mpingo wabwino (wapakatikati) kuti mukhale mboni pa anthu ndi kuti Mtumiki (s.a.w) akhale mboni pa inu. Ndipo chibula (choyang’ana mbali ya ku Yerusalemu) chomwe udali nacho sitidachichite koma kuti timdziwitse (adziwike kwa anthu) amene akutsata Mtumiki (s.a.w), ndi yemwe akutembenukira m’mbuyo. Ndipo ndithudi, chidali chinthu chovuta kupatula kwa omwe Allah wawaongola. Ndipo nkosayenera kwa Allah kusokoneza Swala zanu, pakuti Allah Ngoleza kwabasi kwa anthu, Ngwachifundo chambiri. [6]

قَدۡ نَرَىٰ تَقَلُّبَ وَجۡهِكَ فِی ٱلسَّمَاۤءِۖ فَلَنُوَلِّیَنَّكَ قِبۡلَةࣰ تَرۡضَىٰهَاۚ فَوَلِّ وَجۡهَكَ شَطۡرَ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِۚ وَحَیۡثُ مَا كُنتُمۡ فَوَلُّوا۟ وُجُوهَكُمۡ شَطۡرَهُۥۗ وَإِنَّ ٱلَّذِینَ أُوتُوا۟ ٱلۡكِتَـٰبَ لَیَعۡلَمُونَ أَنَّهُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّهِمۡۗ وَمَا ٱللَّهُ بِغَـٰفِلٍ عَمَّا یَعۡمَلُونَ ﴿144﴾

Ndithudi, taona kutembenukatembenuka kwa nkhope yako (kuyang’ana) kumwamba. Choncho tikutembenuzira ku chibula chimene ukuchifunacho. Tero tembenuzira nkhope yako kumbali ya Msikiti Wopatulika (Al-Kaaba). Ndipo paliponse pamene mulipo yang’anitsani nkhope zanu kumene kuli (msikitiwo). Ndithudi amene adapatsidwa buku akudziwitsitsa kuti chimenecho nchoonadi chochokera kwa Mbuye wawo. Ndipo Allah siwonyalanyaza zimene akuchita. (Koma chilichonse chikulembedwa m’kaundula).

وَلَىِٕنۡ أَتَیۡتَ ٱلَّذِینَ أُوتُوا۟ ٱلۡكِتَـٰبَ بِكُلِّ ءَایَةࣲ مَّا تَبِعُوا۟ قِبۡلَتَكَۚ وَمَاۤ أَنتَ بِتَابِعࣲ قِبۡلَتَهُمۡۚ وَمَا بَعۡضُهُم بِتَابِعࣲ قِبۡلَةَ بَعۡضࣲۚ وَلَىِٕنِ ٱتَّبَعۡتَ أَهۡوَاۤءَهُم مِّنۢ بَعۡدِ مَا جَاۤءَكَ مِنَ ٱلۡعِلۡمِ إِنَّكَ إِذࣰا لَّمِنَ ٱلظَّـٰلِمِینَ ﴿145﴾

Ndipo awo adapatsidwa buku ngakhale utabwera ndi chisonyezo cha mtundu uliwonse satsata chibula chako, ngakhalenso iwe sutsata chibula chawo. Ndipo ena a iwo sali otsatira chibula cha ena (Akhrisitu satsata chibula cha Ayuda, ndipo Ayuda satsata chibula cha Akhrisitu). Ngati utsatira zofuna zawo, pambuyo pakuti kwakudzera kudziwa ndiye kuti ukhala mwa ochita zoipa.

ٱلَّذِینَ ءَاتَیۡنَـٰهُمُ ٱلۡكِتَـٰبَ یَعۡرِفُونَهُۥ كَمَا یَعۡرِفُونَ أَبۡنَاۤءَهُمۡۖ وَإِنَّ فَرِیقࣰا مِّنۡهُمۡ لَیَكۡتُمُونَ ٱلۡحَقَّ وَهُمۡ یَعۡلَمُونَ ﴿146﴾

Aja amene tidawapatsa buku akumuzindikira (Mtumiki Muhammad {s.a.w}) monga momwe amawazindikilira ana awo. Koma ena mwa iwo akubisa choonadi uku akudziwa.

ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُمۡتَرِینَ ﴿147﴾

(Kuyang’ana ku Al-Kaaba popemphera Swala ndicho) choonadi chomwe chachokera kwa Mbuye wako, choncho usakhale mmodzi mwa openekera.

وَلِكُلࣲّ وِجۡهَةٌ هُوَ مُوَلِّیهَاۖ فَٱسۡتَبِقُوا۟ ٱلۡخَیۡرَ ٰ⁠تِۚ أَیۡنَ مَا تَكُونُوا۟ یَأۡتِ بِكُمُ ٱللَّهُ جَمِیعًاۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَیۡءࣲ قَدِیرࣱ ﴿148﴾

Ndipo (mpingo) uliwonse udali ndi chibula chimene udali kuchilunjika. Choncho pikisanani pochita zabwino. Paliponse pamene mungakhale Allah adzakubweretsani nonsenu pamodzi (pa tsiku la chimaliziro). Ndithudi, Allah Ngokhoza chinthu chilichonse.

وَمِنۡ حَیۡثُ خَرَجۡتَ فَوَلِّ وَجۡهَكَ شَطۡرَ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِۖ وَإِنَّهُۥ لَلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَۗ وَمَا ٱللَّهُ بِغَـٰفِلٍ عَمَّا تَعۡمَلُونَ ﴿149﴾

Ndipo paliponse pomwe wapita tembenuzira nkhope yako kumbali ya Msikiti Wopatulika (panthawi yopemphera). Chimenecho nchoonadi chochokera kwa Mbuye wako. Ndipo Allah sali wonyalanyaza zimene mukuchita.

وَمِنۡ حَیۡثُ خَرَجۡتَ فَوَلِّ وَجۡهَكَ شَطۡرَ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِۚ وَحَیۡثُ مَا كُنتُمۡ فَوَلُّوا۟ وُجُوهَكُمۡ شَطۡرَهُۥ لِئَلَّا یَكُونَ لِلنَّاسِ عَلَیۡكُمۡ حُجَّةٌ إِلَّا ٱلَّذِینَ ظَلَمُوا۟ مِنۡهُمۡ فَلَا تَخۡشَوۡهُمۡ وَٱخۡشَوۡنِی وَلِأُتِمَّ نِعۡمَتِی عَلَیۡكُمۡ وَلَعَلَّكُمۡ تَهۡتَدُونَ ﴿150﴾

Paliponse pamene wapita (iwe Mtumiki {s.a.w}) tembenuzira nkhope yako kumbali ya Msikiti Wopatulika. Ndipo paliponse pamene (inu Asilamu) muli tembenuzirani nkhope zanu kumbali yake (ya Msikitio) kuti anthu asakhale ndi mtsutso pa inu, kupatula amene adzichitira zoipa mwa iwo. Tero musawaope, koma opani Ine, ndipo ndikwaniritsa chisomo Changa pa inu kuti muongoke.

كَمَاۤ أَرۡسَلۡنَا فِیكُمۡ رَسُولࣰا مِّنكُمۡ یَتۡلُوا۟ عَلَیۡكُمۡ ءَایَـٰتِنَا وَیُزَكِّیكُمۡ وَیُعَلِّمُكُمُ ٱلۡكِتَـٰبَ وَٱلۡحِكۡمَةَ وَیُعَلِّمُكُم مَّا لَمۡ تَكُونُوا۟ تَعۡلَمُونَ ﴿151﴾

Monganso tamtumizira Mtumiki (s.a.w) kwa inu wochokera mwa inu kuti akuwerengereni Ayah (ndime) Zathu, ndikukuyeretsani (kuuve wopembedza mafano) ndi kukuphunzitsani buku ndi nzeru, ndikukuphunzitsani zimene simunali kuzidziwa.

فَٱذۡكُرُونِیۤ أَذۡكُرۡكُمۡ وَٱشۡكُرُوا۟ لِی وَلَا تَكۡفُرُونِ ﴿152﴾

Choncho ndikumbukireni (pondithokoza pa mtendere umene ndakupatsaniwu). Nanenso ndikukumbukirani (pokulipirani mphoto yaikulu). Ndipo ndiyamikeni; musandikane.

یَـٰۤأَیُّهَا ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ ٱسۡتَعِینُوا۟ بِٱلصَّبۡرِ وَٱلصَّلَوٰةِۚ إِنَّ ٱللَّهَ مَعَ ٱلصَّـٰبِرِینَ ﴿153﴾

E inu amene mwakhulupirira! Dzithandizeni (pa zinthu zanu) popirira, ndi popemphera Swala. Ndithudi, Allah ali pamodzi ndi opirira. [7]

وَلَا تَقُولُوا۟ لِمَن یُقۡتَلُ فِی سَبِیلِ ٱللَّهِ أَمۡوَ ٰ⁠تُۢۚ بَلۡ أَحۡیَاۤءࣱ وَلَـٰكِن لَّا تَشۡعُرُونَ ﴿154﴾

Ndipo musanene za amene aphedwa pa njira ya Allah kuti: “Ngakufa.” Iyayi ngamoyo, koma inu simuzindikira.

وَلَنَبۡلُوَنَّكُم بِشَیۡءࣲ مِّنَ ٱلۡخَوۡفِ وَٱلۡجُوعِ وَنَقۡصࣲ مِّنَ ٱلۡأَمۡوَ ٰ⁠لِ وَٱلۡأَنفُسِ وَٱلثَّمَرَ ٰ⁠تِۗ وَبَشِّرِ ٱلصَّـٰبِرِینَ ﴿155﴾

Ndipo ndithu tikuyesani ndi chinachake monga mantha, njala, kuchepa kwa chuma, kutaika kwa miyoyo ndi kuonongeka kwa mbeu. Tero auze nkhani yabwino opirira.

ٱلَّذِینَ إِذَاۤ أَصَـٰبَتۡهُم مُّصِیبَةࣱ قَالُوۤا۟ إِنَّا لِلَّهِ وَإِنَّاۤ إِلَیۡهِ رَ ٰ⁠جِعُونَ ﴿156﴾

Omwe vuto lililonse likawapeza amati: “Ndithudi, ife nga Allah, ndipo ndithu kwa Iye tidzabwerera.”

أُو۟لَـٰۤىِٕكَ عَلَیۡهِمۡ صَلَوَ ٰ⁠تࣱ مِّن رَّبِّهِمۡ وَرَحۡمَةࣱۖ وَأُو۟لَـٰۤىِٕكَ هُمُ ٱلۡمُهۡتَدُونَ ﴿157﴾

Otero ndi amene pa iwo pali madalitso ochokera kwa Mbuye wawo ndi chifundo. Ndiponso iwo ndi amene ali oongoka.

۞ إِنَّ ٱلصَّفَا وَٱلۡمَرۡوَةَ مِن شَعَاۤىِٕرِ ٱللَّهِۖ فَمَنۡ حَجَّ ٱلۡبَیۡتَ أَوِ ٱعۡتَمَرَ فَلَا جُنَاحَ عَلَیۡهِ أَن یَطَّوَّفَ بِهِمَاۚ وَمَن تَطَوَّعَ خَیۡرࣰا فَإِنَّ ٱللَّهَ شَاكِرٌ عَلِیمٌ ﴿158﴾

Ndithudi, Safaa ndi Marwa ndizizindikiro zolemekezera chipembedzo cha Allah. Choncho, amene akukachita mapemphero a Hajj ku nyumbayo, kapena kuchita Umrah, sikulakwa kwa iye kuzungulira pamenepo (pakati pamapiri amenewo). Ndipo amene achite chabwino modzipereka (adzalipidwa). Ndithudi Allah Ngothokoza; Ngodziwa.[8]

إِنَّ ٱلَّذِینَ یَكۡتُمُونَ مَاۤ أَنزَلۡنَا مِنَ ٱلۡبَیِّنَـٰتِ وَٱلۡهُدَىٰ مِنۢ بَعۡدِ مَا بَیَّنَّـٰهُ لِلنَّاسِ فِی ٱلۡكِتَـٰبِ أُو۟لَـٰۤىِٕكَ یَلۡعَنُهُمُ ٱللَّهُ وَیَلۡعَنُهُمُ ٱللَّـٰعِنُونَ ﴿159﴾

Ndithudi, amene akubisa zimene tavumbulutsa zomwe ndi zisonyezo zoonekera poyera, ndi chiongoko pambuyo pozifotokoza mwatsatanetsatane kwa anthu m’Buku, Allah akuwatembelera iwo. Ndiponso akuwatembelera otembelera.[9]

إِلَّا ٱلَّذِینَ تَابُوا۟ وَأَصۡلَحُوا۟ وَبَیَّنُوا۟ فَأُو۟لَـٰۤىِٕكَ أَتُوبُ عَلَیۡهِمۡ وَأَنَا ٱلتَّوَّابُ ٱلرَّحِیمُ ﴿160﴾

Kupatula amene alapa ndi kukonza (zolakwika) nachilongosola (choonadicho kwa anthu), iwowo ndi amene ndiwalandira kulapa kwao. Ndipo ine Ngolandira kulapa kwambiri, Ngwachisoni chosatha.

إِنَّ ٱلَّذِینَ كَفَرُوا۟ وَمَاتُوا۟ وَهُمۡ كُفَّارٌ أُو۟لَـٰۤىِٕكَ عَلَیۡهِمۡ لَعۡنَةُ ٱللَّهِ وَٱلۡمَلَـٰۤىِٕكَةِ وَٱلنَّاسِ أَجۡمَعِینَ ﴿161﴾

Ndithudi, arnene sadakhulupirire, namwalira ali osakhulupirira, pa iwo pali matembelero a Allah, angelo ndi anthu onse.

خَـٰلِدِینَ فِیهَا لَا یُخَفَّفُ عَنۡهُمُ ٱلۡعَذَابُ وَلَا هُمۡ یُنظَرُونَ ﴿162﴾

M’menemo (m’chilango cha matembelero) adzakhalamo nthawi yaitali. Ndipo chilango sichidzapeputsidwa kwa iwo, ndipo sadzapatsidwa nthawi (yopumula).

وَإِلَـٰهُكُمۡ إِلَـٰهࣱ وَ ٰ⁠حِدࣱۖ لَّاۤ إِلَـٰهَ إِلَّا هُوَ ٱلرَّحۡمَـٰنُ ٱلرَّحِیمُ ﴿163﴾

Ndipo mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi basi. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ngwachifundo chambiri, Ngwachisoni chosatha.[10]

إِنَّ فِی خَلۡقِ ٱلسَّمَـٰوَ ٰ⁠تِ وَٱلۡأَرۡضِ وَٱخۡتِلَـٰفِ ٱلَّیۡلِ وَٱلنَّهَارِ وَٱلۡفُلۡكِ ٱلَّتِی تَجۡرِی فِی ٱلۡبَحۡرِ بِمَا یَنفَعُ ٱلنَّاسَ وَمَاۤ أَنزَلَ ٱللَّهُ مِنَ ٱلسَّمَاۤءِ مِن مَّاۤءࣲ فَأَحۡیَا بِهِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَا وَبَثَّ فِیهَا مِن كُلِّ دَاۤبَّةࣲ وَتَصۡرِیفِ ٱلرِّیَـٰحِ وَٱلسَّحَابِ ٱلۡمُسَخَّرِ بَیۡنَ ٱلسَّمَاۤءِ وَٱلۡأَرۡضِ لَـَٔایَـٰتࣲ لِّقَوۡمࣲ یَعۡقِلُونَ ﴿164﴾

Ndithudi, m’kulenga kwa thambo ndi nthaka, ndi kusinthana kwa usiku ndi usana, ndi (kuyenda kwa) zombo zikulu-zikulu zomwe zikuyenda pa nyanja (zitasenza zinthu) zothandiza anthu, ndi madzi amene Allah wawatsitsa kuchokera ku mitambo, naukitsira nawo nthaka pambuyo pokhala youma, nawanditsa m’menemo mtundu uliwonse wa nyama (chifukwa cha madziwo), ndi m’kusinthanasinthana kwa mphepo, ndi mitambo yomwe yalamulidwa kuyenda pakati pa thambo ndi nthaka; ndithudi, (m’mzimenezo) muli zisonyezo kwa anthu anzeru, (kuti Allah alipo).

وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن یَتَّخِذُ مِن دُونِ ٱللَّهِ أَندَادࣰا یُحِبُّونَهُمۡ كَحُبِّ ٱللَّهِۖ وَٱلَّذِینَ ءَامَنُوۤا۟ أَشَدُّ حُبࣰّا لِّلَّهِۗ وَلَوۡ یَرَى ٱلَّذِینَ ظَلَمُوۤا۟ إِذۡ یَرَوۡنَ ٱلۡعَذَابَ أَنَّ ٱلۡقُوَّةَ لِلَّهِ جَمِیعࣰا وَأَنَّ ٱللَّهَ شَدِیدُ ٱلۡعَذَابِ ﴿165﴾

Pali ena mwa anthu amene akudzipangira milungu naifanizira ndi Allah. Amaikonda monga momwe akadamkondera Allah. Koma (Asilamu) amene akhulupirira amamkonda Allah koposa. Ndipo akadaona amene adzichitira zoipa pamene azikachiona chilango (akadazindikira kuti) ndithu mphamvu zonse nza Allah, ndipo ndithu Allah Ngolanga mwaukali.

إِذۡ تَبَرَّأَ ٱلَّذِینَ ٱتُّبِعُوا۟ مِنَ ٱلَّذِینَ ٱتَّبَعُوا۟ وَرَأَوُا۟ ٱلۡعَذَابَ وَتَقَطَّعَتۡ بِهِمُ ٱلۡأَسۡبَابُ ﴿166﴾

(Akumbutse) nthawi imene otsatidwa adzawakana amene adali kuwatsata uku atachiona chilango. Ndipo mgwirizano pakati pawo udzaduka.

