Settings
Surah Taha [Taha] in Chewa
طه ﴿1﴾
Tâ-Hâ [271]
مَآ أَنزَلْنَا عَلَيْكَ ٱلْقُرْءَانَ لِتَشْقَىٰٓ ﴿2﴾
Sitidakuvumbulutsire iwe Qur’an kuti uvutike (nayo).
إِلَّا تَذْكِرَةًۭ لِّمَن يَخْشَىٰ ﴿3﴾
Koma kuti ikhale ulaliki ndi chikumbutso kwa yemwe akuopa (ndikudzichepetsa kwa Allah).
تَنزِيلًۭا مِّمَّنْ خَلَقَ ٱلْأَرْضَ وَٱلسَّمَٰوَٰتِ ٱلْعُلَى ﴿4﴾
Chovumbulitsidwa chochokera kwa Yemwe adalenga nthaka ndi thambo lotukuka kumwamba.
ٱلرَّحْمَٰنُ عَلَى ٱلْعَرْشِ ٱسْتَوَىٰ ﴿5﴾
(Iye ndi Allah), Wachifundo Chambiri; pa Arsh (Mpando wachifumu) adakhazikika, (kukhazikika koyenerana ndi ulemelero Wake kopanda kukufanizira ndi kukhazikika kwa chilichonse; pakuti Iye salingana ndi chilichonse pa chikhalidwe ndi mbiri Zake).
لَهُۥ مَا فِى ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِى ٱلْأَرْضِ وَمَا بَيْنَهُمَا وَمَا تَحْتَ ٱلثَّرَىٰ ﴿6﴾
Zonse za kumwamba ndi za pansi ndi za pakati pake ndi za pansi pa nthaka, nza Iye.
وَإِن تَجْهَرْ بِٱلْقَوْلِ فَإِنَّهُۥ يَعْلَمُ ٱلسِّرَّ وَأَخْفَى ﴿7﴾
Ndipo ngati ulankhula mokweza mawu, (iwe munthu), ndithu Iye akudziwa zobisika ndi zobisika kwambiri (zomwe mwazibisa mu mtima mwanu).[272]
ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ لَهُ ٱلْأَسْمَآءُ ٱلْحُسْنَىٰ ﴿8﴾
Allah! Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Iye ali ndi maina abwino (ndi mbiri zabwinonso).
وَهَلْ أَتَىٰكَ حَدِيثُ مُوسَىٰٓ ﴿9﴾
Ndipo kodi yakufika nkhani ya Mûsa? (Yomwe njododometsa)?[273]
إِذْ رَءَا نَارًۭا فَقَالَ لِأَهْلِهِ ٱمْكُثُوٓا۟ إِنِّىٓ ءَانَسْتُ نَارًۭا لَّعَلِّىٓ ءَاتِيكُم مِّنْهَا بِقَبَسٍ أَوْ أَجِدُ عَلَى ٱلنَّارِ هُدًۭى ﴿10﴾
Pamene adaona moto adauza banja lake: “Yembekezani (pano); ndithu ndaona moto; mwina ndingakakutengereni chikuni chamoto (kuti muothe), kapena ndikapeza ondiongolera njira pa motopo.
فَلَمَّآ أَتَىٰهَا نُودِىَ يَٰمُوسَىٰٓ ﴿11﴾
Koma pamene adaudzera motowo Anaitanidwa (kuti), “E, iwe Mûsa!
إِنِّىٓ أَنَا۠ رَبُّكَ فَٱخْلَعْ نَعْلَيْكَ ۖ إِنَّكَ بِٱلْوَادِ ٱلْمُقَدَّسِ طُوًۭى ﴿12﴾
Ndithu ine ndine Mbuye wako! Vula nsapato zakozo; ndithu iwe uli pa chigwa chopatulika, chotchedwa Tuwa.”
وَأَنَا ٱخْتَرْتُكَ فَٱسْتَمِعْ لِمَا يُوحَىٰٓ ﴿13﴾
Ndipo Ine ndakusankha (kuti ukhale Mtumiki); choncho mvera zonse zomwe zikuvumbulutsidwa (kwa iwe).
إِنَّنِىٓ أَنَا ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّآ أَنَا۠ فَٱعْبُدْنِى وَأَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ لِذِكْرِىٓ ﴿14﴾
Ndithu Ine ndine Allah palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine; choncho ndipembeze, pemphera Swala moyenera pondikumbukira.
إِنَّ ٱلسَّاعَةَ ءَاتِيَةٌ أَكَادُ أُخْفِيهَا لِتُجْزَىٰ كُلُّ نَفْسٍۭ بِمَا تَسْعَىٰ ﴿15﴾
Ndithu nthawi ya tsiku lachimaliziro idza; (choncho ikonzekere ndi ntchito zabwino); ndikuibisa dala (kwa anthu) kuti mzimu uliwonse udzalipidwe zimene udachita.[274]
فَلَا يَصُدَّنَّكَ عَنْهَا مَن لَّا يُؤْمِنُ بِهَا وَٱتَّبَعَ هَوَىٰهُ فَتَرْدَىٰ ﴿16﴾
Ndipo asakutsekereze (ku khulupirira) zimenezo yemwe saikhulupirira (Kiyamayo), ndipo akungotsata zilakolako za mtima wake; kuopa kuti Ungadzaonongeke.”
وَمَا تِلْكَ بِيَمِينِكَ يَٰمُوسَىٰ ﴿17﴾
“Kodi nchiyani icho chili kudzanja Lako ladzanjadzanja, iwe Mûsa?”
قَالَ هِىَ عَصَاىَ أَتَوَكَّؤُا۟ عَلَيْهَا وَأَهُشُّ بِهَا عَلَىٰ غَنَمِى وَلِىَ فِيهَا مَـَٔارِبُ أُخْرَىٰ ﴿18﴾
(Mûsa) adati: “Iyi ndi ndodo yanga, ndimaitsamira (poyenda) ndi kuphopholera masamba a mbuzi zanga; ndiponso (m’ndodomo) muli zina zondithandiza.”[275]
قَالَ أَلْقِهَا يَٰمُوسَىٰ ﴿19﴾
(Allah) adati: “Iponye iwe Mûsa!”
فَأَلْقَىٰهَا فَإِذَا هِىَ حَيَّةٌۭ تَسْعَىٰ ﴿20﴾
Ndipo adaiponya; pompo idasanduka njoka yoyenda mothamanga. [276]
قَالَ خُذْهَا وَلَا تَخَفْ ۖ سَنُعِيدُهَا سِيرَتَهَا ٱلْأُولَىٰ ﴿21﴾
(Allah) adati: “Igwire, usaope. Tiibwezera m’chikhalidwe chake Choyamba.”
وَٱضْمُمْ يَدَكَ إِلَىٰ جَنَاحِكَ تَخْرُجْ بَيْضَآءَ مِنْ غَيْرِ سُوٓءٍ ءَايَةً أُخْرَىٰ ﴿22﴾
“Ndipo lipane dzanja lako m’khwapa mwako lituluka lili loyera (ngati kuwala kwadzuwa ndi mwezi). Osati mwamatenda, (ichi chikhala) chozizwitsa china.”[277]
لِنُرِيَكَ مِنْ ءَايَٰتِنَا ٱلْكُبْرَى ﴿23﴾
“Kuti tikusonyeze zina mwa zozizwitsa zathu, zazikuluzikulu.”
ٱذْهَبْ إِلَىٰ فِرْعَوْنَ إِنَّهُۥ طَغَىٰ ﴿24﴾
“Pita kwa Farawo, ndithu iye wapyola malire.”
قَالَ رَبِّ ٱشْرَحْ لِى صَدْرِى ﴿25﴾
(Mûsa) adati: “E Mbuye wanga! Nditsakulireni chifuwa changa.”
وَيَسِّرْ لِىٓ أَمْرِى ﴿26﴾
“Ndi kundifewetsera ntchito yangayi (imene mwandipatsa kuti uthengawu ndikaufalitse m’njira yoyenera).”
وَٱحْلُلْ عُقْدَةًۭ مِّن لِّسَانِى ﴿27﴾
“Ndipo masulani mfundo yomwe ili ku lirime kwanga, (ndimasulireni kumangika kwa lirime langa kuti mawu anga akakhale opanda chibwibwi).”[278]
يَفْقَهُوا۟ قَوْلِى ﴿28﴾
“Kuti (anthu) akamvetse mawu anga.”
وَٱجْعَل لِّى وَزِيرًۭا مِّنْ أَهْلِى ﴿29﴾
“Ndipo ndipatseni nduna (mthandizi) yochokera kubanja langa.”
هَٰرُونَ أَخِى ﴿30﴾
“M’bale wanga Harun.”
ٱشْدُدْ بِهِۦٓ أَزْرِى ﴿31﴾
“Limbitsani nyonga zanga ndi iye.”
وَأَشْرِكْهُ فِىٓ أَمْرِى ﴿32﴾
“Ndipo mphatikeni ku ntchito yangayi.”
كَىْ نُسَبِّحَكَ كَثِيرًۭا ﴿33﴾
“Kuti tikulemekezeni kwambiri.”
وَنَذْكُرَكَ كَثِيرًا ﴿34﴾
“Ndi kukutamandani kwabasi.”
إِنَّكَ كُنتَ بِنَا بَصِيرًۭا ﴿35﴾
“Ndithu inu (nthawi zonse) mumationa (ndi kutisunga).”
قَالَ قَدْ أُوتِيتَ سُؤْلَكَ يَٰمُوسَىٰ ﴿36﴾
(Allah) adati: “Ndithu wapatsidwa zomwe wapempha, E, iwe Mûsa.”
وَلَقَدْ مَنَنَّا عَلَيْكَ مَرَّةً أُخْرَىٰٓ ﴿37﴾
“Ndipo ndithu tidakuchitira ubwino nthawi ina (popanda iwe kutipempha).”
إِذْ أَوْحَيْنَآ إِلَىٰٓ أُمِّكَ مَا يُوحَىٰٓ ﴿38﴾
“Pamene mayi wako tidamuzindikiritsa zimene tidamzindikiritsa (kuti azichite).”
أَنِ ٱقْذِفِيهِ فِى ٱلتَّابُوتِ فَٱقْذِفِيهِ فِى ٱلْيَمِّ فَلْيُلْقِهِ ٱلْيَمُّ بِٱلسَّاحِلِ يَأْخُذْهُ عَدُوٌّۭ لِّى وَعَدُوٌّۭ لَّهُۥ ۚ وَأَلْقَيْتُ عَلَيْكَ مَحَبَّةًۭ مِّنِّى وَلِتُصْنَعَ عَلَىٰ عَيْنِىٓ ﴿39﴾
(Kuti): “Mponye (mwanayo) m’bokosi ndipo ponya bokosilo mu mtsinje; ndipo mtsinje umponya m’mbali kuti amtenge mdani wanga ndi mdani wake (ndi kuti aleredwe mwaubwino ndi Farawo); ndipo ndidaika kukondeka pa iwe kochokera kwa Ine (kuti ukhale wokondedwa ndi anthu onse) ndikuti uleredwe moyang’aniridwa ndi Ine.”
إِذْ تَمْشِىٓ أُخْتُكَ فَتَقُولُ هَلْ أَدُلُّكُمْ عَلَىٰ مَن يَكْفُلُهُۥ ۖ فَرَجَعْنَٰكَ إِلَىٰٓ أُمِّكَ كَىْ تَقَرَّ عَيْنُهَا وَلَا تَحْزَنَ ۚ وَقَتَلْتَ نَفْسًۭا فَنَجَّيْنَٰكَ مِنَ ٱلْغَمِّ وَفَتَنَّٰكَ فُتُونًۭا ۚ فَلَبِثْتَ سِنِينَ فِىٓ أَهْلِ مَدْيَنَ ثُمَّ جِئْتَ عَلَىٰ قَدَرٍۢ يَٰمُوسَىٰ ﴿40﴾
(Kumbuka) pomwe mlongo wako ankayenda (kunka kubanja la Farawo) Ndipo adati: “Kodi ndikulondolereni munthu amene angathe kumlera?” Ndipo tidakubwezera kwa mayi wako kuti maso ake atonthole, ndipo asadandaule. Ndipo kenaka udapha munthu (mwangozi), ndipo tidakupulumutsa ku madandaulo; tidakuyesa ndi mayeso ambiri. Udakhala zaka zambiri ndi anthu a ku Madiyan. Kenaka wabwera (apa) monga mwachikonzero, E, iwe Mûsa![279]
وَٱصْطَنَعْتُكَ لِنَفْسِى ﴿41﴾
Ndipo ndakusankha ndekha (kuti ukhale Mtumiki Wanga).