وَقَالَ ٱلَّذِینَ ٱتَّبَعُوا۟ لَوۡ أَنَّ لَنَا كَرَّةࣰ فَنَتَبَرَّأَ مِنۡهُمۡ كَمَا تَبَرَّءُوا۟ مِنَّاۗ كَذَ ٰ⁠لِكَ یُرِیهِمُ ٱللَّهُ أَعۡمَـٰلَهُمۡ حَسَرَ ٰ⁠تٍ عَلَیۡهِمۡۖ وَمَا هُم بِخَـٰرِجِینَ مِنَ ٱلنَّارِ ﴿167﴾

Ndipo otsatirawo adzati: “Kukadakhala kotheka kwa ife kubwerera (ku moyo wa pa dziko) tikadawakana monga iwo atikanira.” Umo ndi momwe Allah adzikawaonetsera zochita zawo kukhala madandaulo awo. Ndipo iwo sadzatulukanso ku Moto.

یَـٰۤأَیُّهَا ٱلنَّاسُ كُلُوا۟ مِمَّا فِی ٱلۡأَرۡضِ حَلَـٰلࣰا طَیِّبࣰا وَلَا تَتَّبِعُوا۟ خُطُوَ ٰ⁠تِ ٱلشَّیۡطَـٰنِۚ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوࣱّ مُّبِینٌ ﴿168﴾

E, inu anthu! Idyani zabwino zimene zili m’nthaka zomwe zili zololedwa; ndipo musatsate mapazi a satana. Iye kwa inu ndi mdani woonekeratu.[11]

إِنَّمَا یَأۡمُرُكُم بِٱلسُّوۤءِ وَٱلۡفَحۡشَاۤءِ وَأَن تَقُولُوا۟ عَلَى ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ ﴿169﴾

Ndithu iye amangokulamulani kuchita zoipa ndi zauve, ndikuti mumnamizire Allah pomunenera zimene simukuzidziwa.

وَإِذَا قِیلَ لَهُمُ ٱتَّبِعُوا۟ مَاۤ أَنزَلَ ٱللَّهُ قَالُوا۟ بَلۡ نَتَّبِعُ مَاۤ أَلۡفَیۡنَا عَلَیۡهِ ءَابَاۤءَنَاۤۚ أَوَلَوۡ كَانَ ءَابَاۤؤُهُمۡ لَا یَعۡقِلُونَ شَیۡـࣰٔا وَلَا یَهۡتَدُونَ ﴿170﴾

Ndipo kukanenedwa kwa iwo (kuti): “Tsatirani zimene Allah wavumbulutsa;” akunena: “Koma tikutsatira zimene tidawapeza nazo atate athu.” Kodi ngakhale kuti atate awo sadali kuzindikira chilichonse ndiponso sadali oongoka (awatsatirabe)?[12]

وَمَثَلُ ٱلَّذِینَ كَفَرُوا۟ كَمَثَلِ ٱلَّذِی یَنۡعِقُ بِمَا لَا یَسۡمَعُ إِلَّا دُعَاۤءࣰ وَنِدَاۤءࣰۚ صُمُّۢ بُكۡمٌ عُمۡیࣱ فَهُمۡ لَا یَعۡقِلُونَ ﴿171﴾

Ndipo fanizo la amene sadakhulupirire (omwe akulalikidwa mawu a Allah, ndi makani awo) lili ngati (mbusa) yemwe akukuwira ziweto zake ndi kuzikalipira pomwe izo sizimva tanthauzo la mawu oitanawo, koma kuitana (chabe) ndi kufuula. (Iwo) ndi agonthi, abubu ndi akhungu. Tero iwo sangazindikire.

یَـٰۤأَیُّهَا ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ كُلُوا۟ مِن طَیِّبَـٰتِ مَا رَزَقۡنَـٰكُمۡ وَٱشۡكُرُوا۟ لِلَّهِ إِن كُنتُمۡ إِیَّاهُ تَعۡبُدُونَ ﴿172﴾

E inu amene mwakhulupirira! Idyani zinthu zabwino zimene takupatsani, ndipo yamikani Allah ngatidi inu mukumpembedza Iye yekha.

إِنَّمَا حَرَّمَ عَلَیۡكُمُ ٱلۡمَیۡتَةَ وَٱلدَّمَ وَلَحۡمَ ٱلۡخِنزِیرِ وَمَاۤ أُهِلَّ بِهِۦ لِغَیۡرِ ٱللَّهِۖ فَمَنِ ٱضۡطُرَّ غَیۡرَ بَاغࣲ وَلَا عَادࣲ فَلَاۤ إِثۡمَ عَلَیۡهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورࣱ رَّحِیمٌ ﴿173﴾

Iye akukuletsani (kudya) nyama yofa yokha, liwende, nyama yankhumba ndi nyama yodulidwa poikuwira mayina a mafano kusiya Allah. Koma amene wasimidwa (nadya) popanda kuchikhumba choletsedwacho ndi mosapyoza muyeso palibe tchimo kwa iye. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi.[13]

إِنَّ ٱلَّذِینَ یَكۡتُمُونَ مَاۤ أَنزَلَ ٱللَّهُ مِنَ ٱلۡكِتَـٰبِ وَیَشۡتَرُونَ بِهِۦ ثَمَنࣰا قَلِیلًا أُو۟لَـٰۤىِٕكَ مَا یَأۡكُلُونَ فِی بُطُونِهِمۡ إِلَّا ٱلنَّارَ وَلَا یُكَلِّمُهُمُ ٱللَّهُ یَوۡمَ ٱلۡقِیَـٰمَةِ وَلَا یُزَكِّیهِمۡ وَلَهُمۡ عَذَابٌ أَلِیمٌ ﴿174﴾

Ndithudi, amene akubisa zomwe Allah adavumbulutsa m’buku (la Baibulo) m’malo mwake nasankha zinthu zamtengo wochepa, iwo sadya china mmimba mwawo koma moto basi; ndipo Allah sadzawayankhula tsiku lachimaliziro (mwachifundo koma mokwiya); ndipo sadzawayeretsa. Ndipo iwo adzapeza chilango chopweteka.[14]

أُو۟لَـٰۤىِٕكَ ٱلَّذِینَ ٱشۡتَرَوُا۟ ٱلضَّلَـٰلَةَ بِٱلۡهُدَىٰ وَٱلۡعَذَابَ بِٱلۡمَغۡفِرَةِۚ فَمَاۤ أَصۡبَرَهُمۡ عَلَى ٱلنَّارِ ﴿175﴾

Iwo ndi amene asinthanitsa kusokera ndi chiongoko, ndiponso chilango ndi chikhululuko. Kodi ndichiyani chikuwachititsa kukhala opirira ndi Moto.

ذَ ٰ⁠لِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ نَزَّلَ ٱلۡكِتَـٰبَ بِٱلۡحَقِّۗ وَإِنَّ ٱلَّذِینَ ٱخۡتَلَفُوا۟ فِی ٱلۡكِتَـٰبِ لَفِی شِقَاقِۭ بَعِیدࣲ ﴿176﴾

Zimenezo nchifukwa chakuti Allah adavumbulutsa buku Lake mwa choonadi (ndipo iwo adalikana). Koma amene asemphana pa zabukuli ali mu nkangano wonkera nawo kutali kusiya choonadi.

۞ لَّیۡسَ ٱلۡبِرَّ أَن تُوَلُّوا۟ وُجُوهَكُمۡ قِبَلَ ٱلۡمَشۡرِقِ وَٱلۡمَغۡرِبِ وَلَـٰكِنَّ ٱلۡبِرَّ مَنۡ ءَامَنَ بِٱللَّهِ وَٱلۡیَوۡمِ ٱلۡـَٔاخِرِ وَٱلۡمَلَـٰۤىِٕكَةِ وَٱلۡكِتَـٰبِ وَٱلنَّبِیِّـۧنَ وَءَاتَى ٱلۡمَالَ عَلَىٰ حُبِّهِۦ ذَوِی ٱلۡقُرۡبَىٰ وَٱلۡیَتَـٰمَىٰ وَٱلۡمَسَـٰكِینَ وَٱبۡنَ ٱلسَّبِیلِ وَٱلسَّاۤىِٕلِینَ وَفِی ٱلرِّقَابِ وَأَقَامَ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتَى ٱلزَّكَوٰةَ وَٱلۡمُوفُونَ بِعَهۡدِهِمۡ إِذَا عَـٰهَدُوا۟ۖ وَٱلصَّـٰبِرِینَ فِی ٱلۡبَأۡسَاۤءِ وَٱلضَّرَّاۤءِ وَحِینَ ٱلۡبَأۡسِۗ أُو۟لَـٰۤىِٕكَ ٱلَّذِینَ صَدَقُوا۟ۖ وَأُو۟لَـٰۤىِٕكَ هُمُ ٱلۡمُتَّقُونَ ﴿177﴾

Ubwino suli potembenuzira nkhope zanu mbali yakuvuma ndi kuzambwe (popemphera Swala); koma ubwino weniweni ndi (wa omwe) akukhulupirira Allah, tsiku lachimaliziro, angelo, buku ndi aneneri; napereka chuma - uku eni akuchifunabe - kwa achibale ndi amasiye, ndi masikini ndi a paulendo (omwe alibe choyendera), ndi opempha, ndi kuombolera akapolo; napemphera Swala, napereka chopereka (Zakaat); ndi okwaniritsa malonjezo awo akalonjeza, ndi opirira ndi umphawi ndi matenda ndi panthawi yankhondo. Iwowo ndi amene atsimikiza (Chisilamu chawo). Ndiponso iwowo ndi omwe ali oopa Allah.

یَـٰۤأَیُّهَا ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ كُتِبَ عَلَیۡكُمُ ٱلۡقِصَاصُ فِی ٱلۡقَتۡلَىۖ ٱلۡحُرُّ بِٱلۡحُرِّ وَٱلۡعَبۡدُ بِٱلۡعَبۡدِ وَٱلۡأُنثَىٰ بِٱلۡأُنثَىٰۚ فَمَنۡ عُفِیَ لَهُۥ مِنۡ أَخِیهِ شَیۡءࣱ فَٱتِّبَاعُۢ بِٱلۡمَعۡرُوفِ وَأَدَاۤءٌ إِلَیۡهِ بِإِحۡسَـٰنࣲۗ ذَ ٰ⁠لِكَ تَخۡفِیفࣱ مِّن رَّبِّكُمۡ وَرَحۡمَةࣱۗ فَمَنِ ٱعۡتَدَىٰ بَعۡدَ ذَ ٰ⁠لِكَ فَلَهُۥ عَذَابٌ أَلِیمࣱ ﴿178﴾

E inu amene mwakhulupirira! Kwalamulidwa kwa inu Qiswas (kubwezerana) molingana kwa ophedwa; mfulu kwa mfulu, kapolo kwa kapolo, mkazi kwa mkazi. Koma amene wakhululukidwa ndi m’bale wakeyo pa chinthu Chilichonse, atsatire ndi kulonjelera dipolo mwaubwino. (Nayenso wolipa) apereke kwa iye mwa ubwino. Kumeneko ndikufewetsa kumene kwachokera kwa Mbuye wanu, ndiponso chifundo. Ndipo amene alumphe malire pambuyo pa izi, iye adzapeza chilango chopweteka.[15]

وَلَكُمۡ فِی ٱلۡقِصَاصِ حَیَوٰةࣱ یَـٰۤأُو۟لِی ٱلۡأَلۡبَـٰبِ لَعَلَّكُمۡ تَتَّقُونَ ﴿179﴾

Mu Qiswas (kubwezerana kofanana) muli kusunga moyo kwa inu, E, inu eni nzeru! Kuti mudzitchinjirize (ku mchitidwe ophana).[16]

كُتِبَ عَلَیۡكُمۡ إِذَا حَضَرَ أَحَدَكُمُ ٱلۡمَوۡتُ إِن تَرَكَ خَیۡرًا ٱلۡوَصِیَّةُ لِلۡوَ ٰ⁠لِدَیۡنِ وَٱلۡأَقۡرَبِینَ بِٱلۡمَعۡرُوفِۖ حَقًّا عَلَى ٱلۡمُتَّقِینَ ﴿180﴾

Kwalamulidwa kwa inu kuti mmodzi wanu imfa ikamuyandikira, ngati asiya chuma, apereke malangizo (pa zachumacho) kwa makolo ake awiri ndi achibale ake, mwa ubwino. Ichi nchilamulo kwa oopa Allah.[17]

فَمَنۢ بَدَّلَهُۥ بَعۡدَ مَا سَمِعَهُۥ فَإِنَّمَاۤ إِثۡمُهُۥ عَلَى ٱلَّذِینَ یُبَدِّلُونَهُۥۤۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَمِیعٌ عَلِیمࣱ ﴿181﴾

Ndipo amene asinthe malangizowo pambuyo pakuwamva; uchimo wake uli pa amene akusinthawo. Ndithudi, Allah Ngwakumva; Ngodziwa.[18]

فَمَنۡ خَافَ مِن مُّوصࣲ جَنَفًا أَوۡ إِثۡمࣰا فَأَصۡلَحَ بَیۡنَهُمۡ فَلَاۤ إِثۡمَ عَلَیۡهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورࣱ رَّحِیمࣱ ﴿182﴾

Ndipo amene waopa kuti wopereka wasiya angapendekere kumbali yokhota kapena ku uchimo, nalinganiza pakati pawo, palibe tchimo kwa iye. Ndithudi, Allah ngokhululuka zedi, Ngwachifundo chambiri.

یَـٰۤأَیُّهَا ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ كُتِبَ عَلَیۡكُمُ ٱلصِّیَامُ كَمَا كُتِبَ عَلَى ٱلَّذِینَ مِن قَبۡلِكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تَتَّقُونَ ﴿183﴾

E inu amene mwakhulupirira! Kwalamulidwa kwa inu kusala (m’mwezi wa Ramadan) monga momwe kudalamulidwira kwa anthu akale, inu musadabwere kuti muope Allah (popewa zoletsedwa).

أَیَّامࣰا مَّعۡدُودَ ٰ⁠تࣲۚ فَمَن كَانَ مِنكُم مَّرِیضًا أَوۡ عَلَىٰ سَفَرࣲ فَعِدَّةࣱ مِّنۡ أَیَّامٍ أُخَرَۚ وَعَلَى ٱلَّذِینَ یُطِیقُونَهُۥ فِدۡیَةࣱ طَعَامُ مِسۡكِینࣲۖ فَمَن تَطَوَّعَ خَیۡرࣰا فَهُوَ خَیۡرࣱ لَّهُۥۚ وَأَن تَصُومُوا۟ خَیۡرࣱ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ ﴿184﴾

(Kusalaku nkwa) masiku owerengeka. Koma amene akhale odwala mwa inu kapena akhale paulendo, (namasula masiku ena), akwaniritse chiwerengerocho m’masiku ena. Ndipo kwa amene sangathe kusala apereke dipo lodyetsa masikini. Ndipo amene achite zabwino mwa chifuniro chake, kutero ndibwino kwa iye. Ndipo kusala (pamene kukulolezedwa kumasula) ndibwino kwa inu, ngati muli odziwadi (kufunika kwa kusala).[19]

شَهۡرُ رَمَضَانَ ٱلَّذِیۤ أُنزِلَ فِیهِ ٱلۡقُرۡءَانُ هُدࣰى لِّلنَّاسِ وَبَیِّنَـٰتࣲ مِّنَ ٱلۡهُدَىٰ وَٱلۡفُرۡقَانِۚ فَمَن شَهِدَ مِنكُمُ ٱلشَّهۡرَ فَلۡیَصُمۡهُۖ وَمَن كَانَ مَرِیضًا أَوۡ عَلَىٰ سَفَرࣲ فَعِدَّةࣱ مِّنۡ أَیَّامٍ أُخَرَۗ یُرِیدُ ٱللَّهُ بِكُمُ ٱلۡیُسۡرَ وَلَا یُرِیدُ بِكُمُ ٱلۡعُسۡرَ وَلِتُكۡمِلُوا۟ ٱلۡعِدَّةَ وَلِتُكَبِّرُوا۟ ٱللَّهَ عَلَىٰ مَا هَدَىٰكُمۡ وَلَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ ﴿185﴾

(Mwezi mwalamulidwa kusalawu ndi) mwezi wa Ramadan womwe mkati mwake Qur’an idavumbulutsidwa kuti ikhale chiongoko kwa anthu ndi zizindikiro zoonekera poyera za chiongoko. Ndikutinso ikhale cholekanitsa (pakati pa choonadi ndi bodza). Ndipo mwa inu amene akhalepo (pa mudzi) m’mweziwu, asale. Koma amene ali wodwala, kapena ali pa ulendo, akwaniritse chiwerengero m’masiku ena (cha masiku amene sadasale). Allah akukufunirani zopepuka ndipo samakufunirani zovuta, ndiponso (akufuna) kuti mukwaniritse chiwerengerocho ndi kumlemekeza Allah chifukwa chakuti wakutsogolerani, ndikutinso mukhale othokoza.[20]

وَإِذَا سَأَلَكَ عِبَادِی عَنِّی فَإِنِّی قَرِیبٌۖ أُجِیبُ دَعۡوَةَ ٱلدَّاعِ إِذَا دَعَانِۖ فَلۡیَسۡتَجِیبُوا۟ لِی وَلۡیُؤۡمِنُوا۟ بِی لَعَلَّهُمۡ یَرۡشُدُونَ ﴿186﴾

Ndipo akapolo anga akakufunsa za ine, (auze kuti) Ine ndili pafupi nawo. Ndimayankha zopempha za wopempha pamene akundipempha. Choncho iwo ayankhe kuitana kwanga ndipo andikhulupirire kuti aongoke. [21]