ٱذْهَبْ أَنتَ وَأَخُوكَ بِـَٔايَٰتِى وَلَا تَنِيَا فِى ذِكْرِى ﴿42﴾
Pita iwe ndi m’bale wako ndi zozizwitsa Zanga, ndipo musatope (musasiye) kundikumbukira.
ٱذْهَبَآ إِلَىٰ فِرْعَوْنَ إِنَّهُۥ طَغَىٰ ﴿43﴾
Pitani kwa Farawo, ndithu iye wapyola malire.
فَقُولَا لَهُۥ قَوْلًۭا لَّيِّنًۭا لَّعَلَّهُۥ يَتَذَكَّرُ أَوْ يَخْشَىٰ ﴿44﴾
Kamuuzeni mawu ofewa mwina akalingalira (uthengawo) kapena akaopa.
قَالَا رَبَّنَآ إِنَّنَا نَخَافُ أَن يَفْرُطَ عَلَيْنَآ أَوْ أَن يَطْغَىٰ ﴿45﴾
(Iwo) adati: “Mbuye wathu ndithu ife tikuopa kuti angatimbwandire kapena kutipyolera malire (tisananene kanthu).”
قَالَ لَا تَخَافَآ ۖ إِنَّنِى مَعَكُمَآ أَسْمَعُ وَأَرَىٰ ﴿46﴾
(Allah) adati: “Musaope. Ndithu Ine ndili nanu pamodzi. ndikumva, ndiponso ndikuona.”
فَأْتِيَاهُ فَقُولَآ إِنَّا رَسُولَا رَبِّكَ فَأَرْسِلْ مَعَنَا بَنِىٓ إِسْرَٰٓءِيلَ وَلَا تُعَذِّبْهُمْ ۖ قَدْ جِئْنَٰكَ بِـَٔايَةٍۢ مِّن رَّبِّكَ ۖ وَٱلسَّلَٰمُ عَلَىٰ مَنِ ٱتَّبَعَ ٱلْهُدَىٰٓ ﴿47﴾
Choncho mpitireni, ndikumuuza (kuti): “Ndithu ife ndife atumiki a Mbuye wako. Asiye ana a Israyeli achoke ndi ife, ndipo usawazunze; ndithu takudzera ndi chozizwitsa chochokera kwa Mbuye wako (chomwe ndi mboni yathu pa zomwe tikukuuzazi), ndipo mtendere ukhala pa yemwe atsate chiwongoko.”
إِنَّا قَدْ أُوحِىَ إِلَيْنَآ أَنَّ ٱلْعَذَابَ عَلَىٰ مَن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ ﴿48﴾
“Ndithu zavumbulutsidwa kwa ife kuti chilango chiwapeza amene akutsutsa (zimenezi) ndikuzitembenukira kumbali.”
قَالَ فَمَن رَّبُّكُمَا يَٰمُوسَىٰ ﴿49﴾
(Farawo) adati: “Kodi Mbuye wanu ndani, iwe Mûsa?”
قَالَ رَبُّنَا ٱلَّذِىٓ أَعْطَىٰ كُلَّ شَىْءٍ خَلْقَهُۥ ثُمَّ هَدَىٰ ﴿50﴾
(Mûsa) adati: “Mbuye wathu ndi yemwe adapatsa chinthu chilichonse chilengedwe chake, kenako adachiongolera (kutsata chimene chikulingana ndi chilengedwe chake).”
قَالَ فَمَا بَالُ ٱلْقُرُونِ ٱلْأُولَىٰ ﴿51﴾
(Farawo) adati: “Nanga mibadwo yakale ili bwanji, (imene idapita iwe usadadze?”)
قَالَ عِلْمُهَا عِندَ رَبِّى فِى كِتَٰبٍۢ ۖ لَّا يَضِلُّ رَبِّى وَلَا يَنسَى ﴿52﴾
(Mûsa) adati: “Kudziwa kwa zimenezo nkwa Mbuye wanga, m’kaundula (Wake momwe mwasonkhanitsidwa chilichonse), Mbuye wanga sasokera, ndipo saiwala.
ٱلَّذِى جَعَلَ لَكُمُ ٱلْأَرْضَ مَهْدًۭا وَسَلَكَ لَكُمْ فِيهَا سُبُلًۭا وَأَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءًۭ فَأَخْرَجْنَا بِهِۦٓ أَزْوَٰجًۭا مِّن نَّبَاتٍۢ شَتَّىٰ ﴿53﴾
Yemwe adakupangirani nthaka monga choyala, ndipo m’menemo adakuikirani njira ndikutsitsa madzi kuchokera kumwamba.” Ndipo kupyolera m’madziwo tidameretsa mmera wosiyanasiyana.
كُلُوا۟ وَٱرْعَوْا۟ أَنْعَٰمَكُمْ ۗ إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَءَايَٰتٍۢ لِّأُو۟لِى ٱلنُّهَىٰ ﴿54﴾
Idyani ndikudyetsa ziweto zanu. Ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa eni nzeru.
۞ مِنْهَا خَلَقْنَٰكُمْ وَفِيهَا نُعِيدُكُمْ وَمِنْهَا نُخْرِجُكُمْ تَارَةً أُخْرَىٰ ﴿55﴾
Kuchokera (m’nthaka) umu tidakulengani, ndipo momwemo tidzakubwezani, ndipo kuchokera m’menemo tidzakutulutsani nthawi ina (muli moyo).
وَلَقَدْ أَرَيْنَٰهُ ءَايَٰتِنَا كُلَّهَا فَكَذَّبَ وَأَبَىٰ ﴿56﴾
Ndipo, ndithu tidamuonetsa (Farawo) zozizwitsa zathu zonse, koma adatsutsa ndipo adakana.
قَالَ أَجِئْتَنَا لِتُخْرِجَنَا مِنْ أَرْضِنَا بِسِحْرِكَ يَٰمُوسَىٰ ﴿57﴾
Adati: “Kodi watidzera kuti utitulutse m’dziko lathu, ndi matsenga ako, E, iwe Mûsa!
فَلَنَأْتِيَنَّكَ بِسِحْرٍۢ مِّثْلِهِۦ فَٱجْعَلْ بَيْنَنَا وَبَيْنَكَ مَوْعِدًۭا لَّا نُخْلِفُهُۥ نَحْنُ وَلَآ أَنتَ مَكَانًۭا سُوًۭى ﴿58﴾
Choncho nafe tikubweretsera matsenga onga amenewo! Choncho ika lonjezo (la msonkhano) pakati pathu ndi iwe; lonjezo lomwe tisaliswe ife ndi iwe, (tidzakumane) pamalo poyenera.”
قَالَ مَوْعِدُكُمْ يَوْمُ ٱلزِّينَةِ وَأَن يُحْشَرَ ٱلنَّاسُ ضُحًۭى ﴿59﴾
(Mûsa) adati: “Lonjezo lanu likhale pa tsiku lodzikongoletsa (tsiku la chikondwelero), ndipo anthu adzasonkhanitsidwe m’mawa.”
فَتَوَلَّىٰ فِرْعَوْنُ فَجَمَعَ كَيْدَهُۥ ثُمَّ أَتَىٰ ﴿60﴾
Ndipo Farawo adabwerera ndikusonkhanitsa matsenga ake, ndipo kenako adabwera (ndi amatsenga ake pa tsiku la chipanganolo).[280]
قَالَ لَهُم مُّوسَىٰ وَيْلَكُمْ لَا تَفْتَرُوا۟ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًۭا فَيُسْحِتَكُم بِعَذَابٍۢ ۖ وَقَدْ خَابَ مَنِ ٱفْتَرَىٰ ﴿61﴾
Mûsa adawauza: “Tsoka kwa inu! Musampekere bodza Allah, kuopera kuti angakuphwasuleni ndi chilango. Ndipo, ndithu wataika amene akupeka bodza.”
فَتَنَٰزَعُوٓا۟ أَمْرَهُم بَيْنَهُمْ وَأَسَرُّوا۟ ٱلنَّجْوَىٰ ﴿62﴾
Choncho (amatsengawo) adakangana pakati pawo pa zinthu zawo ndipo adakambirana mwachinsinsi.
قَالُوٓا۟ إِنْ هَٰذَٰنِ لَسَٰحِرَٰنِ يُرِيدَانِ أَن يُخْرِجَاكُم مِّنْ أَرْضِكُم بِسِحْرِهِمَا وَيَذْهَبَا بِطَرِيقَتِكُمُ ٱلْمُثْلَىٰ ﴿63﴾
(Iwo) adati (mkunong’onezana kwawo): “Ndithu anthu awiriwa ndi amatsenga; kupyolera mmatsenga awo akufuna kukutulutsani m’dziko mwanu, ndikuchotsa chikhalidwe chanu chomwe chili chabwino.”
فَأَجْمِعُوا۟ كَيْدَكُمْ ثُمَّ ٱئْتُوا۟ صَفًّۭا ۚ وَقَدْ أَفْلَحَ ٱلْيَوْمَ مَنِ ٱسْتَعْلَىٰ ﴿64﴾
“Choncho sonkhanitsani matsenga anu (onse), kenako mudze (kwa iwo) mutandanda pamzere; ndithu lero, apambana amene akhale wapamwamba.”
قَالُوا۟ يَٰمُوسَىٰٓ إِمَّآ أَن تُلْقِىَ وَإِمَّآ أَن نَّكُونَ أَوَّلَ مَنْ أَلْقَىٰ ﴿65﴾
(Iwo) adati: “E iwe Mûsa! Kodi ukhale ndiwe woyamba kuponya (matsenga ako), kapena tikhale oyamba ndife kuponya?”
قَالَ بَلْ أَلْقُوا۟ ۖ فَإِذَا حِبَالُهُمْ وَعِصِيُّهُمْ يُخَيَّلُ إِلَيْهِ مِن سِحْرِهِمْ أَنَّهَا تَسْعَىٰ ﴿66﴾
(Mûsa) adati: “Koma inu ndinu muponye!” (Choncho adaponya matsengawo). Mwadzidzidzi zingwe zawo ndi ndodo zawo zamatsenga awo, zimaoneka pamaso pake (Mûsa) kuti zikuyenda mothamanga.
فَأَوْجَسَ فِى نَفْسِهِۦ خِيفَةًۭ مُّوسَىٰ ﴿67﴾
Ndipo Mûsa adadzazidwa ndi mantha mu mtima mwake.
قُلْنَا لَا تَخَفْ إِنَّكَ أَنتَ ٱلْأَعْلَىٰ ﴿68﴾
Tidati: “Usaope (zomwe ukuzionazi), ndithu iwe ukhala wopambana.”
وَأَلْقِ مَا فِى يَمِينِكَ تَلْقَفْ مَا صَنَعُوٓا۟ ۖ إِنَّمَا صَنَعُوا۟ كَيْدُ سَٰحِرٍۢ ۖ وَلَا يُفْلِحُ ٱلسَّاحِرُ حَيْثُ أَتَىٰ ﴿69﴾
“Ndipo ponya chimene chili kudzanja lako ladzanjadzanja (ndodo); chimeza zomwe apanga; ndithu iwo apanga matsenga a mfiti ndipo mfiti siingapambane paliponse pamene yadza.”[281]
فَأُلْقِىَ ٱلسَّحَرَةُ سُجَّدًۭا قَالُوٓا۟ ءَامَنَّا بِرَبِّ هَٰرُونَ وَمُوسَىٰ ﴿70﴾
Choncho amatsenga adagwa molambira uku akuti: “Tamkhulupirira Mbuye wa Harun ndi Mûsa.”