أُحِلَّ لَكُمۡ لَیۡلَةَ ٱلصِّیَامِ ٱلرَّفَثُ إِلَىٰ نِسَاۤىِٕكُمۡۚ هُنَّ لِبَاسࣱ لَّكُمۡ وَأَنتُمۡ لِبَاسࣱ لَّهُنَّۗ عَلِمَ ٱللَّهُ أَنَّكُمۡ كُنتُمۡ تَخۡتَانُونَ أَنفُسَكُمۡ فَتَابَ عَلَیۡكُمۡ وَعَفَا عَنكُمۡۖ فَٱلۡـَٔـٰنَ بَـٰشِرُوهُنَّ وَٱبۡتَغُوا۟ مَا كَتَبَ ٱللَّهُ لَكُمۡۚ وَكُلُوا۟ وَٱشۡرَبُوا۟ حَتَّىٰ یَتَبَیَّنَ لَكُمُ ٱلۡخَیۡطُ ٱلۡأَبۡیَضُ مِنَ ٱلۡخَیۡطِ ٱلۡأَسۡوَدِ مِنَ ٱلۡفَجۡرِۖ ثُمَّ أَتِمُّوا۟ ٱلصِّیَامَ إِلَى ٱلَّیۡلِۚ وَلَا تُبَـٰشِرُوهُنَّ وَأَنتُمۡ عَـٰكِفُونَ فِی ٱلۡمَسَـٰجِدِۗ تِلۡكَ حُدُودُ ٱللَّهِ فَلَا تَقۡرَبُوهَاۗ كَذَ ٰ⁠لِكَ یُبَیِّنُ ٱللَّهُ ءَایَـٰتِهِۦ لِلنَّاسِ لَعَلَّهُمۡ یَتَّقُونَ ﴿187﴾

Kwaloledwa kwa inu mu usiku wosala kukumana ndi akazi anu. Iwo ali ngati chovala chanu, inunso muli ngati chovala chawo. Allah wadziwa kuti mudali kudzichitira chinyengo nokha. Choncho walandira kulapa kwanu ndipo wakukhululukirani. Tsopano khudzanani nawo ndipo funani chimene Allah wakulamulirani, ndipo idyani ndi kumwa mpaka udziwike bwinobwino kwa inu ulusi woyera kuchokera ku ulusi wakuda kum’bandakucha (kufikira mudziwe kuti kucha kwalowa, usiku watha). Kenako kwaniritsani kusala mpaka dzuwa litalowa. Ndipo musakhudzane nawo (akazi anu) pamene inu mukuchita mbindikiro m’misikiti. Amenewo ndi malire a Allah; choncho musaayandikire. Motere ndimo Allah akulongosolera mwatsatanetsatane zisonyezo zake kwa anthu kuti akhale oopa Allah (potsatira malamulo ake ndi kusiya zoletsedwa). [22]

وَلَا تَأۡكُلُوۤا۟ أَمۡوَ ٰ⁠لَكُم بَیۡنَكُم بِٱلۡبَـٰطِلِ وَتُدۡلُوا۟ بِهَاۤ إِلَى ٱلۡحُكَّامِ لِتَأۡكُلُوا۟ فَرِیقࣰا مِّنۡ أَمۡوَ ٰ⁠لِ ٱلنَّاسِ بِٱلۡإِثۡمِ وَأَنتُمۡ تَعۡلَمُونَ ﴿188﴾

Ndipo musadye chuma chanu pakati panu mwachinyengo pochipereka kwa oweruza (m’njira ya ziphuphu) ndi cholinga choti mudye gawo la chuma cha anthu mwa uchimo uku inu mukudziwa.

۞ یَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلۡأَهِلَّةِۖ قُلۡ هِیَ مَوَ ٰ⁠قِیتُ لِلنَّاسِ وَٱلۡحَجِّۗ وَلَیۡسَ ٱلۡبِرُّ بِأَن تَأۡتُوا۟ ٱلۡبُیُوتَ مِن ظُهُورِهَا وَلَـٰكِنَّ ٱلۡبِرَّ مَنِ ٱتَّقَىٰۗ وَأۡتُوا۟ ٱلۡبُیُوتَ مِنۡ أَبۡوَ ٰ⁠بِهَاۚ وَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ لَعَلَّكُمۡ تُفۡلِحُونَ ﴿189﴾

Akukufunsa za miyezi nena: “Imeneyi ndi miyeso ya nthawi yozindikilira anthu zinthu zawo ndi nthawi ya Hajj.” Ndipo Siubwino kulowera m’nyumba zanu mbali ya kumbuyo kwake, koma ubwino ndiwayemwe akuopa Allah. Ndipo lowerani m’nyumba podzera m’makomo ake. Opani Allah kuti inu mupambane.[23]

وَقَـٰتِلُوا۟ فِی سَبِیلِ ٱللَّهِ ٱلَّذِینَ یُقَـٰتِلُونَكُمۡ وَلَا تَعۡتَدُوۤا۟ۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا یُحِبُّ ٱلۡمُعۡتَدِینَ ﴿190﴾

Ndipo menyanani nao nkhondo pa njira ya Allah (modziteteza) amene akukuthirani nkhondo. Koma musalumphe malire (powamenya amene sadakuputeni), ndithu Allah sakonda olumpha malire.[24]

وَٱقۡتُلُوهُمۡ حَیۡثُ ثَقِفۡتُمُوهُمۡ وَأَخۡرِجُوهُم مِّنۡ حَیۡثُ أَخۡرَجُوكُمۡۚ وَٱلۡفِتۡنَةُ أَشَدُّ مِنَ ٱلۡقَتۡلِۚ وَلَا تُقَـٰتِلُوهُمۡ عِندَ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِ حَتَّىٰ یُقَـٰتِلُوكُمۡ فِیهِۖ فَإِن قَـٰتَلُوكُمۡ فَٱقۡتُلُوهُمۡۗ كَذَ ٰ⁠لِكَ جَزَاۤءُ ٱلۡكَـٰفِرِینَ ﴿191﴾

Ndipo athireni nkhondo (amene akukuthirani nkhondo popanda chifukwa) paliponse pamene mwawapeza; ndipo atulutseni paliponse pamene adakutulutsani; chifukwa kusokoneza anthu pa chipembedzo chawo nkoipitsitsa kuposa kupha. Koma musamenyane nawo pafupi ndi Msikiti Wopatulika pokhapokha atayamba ndiwo kukumenyani pamenepo. Chomwecho ngati atamenyana nanu pamenepo inunso amenyeni. Motero ndi momwe ilili mphoto ya osakhulupirira.

فَإِنِ ٱنتَهَوۡا۟ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَفُورࣱ رَّحِیمࣱ ﴿192﴾

Koma ngati asiya, ndithudi Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.

وَقَـٰتِلُوهُمۡ حَتَّىٰ لَا تَكُونَ فِتۡنَةࣱ وَیَكُونَ ٱلدِّینُ لِلَّهِۖ فَإِنِ ٱنتَهَوۡا۟ فَلَا عُدۡوَ ٰ⁠نَ إِلَّا عَلَى ٱلظَّـٰلِمِینَ ﴿193﴾

Ndipo menyanani nao kufikira pasakhale masautso (ochokera kwa iwo powasautsa asilamu popanda chifukwa). Ndipo chipembedzo chikhale cha Allah (osati kupembedza anthu). Koma ngati asiya, pasakhale mtopola kupatula kwa okhawo amene ali ochita zoipa.

ٱلشَّهۡرُ ٱلۡحَرَامُ بِٱلشَّهۡرِ ٱلۡحَرَامِ وَٱلۡحُرُمَـٰتُ قِصَاصࣱۚ فَمَنِ ٱعۡتَدَىٰ عَلَیۡكُمۡ فَٱعۡتَدُوا۟ عَلَیۡهِ بِمِثۡلِ مَا ٱعۡتَدَىٰ عَلَیۡكُمۡۚ وَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ وَٱعۡلَمُوۤا۟ أَنَّ ٱللَّهَ مَعَ ٱلۡمُتَّقِینَ ﴿194﴾

Mwezi wopatulika kwa mwezi wopatulika; ndipo zinthu zopatulika paikidwa kubwezerana. Ndipo amene wakuchitirani mtopola, inunso mchitireni mtopola molingana ndi momwe wakuchitirani mtopola, ndipo opani Allah (musapyoze kuposa momwe wakuchitirani). Ndipo dziwani kuti Allah ali pamodzi ndi oopa.

وَأَنفِقُوا۟ فِی سَبِیلِ ٱللَّهِ وَلَا تُلۡقُوا۟ بِأَیۡدِیكُمۡ إِلَى ٱلتَّهۡلُكَةِ وَأَحۡسِنُوۤا۟ۚ إِنَّ ٱللَّهَ یُحِبُّ ٱلۡمُحۡسِنِینَ ﴿195﴾

Ndipo perekani chuma chanu pa njira ya Allah, ndiponso musadziponye ku chionongeko ndi manja anu; chitani zabwino. Ndithudi, Allah amakonda ochita zabwino.

وَأَتِمُّوا۟ ٱلۡحَجَّ وَٱلۡعُمۡرَةَ لِلَّهِۚ فَإِنۡ أُحۡصِرۡتُمۡ فَمَا ٱسۡتَیۡسَرَ مِنَ ٱلۡهَدۡیِۖ وَلَا تَحۡلِقُوا۟ رُءُوسَكُمۡ حَتَّىٰ یَبۡلُغَ ٱلۡهَدۡیُ مَحِلَّهُۥۚ فَمَن كَانَ مِنكُم مَّرِیضًا أَوۡ بِهِۦۤ أَذࣰى مِّن رَّأۡسِهِۦ فَفِدۡیَةࣱ مِّن صِیَامٍ أَوۡ صَدَقَةٍ أَوۡ نُسُكࣲۚ فَإِذَاۤ أَمِنتُمۡ فَمَن تَمَتَّعَ بِٱلۡعُمۡرَةِ إِلَى ٱلۡحَجِّ فَمَا ٱسۡتَیۡسَرَ مِنَ ٱلۡهَدۡیِۚ فَمَن لَّمۡ یَجِدۡ فَصِیَامُ ثَلَـٰثَةِ أَیَّامࣲ فِی ٱلۡحَجِّ وَسَبۡعَةٍ إِذَا رَجَعۡتُمۡۗ تِلۡكَ عَشَرَةࣱ كَامِلَةࣱۗ ذَ ٰ⁠لِكَ لِمَن لَّمۡ یَكُنۡ أَهۡلُهُۥ حَاضِرِی ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِۚ وَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ وَٱعۡلَمُوۤا۟ أَنَّ ٱللَّهَ شَدِیدُ ٱلۡعِقَابِ ﴿196﴾

Ndipo kwaniritsani Hajj ndi Umrah chifukwa chofuna kukondweretsa Allah. (Izi zili mkutsimikiza kulowa m’mapemphero a Hajj). Ndipo ngati mutatsekerezedwa (kukwaniritsa mapempherowo), choncho zingani nyama zimene zili zosavuta kuzipeza (monga mbuzi), ndipo musamete mitu yanu kufikira nsembeyo ifike pamalo pake pozingirapo (pomwe ndi pamalo pamene mwatsekerezedwapo). Ndipo amene mwa inu ali odwala kapena ali ndi zovutitsa ku mutu kwake, (nachita zomwe zidali zoletsedwa monga kumeta) apereke dipo la kusala kapena kupereka sadaka (chopereka chaulere), kapena kuzinga chinyama. Ndipo ngati muli pa mtendere, choncho amene angadzisangalatse pochita Umrah kenako nkuchita Hajj, azinge nyama imene ili yosavuta kupezeka (monga mbuzi). Ndipo Amene sadapeze, asale masiku atatu konko ku hajjiko ndipo asalenso masiku asanu ndi awiri mutabwerera (kwanu). Amenewo ndi masiku khumi okwanira. Lamuloli ndi la yemwe banja lake silili pafupi ndi Msikiti Wopatulika. Ndipo opani Allah, dziwani kuti Allah Ngwaukali polanga.

ٱلۡحَجُّ أَشۡهُرࣱ مَّعۡلُومَـٰتࣱۚ فَمَن فَرَضَ فِیهِنَّ ٱلۡحَجَّ فَلَا رَفَثَ وَلَا فُسُوقَ وَلَا جِدَالَ فِی ٱلۡحَجِّۗ وَمَا تَفۡعَلُوا۟ مِنۡ خَیۡرࣲ یَعۡلَمۡهُ ٱللَّهُۗ وَتَزَوَّدُوا۟ فَإِنَّ خَیۡرَ ٱلزَّادِ ٱلتَّقۡوَىٰۖ وَٱتَّقُونِ یَـٰۤأُو۟لِی ٱلۡأَلۡبَـٰبِ ﴿197﴾

(Mapemphero a) Hajj ali ndi miyezi yodziwika, (yomwe ndi: Shawwal, Dhul Qa’da ndi Dhul Hijjah). Amene watsimikiza kuchita Hajj m’miyezi imeneyo, asachite ndi kuyankhula zauve, ndiponso asapandukire malamulo (pochita zoletsedwa uku iye ali m’mapemphero a Hajj), ndiponso asakangane ali m’Hajjimo. Ndipo chabwino chilichonse chimene mungachite, Allah achidziwa. Ndipo dzikonzereni kamba wa paulendo, ndithu kamba wabwino (wadziko lapansi) ndi amene angakupewetseni kupemphapempha, (koma kamba wabwino wa tsiku lachimaliziro ndiko kuopa Allah). Choncho ndiopeni inu eni nzeru.

لَیۡسَ عَلَیۡكُمۡ جُنَاحٌ أَن تَبۡتَغُوا۟ فَضۡلࣰا مِّن رَّبِّكُمۡۚ فَإِذَاۤ أَفَضۡتُم مِّنۡ عَرَفَـٰتࣲ فَٱذۡكُرُوا۟ ٱللَّهَ عِندَ ٱلۡمَشۡعَرِ ٱلۡحَرَامِۖ وَٱذۡكُرُوهُ كَمَا هَدَىٰكُمۡ وَإِن كُنتُم مِّن قَبۡلِهِۦ لَمِنَ ٱلضَّاۤلِّینَ ﴿198﴾

Sikulakwa kwa inu kufunafuna zabwino kwa Mbuye wanu (pogulitsa zinthu zanu uku muli m’mapemphero a Hajj, kapena kugula). Ndipo mukabwerera kuchokera ku Arafat, tamandani Allah pamalo otchedwa Masha’r Harâm (Muzdalifa). Ndipo mkumbukireni monga momwe adakutsogolerani, chikhalirecho kale mudali mwa osokera.

ثُمَّ أَفِیضُوا۟ مِنۡ حَیۡثُ أَفَاضَ ٱلنَّاسُ وَٱسۡتَغۡفِرُوا۟ ٱللَّهَۚ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورࣱ رَّحِیمࣱ ﴿199﴾

Kenako yendani limodzi kuchokera pamalo pamene akuchokerapo anthu onse (pomwe ndi pa Arafat), ndipo pemphani chikhululuko kwa Allah. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.

فَإِذَا قَضَیۡتُم مَّنَـٰسِكَكُمۡ فَٱذۡكُرُوا۟ ٱللَّهَ كَذِكۡرِكُمۡ ءَابَاۤءَكُمۡ أَوۡ أَشَدَّ ذِكۡرࣰاۗ فَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن یَقُولُ رَبَّنَاۤ ءَاتِنَا فِی ٱلدُّنۡیَا وَمَا لَهُۥ فِی ٱلۡـَٔاخِرَةِ مِنۡ خَلَـٰقࣲ ﴿200﴾

Ndipo mukamaliza mapemphero anu (tsiku la Idi komwe ndikuponya sangalawe, kuzinga nyama za nsembe, kumeta ndi kuzungulira Ka’aba (Tawaful Ifâda), mtamandeni Allah monga momwe mudali kutamandira makolo anu kapena mtamandeni koposa. Ndipo alipo ena mwa anthu amene akunena (kuti): “E Mbuye wathu! Tipatseni padziko lapansi.” Ndipo iwo alibe gawo lililonse pa tsiku lachimaliziro.

وَمِنۡهُم مَّن یَقُولُ رَبَّنَاۤ ءَاتِنَا فِی ٱلدُّنۡیَا حَسَنَةࣰ وَفِی ٱلۡـَٔاخِرَةِ حَسَنَةࣰ وَقِنَا عَذَابَ ٱلنَّارِ ﴿201﴾

Ndipo alipo ena mwa iwo omwe akunena kuti: “E Mbuye wathu! tipatseni zabwino pa dziko lapansi komanso pa tsiku lachimaliziro mudzatipatsenso zabwino, ndi kutitchinjiriza ku chilango cha Moto.”

أُو۟لَـٰۤىِٕكَ لَهُمۡ نَصِیبࣱ مِّمَّا كَسَبُوا۟ۚ وَٱللَّهُ سَرِیعُ ٱلۡحِسَابِ ﴿202﴾

Iwo ali ndi gawo la zimene adachita; ndipo Allah Ngwachangu pakuwerengera.

۞ وَٱذۡكُرُوا۟ ٱللَّهَ فِیۤ أَیَّامࣲ مَّعۡدُودَ ٰ⁠تࣲۚ فَمَن تَعَجَّلَ فِی یَوۡمَیۡنِ فَلَاۤ إِثۡمَ عَلَیۡهِ وَمَن تَأَخَّرَ فَلَاۤ إِثۡمَ عَلَیۡهِۖ لِمَنِ ٱتَّقَىٰۗ وَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ وَٱعۡلَمُوۤا۟ أَنَّكُمۡ إِلَیۡهِ تُحۡشَرُونَ ﴿203﴾

Ndipo mtamandeni Allah m’masiku owerengeka. Koma amene wachita changu pa masiku awiri okha (nabwerera kwawo) palibe tchimo pa iye. Ndipo amene wachedwerapo palibenso tchimo pa iye kwa amene akuopa Allah. Choncho opani Allah, ndipo dziwani kuti kwa Iye nkumene mudzasonkhanitsidwa.

وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن یُعۡجِبُكَ قَوۡلُهُۥ فِی ٱلۡحَیَوٰةِ ٱلدُّنۡیَا وَیُشۡهِدُ ٱللَّهَ عَلَىٰ مَا فِی قَلۡبِهِۦ وَهُوَ أَلَدُّ ٱلۡخِصَامِ ﴿204﴾

Ndipo mwa anthu alipo amene zoyankhula zake zikukondweretsa (iwe) pano pa dziko la pansi, (koma tsiku lachimaliziro kuipa kwake kudzadziwika). Ndipo iye akutsimikizira Allah kuti akhale mboni pa zomwe zili mu mtima mwake pomwe iye ndi wa makani kwambiri.[25]

وَإِذَا تَوَلَّىٰ سَعَىٰ فِی ٱلۡأَرۡضِ لِیُفۡسِدَ فِیهَا وَیُهۡلِكَ ٱلۡحَرۡثَ وَٱلنَّسۡلَۚ وَٱللَّهُ لَا یُحِبُّ ٱلۡفَسَادَ ﴿205﴾

Koma akachoka (kwa iwe) akuyenda pa dziko (uku ndi uku) ncholinga chofuna kuyipitsapo ndi kuononga zomera ndi miyoyo. Komatu Allah sakonda kuononga.

وَإِذَا قِیلَ لَهُ ٱتَّقِ ٱللَّهَ أَخَذَتۡهُ ٱلۡعِزَّةُ بِٱلۡإِثۡمِۚ فَحَسۡبُهُۥ جَهَنَّمُۖ وَلَبِئۡسَ ٱلۡمِهَادُ ﴿206﴾

Ndipo akauzidwa kuti: “Opa Allah”, Akugwidwa ndi mwano womupititsa ku machimo, choncho Jahannam ikukwana kwa iye (kuwuchotsa mwano wakewo). Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!

وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن یَشۡرِی نَفۡسَهُ ٱبۡتِغَاۤءَ مَرۡضَاتِ ٱللَّهِۚ وَٱللَّهُ رَءُوفُۢ بِٱلۡعِبَادِ ﴿207﴾

Ndipo pali wina mwa anthu amene akugulitsa mzimu wake chifukwa chofuna chiyanjo cha Allah; ndipo Allah Ngodekha kwa akapolo ake.[26]

یَـٰۤأَیُّهَا ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ ٱدۡخُلُوا۟ فِی ٱلسِّلۡمِ كَاۤفَّةࣰ وَلَا تَتَّبِعُوا۟ خُطُوَ ٰ⁠تِ ٱلشَّیۡطَـٰنِۚ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوࣱّ مُّبِینࣱ ﴿208﴾

E inu amene mwakhulupirira! Lowani m’Chisilamu chonse ndipo musatsatire mapazi a satana. Ndithu iye ndi mdani wanu woonekera poyera.[27]

فَإِن زَلَلۡتُم مِّنۢ بَعۡدِ مَا جَاۤءَتۡكُمُ ٱلۡبَیِّنَـٰتُ فَٱعۡلَمُوۤا۟ أَنَّ ٱللَّهَ عَزِیزٌ حَكِیمٌ ﴿209﴾

Ndipo ngati mutaterezuka (kuchimwa) pambuyo pokudzerani zisonyezo (za Allah) zoonekera poyera, dziwani kuti Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya.

هَلۡ یَنظُرُونَ إِلَّاۤ أَن یَأۡتِیَهُمُ ٱللَّهُ فِی ظُلَلࣲ مِّنَ ٱلۡغَمَامِ وَٱلۡمَلَـٰۤىِٕكَةُ وَقُضِیَ ٱلۡأَمۡرُۚ وَإِلَى ٱللَّهِ تُرۡجَعُ ٱلۡأُمُورُ ﴿210﴾

Kodi pali china chimene akuyembekeza posakhala kuwadzera Allah m’mithunzi ya mitambo ndi (kuwadzera) angelo; nkuweruzidwa chilamulo (chakuonongeka kwawo)? Komatu zinthu zonse zimabwezedwa kwa Allah.

سَلۡ بَنِیۤ إِسۡرَ ٰ⁠ۤءِیلَ كَمۡ ءَاتَیۡنَـٰهُم مِّنۡ ءَایَةِۭ بَیِّنَةࣲۗ وَمَن یُبَدِّلۡ نِعۡمَةَ ٱللَّهِ مِنۢ بَعۡدِ مَا جَاۤءَتۡهُ فَإِنَّ ٱللَّهَ شَدِیدُ ٱلۡعِقَابِ ﴿211﴾

Afunse ana a Israyeli kuti ndizizindikiro zingati zopenyeka zomwe tidawapatsa? Komatu amene angasinthe chisomo cha Allah pambuyo pomudzera, (Allah adzamulanga), ndithudi, Allah ngolanga mwaukali.

زُیِّنَ لِلَّذِینَ كَفَرُوا۟ ٱلۡحَیَوٰةُ ٱلدُّنۡیَا وَیَسۡخَرُونَ مِنَ ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ۘ وَٱلَّذِینَ ٱتَّقَوۡا۟ فَوۡقَهُمۡ یَوۡمَ ٱلۡقِیَـٰمَةِۗ وَٱللَّهُ یَرۡزُقُ مَن یَشَاۤءُ بِغَیۡرِ حِسَابࣲ ﴿212﴾

Moyo wa pa dziko lapansi wakometsedwa kwa amene sadakhulupirire, ndipo amawachitira chipongwe amene akhulupirira. Koma amene aopa Allah adzakhala pamwamba pawo tsiku la chiweruziro, ndipo Allah amapatsa amene wamfuna popanda chiwerengero.

كَانَ ٱلنَّاسُ أُمَّةࣰ وَ ٰ⁠حِدَةࣰ فَبَعَثَ ٱللَّهُ ٱلنَّبِیِّـۧنَ مُبَشِّرِینَ وَمُنذِرِینَ وَأَنزَلَ مَعَهُمُ ٱلۡكِتَـٰبَ بِٱلۡحَقِّ لِیَحۡكُمَ بَیۡنَ ٱلنَّاسِ فِیمَا ٱخۡتَلَفُوا۟ فِیهِۚ وَمَا ٱخۡتَلَفَ فِیهِ إِلَّا ٱلَّذِینَ أُوتُوهُ مِنۢ بَعۡدِ مَا جَاۤءَتۡهُمُ ٱلۡبَیِّنَـٰتُ بَغۡیَۢا بَیۡنَهُمۡۖ فَهَدَى ٱللَّهُ ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ لِمَا ٱخۡتَلَفُوا۟ فِیهِ مِنَ ٱلۡحَقِّ بِإِذۡنِهِۦۗ وَٱللَّهُ یَهۡدِی مَن یَشَاۤءُ إِلَىٰ صِرَ ٰ⁠طࣲ مُّسۡتَقِیمٍ ﴿213﴾

Anthu onse adali a chipembedzo chimodzi (cha Chisilamu panthawi ya Adam kufikira Nuh kenako adayamba kupatukana), ndipo Allah adatumiza aneneri onena nkhani zabwino ndi ochenjeza; ndipo pamodzi nawo adavumbulutsa mabuku achoonadi kuti aweruzire pakati pa anthu pa zimene adasemphana. Ndipo sadasemphane pa zimenezo koma aja amene adapatsidwa mabukuwo pambuyo powadzera zizindikiro zoonekera poyera, chifukwa chakuchitirana dumbo pakati pawo. Koma Allah adawaongolera amene adakhulupirira kuchoonadi cha zomwe adasempaniranazo, mwachifuniro chake. Ndipo Allah amamutsogolera ku njira yolunjika amene wamfuna.

أَمۡ حَسِبۡتُمۡ أَن تَدۡخُلُوا۟ ٱلۡجَنَّةَ وَلَمَّا یَأۡتِكُم مَّثَلُ ٱلَّذِینَ خَلَوۡا۟ مِن قَبۡلِكُمۖ مَّسَّتۡهُمُ ٱلۡبَأۡسَاۤءُ وَٱلضَّرَّاۤءُ وَزُلۡزِلُوا۟ حَتَّىٰ یَقُولَ ٱلرَّسُولُ وَٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ مَعَهُۥ مَتَىٰ نَصۡرُ ٱللَّهِۗ أَلَاۤ إِنَّ نَصۡرَ ٱللَّهِ قَرِیبࣱ ﴿214﴾

Kodi mukuganiza kuti mukalowa ku Munda wamtendere pomwe sanakudzereni masautso olingana (ndi omwe) adawapeza amene adamuka kale inu musanabadwe? Kusauka ndi matenda zidawakhudza, ndipo adanjenjemeretsedwa koopsa kufikira mtumiki pamodzi ndi amene adakhulupirira naye adati: “Chipulumutso cha Allah chibwera liti?” Dziwani kuti ndithu chipulumutso cha Allah chili pafupi![28]

یَسۡـَٔلُونَكَ مَاذَا یُنفِقُونَۖ قُلۡ مَاۤ أَنفَقۡتُم مِّنۡ خَیۡرࣲ فَلِلۡوَ ٰ⁠لِدَیۡنِ وَٱلۡأَقۡرَبِینَ وَٱلۡیَتَـٰمَىٰ وَٱلۡمَسَـٰكِینِ وَٱبۡنِ ٱلسَّبِیلِۗ وَمَا تَفۡعَلُوا۟ مِنۡ خَیۡرࣲ فَإِنَّ ٱللَّهَ بِهِۦ عَلِیمࣱ ﴿215﴾

Akukufunsa kuti apereke chiyani? Nena: “Chuma chilichonse chimene mungachipereke, (chiperekeni) kwa makolo awiri, achibale, kwa ana amasiye, kwa osauka, ndi kwa apaulendo. Ndipo chabwino chilichonse chimene mungachite, ndithudi, Allah akuchidziwa. ”[29]

كُتِبَ عَلَیۡكُمُ ٱلۡقِتَالُ وَهُوَ كُرۡهࣱ لَّكُمۡۖ وَعَسَىٰۤ أَن تَكۡرَهُوا۟ شَیۡـࣰٔا وَهُوَ خَیۡرࣱ لَّكُمۡۖ وَعَسَىٰۤ أَن تُحِبُّوا۟ شَیۡـࣰٔا وَهُوَ شَرࣱّ لَّكُمۡۚ وَٱللَّهُ یَعۡلَمُ وَأَنتُمۡ لَا تَعۡلَمُونَ ﴿216﴾

Kwalamulidwa kwa inu kumenya nkhondo (yotetezera chipembedzo cha Allah ) pomwe iyo (nkhondoyo) njodedwa ndi inu. Komatu mwina mungachide chinthu pomwe icho chili chahwino kwa inu. Mwinanso mungakonde chinthu pomwe icho chili choipa kwa inu. Koma Allah ndiyemwe akudziwa, ndipo inu simudziwa.

یَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلشَّهۡرِ ٱلۡحَرَامِ قِتَالࣲ فِیهِۖ قُلۡ قِتَالࣱ فِیهِ كَبِیرࣱۚ وَصَدٌّ عَن سَبِیلِ ٱللَّهِ وَكُفۡرُۢ بِهِۦ وَٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِ وَإِخۡرَاجُ أَهۡلِهِۦ مِنۡهُ أَكۡبَرُ عِندَ ٱللَّهِۚ وَٱلۡفِتۡنَةُ أَكۡبَرُ مِنَ ٱلۡقَتۡلِۗ وَلَا یَزَالُونَ یُقَـٰتِلُونَكُمۡ حَتَّىٰ یَرُدُّوكُمۡ عَن دِینِكُمۡ إِنِ ٱسۡتَطَـٰعُوا۟ۚ وَمَن یَرۡتَدِدۡ مِنكُمۡ عَن دِینِهِۦ فَیَمُتۡ وَهُوَ كَافِرࣱ فَأُو۟لَـٰۤىِٕكَ حَبِطَتۡ أَعۡمَـٰلُهُمۡ فِی ٱلدُّنۡیَا وَٱلۡـَٔاخِرَةِۖ وَأُو۟لَـٰۤىِٕكَ أَصۡحَـٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِیهَا خَـٰلِدُونَ ﴿217﴾

Akukufunsa za (lamulo la) kumenya nkhondo m’miyezi yopatulika. nena: “Kumenya nkhondo m’miyeziyo ndi tchimo lalikulu. Komatu kuwatsekereza anthu ku njira ya Allah, ndi kumkana Allah, (ndi kuletsa anthu) ku Msikiti Wopatulikawo, ndi kutulutsa anthu m’menemo nditchimo loposa kwa Allah. Ndipo kutsekereza anthu kuchipembedzo chawo nzoipa kwabasi kuposa kupha. Ndipo sasiya kumenyana nanu kufikira akuchotseni m’chipembedzo chanu ngati angathe. Ndipo mwa inu amene atuluke m’chipembedzo chake, kenako namwalira uku ali osakhulipirira, iwo ndi omwe ntchito zawo zaonongeka pa dziko lapansi mpaka tsiku lachimaliziro. Ndipo iwo ndi anthu a ku Moto. M’menemo adzakhalamo nthawi yaitali.[30]

إِنَّ ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ وَٱلَّذِینَ هَاجَرُوا۟ وَجَـٰهَدُوا۟ فِی سَبِیلِ ٱللَّهِ أُو۟لَـٰۤىِٕكَ یَرۡجُونَ رَحۡمَتَ ٱللَّهِۚ وَٱللَّهُ غَفُورࣱ رَّحِیمࣱ ﴿218﴾

Ndithudi, amene akhulupirira, ndi amene asamuka namenya nkhondo pa njira ya Allah, iwo ndi amene akuyembekezera chifundo cha Allah. Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.

۞ یَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلۡخَمۡرِ وَٱلۡمَیۡسِرِۖ قُلۡ فِیهِمَاۤ إِثۡمࣱ كَبِیرࣱ وَمَنَـٰفِعُ لِلنَّاسِ وَإِثۡمُهُمَاۤ أَكۡبَرُ مِن نَّفۡعِهِمَاۗ وَیَسۡـَٔلُونَكَ مَاذَا یُنفِقُونَۖ قُلِ ٱلۡعَفۡوَۗ كَذَ ٰ⁠لِكَ یُبَیِّنُ ٱللَّهُ لَكُمُ ٱلۡـَٔایَـٰتِ لَعَلَّكُمۡ تَتَفَكَّرُونَ ﴿219﴾

Akukufunsa za mowa ndi njuga. Nena: “M’zimenezo muli (masautso ndi) uchimo waukulu, ndi zina zothandiza kwa anthu. Koma uchimo wake ngwaukulu zedi kuposa zothandiza zake.” Ndipo akukufunsa kuti aperekenji: Auze: “Chimene chapyolerapo (pa zofuna zanu).” Umo ndi momwe Allah akukufotokozerani ma Ayah (malamulo) kuti mulingalire.[31]

فِی ٱلدُّنۡیَا وَٱلۡـَٔاخِرَةِۗ وَیَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلۡیَتَـٰمَىٰۖ قُلۡ إِصۡلَاحࣱ لَّهُمۡ خَیۡرࣱۖ وَإِن تُخَالِطُوهُمۡ فَإِخۡوَ ٰ⁠نُكُمۡۚ وَٱللَّهُ یَعۡلَمُ ٱلۡمُفۡسِدَ مِنَ ٱلۡمُصۡلِحِۚ وَلَوۡ شَاۤءَ ٱللَّهُ لَأَعۡنَتَكُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَزِیزٌ حَكِیمࣱ ﴿220﴾

Za m’dziko lapansi ndi (zinthu) za tsiku lachimaliziro. Ndipo akukufunsa za ana amasiye, nena: “Kuwachitira zabwino ndiwo ubwino; ngati mutasakanikirana nawo, (ndibwinonso). Iwo ndi abale anu; ndipo Allah akumdziwa woononga ndi wochita zabwino. Ndipo Allah akadafuna, akadakukhwimitsirani malamulo. Ndithudi, Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya.”

وَلَا تَنكِحُوا۟ ٱلۡمُشۡرِكَـٰتِ حَتَّىٰ یُؤۡمِنَّۚ وَلَأَمَةࣱ مُّؤۡمِنَةٌ خَیۡرࣱ مِّن مُّشۡرِكَةࣲ وَلَوۡ أَعۡجَبَتۡكُمۡۗ وَلَا تُنكِحُوا۟ ٱلۡمُشۡرِكِینَ حَتَّىٰ یُؤۡمِنُوا۟ۚ وَلَعَبۡدࣱ مُّؤۡمِنٌ خَیۡرࣱ مِّن مُّشۡرِكࣲ وَلَوۡ أَعۡجَبَكُمۡۗ أُو۟لَـٰۤىِٕكَ یَدۡعُونَ إِلَى ٱلنَّارِۖ وَٱللَّهُ یَدۡعُوۤا۟ إِلَى ٱلۡجَنَّةِ وَٱلۡمَغۡفِرَةِ بِإِذۡنِهِۦۖ وَیُبَیِّنُ ءَایَـٰتِهِۦ لِلنَّاسِ لَعَلَّهُمۡ یَتَذَكَّرُونَ ﴿221﴾

Ndipo musakwatire akazi opembedza mafano mpaka atakhulupirira. Ndithudi, mdzakazi wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa mfulu ya chikazi yopembedza mafano, ngakhale itakukondweretsani. (Ndipo ana anu aakazi a Chisilamu) musawakwatitse kwa amuna osakhulupirira, mpaka akhulupirire. Ndipo kapolo wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa mfulu yopembedza mafano, ngakhale ikukukondweretsani. Iwowo akuitanira ku Moto. Koma Allah akuitanira ku Munda wamtendere ndi ku chikhululuko mwa lamulo lake. Ndipo Iye akulongosola mwatsatanetsatane ndime za mawu ake kwa anthu, kuti athe kukumbukira.[32]

وَیَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلۡمَحِیضِۖ قُلۡ هُوَ أَذࣰى فَٱعۡتَزِلُوا۟ ٱلنِّسَاۤءَ فِی ٱلۡمَحِیضِ وَلَا تَقۡرَبُوهُنَّ حَتَّىٰ یَطۡهُرۡنَۖ فَإِذَا تَطَهَّرۡنَ فَأۡتُوهُنَّ مِنۡ حَیۡثُ أَمَرَكُمُ ٱللَّهُۚ إِنَّ ٱللَّهَ یُحِبُّ ٱلتَّوَّ ٰ⁠بِینَ وَیُحِبُّ ٱلۡمُتَطَهِّرِینَ ﴿222﴾

Ndipo (iwo) akukufunsa za kukhala malo amodzi ndi azimayi panthawi imene akusamba, auze (kuti): “Zimenezo ndizovulaza (ndiponso ndiuve). Choncho apatukireni akazi m’nthawi ya matenda akumwezi, ndipo musawayandikire mpaka ayere. Ngati atayera, kumananaoni kupyolera m’njira yomwe Allah wakulamulani. Ndithu Allah amakonda olapa, ndiponso amakonda odziyeretsa. ”

نِسَاۤؤُكُمۡ حَرۡثࣱ لَّكُمۡ فَأۡتُوا۟ حَرۡثَكُمۡ أَنَّىٰ شِئۡتُمۡۖ وَقَدِّمُوا۟ لِأَنفُسِكُمۡۚ وَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ وَٱعۡلَمُوۤا۟ أَنَّكُم مُّلَـٰقُوهُۗ وَبَشِّرِ ٱلۡمُؤۡمِنِینَ ﴿223﴾

Akazi anu ali ngati minda yanu; choncho idzereni minda yanu mmene mungafunire; koma dzitsogozereni zabwino nokha, ndipo opani Allah, ndipo dziwaninso kuti mudzakumana naye. Ndipo auze nkhani yabwino amene akhulupirira.