قَالَ ءَامَنتُمْ لَهُۥ قَبْلَ أَنْ ءَاذَنَ لَكُمْ ۖ إِنَّهُۥ لَكَبِيرُكُمُ ٱلَّذِى عَلَّمَكُمُ ٱلسِّحْرَ ۖ فَلَأُقَطِّعَنَّ أَيْدِيَكُمْ وَأَرْجُلَكُم مِّنْ خِلَٰفٍۢ وَلَأُصَلِّبَنَّكُمْ فِى جُذُوعِ ٱلنَّخْلِ وَلَتَعْلَمُنَّ أَيُّنَآ أَشَدُّ عَذَابًۭا وَأَبْقَىٰ ﴿71﴾
(Farawo) adanena: “Ha! Mwamkhulupirira ndisadakupatseni chilolezo? Ndithu iye ndi mkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga! Choncho ndikudulani manja anu ndi miyendo yanu, mosemphanitsa:; (dzanja lakudzanjadzanja ndi mwendo wakumanzere. Pomwe wina, mkono wakumanzere ndi mwendo wakudzanjadzanja), ndipo kenako ndikupachikani pa mathunthu a mitengo ya kanjeza; ndithu mudziwa (panthawiyo) kuti ndani mwa ife, (ine kapena Mulungu wa Mûsa), wachilango chaukali ndi chopitilira.”[282]
قَالُوا۟ لَن نُّؤْثِرَكَ عَلَىٰ مَا جَآءَنَا مِنَ ٱلْبَيِّنَٰتِ وَٱلَّذِى فَطَرَنَا ۖ فَٱقْضِ مَآ أَنتَ قَاضٍ ۖ إِنَّمَا تَقْضِى هَٰذِهِ ٱلْحَيَوٰةَ ٱلدُّنْيَآ ﴿72﴾
(Amatsenga) adati: “Sitisankha iwe kusiya zomwe zatidzera; zisonyezo zachoonadi zoonekera poyera! Ndipo tikumlumbilira Yemwe adatilenga, (sitikusankha iwe), chita zomwe ufuna kuchita; ndithu iwe utha kupititsa chiweruzo chokhudzana ndi moyo uno wapansi, basi.”
إِنَّآ ءَامَنَّا بِرَبِّنَا لِيَغْفِرَ لَنَا خَطَٰيَٰنَا وَمَآ أَكْرَهْتَنَا عَلَيْهِ مِنَ ٱلسِّحْرِ ۗ وَٱللَّهُ خَيْرٌۭ وَأَبْقَىٰٓ ﴿73﴾
“Ndithu takhulupirira Mbuye wathu kuti atikhululukire zolakwa zathu ndi matsenga amene watikakamiza (kuchita); ndipo Allah ndi Yemwe ali Wabwino ndi Wamuyaya (osati iwe).”
إِنَّهُۥ مَن يَأْتِ رَبَّهُۥ مُجْرِمًۭا فَإِنَّ لَهُۥ جَهَنَّمَ لَا يَمُوتُ فِيهَا وَلَا يَحْيَىٰ ﴿74﴾
Ndithu amene adzadze kwa Mbuye wake uku ali wamachimo, adzapeza moto wa Jahannam; sadzafa m’menemo, ndipo sadzakhalanso ndi moyo wabwino.
وَمَن يَأْتِهِۦ مُؤْمِنًۭا قَدْ عَمِلَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَأُو۟لَٰٓئِكَ لَهُمُ ٱلدَّرَجَٰتُ ٱلْعُلَىٰ ﴿75﴾
Koma amene adzamdzera uku ali wokhulupirira, yemwe adachita ntchito zabwino, iwo ndi amene adzapeze ulemewero wapamwamba.
جَنَّٰتُ عَدْنٍۢ تَجْرِى مِن تَحْتِهَا ٱلْأَنْهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَا ۚ وَذَٰلِكَ جَزَآءُ مَن تَزَكَّىٰ ﴿76﴾
Minda yamuyaya, yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) pakuyenda mitsinje. Adzakhala mmenemo nthawi yaitali. Ndipo zimenezo ndi mphoto za yemwe wadziyeretsa.
وَلَقَدْ أَوْحَيْنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ أَنْ أَسْرِ بِعِبَادِى فَٱضْرِبْ لَهُمْ طَرِيقًۭا فِى ٱلْبَحْرِ يَبَسًۭا لَّا تَخَٰفُ دَرَكًۭا وَلَا تَخْشَىٰ ﴿77﴾
Ndipo ndithu Mûsa tidamtumizira chivumbulutso, (tidamzindikiritsa kuti): “Yenda usiku ndi akapolo Anga (kutuluka m’dziko la Iguputo,) ndipo ukawapangire panyanja njira youma, ndipo usaope kukupeza adani ndiponso usaope (kumira).”
فَأَتْبَعَهُمْ فِرْعَوْنُ بِجُنُودِهِۦ فَغَشِيَهُم مِّنَ ٱلْيَمِّ مَا غَشِيَهُمْ ﴿78﴾
Choncho Farawo pamodzi ndi ankhondo ake, adawatsata, ndipo m’nyanjamo chidawaphimba chimene chidawaphimba.
وَأَضَلَّ فِرْعَوْنُ قَوْمَهُۥ وَمَا هَدَىٰ ﴿79﴾
Ndipo Farawo adawasokeretsa anthu ake, ndipo sadawaongolere.
يَٰبَنِىٓ إِسْرَٰٓءِيلَ قَدْ أَنجَيْنَٰكُم مِّنْ عَدُوِّكُمْ وَوَٰعَدْنَٰكُمْ جَانِبَ ٱلطُّورِ ٱلْأَيْمَنَ وَنَزَّلْنَا عَلَيْكُمُ ٱلْمَنَّ وَٱلسَّلْوَىٰ ﴿80﴾
E inu ana a Israyeli! Ndithu tidakupulumutsani kwa mdani wanu, ndipo tidakulonjezani (kuti mudze) mbali yakudzanjadzanja ya phiri (kuti tikupatseni malamulo ndi zina), ndipo tidakutsitsirani Manna ndi Saluwa.
كُلُوا۟ مِن طَيِّبَٰتِ مَا رَزَقْنَٰكُمْ وَلَا تَطْغَوْا۟ فِيهِ فَيَحِلَّ عَلَيْكُمْ غَضَبِى ۖ وَمَن يَحْلِلْ عَلَيْهِ غَضَبِى فَقَدْ هَوَىٰ ﴿81﴾
Idyani zinthu zabwino zomwe takupatsani, ndipo musapyole malire pa zimenezo kuti mkwiyo Wanga usakutsikireni; ndipo amene mkwiyo Wanga wamtsikira, ndiye kuti ameneyo waonongeka.