وَلَا تَجۡعَلُوا۟ ٱللَّهَ عُرۡضَةࣰ لِّأَیۡمَـٰنِكُمۡ أَن تَبَرُّوا۟ وَتَتَّقُوا۟ وَتُصۡلِحُوا۟ بَیۡنَ ٱلنَّاسِۚ وَٱللَّهُ سَمِیعٌ عَلِیمࣱ ﴿224﴾

Ndipo kulumbilira kwanu dzina la Allah musakuchite kukhala chokuletsani kuchita zinthu zabwino (za m’Chisilamu) ndi kuopa Allah, ndi kuyanjanitsa pakati pa anthu. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa.[33]

لَّا یُؤَاخِذُكُمُ ٱللَّهُ بِٱللَّغۡوِ فِیۤ أَیۡمَـٰنِكُمۡ وَلَـٰكِن یُؤَاخِذُكُم بِمَا كَسَبَتۡ قُلُوبُكُمۡۗ وَٱللَّهُ غَفُورٌ حَلِیمࣱ ﴿225﴾

Allah sangakulangeni pa kulumbira kwanu kopanda pake, koma adzakulangani chifukwa cha malumbiro anu amene mitima yanu yatsimikiza mwa mphamvu. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza.

لِّلَّذِینَ یُؤۡلُونَ مِن نِّسَاۤىِٕهِمۡ تَرَبُّصُ أَرۡبَعَةِ أَشۡهُرࣲۖ فَإِن فَاۤءُو فَإِنَّ ٱللَّهَ غَفُورࣱ رَّحِیمࣱ ﴿226﴾

Kwa omwe akulumbilira kuti adzipatula kwa akazi awo, (nyengo yawo) ayembekezere miyezi inayi. Koma ngati atabwerera (nakhala pamodzi ndi akazi awo), ndithudi Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi. [34]

وَإِنۡ عَزَمُوا۟ ٱلطَّلَـٰقَ فَإِنَّ ٱللَّهَ سَمِیعٌ عَلِیمࣱ ﴿227﴾

Ndipo ngati atatsimikiza kulekana, ndithudi Allah Ngwakumva, Ngodziwa.

وَٱلۡمُطَلَّقَـٰتُ یَتَرَبَّصۡنَ بِأَنفُسِهِنَّ ثَلَـٰثَةَ قُرُوۤءࣲۚ وَلَا یَحِلُّ لَهُنَّ أَن یَكۡتُمۡنَ مَا خَلَقَ ٱللَّهُ فِیۤ أَرۡحَامِهِنَّ إِن كُنَّ یُؤۡمِنَّ بِٱللَّهِ وَٱلۡیَوۡمِ ٱلۡـَٔاخِرِۚ وَبُعُولَتُهُنَّ أَحَقُّ بِرَدِّهِنَّ فِی ذَ ٰ⁠لِكَ إِنۡ أَرَادُوۤا۟ إِصۡلَـٰحࣰاۚ وَلَهُنَّ مِثۡلُ ٱلَّذِی عَلَیۡهِنَّ بِٱلۡمَعۡرُوفِۚ وَلِلرِّجَالِ عَلَیۡهِنَّ دَرَجَةࣱۗ وَٱللَّهُ عَزِیزٌ حَكِیمٌ ﴿228﴾

Ndipo akazi osiidwa (asakwatiwe) ayembekezere mpaka kuyeretsedwa kutatu kukwanire. Ndipo nkosafunika kwa iwo kubisa chimene Allah walenga m’mimba zawo, ngati akukhulupiriradi Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amuna awo ali ndi udindo wowayenereza kuwabwerera m’nthawi imeneyi ngati akufuna kuchita chimvano. Nawonso azimayi ali ndi zofunika kuchitiridwa (ndi amuna awo) monga m’mene ziliri kwa azimayiwo kuchitira amuna awo mwachilamulo cha Shariya. Koma amuna ali ndi udindo okulirapo kuposa iwo. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya. [35]

ٱلطَّلَـٰقُ مَرَّتَانِۖ فَإِمۡسَاكُۢ بِمَعۡرُوفٍ أَوۡ تَسۡرِیحُۢ بِإِحۡسَـٰنࣲۗ وَلَا یَحِلُّ لَكُمۡ أَن تَأۡخُذُوا۟ مِمَّاۤ ءَاتَیۡتُمُوهُنَّ شَیۡـًٔا إِلَّاۤ أَن یَخَافَاۤ أَلَّا یُقِیمَا حُدُودَ ٱللَّهِۖ فَإِنۡ خِفۡتُمۡ أَلَّا یُقِیمَا حُدُودَ ٱللَّهِ فَلَا جُنَاحَ عَلَیۡهِمَا فِیمَا ٱفۡتَدَتۡ بِهِۦۗ تِلۡكَ حُدُودُ ٱللَّهِ فَلَا تَعۡتَدُوهَاۚ وَمَن یَتَعَدَّ حُدُودَ ٱللَّهِ فَأُو۟لَـٰۤىِٕكَ هُمُ ٱلظَّـٰلِمُونَ ﴿229﴾

Twalaq (mawu achilekaniro cha ukwati omwe akupereka mwayi kwa mwamuna kubwereranso kwa mkazi wake), ndi omwe anenedwa kawiri. Kenako amkhazike (mkaziyo) mwa ubwino (ngati afuna kubwererana naye) kapena alekane mwa ubwino (ngati atafunadi kumleka. Ndipo sangathe kubwererana naye ngati atamunenera kachitatu mawu achilekano pokhapokha atakwatiwa kaye ndi mwamuna wina ndi kusiidwa ndi mwamunayo). Ndipo sizili zololedwa kwa inu kuti mutenge (kulanda) chilichonse chimene mudawapatsa (akazi anu) pokhapokha (onse awiri) ngati akuopa kuti satha kusunga malire a Allah (malamulo a Allah). Ngati muopa kuti sasunga malire a Allah, ndiye kuti pamenepo pakhala popanda tchimo kwa iwo (mwamuna woyamba ndi mkaziyu) kulandira (kapena kupereka) chodziombolera mkazi. Awa ndiwo malire a Allah; choncho musawalumphe. Ndipo amene alumphe malire a Allah (powaswa), iwowo ndiwo anthu ochita zoipa.[36]

فَإِن طَلَّقَهَا فَلَا تَحِلُّ لَهُۥ مِنۢ بَعۡدُ حَتَّىٰ تَنكِحَ زَوۡجًا غَیۡرَهُۥۗ فَإِن طَلَّقَهَا فَلَا جُنَاحَ عَلَیۡهِمَاۤ أَن یَتَرَاجَعَاۤ إِن ظَنَّاۤ أَن یُقِیمَا حُدُودَ ٱللَّهِۗ وَتِلۡكَ حُدُودُ ٱللَّهِ یُبَیِّنُهَا لِقَوۡمࣲ یَعۡلَمُونَ ﴿230﴾

Tero ngati atamuleka (ndi kunena katatu mawu achilekaniro, choncho mkazi ameneyo) ngosaloledwa kwa iye pambuyo pakutero, kufikira akwatiwe ndi mwamuna wina. (Ngati mwamuna winayo atamusiya), palibe kulakwa kwa awiriwo kubwererana ngati akuona kuti adzasunga malire a Allah. Ndipo awa ndi malire a Allah omwe akuwalongosola kwa anthu odziwa.

وَإِذَا طَلَّقۡتُمُ ٱلنِّسَاۤءَ فَبَلَغۡنَ أَجَلَهُنَّ فَأَمۡسِكُوهُنَّ بِمَعۡرُوفٍ أَوۡ سَرِّحُوهُنَّ بِمَعۡرُوفࣲۚ وَلَا تُمۡسِكُوهُنَّ ضِرَارࣰا لِّتَعۡتَدُوا۟ۚ وَمَن یَفۡعَلۡ ذَ ٰ⁠لِكَ فَقَدۡ ظَلَمَ نَفۡسَهُۥۚ وَلَا تَتَّخِذُوۤا۟ ءَایَـٰتِ ٱللَّهِ هُزُوࣰاۚ وَٱذۡكُرُوا۟ نِعۡمَتَ ٱللَّهِ عَلَیۡكُمۡ وَمَاۤ أَنزَلَ عَلَیۡكُم مِّنَ ٱلۡكِتَـٰبِ وَٱلۡحِكۡمَةِ یَعِظُكُم بِهِۦۚ وَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ وَٱعۡلَمُوۤا۟ أَنَّ ٱللَّهَ بِكُلِّ شَیۡءٍ عَلِیمࣱ ﴿231﴾

Ndipo pamene musiya akazi powanenera mawu achilekaniro, niiyandikira kukwana nyengo ya edda yawo (chiyembekezero chawo), abwelereni mwa ubwino; kapena lekananaoni mwa ubwino, ndipo musawabwelere mowavutitsa kuti mupyole malire a Allah (poswa malamulo ake). Ndipo amene achite zimenezo ndiye kuti wadzichitira yekha zoipa. Ndipo ndime za mawu a Allah musazichitire chibwana. Ndipo kumbukirani mtendere wa Allah umene uli pa inu; makamaka chisomo chokuvumbulutsirani buku (la Qur’an) ndi kudziwitsidwa nzeru zomwe akukulangizani nazo. Ndipo opani Allah, ndithudi dziwani kuti Allah Ngodziwa chirichonse.[37]

وَإِذَا طَلَّقۡتُمُ ٱلنِّسَاۤءَ فَبَلَغۡنَ أَجَلَهُنَّ فَلَا تَعۡضُلُوهُنَّ أَن یَنكِحۡنَ أَزۡوَ ٰ⁠جَهُنَّ إِذَا تَرَ ٰ⁠ضَوۡا۟ بَیۡنَهُم بِٱلۡمَعۡرُوفِۗ ذَ ٰ⁠لِكَ یُوعَظُ بِهِۦ مَن كَانَ مِنكُمۡ یُؤۡمِنُ بِٱللَّهِ وَٱلۡیَوۡمِ ٱلۡـَٔاخِرِۗ ذَ ٰ⁠لِكُمۡ أَزۡكَىٰ لَكُمۡ وَأَطۡهَرُۚ وَٱللَّهُ یَعۡلَمُ وَأَنتُمۡ لَا تَعۡلَمُونَ ﴿232﴾

Ndipo akazi mukawanenera mawu achilekaniro (oyamba ndi achiwiri), iwo nakwaniritsa chiyembekezero chawo, choncho (inu abale amkazi), musawaletse kukwatiwanso ndi amuna awo (kubwererana) ngati pali chimvano pakati pawo mwa ubwino. Zimenezo akulangizidwa nazo mwa inu yemwe akukhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro. Zimenezo nzabwino kwa inu, ndiponso zoyeretsa. Ndipo Allah akudziwa, pomwe inu simudziwa.

۞ وَٱلۡوَ ٰ⁠لِدَ ٰ⁠تُ یُرۡضِعۡنَ أَوۡلَـٰدَهُنَّ حَوۡلَیۡنِ كَامِلَیۡنِۖ لِمَنۡ أَرَادَ أَن یُتِمَّ ٱلرَّضَاعَةَۚ وَعَلَى ٱلۡمَوۡلُودِ لَهُۥ رِزۡقُهُنَّ وَكِسۡوَتُهُنَّ بِٱلۡمَعۡرُوفِۚ لَا تُكَلَّفُ نَفۡسٌ إِلَّا وُسۡعَهَاۚ لَا تُضَاۤرَّ وَ ٰ⁠لِدَةُۢ بِوَلَدِهَا وَلَا مَوۡلُودࣱ لَّهُۥ بِوَلَدِهِۦۚ وَعَلَى ٱلۡوَارِثِ مِثۡلُ ذَ ٰ⁠لِكَۗ فَإِنۡ أَرَادَا فِصَالًا عَن تَرَاضࣲ مِّنۡهُمَا وَتَشَاوُرࣲ فَلَا جُنَاحَ عَلَیۡهِمَاۗ وَإِنۡ أَرَدتُّمۡ أَن تَسۡتَرۡضِعُوۤا۟ أَوۡلَـٰدَكُمۡ فَلَا جُنَاحَ عَلَیۡكُمۡ إِذَا سَلَّمۡتُم مَّاۤ ءَاتَیۡتُم بِٱلۡمَعۡرُوفِۗ وَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ وَٱعۡلَمُوۤا۟ أَنَّ ٱللَّهَ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِیرࣱ ﴿233﴾

Ndipo akazi omwe angobereka kumene ayamwitse ana awo zaka ziwiri zathunthu kwa yemwe akufuna kukwaniritsa kuyamwitsa. Ndiudindo wa abambo kuwapezera chakudya chawo ndi chovala chawo (ana awo ndi ) amayiwo, motsatira malamulo a Shariya. Ndipo mzimu wa munthu aliyense sukakamizidwa, koma m’mene ungathere. Ndipo mayi wa mwanayo asazunzidwe chifukwa cha mwana wakeyo. Nayenso bambo wa mwanayo asazunzike chifukwa cha mwana wakeyo. Ndipo lamuloli lilinso chimodzimodzi pa mlowam’malo (ngati bambo atamwalira). Ndipo onse awiri ngati atafuna kumletsa kuyamwa, mogwirizana pakati pa awiriwo, ndi mokambirana palibe kulakwa pa iwo awiriwo. Ndipo ngati mutafuna kuwapezera ana anu akazi ena owayamwitsa (omwe si amayi awo), palibe uchimo mwa inu ngati mwapereka chimene udalonjeza kuwapatsa (oyamwitsawo) mwa ubwino. Ndipo opani Allah; dziwaninso kuti Allah akuona zonse zimene mukuchita.[38]

وَٱلَّذِینَ یُتَوَفَّوۡنَ مِنكُمۡ وَیَذَرُونَ أَزۡوَ ٰ⁠جࣰا یَتَرَبَّصۡنَ بِأَنفُسِهِنَّ أَرۡبَعَةَ أَشۡهُرࣲ وَعَشۡرࣰاۖ فَإِذَا بَلَغۡنَ أَجَلَهُنَّ فَلَا جُنَاحَ عَلَیۡكُمۡ فِیمَا فَعَلۡنَ فِیۤ أَنفُسِهِنَّ بِٱلۡمَعۡرُوفِۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِیرࣱ ﴿234﴾

234, Ndipo mwa inu amene amwalira nasiya akazi, choncho (akaziwo) ayembekezere (asakwatiwe) miyezi inayi ndi masiku khumi. Ndipo akakwanitsa nyengo ya chiyembekezero chawo cha edda, sitchimo kwa inu pazimene akaziwo adzichitira okha (monga kudzikongoletsa ndi kudziwonetsa kwa ofunsira ukwati); motsatira malamulo a Shariya. Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene mukuchita.

وَلَا جُنَاحَ عَلَیۡكُمۡ فِیمَا عَرَّضۡتُم بِهِۦ مِنۡ خِطۡبَةِ ٱلنِّسَاۤءِ أَوۡ أَكۡنَنتُمۡ فِیۤ أَنفُسِكُمۡۚ عَلِمَ ٱللَّهُ أَنَّكُمۡ سَتَذۡكُرُونَهُنَّ وَلَـٰكِن لَّا تُوَاعِدُوهُنَّ سِرًّا إِلَّاۤ أَن تَقُولُوا۟ قَوۡلࣰا مَّعۡرُوفࣰاۚ وَلَا تَعۡزِمُوا۟ عُقۡدَةَ ٱلنِّكَاحِ حَتَّىٰ یَبۡلُغَ ٱلۡكِتَـٰبُ أَجَلَهُۥۚ وَٱعۡلَمُوۤا۟ أَنَّ ٱللَّهَ یَعۡلَمُ مَا فِیۤ أَنفُسِكُمۡ فَٱحۡذَرُوهُۚ وَٱعۡلَمُوۤا۟ أَنَّ ٱللَّهَ غَفُورٌ حَلِیمࣱ ﴿235﴾

Ndipo sitchimo kwa inu kupereka mawu okuluwika ofunsira ukwati kwa akaziwo (pamene chiyembekezero cha edda yawo chisanathe. Ndiponso palibe uchimo) kapena kubisa mu mtima mwanu, kuwakwatira (chiyembekezo chawo chikadzatha). Allah wadziwa kuti mukhala mukuwakumbukira akaziwo. Koma musawalonjeze mobisa (kuti: “Ikatha edda ndidzakukwatira).” Koma nenani mawu abwino. Ndipo musatsimikize kumanga ukwati mpaka nyengo yolembedwayo ikwanire. Ndipo dziwani kuti Allah akudziwa zomwe zili m’mitima mwanu. Tero muopeni (Allah), dziwaninso kuti Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza.

لَّا جُنَاحَ عَلَیۡكُمۡ إِن طَلَّقۡتُمُ ٱلنِّسَاۤءَ مَا لَمۡ تَمَسُّوهُنَّ أَوۡ تَفۡرِضُوا۟ لَهُنَّ فَرِیضَةࣰۚ وَمَتِّعُوهُنَّ عَلَى ٱلۡمُوسِعِ قَدَرُهُۥ وَعَلَى ٱلۡمُقۡتِرِ قَدَرُهُۥ مَتَـٰعَۢا بِٱلۡمَعۡرُوفِۖ حَقًّا عَلَى ٱلۡمُحۡسِنِینَ ﴿236﴾

Palibe tchimo pa inu mutawapatsa akazi mawu achilekaniro pomwe simudakhudzane nawo; pomwenso simudawadziwitse gawo la chiwongo chawo; koma asangalatseni (powapatsa chilekaniro). Wopeza bwino apereke malinga ndikupeza bwino kwake; wochepekedwa apereke malingana ndikuchepekedwa kwake. Chilekaniro chosangalatsacho chikhale molingana ndi malamulo a Shariya, ndipo ndilamulo kwa ochita zabwino.[39]

وَإِن طَلَّقۡتُمُوهُنَّ مِن قَبۡلِ أَن تَمَسُّوهُنَّ وَقَدۡ فَرَضۡتُمۡ لَهُنَّ فَرِیضَةࣰ فَنِصۡفُ مَا فَرَضۡتُمۡ إِلَّاۤ أَن یَعۡفُونَ أَوۡ یَعۡفُوَا۟ ٱلَّذِی بِیَدِهِۦ عُقۡدَةُ ٱلنِّكَاحِۚ وَأَن تَعۡفُوۤا۟ أَقۡرَبُ لِلتَّقۡوَىٰۚ وَلَا تَنسَوُا۟ ٱلۡفَضۡلَ بَیۡنَكُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِیرٌ ﴿237﴾

Ndipo ngati mwalekana nawo (akaziwo) musanakhudzane nawo mutawadziwitsa gawo la chiwongo chawo, apatseni theka la chimene mudagwirizana kuwapatsa pokhapokha ngati akaziwo atakana okha (theka la chiwongocho), kapena (mwamuna) uja yemwe kumangitsa kwa ukwati kuli m’manja mwake amusiire (chiwongo chonsecho mkaziyo). Ndipo ngati mutasiirana (zimenezo) zingakuyandikitseni kumbali yoopa Allah. Ndipo musaiwale kuchitirana zabwino pakati panu (ngakhale kuti mukulekana). Ndithudi Allah akuona zonse zimene mukuchita.[40]

حَـٰفِظُوا۟ عَلَى ٱلصَّلَوَ ٰ⁠تِ وَٱلصَّلَوٰةِ ٱلۡوُسۡطَىٰ وَقُومُوا۟ لِلَّهِ قَـٰنِتِینَ ﴿238﴾

Sungani mokwanira Swala makamaka Swala yapakatikati; ndipo imilirani modzichepetsa kwa Allah.[41]

فَإِنۡ خِفۡتُمۡ فَرِجَالًا أَوۡ رُكۡبَانࣰاۖ فَإِذَاۤ أَمِنتُمۡ فَٱذۡكُرُوا۟ ٱللَّهَ كَمَا عَلَّمَكُم مَّا لَمۡ تَكُونُوا۟ تَعۡلَمُونَ ﴿239﴾

Ndipo ngati muli ndi mantha (kupemphera mwalamulo pamene mukumenyana ndi adani anu), pempherani uku mukuyenda, kapena mutakwera chokwera. Ndipo mukakhala pachitetezo mkumbukireni Allah (pempherani) monga momwe wakuphunzitsirani zomwe simudali kuzidziwa.

وَٱلَّذِینَ یُتَوَفَّوۡنَ مِنكُمۡ وَیَذَرُونَ أَزۡوَ ٰ⁠جࣰا وَصِیَّةࣰ لِّأَزۡوَ ٰ⁠جِهِم مَّتَـٰعًا إِلَى ٱلۡحَوۡلِ غَیۡرَ إِخۡرَاجࣲۚ فَإِنۡ خَرَجۡنَ فَلَا جُنَاحَ عَلَیۡكُمۡ فِی مَا فَعَلۡنَ فِیۤ أَنفُسِهِنَّ مِن مَّعۡرُوفࣲۗ وَٱللَّهُ عَزِیزٌ حَكِیمࣱ ﴿240﴾

Ndipo mwa inu amene amwalira nasiya akazi awo, alangize (amlowam’malo awo, monga makolo ndi achibale) za akazi awo kuti awapatse zodyera m’nyengo ya chaka chimodzi popanda kutulutsidwa (m’nyumba zomwe ankakhala ndi amuna awo). Koma ngati akaziwo atuluka (okha), palibe kulakwa pa inu pa zimene adzichitira okha zomwe nzogwirizana ndi chilamulo cha Shariya. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya.

وَلِلۡمُطَلَّقَـٰتِ مَتَـٰعُۢ بِٱلۡمَعۡرُوفِۖ حَقًّا عَلَى ٱلۡمُتَّقِینَ ﴿241﴾

Ndipo akazi osiidwa ukwati, apatsidwe chilekaniro chowasangalatsa m’chilamulo cha Shariya. Ili ndi lamulo kwa amene akuopa Allah.[42]

كَذَ ٰ⁠لِكَ یُبَیِّنُ ٱللَّهُ لَكُمۡ ءَایَـٰتِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ ﴿242﴾

Umu ndi momwe Allah akukulongosolerani ma Ayah ake (ndime zake) kuti inu mukhale ndi nzeru.

۞ أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِینَ خَرَجُوا۟ مِن دِیَـٰرِهِمۡ وَهُمۡ أُلُوفٌ حَذَرَ ٱلۡمَوۡتِ فَقَالَ لَهُمُ ٱللَّهُ مُوتُوا۟ ثُمَّ أَحۡیَـٰهُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَذُو فَضۡلٍ عَلَى ٱلنَّاسِ وَلَـٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا یَشۡكُرُونَ ﴿243﴾

Kodi sudamve (nkhani za) amene adatuluka m’nyumba zawo ali zikwizikwi kuopa imfa? Ndipo Allah adawauza: “Mwalirani,” (ndipo adamwalira chabe popanda chifukwa chilichonse). Kenako Adawaukitsa (kuti adziwe kuti imfa njosathawika). Ndithudi, Allah Ndimwini kuchita zabwino pa anthu, koma anthu ambiri sathokoza.[43]

وَقَـٰتِلُوا۟ فِی سَبِیلِ ٱللَّهِ وَٱعۡلَمُوۤا۟ أَنَّ ٱللَّهَ سَمِیعٌ عَلِیمࣱ ﴿244﴾

Ndipo menyani nkhondo panjira ya Allah, ndipo dziwani kuti Allah Ngwakumva, Ngodziwa chilichonse.

مَّن ذَا ٱلَّذِی یُقۡرِضُ ٱللَّهَ قَرۡضًا حَسَنࣰا فَیُضَـٰعِفَهُۥ لَهُۥۤ أَضۡعَافࣰا كَثِیرَةࣰۚ وَٱللَّهُ یَقۡبِضُ وَیَبۡصُۜطُ وَإِلَیۡهِ تُرۡجَعُونَ ﴿245﴾

Kodi ndani angamkongoze Allah ngongole yabwino (yochokera m’chuma chake powapatsa amphawi ndi kupereka pa njira ya Allah) kuti amuonjezere zoonjezera zambiri? Ndipo Allah ndi yemwe amafumbata ndi kutambasula, ndipo kwa Iye nkumene mudzabwezedwa.[44]

أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلۡمَلَإِ مِنۢ بَنِیۤ إِسۡرَ ٰ⁠ۤءِیلَ مِنۢ بَعۡدِ مُوسَىٰۤ إِذۡ قَالُوا۟ لِنَبِیࣲّ لَّهُمُ ٱبۡعَثۡ لَنَا مَلِكࣰا نُّقَـٰتِلۡ فِی سَبِیلِ ٱللَّهِۖ قَالَ هَلۡ عَسَیۡتُمۡ إِن كُتِبَ عَلَیۡكُمُ ٱلۡقِتَالُ أَلَّا تُقَـٰتِلُوا۟ۖ قَالُوا۟ وَمَا لَنَاۤ أَلَّا نُقَـٰتِلَ فِی سَبِیلِ ٱللَّهِ وَقَدۡ أُخۡرِجۡنَا مِن دِیَـٰرِنَا وَأَبۡنَاۤىِٕنَاۖ فَلَمَّا كُتِبَ عَلَیۡهِمُ ٱلۡقِتَالُ تَوَلَّوۡا۟ إِلَّا قَلِیلࣰا مِّنۡهُمۡۚ وَٱللَّهُ عَلِیمُۢ بِٱلظَّـٰلِمِینَ ﴿246﴾

Kodi sudamve nkhani ya akuluakulu a ana a Israyeli pambuyo pa Mûsa? Adanena kwa mneneri wawo: “Tidzozere mfumu kuti timenye nkhondo pa njira ya Allah.” Iye (mneneri wawoyo) adati: “Mwinatu simungamenye nkhondoyo ngati kutalamulidwa kwa inu. (Iwo) adati: “Nchotani kuti tisamenye nkhondo pa njira ya Allah pomwe tatulutsidwa m’nyumba zathu pamodzi ndi ana athu?” Koma pamene adalamulidwa kumenya nkhondoyo, adatembenuka, kupatula ochepa mwa iwo. Ndipo Allah akudziwa bwinobwino za anthu ochita zoipa.

وَقَالَ لَهُمۡ نَبِیُّهُمۡ إِنَّ ٱللَّهَ قَدۡ بَعَثَ لَكُمۡ طَالُوتَ مَلِكࣰاۚ قَالُوۤا۟ أَنَّىٰ یَكُونُ لَهُ ٱلۡمُلۡكُ عَلَیۡنَا وَنَحۡنُ أَحَقُّ بِٱلۡمُلۡكِ مِنۡهُ وَلَمۡ یُؤۡتَ سَعَةࣰ مِّنَ ٱلۡمَالِۚ قَالَ إِنَّ ٱللَّهَ ٱصۡطَفَىٰهُ عَلَیۡكُمۡ وَزَادَهُۥ بَسۡطَةࣰ فِی ٱلۡعِلۡمِ وَٱلۡجِسۡمِۖ وَٱللَّهُ یُؤۡتِی مُلۡكَهُۥ مَن یَشَاۤءُۚ وَٱللَّهُ وَ ٰ⁠سِعٌ عَلِیمࣱ ﴿247﴾

Ndipo mneneri wawoyo adawauza: “Allah wakusankhirani Taluti kukhala mfumu. (Iwo ) adati: “Nchotani kuti iye akhale ndi ufumu pa ife pomwe ife ngoyenera kupeza ufumu kuposa iye, ndipo sadapatsidwe chuma chambiri?” (Iye) adati: “Ndithu Allah wamusankha pa inu, ndipo wamuonjezera kukhala ndi nzeru zopambana ndi kukhala ndi thupi (lamphamvu). Ndipo Allah amampatsa ufumu wake amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mwini zopereka zambiri, Ngodziwa.”

وَقَالَ لَهُمۡ نَبِیُّهُمۡ إِنَّ ءَایَةَ مُلۡكِهِۦۤ أَن یَأۡتِیَكُمُ ٱلتَّابُوتُ فِیهِ سَكِینَةࣱ مِّن رَّبِّكُمۡ وَبَقِیَّةࣱ مِّمَّا تَرَكَ ءَالُ مُوسَىٰ وَءَالُ هَـٰرُونَ تَحۡمِلُهُ ٱلۡمَلَـٰۤىِٕكَةُۚ إِنَّ فِی ذَ ٰ⁠لِكَ لَـَٔایَةࣰ لَّكُمۡ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِینَ ﴿248﴾

Ndipo mneneri wawo adawauza (kuti): “Ndithu chizindikiro cha ufumu wake, ndikukudzerani bokosi lomwe mkati mwake muli mpumulo wa miyoyo yanu wochokera kwa Mbuye wanu, ndi zotsalira zomwe adazisiya anthu a Mûsa ndi anthu a Harun, atanyamula angelo. Ndithu m’zimenezo muli chisonyezo kwa inu (chosonyeza kuyenera kwa ufumu wake pa inu) ngati mulidi okhulupirira.”

فَلَمَّا فَصَلَ طَالُوتُ بِٱلۡجُنُودِ قَالَ إِنَّ ٱللَّهَ مُبۡتَلِیكُم بِنَهَرࣲ فَمَن شَرِبَ مِنۡهُ فَلَیۡسَ مِنِّی وَمَن لَّمۡ یَطۡعَمۡهُ فَإِنَّهُۥ مِنِّیۤ إِلَّا مَنِ ٱغۡتَرَفَ غُرۡفَةَۢ بِیَدِهِۦۚ فَشَرِبُوا۟ مِنۡهُ إِلَّا قَلِیلࣰا مِّنۡهُمۡۚ فَلَمَّا جَاوَزَهُۥ هُوَ وَٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ مَعَهُۥ قَالُوا۟ لَا طَاقَةَ لَنَا ٱلۡیَوۡمَ بِجَالُوتَ وَجُنُودِهِۦۚ قَالَ ٱلَّذِینَ یَظُنُّونَ أَنَّهُم مُّلَـٰقُوا۟ ٱللَّهِ كَم مِّن فِئَةࣲ قَلِیلَةٍ غَلَبَتۡ فِئَةࣰ كَثِیرَةَۢ بِإِذۡنِ ٱللَّهِۗ وَٱللَّهُ مَعَ ٱلصَّـٰبِرِینَ ﴿249﴾

Choncho, Taluti pamene adapita ndi magulu (ake) a nkhondo, adati: “Allah akuyesani mayeso ndi mtsinje (womwe mukumane nawo panjira komwe mukupitako). Choncho amene akamwe mmenemo sali nane. Koma amene sakamwa adzakhala pamodzi nane kupatula amene watunga ndi dzanja lake (ndikumwa; iyeyo ndiye kuti sadalakwe). Koma (iwo) adamwa m’menemo kupatula ochepa mwa iwo. Choncho pamene adaoloka iye pamodzi ndi aja omwe adakhulupirira limodzi naye, (iwo) adati: “Lero sitingamuthe Jaluti ndi magulu ake a nkhondo.” Omwe adali ndi chitsimikizo chokumana ndi Allah adati: “Kodi ndimagulu angati ochepa amene adagonjetsa magulu ambiri mwa chilolezo cha Allah! Ndipo Allah Ali pamodzi ndi opirira.[45]

وَلَمَّا بَرَزُوا۟ لِجَالُوتَ وَجُنُودِهِۦ قَالُوا۟ رَبَّنَاۤ أَفۡرِغۡ عَلَیۡنَا صَبۡرࣰا وَثَبِّتۡ أَقۡدَامَنَا وَٱنصُرۡنَا عَلَى ٱلۡقَوۡمِ ٱلۡكَـٰفِرِینَ ﴿250﴾

Ndipo pamene adapita kukalimbana ndi Jaluti (mfumu ya adaniwo), pamodzi ndi magulu ake a nkhondo (anthu a Taluti) adati: “E Mbuye wathu! Titsanulireni chipiliro, ndipo limbikitsani mapazi athu: Tithangateni kwa anthu osakhulupirira.”

فَهَزَمُوهُم بِإِذۡنِ ٱللَّهِ وَقَتَلَ دَاوُۥدُ جَالُوتَ وَءَاتَىٰهُ ٱللَّهُ ٱلۡمُلۡكَ وَٱلۡحِكۡمَةَ وَعَلَّمَهُۥ مِمَّا یَشَاۤءُۗ وَلَوۡلَا دَفۡعُ ٱللَّهِ ٱلنَّاسَ بَعۡضَهُم بِبَعۡضࣲ لَّفَسَدَتِ ٱلۡأَرۡضُ وَلَـٰكِنَّ ٱللَّهَ ذُو فَضۡلٍ عَلَى ٱلۡعَـٰلَمِینَ ﴿251﴾

Choncho, adawagonjetsa mwa chilolezo cha Allah. Ndipo Daud adapha Jaluti; ndipo Allah adampatsa ufumu ndi uneneri, namphunzitsanso zimene adafuna. Allah akadapanda kuwakankha anthu ena kupyolera mwa ena ndiye kuti dziko likadaonongeka. Koma Allah ndi mwini kuchita zabwino pa zolengedwa zonse.[46]

تِلۡكَ ءَایَـٰتُ ٱللَّهِ نَتۡلُوهَا عَلَیۡكَ بِٱلۡحَقِّۚ وَإِنَّكَ لَمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِینَ ﴿252﴾

Awa ndi ma Ayah (ndime) a Allah; tikuwawerenga kwa iwe (Mtumiki s.a.w) mwachoonadi. Ndithudi, iwe ndiwe mmodzi mwa atumiki.