وَإِنِّى لَغَفَّارٌۭ لِّمَن تَابَ وَءَامَنَ وَعَمِلَ صَٰلِحًۭا ثُمَّ ٱهْتَدَىٰ ﴿82﴾
Ndipo ndithu Ine ndi Wokhululuka kwambiri kwa amene walapa ndi kukhulupirira, ndikuchita ntchito zabwino, kenako ndikutsata chiongoko mwaubwino.
۞ وَمَآ أَعْجَلَكَ عَن قَوْمِكَ يَٰمُوسَىٰ ﴿83﴾
“Nchiyani chakufulumizitsa (kudza kuno) kusiya anthu ako, E, iwe Mûsa?”[283]
قَالَ هُمْ أُو۟لَآءِ عَلَىٰٓ أَثَرِى وَعَجِلْتُ إِلَيْكَ رَبِّ لِتَرْضَىٰ ﴿84﴾
Adati: “Iwo ali pambuyo panga akunditsata. Ndachita changu kudza kwa Inu, Mbuye wanga, kuti mundiyanje kwambiri.”
قَالَ فَإِنَّا قَدْ فَتَنَّا قَوْمَكَ مِنۢ بَعْدِكَ وَأَضَلَّهُمُ ٱلسَّامِرِىُّ ﴿85﴾
(Allah) adati: “Ndithu Ife tawayesa Mmayeso anthu ako pambuyo pako; tero Samiriyyu wawasokeretsa.”[284]
فَرَجَعَ مُوسَىٰٓ إِلَىٰ قَوْمِهِۦ غَضْبَٰنَ أَسِفًۭا ۚ قَالَ يَٰقَوْمِ أَلَمْ يَعِدْكُمْ رَبُّكُمْ وَعْدًا حَسَنًا ۚ أَفَطَالَ عَلَيْكُمُ ٱلْعَهْدُ أَمْ أَرَدتُّمْ أَن يَحِلَّ عَلَيْكُمْ غَضَبٌۭ مِّن رَّبِّكُمْ فَأَخْلَفْتُم مَّوْعِدِى ﴿86﴾
Mûsa adabwerera kwa anthu ake ali wokwiya ndi wodandaula. Adati: “E inu anthu anga! Kodi Mbuye wanu sadakulonjezeni lonjezo labwino? Kapena nyengo yalonjezolo idatalika kwa inu? Kapena mudafuna kuti mkwiyo ukutsikireni kuchokera kwa Mbuye wanu; tero mwaswa lonjezo langa”?
قَالُوا۟ مَآ أَخْلَفْنَا مَوْعِدَكَ بِمَلْكِنَا وَلَٰكِنَّا حُمِّلْنَآ أَوْزَارًۭا مِّن زِينَةِ ٱلْقَوْمِ فَقَذَفْنَٰهَا فَكَذَٰلِكَ أَلْقَى ٱلسَّامِرِىُّ ﴿87﴾
(Iwo) adati: “Sitidaswe lonjezo lako mwachifuniro chathu; koma tidasenzetsedwa mitolo ya zodzikometsera za anthu (ziwiya zagolide zomwe tidabwereka kwa akazi a chimisiri), ndipo tidaziponya (pa moto, ndipo zidasungunuka ndikupangidwa mwana wang’ombe.) Ndipo momwemonso Samiriyyu adaponya.”
فَأَخْرَجَ لَهُمْ عِجْلًۭا جَسَدًۭا لَّهُۥ خُوَارٌۭ فَقَالُوا۟ هَٰذَآ إِلَٰهُكُمْ وَإِلَٰهُ مُوسَىٰ فَنَسِىَ ﴿88﴾
Ndipo adawatulutsira (kuchokera m’golide wosungunukayo) mwana wang’ombe wokhala ndi thupi lokwanira, yemwe amatulutsa mawu (ngati kulira kwa ng’ombe), (iwo) adati: “Uyu ndi mulungu wanu ndiponso mulungu wa Mûsa, koma (Mûsa) wamuiwala, (choncho wapita kukamfuna ku phiri)!”
أَفَلَا يَرَوْنَ أَلَّا يَرْجِعُ إِلَيْهِمْ قَوْلًۭا وَلَا يَمْلِكُ لَهُمْ ضَرًّۭا وَلَا نَفْعًۭا ﴿89﴾
Kodi sadaone kuti (mwana wang’ombe) sabweza mawu kwa iwo, ndiponso sangathe kudzetsa matsautso kwa iwo ngakhale zothandiza.
وَلَقَدْ قَالَ لَهُمْ هَٰرُونُ مِن قَبْلُ يَٰقَوْمِ إِنَّمَا فُتِنتُم بِهِۦ ۖ وَإِنَّ رَبَّكُمُ ٱلرَّحْمَٰنُ فَٱتَّبِعُونِى وَأَطِيعُوٓا۟ أَمْرِى ﴿90﴾
Ndipo ndithu Harun adawauza kale (kuti): “E inu anthu anga! Ndithu inu mwasokonezeka ndi (chinthu) ichi. Ndithu Mbuye wanu ndi (Allah) Wachifundo chambiri; choncho nditsateni, ndipo mverani lamulo langa, (siyani kupembedza fano ili).”
قَالُوا۟ لَن نَّبْرَحَ عَلَيْهِ عَٰكِفِينَ حَتَّىٰ يَرْجِعَ إِلَيْنَا مُوسَىٰ ﴿91﴾
(Iwo) adati: “Sitisiya ngakhale pang’ono kumpembedza. Kufikira Mûsa abwelere kwa ife.”
قَالَ يَٰهَٰرُونُ مَا مَنَعَكَ إِذْ رَأَيْتَهُمْ ضَلُّوٓا۟ ﴿92﴾
(Pamene Mûsa adabwerera) adati: “E iwe Harun! Nchiyani chidakuletsa pamene udawaona atasokera,”
أَلَّا تَتَّبِعَنِ ۖ أَفَعَصَيْتَ أَمْرِى ﴿93﴾
Kuti usanditsate? Udanyozera lamulo langa?”