۞ تِلۡكَ ٱلرُّسُلُ فَضَّلۡنَا بَعۡضَهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضࣲۘ مِّنۡهُم مَّن كَلَّمَ ٱللَّهُۖ وَرَفَعَ بَعۡضَهُمۡ دَرَجَـٰتࣲۚ وَءَاتَیۡنَا عِیسَى ٱبۡنَ مَرۡیَمَ ٱلۡبَیِّنَـٰتِ وَأَیَّدۡنَـٰهُ بِرُوحِ ٱلۡقُدُسِۗ وَلَوۡ شَاۤءَ ٱللَّهُ مَا ٱقۡتَتَلَ ٱلَّذِینَ مِنۢ بَعۡدِهِم مِّنۢ بَعۡدِ مَا جَاۤءَتۡهُمُ ٱلۡبَیِّنَـٰتُ وَلَـٰكِنِ ٱخۡتَلَفُوا۟ فَمِنۡهُم مَّنۡ ءَامَنَ وَمِنۡهُم مَّن كَفَرَۚ وَلَوۡ شَاۤءَ ٱللَّهُ مَا ٱقۡتَتَلُوا۟ وَلَـٰكِنَّ ٱللَّهَ یَفۡعَلُ مَا یُرِیدُ ﴿253﴾

۞ Amenewo ndi aneneri tidawapatsa ulemelero mosiyanitsa pakati pawo, ena kuposa ena. Mwa iwo alipo amene Allah adawalankhula; ndipo ena adawakwezera kwambiri maulemelero awo. Naye Isa (Yesu) mwana wa Mariya tidampatsa zisonyezo zooneka, ndi kumlimbikitsa ndi Mzimu Woyera (rnngelo Gabriel). Allah akadafuna skadamenyana amene adalipo pambuyo pawo, (pa atumikiwo) pambuyo powadzera zizindikiro zooneka, koma adasiyana. Choncho mwa iwo alipo amene adakhulupirira, ndipo ena mwa iwo sadakhulupirire. Ndipo Allah akadafuna, sakadamenyana; koma Allah amachita zimene akufuna.[47]

یَـٰۤأَیُّهَا ٱلَّذِینَ ءَامَنُوۤا۟ أَنفِقُوا۟ مِمَّا رَزَقۡنَـٰكُم مِّن قَبۡلِ أَن یَأۡتِیَ یَوۡمࣱ لَّا بَیۡعࣱ فِیهِ وَلَا خُلَّةࣱ وَلَا شَفَـٰعَةࣱۗ وَٱلۡكَـٰفِرُونَ هُمُ ٱلظَّـٰلِمُونَ ﴿254﴾

E inu amene mwakhulupirira! Perekani mwa zimene takupatsani lisanadze tsiku lomwe lilibe kugula (chilichonse chokupulumutsani) ngakhale ubwenzi ngakhalenso dandaulo. Ndipo osakhulupirira ndiwo anthu oipa.

ٱللَّهُ لَاۤ إِلَـٰهَ إِلَّا هُوَ ٱلۡحَیُّ ٱلۡقَیُّومُۚ لَا تَأۡخُذُهُۥ سِنَةࣱ وَلَا نَوۡمࣱۚ لَّهُۥ مَا فِی ٱلسَّمَـٰوَ ٰ⁠تِ وَمَا فِی ٱلۡأَرۡضِۗ مَن ذَا ٱلَّذِی یَشۡفَعُ عِندَهُۥۤ إِلَّا بِإِذۡنِهِۦۚ یَعۡلَمُ مَا بَیۡنَ أَیۡدِیهِمۡ وَمَا خَلۡفَهُمۡۖ وَلَا یُحِیطُونَ بِشَیۡءࣲ مِّنۡ عِلۡمِهِۦۤ إِلَّا بِمَا شَاۤءَۚ وَسِعَ كُرۡسِیُّهُ ٱلسَّمَـٰوَ ٰ⁠تِ وَٱلۡأَرۡضَۖ وَلَا یَـُٔودُهُۥ حِفۡظُهُمَاۚ وَهُوَ ٱلۡعَلِیُّ ٱلۡعَظِیمُ ﴿255﴾

Allah palibe wopembedzedwa wina koma Iye, Wamoyo wamuyaya, Woimira ndi Woteteza chilichonse. Kusinza sikumgwira ngakhale tulo. Zonse za kumwamba ndi za pansi nza Iye. Kodi ndani angathe kuombola kwa Iye popanda chilolezo chake? Akudziwa za patsogolo ndi zomwe zili pambuyo pawo ndipo zolengedwazo sizidziwa chilichonse pa zomwe zili m’kudziwa Kwake kupatula chimene wafuna. Mpando wake wachifumu wakwanira kumwamba ndi pansi ndipo sizimamvuta kuzisunga zimenezo. Ndipo Iye (Yekha) Njemwe ali Wapamwambamwamba, Ngwamkulu kwabasi, (Ngolemekezeka kwambiri).[48]

لَاۤ إِكۡرَاهَ فِی ٱلدِّینِۖ قَد تَّبَیَّنَ ٱلرُّشۡدُ مِنَ ٱلۡغَیِّۚ فَمَن یَكۡفُرۡ بِٱلطَّـٰغُوتِ وَیُؤۡمِنۢ بِٱللَّهِ فَقَدِ ٱسۡتَمۡسَكَ بِٱلۡعُرۡوَةِ ٱلۡوُثۡقَىٰ لَا ٱنفِصَامَ لَهَاۗ وَٱللَّهُ سَمِیعٌ عَلِیمٌ ﴿256﴾

Palibe kukakamiza (munthu kulowa) m’chipembedzo; kulungama kwaonekera poyera kusiyana ndi kusalungama. Choncho amene akumkana satana nakhulupirira Allah, ndiye kuti wagwira chigwiliro cholimba, chomwe sichisweka. Ndipo Allah Ngwakumva; Ngodziwa.[49]

ٱللَّهُ وَلِیُّ ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ یُخۡرِجُهُم مِّنَ ٱلظُّلُمَـٰتِ إِلَى ٱلنُّورِۖ وَٱلَّذِینَ كَفَرُوۤا۟ أَوۡلِیَاۤؤُهُمُ ٱلطَّـٰغُوتُ یُخۡرِجُونَهُم مِّنَ ٱلنُّورِ إِلَى ٱلظُّلُمَـٰتِۗ أُو۟لَـٰۤىِٕكَ أَصۡحَـٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِیهَا خَـٰلِدُونَ ﴿257﴾

Allah ndi Mtetezi wa amene akhulupirira, amawatulutsa kumdima ndikuwalowetsa mkuunika, koma amene sadakhulupirire, atetezi awo ndi asatana. Amawatulutsa m’kuunika ndi kuwalowetsa mu mdima; iwo ndi anthu a ku Moto. M’menemo adzakhalamo nthawi yaitali.

أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِی حَاۤجَّ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمَ فِی رَبِّهِۦۤ أَنۡ ءَاتَىٰهُ ٱللَّهُ ٱلۡمُلۡكَ إِذۡ قَالَ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمُ رَبِّیَ ٱلَّذِی یُحۡیِۦ وَیُمِیتُ قَالَ أَنَا۠ أُحۡیِۦ وَأُمِیتُۖ قَالَ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمُ فَإِنَّ ٱللَّهَ یَأۡتِی بِٱلشَّمۡسِ مِنَ ٱلۡمَشۡرِقِ فَأۡتِ بِهَا مِنَ ٱلۡمَغۡرِبِ فَبُهِتَ ٱلَّذِی كَفَرَۗ وَٱللَّهُ لَا یَهۡدِی ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّـٰلِمِینَ ﴿258﴾

Kodi sudamve za yemwe adatsutsana ndi Ibrahim pa za Mbuye wake (Allah)? (Ankanyada) pachifukwa chakuti Allah adampatsa ufumu. Ibrahim adati: “Mbuye wanga ndi yemwe amapereka moyo ndi imfa.” Iye adati: “Inenso ndimapereka moyo ndi imfa.” Ibrahim Adati: “Ndithu Allah amatulutsa dzuwa ku vuma, choncho iwe ulitulutse ku zambwe.” Ndipo uja wosakhulupirira adangoti kakasi, (kusowa chonena). Ndipo Allah satsogolera anthu ochita zoipa.[50]

أَوۡ كَٱلَّذِی مَرَّ عَلَىٰ قَرۡیَةࣲ وَهِیَ خَاوِیَةٌ عَلَىٰ عُرُوشِهَا قَالَ أَنَّىٰ یُحۡیِۦ هَـٰذِهِ ٱللَّهُ بَعۡدَ مَوۡتِهَاۖ فَأَمَاتَهُ ٱللَّهُ مِا۟ئَةَ عَامࣲ ثُمَّ بَعَثَهُۥۖ قَالَ كَمۡ لَبِثۡتَۖ قَالَ لَبِثۡتُ یَوۡمًا أَوۡ بَعۡضَ یَوۡمࣲۖ قَالَ بَل لَّبِثۡتَ مِا۟ئَةَ عَامࣲ فَٱنظُرۡ إِلَىٰ طَعَامِكَ وَشَرَابِكَ لَمۡ یَتَسَنَّهۡۖ وَٱنظُرۡ إِلَىٰ حِمَارِكَ وَلِنَجۡعَلَكَ ءَایَةࣰ لِّلنَّاسِۖ وَٱنظُرۡ إِلَى ٱلۡعِظَامِ كَیۡفَ نُنشِزُهَا ثُمَّ نَكۡسُوهَا لَحۡمࣰاۚ فَلَمَّا تَبَیَّنَ لَهُۥ قَالَ أَعۡلَمُ أَنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَیۡءࣲ قَدِیرࣱ ﴿259﴾

Kapena ngati fanizo la uja amene adadutsa pafupi ndi mudzi umene madenga ndi zipupa zake zidaphwasuka (udaferatu) adati: “Kodi Allah adzaukitsa chotani mudzi uwu pambuyo pakufa kwake?” Ndipo Allah adampatsa imfa kwa nthawi yokwana zaka zana limodzi (100), kenako adamuukitsa namufunsa: “Kodi wakhala nyengo yaitali bwanji?” Adati: “Ndakhala nthawi yatsiku limodzi, kapena theka latsiku.” (Allah) adati: “Korna wakhala zaka zana limodzi, ndipo ona chakudya chako ndi zakumwa zako, sizinaonongeke (sizinavunde). Ndipo yang’ana bulu wako (ali mafupa okhaokha oyoyoka); ndi kuti ukhale chisonyezo kwa anthu, (nchifukwa chake takuukitsa ku imfa). Ndipo yang’ana mafupa (a bulu wako) momwe tingawaukitsire, kenako nkumaaveka minofu.” Choncho pamene zidazindikirika (kwa iye, woukitsidwayo), adati: “Ndikudziwa kuti Allah Ngokhoza chilichonse.”[51]

وَإِذۡ قَالَ إِبۡرَ ٰ⁠هِـۧمُ رَبِّ أَرِنِی كَیۡفَ تُحۡیِ ٱلۡمَوۡتَىٰۖ قَالَ أَوَلَمۡ تُؤۡمِنۖ قَالَ بَلَىٰ وَلَـٰكِن لِّیَطۡمَىِٕنَّ قَلۡبِیۖ قَالَ فَخُذۡ أَرۡبَعَةࣰ مِّنَ ٱلطَّیۡرِ فَصُرۡهُنَّ إِلَیۡكَ ثُمَّ ٱجۡعَلۡ عَلَىٰ كُلِّ جَبَلࣲ مِّنۡهُنَّ جُزۡءࣰا ثُمَّ ٱدۡعُهُنَّ یَأۡتِینَكَ سَعۡیࣰاۚ وَٱعۡلَمۡ أَنَّ ٱللَّهَ عَزِیزٌ حَكِیمࣱ ﴿260﴾

Ndipo (kumbukira) pamene Ibrahim adati: “E Mbuye wanga!, Ndionetseni mmene mudzaaukitsire akufa.” (Allah) adati: “Kodi sunakhulupirirebe?” Adati: “Iyayi, (ndikukhulupirira), koma (ndikufuna kuona zimenezo) kuti mtima wanga ukhazikike.” (Allah) adati: “Choncho katenge mbalame zinayi; uzisonkhanitse kwa iwe (mpaka uyizindikire mbalame iliyonse mmene ilili, ndipo kenako uziduledule zonsezo zidutswazidutswa ndikuzisakaniza ndi kuzigawa mzigawo zinayi). Ndipo paphiri lililonse ukaikepo gawo limodzi la zimenezo, ndipo kenako uziitane. Zikudzera zikuthamanga. Ndipo dziwa kuti Allah ndi Mwini mphamvu zoposa, Ngwanzem zakuya.”[52]

مَّثَلُ ٱلَّذِینَ یُنفِقُونَ أَمۡوَ ٰ⁠لَهُمۡ فِی سَبِیلِ ٱللَّهِ كَمَثَلِ حَبَّةٍ أَنۢبَتَتۡ سَبۡعَ سَنَابِلَ فِی كُلِّ سُنۢبُلَةࣲ مِّا۟ئَةُ حَبَّةࣲۗ وَٱللَّهُ یُضَـٰعِفُ لِمَن یَشَاۤءُۚ وَٱللَّهُ وَ ٰ⁠سِعٌ عَلِیمٌ ﴿261﴾

Fanizo la amene akupereka chuma chawo pa njira ya Allah lili ngati fanizo la njere imodzi yomwe yatulutsa ngala zisanu ndi ziwiri. Ndipo ngala iliyonse nkukhalamo njere zana limodzi. Ndipo Allah amamuonjezera amene wamfuna (kuposera pamenepa). Ndipo Allah alinazo zambiri, Ngodziwa.[53]

ٱلَّذِینَ یُنفِقُونَ أَمۡوَ ٰ⁠لَهُمۡ فِی سَبِیلِ ٱللَّهِ ثُمَّ لَا یُتۡبِعُونَ مَاۤ أَنفَقُوا۟ مَنࣰّا وَلَاۤ أَذࣰى لَّهُمۡ أَجۡرُهُمۡ عِندَ رَبِّهِمۡ وَلَا خَوۡفٌ عَلَیۡهِمۡ وَلَا هُمۡ یَحۡزَنُونَ ﴿262﴾

(Anthu) amene akupereka chuma chawo pa njira ya Allah napanda kutsatiza pa zomwe aperekazo kukumba, ndiponso masautso, iwo ali ndi mphoto kwa Mbuye wawo ndipo pa iwo sipadzakhala mantha; ndiponso sadzadandaula.

۞ قَوۡلࣱ مَّعۡرُوفࣱ وَمَغۡفِرَةٌ خَیۡرࣱ مِّن صَدَقَةࣲ یَتۡبَعُهَاۤ أَذࣰىۗ وَٱللَّهُ غَنِیٌّ حَلِیمࣱ ﴿263﴾

Mawu abwino, ndi kukhululukira (amene wakulakwira) nzabwino zedi kuposa sadaka yotsatizidwa ndi masautso. Ndipo Allah ndiyemwe ali Wolemera kwambiri ndiponso Woleza (kwa zolengedwa Zake).

یَـٰۤأَیُّهَا ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ لَا تُبۡطِلُوا۟ صَدَقَـٰتِكُم بِٱلۡمَنِّ وَٱلۡأَذَىٰ كَٱلَّذِی یُنفِقُ مَالَهُۥ رِئَاۤءَ ٱلنَّاسِ وَلَا یُؤۡمِنُ بِٱللَّهِ وَٱلۡیَوۡمِ ٱلۡـَٔاخِرِۖ فَمَثَلُهُۥ كَمَثَلِ صَفۡوَانٍ عَلَیۡهِ تُرَابࣱ فَأَصَابَهُۥ وَابِلࣱ فَتَرَكَهُۥ صَلۡدࣰاۖ لَّا یَقۡدِرُونَ عَلَىٰ شَیۡءࣲ مِّمَّا كَسَبُوا۟ۗ وَٱللَّهُ لَا یَهۡدِی ٱلۡقَوۡمَ ٱلۡكَـٰفِرِینَ ﴿264﴾

E inu amene mwakhulupirira! Musaononge sadaka zanu pokumba ndiponso popereka masautso, monga yemwe akupereka chuma chake modzionetsera kwa anthu, ndipo sakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro. Choncho fanizo lake lili ngati thanthwe lomwe pamwamba pake pali dothi. Kenako nkulifikira chimvula (nkuchotsa dothi lonse lija), nkulisiya lopanda kanthu. Tero sadzatha kupeza chilichonse pazimene adachita. Ndipo Allah satsogolera anthu osakhulupirira.

وَمَثَلُ ٱلَّذِینَ یُنفِقُونَ أَمۡوَ ٰ⁠لَهُمُ ٱبۡتِغَاۤءَ مَرۡضَاتِ ٱللَّهِ وَتَثۡبِیتࣰا مِّنۡ أَنفُسِهِمۡ كَمَثَلِ جَنَّةِۭ بِرَبۡوَةٍ أَصَابَهَا وَابِلࣱ فَـَٔاتَتۡ أُكُلَهَا ضِعۡفَیۡنِ فَإِن لَّمۡ یُصِبۡهَا وَابِلࣱ فَطَلࣱّۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِیرٌ ﴿265﴾

Ndipo fanizo la anthu amene akupereka chuma chawo chifukwa chofuna chiyanjo cha Allah ndi kulimbikitsa mitima yawo (pa chipembedzo cha Allah) lili ngati fanizo la munda umene uli pachitunda, chiufikira chimvula tero nubweretsa zinthu zake dzochuluka moonjeza kawiri (kuposera pachikhalidwe chake). Ndipo ngati chimvula sichidaudzere, ndiye kuti yamawawa (nkuukwanira mundawo). Ndipo Allah akuona zonse zimene mukuchita.

أَیَوَدُّ أَحَدُكُمۡ أَن تَكُونَ لَهُۥ جَنَّةࣱ مِّن نَّخِیلࣲ وَأَعۡنَابࣲ تَجۡرِی مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَـٰرُ لَهُۥ فِیهَا مِن كُلِّ ٱلثَّمَرَ ٰ⁠تِ وَأَصَابَهُ ٱلۡكِبَرُ وَلَهُۥ ذُرِّیَّةࣱ ضُعَفَاۤءُ فَأَصَابَهَاۤ إِعۡصَارࣱ فِیهِ نَارࣱ فَٱحۡتَرَقَتۡۗ كَذَ ٰ⁠لِكَ یُبَیِّنُ ٱللَّهُ لَكُمُ ٱلۡـَٔایَـٰتِ لَعَلَّكُمۡ تَتَفَكَّرُونَ ﴿266﴾

Kodi mmodzi wa inu angakonde kukhala ndi munda wa mitengo ya kanjedza ndi mphesa womwe pansi pake mitsinje ikuyenda, iye mmenemo napeza dzinthu dzamitundumitundu, numpeza ukalamba uku ali ndi ana ofooka; ndipo kamvuluvulu wa moto naugwera (mundawo), nupseleratu (angazikonde zimenezi)? Umo ndimomwe Allah akukulongosolerani ma Ayah (ndime za mawu Ake) kuti muganizire.