قَالَ يَبْنَؤُمَّ لَا تَأْخُذْ بِلِحْيَتِى وَلَا بِرَأْسِىٓ ۖ إِنِّى خَشِيتُ أَن تَقُولَ فَرَّقْتَ بَيْنَ بَنِىٓ إِسْرَٰٓءِيلَ وَلَمْ تَرْقُبْ قَوْلِى ﴿94﴾
(Harun) adati: E iwe mwana wa mayi anga! Usagwire ndevu zanga, ngakhale mutu wanga (poukoka chifukwa cha mkwiyo). Ndithu ine ndidaopa (kuchoka ndi ena, kusiya ena) kuti ungati: “Wawagawa ana a Israyeli, ndipo sudayembekezere mawu anga.”
قَالَ فَمَا خَطْبُكَ يَٰسَٰمِرِىُّ ﴿95﴾
(Mûsa) adati: “E iwe Samiriyyu! Nchiyani wachita?”
قَالَ بَصُرْتُ بِمَا لَمْ يَبْصُرُوا۟ بِهِۦ فَقَبَضْتُ قَبْضَةًۭ مِّنْ أَثَرِ ٱلرَّسُولِ فَنَبَذْتُهَا وَكَذَٰلِكَ سَوَّلَتْ لِى نَفْسِى ﴿96﴾
(Iye adati:) “Ndidaona zomwe sadazione (ena) ndipo ndidatapa pang’ono mapazi a Mtumiki (Gabriele) ndikuwaponya (mu fano la mwana wa ng’ombe). Ndipo zimenezi ndi zomwe zidakomera mtima wanga.”[285]
قَالَ فَٱذْهَبْ فَإِنَّ لَكَ فِى ٱلْحَيَوٰةِ أَن تَقُولَ لَا مِسَاسَ ۖ وَإِنَّ لَكَ مَوْعِدًۭا لَّن تُخْلَفَهُۥ ۖ وَٱنظُرْ إِلَىٰٓ إِلَٰهِكَ ٱلَّذِى ظَلْتَ عَلَيْهِ عَاكِفًۭا ۖ لَّنُحَرِّقَنَّهُۥ ثُمَّ لَنَنسِفَنَّهُۥ فِى ٱلْيَمِّ نَسْفًا ﴿97﴾
(Mûsa) adati: “ Choka, ndithu pa iwe (pali chilango) pa moyo (wako) choti uzingonena (kuti): “Musandikhudze musandikhudze.” (Ndipo palibe amene adzakuyandikira ndipo iwe sudzayandikira aliyense). Ndithu pa iwe pali lonjezo la (Allah) losaswedwa; ndipo muyang’ane mulungu wako, yemwe wakhala ukupitiriza kumpembedza. Timtentha, kenako chipala chakecho tichimwaza m’nyanja.
إِنَّمَآ إِلَٰهُكُمُ ٱللَّهُ ٱلَّذِى لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۚ وَسِعَ كُلَّ شَىْءٍ عِلْمًۭا ﴿98﴾
Ndithu wompembedza wanu, ndi Allah Yekha, Yemwe, palibe woti nkupembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ndipo wakwanira pa chilichonse kuchidziwa ndi nzeru (Zake zopanda malire).
كَذَٰلِكَ نَقُصُّ عَلَيْكَ مِنْ أَنۢبَآءِ مَا قَدْ سَبَقَ ۚ وَقَدْ ءَاتَيْنَٰكَ مِن لَّدُنَّا ذِكْرًۭا ﴿99﴾
Umo ndi momwe tikukusimbira nkhani za (zinthu) zomwe zidatsogola (za aneneri). Ndithu takupatsa uthenga waukulu kuchokera kwa Ife (omwe ndi Qur’an).
مَّنْ أَعْرَضَ عَنْهُ فَإِنَّهُۥ يَحْمِلُ يَوْمَ ٱلْقِيَٰمَةِ وِزْرًا ﴿100﴾
Amene aunyozere, ndithu iye tsiku la Qiyâma adzasenza mitolo (ya machimo).
خَٰلِدِينَ فِيهِ ۖ وَسَآءَ لَهُمْ يَوْمَ ٱلْقِيَٰمَةِ حِمْلًۭا ﴿101﴾
Adzakhala m’menemo m’chilango. Ndipo ndi zoipa zedi (kwa anthu) kusenza mitolo (imeneyo) tsiku la Qiyâma,
يَوْمَ يُنفَخُ فِى ٱلصُّورِ ۚ وَنَحْشُرُ ٱلْمُجْرِمِينَ يَوْمَئِذٍۢ زُرْقًۭا ﴿102﴾
(Kumbuka Mtumiki Muhammad {s.a.w}), tsiku lomwe lipenga lidzaimbidwa. Ndipo tidzasonkhanitsa oipa tsiku limenelo maso awo ali a buluu (blue, chifukwa cha mantha).
يَتَخَٰفَتُونَ بَيْنَهُمْ إِن لَّبِثْتُمْ إِلَّا عَشْرًۭا ﴿103﴾
Adzanong’onezana pakati pawo (ponena kuti): “Simudakhalitse pa dziko lapansi koma masiku khumi okha basi.”
نَّحْنُ أَعْلَمُ بِمَا يَقُولُونَ إِذْ يَقُولُ أَمْثَلُهُمْ طَرِيقَةً إِن لَّبِثْتُمْ إِلَّا يَوْمًۭا ﴿104﴾
Ife tikudziwa kwambiri zimene azidzanena pamene abwino awo pamayendedwe azidzanena: “Inu simudakhale koma tsiku limodzi basi (poyerekeza ndi kuchuluka kwa masiku a ku Moto).”
وَيَسْـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلْجِبَالِ فَقُلْ يَنسِفُهَا رَبِّى نَسْفًۭا ﴿105﴾
Ndipo akukufunsa zamapiri (kuti adzatani tsiku la Qiyâma); auze: “Mbuye wanga adzawagumulagumula ndikuwaululutsa (ngati fumbi).”
فَيَذَرُهَا قَاعًۭا صَفْصَفًۭا ﴿106﴾
“Ndipo adzaisiya (nthaka yonse) ngati bwalo losalazidwa myaa!”