یَـٰۤأَیُّهَا ٱلَّذِینَ ءَامَنُوۤا۟ أَنفِقُوا۟ مِن طَیِّبَـٰتِ مَا كَسَبۡتُمۡ وَمِمَّاۤ أَخۡرَجۡنَا لَكُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِۖ وَلَا تَیَمَّمُوا۟ ٱلۡخَبِیثَ مِنۡهُ تُنفِقُونَ وَلَسۡتُم بِـَٔاخِذِیهِ إِلَّاۤ أَن تُغۡمِضُوا۟ فِیهِۚ وَٱعۡلَمُوۤا۟ أَنَّ ٱللَّهَ غَنِیٌّ حَمِیدٌ ﴿267﴾

E inu amene mwakhulupirira! Perekani zabwino zochokera m’zimene mwapeza ndi zimene takutulutsirani m’nthaka, ndipo musalinge kupereka choipa chomwe inu simukadachilandira (ngati akanakupatsani) pokhapokha mochitsinzinira. (Nanga Allah ndiye alandire choipacho)? Ndipo dziwani kuti Allah Ngolemera (ndiponso) Ngotamandidwa.

ٱلشَّیۡطَـٰنُ یَعِدُكُمُ ٱلۡفَقۡرَ وَیَأۡمُرُكُم بِٱلۡفَحۡشَاۤءِۖ وَٱللَّهُ یَعِدُكُم مَّغۡفِرَةࣰ مِّنۡهُ وَفَضۡلࣰاۗ وَٱللَّهُ وَ ٰ⁠سِعٌ عَلِیمࣱ ﴿268﴾

Satana amakuopsezani ndi umphawi ndi kukulamulirani kuchita zoipa (monga umbombo), pomwe Allah akukulonjezani chikhululuko kuchokera kwa Iye ndi ubwino (waukulu ngati mupereka); ndipo Allah ali nazo zambiri, Ngodziwa.[54]

یُؤۡتِی ٱلۡحِكۡمَةَ مَن یَشَاۤءُۚ وَمَن یُؤۡتَ ٱلۡحِكۡمَةَ فَقَدۡ أُوتِیَ خَیۡرࣰا كَثِیرࣰاۗ وَمَا یَذَّكَّرُ إِلَّاۤ أُو۟لُوا۟ ٱلۡأَلۡبَـٰبِ ﴿269﴾

Amapatsa nzeru (zothandiza) amene wamfuna; ndipo amene wapatsidwa nzeru, ndithudi, wapatsidwa zabwino zambiri. Ndipo (zoterezi) sakumbukira koma eni nzeru okha.

وَمَاۤ أَنفَقۡتُم مِّن نَّفَقَةٍ أَوۡ نَذَرۡتُم مِّن نَّذۡرࣲ فَإِنَّ ٱللَّهَ یَعۡلَمُهُۥۗ وَمَا لِلظَّـٰلِمِینَ مِنۡ أَنصَارٍ ﴿270﴾

Ndipo chilichonse chomwe mungapereke kapena naziri (lonjezo) iliyonse yomwe mwalonjeza Allah, ndithudi, Allah akudziwa zonsezi. Ndipo anthu ochita zoipa sadzakhala ndi athandizi.

إِن تُبۡدُوا۟ ٱلصَّدَقَـٰتِ فَنِعِمَّا هِیَۖ وَإِن تُخۡفُوهَا وَتُؤۡتُوهَا ٱلۡفُقَرَاۤءَ فَهُوَ خَیۡرࣱ لَّكُمۡۚ وَیُكَفِّرُ عَنكُم مِّن سَیِّـَٔاتِكُمۡۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِیرࣱ ﴿271﴾

Ngati mupereka sadaka moonetsera, ndibwino; ngati mungaipereke mobisa, ndikuipereka kwa osauka, umenewo ndiubwino woposa kwa inu. Ndipo akufafanizirani zoipa zanu (ngati mutero). Ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita.

۞ لَّیۡسَ عَلَیۡكَ هُدَىٰهُمۡ وَلَـٰكِنَّ ٱللَّهَ یَهۡدِی مَن یَشَاۤءُۗ وَمَا تُنفِقُوا۟ مِنۡ خَیۡرࣲ فَلِأَنفُسِكُمۡۚ وَمَا تُنفِقُونَ إِلَّا ٱبۡتِغَاۤءَ وَجۡهِ ٱللَّهِۚ وَمَا تُنفِقُوا۟ مِنۡ خَیۡرࣲ یُوَفَّ إِلَیۡكُمۡ وَأَنتُمۡ لَا تُظۡلَمُونَ ﴿272﴾

Siudindo wako kuwaongola, koma Allah amamuongola amene wamfuna, (udindo wako nkulalikira kokha). Ndipo chuma chilichonse chimene mungachipereke, (phindu lake) lili pa inu eni, ndipo musapereke pokhapokha pofunafuna chikondi cha Allah. Ndipo chuma chilichonse chimene mungachipereke adzakubwezerani mokwanira (mphoto yake), ndipo simudzaponderezedwa.[55]

لِلۡفُقَرَاۤءِ ٱلَّذِینَ أُحۡصِرُوا۟ فِی سَبِیلِ ٱللَّهِ لَا یَسۡتَطِیعُونَ ضَرۡبࣰا فِی ٱلۡأَرۡضِ یَحۡسَبُهُمُ ٱلۡجَاهِلُ أَغۡنِیَاۤءَ مِنَ ٱلتَّعَفُّفِ تَعۡرِفُهُم بِسِیمَـٰهُمۡ لَا یَسۡـَٔلُونَ ٱلنَّاسَ إِلۡحَافࣰاۗ وَمَا تُنفِقُوا۟ مِنۡ خَیۡرࣲ فَإِنَّ ٱللَّهَ بِهِۦ عَلِیمٌ ﴿273﴾

(Sadakazo ziperekedwe) kwa amphawi amene atsekerezedwa pa njira ya Allah, amene sangathe kuyenda pa dziko (kukachita ntchito yopezera zofunika pamoyo wawo). Amene sadziwa za chikhalidwe chawo, amawaganizira kuti ngolemera chifukwa chakudziletsa kwawo (kupemphapempha). Ungawazindikire (kuti ngosowedwa) ndi zizindikiro zawo. Sapempha anthu mwaliuma. Ndipo chabwino chilichonse chimene mukupereka, ndithudi, Allah ali Wodziwa za icho.

ٱلَّذِینَ یُنفِقُونَ أَمۡوَ ٰ⁠لَهُم بِٱلَّیۡلِ وَٱلنَّهَارِ سِرࣰّا وَعَلَانِیَةࣰ فَلَهُمۡ أَجۡرُهُمۡ عِندَ رَبِّهِمۡ وَلَا خَوۡفٌ عَلَیۡهِمۡ وَلَا هُمۡ یَحۡزَنُونَ ﴿274﴾

Amene akupereka chuma chawo usiku ndi usana, mobisa ndi moonekera, ali ndi malipiro awo kwa Mbuye wawo; ndipo pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso sadzadandaula.

ٱلَّذِینَ یَأۡكُلُونَ ٱلرِّبَوٰا۟ لَا یَقُومُونَ إِلَّا كَمَا یَقُومُ ٱلَّذِی یَتَخَبَّطُهُ ٱلشَّیۡطَـٰنُ مِنَ ٱلۡمَسِّۚ ذَ ٰ⁠لِكَ بِأَنَّهُمۡ قَالُوۤا۟ إِنَّمَا ٱلۡبَیۡعُ مِثۡلُ ٱلرِّبَوٰا۟ۗ وَأَحَلَّ ٱللَّهُ ٱلۡبَیۡعَ وَحَرَّمَ ٱلرِّبَوٰا۟ۚ فَمَن جَاۤءَهُۥ مَوۡعِظَةࣱ مِّن رَّبِّهِۦ فَٱنتَهَىٰ فَلَهُۥ مَا سَلَفَ وَأَمۡرُهُۥۤ إِلَى ٱللَّهِۖ وَمَنۡ عَادَ فَأُو۟لَـٰۤىِٕكَ أَصۡحَـٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِیهَا خَـٰلِدُونَ ﴿275﴾

Amene akudya riba (chuma cha katapira) sadzauka (m’manda) koma monga momwe amaimira munthu okhudzidwa ndi ziwanda, mwamisala. (Ndipo) izi nchifukwa chakuti amanena: “Malonda ngolingana ndi katapira,” pomwe Allah waloleza malonda ndipo waletsa katapira. Ndipo amene wamufika ulaliki wochokera kwa Mbuye wake (woletsa katapira) nasiya, choncho chomwe chidapita nchake. Ndipo chiweruzo chake chili kwa Allah (akaona chochita naye). Koma amene abwerera (kuchita malonda a katapira), amenewo ndiwo anthu a ku Moto, mmenemo adzakhalamo nthawi yaitali.[56]

یَمۡحَقُ ٱللَّهُ ٱلرِّبَوٰا۟ وَیُرۡبِی ٱلصَّدَقَـٰتِۗ وَٱللَّهُ لَا یُحِبُّ كُلَّ كَفَّارٍ أَثِیمٍ ﴿276﴾

Allah amachotsa madalitso pa (chuma cha) katapira ndipo amaika madalitso pa chaulere. Ndipo Allah sakonda aliyense wosakhulupirira, wamachimo ambiri.

إِنَّ ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ وَعَمِلُوا۟ ٱلصَّـٰلِحَـٰتِ وَأَقَامُوا۟ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتَوُا۟ ٱلزَّكَوٰةَ لَهُمۡ أَجۡرُهُمۡ عِندَ رَبِّهِمۡ وَلَا خَوۡفٌ عَلَیۡهِمۡ وَلَا هُمۡ یَحۡزَنُونَ ﴿277﴾

Ndithudi, amene akhulupirira, nachita zabwino, napemphera Swala moyenera ndi kupereka chopereka (Zakaat), iwo akapeza malipiro awo kwa Mbuye wawo. Ndipo pa iwo sipadzakhala mantha ndiponso sadzadandaula.

یَـٰۤأَیُّهَا ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ ٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ وَذَرُوا۟ مَا بَقِیَ مِنَ ٱلرِّبَوٰۤا۟ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِینَ ﴿278﴾

E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah, ndipo siyani zimene zatsalira m’katapira, ngati inu mulidi okhulupirira.

فَإِن لَّمۡ تَفۡعَلُوا۟ فَأۡذَنُوا۟ بِحَرۡبࣲ مِّنَ ٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦۖ وَإِن تُبۡتُمۡ فَلَكُمۡ رُءُوسُ أَمۡوَ ٰ⁠لِكُمۡ لَا تَظۡلِمُونَ وَلَا تُظۡلَمُونَ ﴿279﴾

Ngati simuchita (zimenezo), dziwani kuti mukulimbana ndi Allah ndi Mtumiki Wake. Ndipo ngati mulapa, maziko a chuma chanu ndi anu. Musapondereze, ndiponso musaponderezedwe.

وَإِن كَانَ ذُو عُسۡرَةࣲ فَنَظِرَةٌ إِلَىٰ مَیۡسَرَةࣲۚ وَأَن تَصَدَّقُوا۟ خَیۡرࣱ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ ﴿280﴾

Ndipo ngati wokongola ali ndi mavuto, choncho (wokongoza) amdikire mpaka apeze bwino. Koma ngati inu (okongoza mungakhululuke pakusiya kuitanitsa ngongole) muisintha kuti ikhale sadaka, ndibwino kwa inu ngati mukudziwa (zimenezo).

وَٱتَّقُوا۟ یَوۡمࣰا تُرۡجَعُونَ فِیهِ إِلَى ٱللَّهِۖ ثُمَّ تُوَفَّىٰ كُلُّ نَفۡسࣲ مَّا كَسَبَتۡ وَهُمۡ لَا یُظۡلَمُونَ ﴿281﴾

Ndipo liopeni tsiku lomwe inu mudzabwezedwa kwa Allah. Ndipo kenako munthu aliyense adzalipidwa mokwanira pa zonse zimene adachita (ndi manja ake), ndipo iwo sadzaponderezedwa.

۞ وَإِن كُنتُمۡ عَلَىٰ سَفَرࣲ وَلَمۡ تَجِدُوا۟ كَاتِبࣰا فَرِهَـٰنࣱ مَّقۡبُوضَةࣱۖ فَإِنۡ أَمِنَ بَعۡضُكُم بَعۡضࣰا فَلۡیُؤَدِّ ٱلَّذِی ٱؤۡتُمِنَ أَمَـٰنَتَهُۥ وَلۡیَتَّقِ ٱللَّهَ رَبَّهُۥۗ وَلَا تَكۡتُمُوا۟ ٱلشَّهَـٰدَةَۚ وَمَن یَكۡتُمۡهَا فَإِنَّهُۥۤ ءَاثِمࣱ قَلۡبُهُۥۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ عَلِیمࣱ ﴿283﴾

Ndipo ngati muli pa ulendo, ndipo simudapeze mlembi, choncho (wokongoza) apatsidwe chikole (pinyolo) m’manja mwake. Ngati wina wasungitsa mmodzi wa inu chinthu (pomudalira wokhulupirika) choncho amene wayesedwa wokhulupirikayo abweze chinthucho kwa mwini wake, ndipo aope Allah, Mbuye wake. Ndipo musabise umboni (ngakhale uli wokuipirani). Ndipo amene abise ndiye kuti mu mtima mwake mwalowa uchimo; ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita.[58]

لِّلَّهِ مَا فِی ٱلسَّمَـٰوَ ٰ⁠تِ وَمَا فِی ٱلۡأَرۡضِۗ وَإِن تُبۡدُوا۟ مَا فِیۤ أَنفُسِكُمۡ أَوۡ تُخۡفُوهُ یُحَاسِبۡكُم بِهِ ٱللَّهُۖ فَیَغۡفِرُ لِمَن یَشَاۤءُ وَیُعَذِّبُ مَن یَشَاۤءُۗ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَیۡءࣲ قَدِیرٌ ﴿284﴾

Zonse zakumwamba ndi zapansi nza Allah. Kaya muonetsera poyera zomwe zili m’mitima mwanu kapena kuzibisa, Allah adzakuchitirani nazo chiwerengero. Kenako adzakhululukira amene wamfuna (atalapa). Ndipo adzamlanga amene wamfuna (akapanda kulapa). Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.

ءَامَنَ ٱلرَّسُولُ بِمَاۤ أُنزِلَ إِلَیۡهِ مِن رَّبِّهِۦ وَٱلۡمُؤۡمِنُونَۚ كُلٌّ ءَامَنَ بِٱللَّهِ وَمَلَـٰۤىِٕكَتِهِۦ وَكُتُبِهِۦ وَرُسُلِهِۦ لَا نُفَرِّقُ بَیۡنَ أَحَدࣲ مِّن رُّسُلِهِۦۚ وَقَالُوا۟ سَمِعۡنَا وَأَطَعۡنَاۖ غُفۡرَانَكَ رَبَّنَا وَإِلَیۡكَ ٱلۡمَصِیرُ ﴿285﴾

Mtumiki wakhulupirira zimene zavumbulutsidwa kwa iye kuchokera kwa Mbuye wake. Naonso asilamu (akhulupirira). Onse akhulupirira Allah, angelo Ake, mabuku Ake ndi atumiki Ake. (Iwo pamodzi ndi Mtumiki wawoyo akunena kuti): “Sitingalekanitse aliyense pakati pa atumiki Ake, (onse tikuwakhulupirira).” Ndipo akunena: “Tamva ndiponso tamvera, (choncho tikukupemphani) chikhululuko chanu. E Mbuye wathu! Ndipo kwa Inu nkobwerera.”[59]

لَا یُكَلِّفُ ٱللَّهُ نَفۡسًا إِلَّا وُسۡعَهَاۚ لَهَا مَا كَسَبَتۡ وَعَلَیۡهَا مَا ٱكۡتَسَبَتۡۗ رَبَّنَا لَا تُؤَاخِذۡنَاۤ إِن نَّسِینَاۤ أَوۡ أَخۡطَأۡنَاۚ رَبَّنَا وَلَا تَحۡمِلۡ عَلَیۡنَاۤ إِصۡرࣰا كَمَا حَمَلۡتَهُۥ عَلَى ٱلَّذِینَ مِن قَبۡلِنَاۚ رَبَّنَا وَلَا تُحَمِّلۡنَا مَا لَا طَاقَةَ لَنَا بِهِۦۖ وَٱعۡفُ عَنَّا وَٱغۡفِرۡ لَنَا وَٱرۡحَمۡنَاۤۚ أَنتَ مَوۡلَىٰنَا فَٱنصُرۡنَا عَلَى ٱلۡقَوۡمِ ٱلۡكَـٰفِرِینَ ﴿286﴾

Allah sakakamiza mzimu uliwonse koma chimene chili cholingana ndi kukhoza kwake. (Ndipo phindu la) zimene mzimuwo udapeza ndilake ndiponso kuluza kwa zomwe udapeza nkwake. (Asilamuwo amanena) “E Mbuye wathu! Musatilange tikaiwala kapena tikalakwitsa, E Mbuye wathu! Musatisenzetse mtolo (wamalamulo) monga munawasenzetsera amene adalipo patsogolo pathu. E Mbuye wathu! Musatisenzetse chimene sitingachithe. Tifafanizireni machimo athu, tikhululukireni zolakwa zathu, ndiponso tichitireni chifundo. Inu Ndinu Mtetezi wathu. Choncho tithangateni ku anthu osakhulupirira.”