لَّا تَرَىٰ فِيهَا عِوَجًۭا وَلَآ أَمْتًۭا ﴿107﴾
“Sudzaona kukhota m’menemo ngakhale chitunda (chikweza).”
يَوْمَئِذٍۢ يَتَّبِعُونَ ٱلدَّاعِىَ لَا عِوَجَ لَهُۥ ۖ وَخَشَعَتِ ٱلْأَصْوَاتُ لِلرَّحْمَٰنِ فَلَا تَسْمَعُ إِلَّا هَمْسًۭا ﴿108﴾
Tsiku limenelo adzamtsatira woitana; sadzatha kumpatuka, ndipo mawu (azolengedwa) adzatonthola (kuti chete) kwa (Allah) Wachifundo chambiri; ndipo sudzamva, koma kunong’ona basi (ndi mididi ya mapazi).
يَوْمَئِذٍۢ لَّا تَنفَعُ ٱلشَّفَٰعَةُ إِلَّا مَنْ أَذِنَ لَهُ ٱلرَّحْمَٰنُ وَرَضِىَ لَهُۥ قَوْلًۭا ﴿109﴾
Tsiku limenelo chiombolo (cha aliyense) sichidzathandiza, kupatula yemwe wapatsidwa chilolezo ndi (Allah) Wachifundo chambiri, ndi kumuyanja kuti alankhule.
يَعْلَمُ مَا بَيْنَ أَيْدِيهِمْ وَمَا خَلْفَهُمْ وَلَا يُحِيطُونَ بِهِۦ عِلْمًۭا ﴿110﴾
(Allah) akudziwa za patsogolo pawo ndi zapambuyo pawo. Ndipo iwo sangathe kumzindikira (Allah) mmene alili.
۞ وَعَنَتِ ٱلْوُجُوهُ لِلْحَىِّ ٱلْقَيُّومِ ۖ وَقَدْ خَابَ مَنْ حَمَلَ ظُلْمًۭا ﴿111﴾
Ndipo nkhope (tsiku limenelo) zidzalobodoka pamaso pa (Allah) Wamoyo wamuyaya, Wochita chilichonse. Ndithu adzataika kwathunthu yense wochita zosalungama.
وَمَن يَعْمَلْ مِنَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَهُوَ مُؤْمِنٌۭ فَلَا يَخَافُ ظُلْمًۭا وَلَا هَضْمًۭا ﴿112﴾
Ndipo amene achite zabwino uku ali wokhulupirira, sadzaopa kuchitiridwa zoipa kapena kumchepetsera (choyenera chake).
وَكَذَٰلِكَ أَنزَلْنَٰهُ قُرْءَانًا عَرَبِيًّۭا وَصَرَّفْنَا فِيهِ مِنَ ٱلْوَعِيدِ لَعَلَّهُمْ يَتَّقُونَ أَوْ يُحْدِثُ لَهُمْ ذِكْرًۭا ﴿113﴾
Ndipo momwemo taivumbulutsa (Qur’an) m’Chiarabu ndipo tafotokoza m’menemo mwatsatanetsatane za machenjezo (amtundu uliwonse), kuti aope (Allah), ndikuti nthawi iliyonse (Qur’aniyo), iwapatse chikumbutso chatsopano.
فَتَعَٰلَى ٱللَّهُ ٱلْمَلِكُ ٱلْحَقُّ ۗ وَلَا تَعْجَلْ بِٱلْقُرْءَانِ مِن قَبْلِ أَن يُقْضَىٰٓ إِلَيْكَ وَحْيُهُۥ ۖ وَقُل رَّبِّ زِدْنِى عِلْمًۭا ﴿114﴾
Chomwecho watukuka Allah, Mfumu ya choonadi, ndipo usaifulumizitse Qur’an (powerenga) chivumbulutso chake chisanamalizike kwa iwe, ndipo nena (popempha) kuti: “Mbuye wanga! Ndionjezereni nzeru (kuzindikira).”
وَلَقَدْ عَهِدْنَآ إِلَىٰٓ ءَادَمَ مِن قَبْلُ فَنَسِىَ وَلَمْ نَجِدْ لَهُۥ عَزْمًۭا ﴿115﴾
Ndipo tidamulangiza (Mneneri) Adam kale, koma adaiwala. Ndipo sitidapeze Mwa iye kulimba mtima (potsatira lamulo Lathu loti asadye zipatso za mtengo woletsedwa).
وَإِذْ قُلْنَا لِلْمَلَٰٓئِكَةِ ٱسْجُدُوا۟ لِءَادَمَ فَسَجَدُوٓا۟ إِلَّآ إِبْلِيسَ أَبَىٰ ﴿116﴾
Ndipo (kumbukirani) pamene tidauza angelo: “Muchitireni sajida (mugwadireni momulemekeza) Adam,” dipo adachita Sajida kupatula Iblis, adakana.
فَقُلْنَا يَٰٓـَٔادَمُ إِنَّ هَٰذَا عَدُوٌّۭ لَّكَ وَلِزَوْجِكَ فَلَا يُخْرِجَنَّكُمَا مِنَ ٱلْجَنَّةِ فَتَشْقَىٰٓ ﴿117﴾
Tsono tidati: “E iwe Adam! Ndithu uyu ndi mdani wako iwe ndi mkazi wako; choncho asakutulutseni m’Munda wamtendere, mungadzavutike.”
إِنَّ لَكَ أَلَّا تَجُوعَ فِيهَا وَلَا تَعْرَىٰ ﴿118﴾
“Ndithu iwe sumva njala m’menemo ndipo sukhala wamaliseche.”
وَأَنَّكَ لَا تَظْمَؤُا۟ فِيهَا وَلَا تَضْحَىٰ ﴿119﴾
“Ndipo iwe sumva ludzu m’menemo, ndiponso sumva kutentha (kwa dzuwa).”
فَوَسْوَسَ إِلَيْهِ ٱلشَّيْطَٰنُ قَالَ يَٰٓـَٔادَمُ هَلْ أَدُلُّكَ عَلَىٰ شَجَرَةِ ٱلْخُلْدِ وَمُلْكٍۢ لَّا يَبْلَىٰ ﴿120﴾
Koma satana (adamsokoneza) pomunong’oneza (zoipa) adati: “E iwe Adam! Kodi ndikusonyeze mtengo wamuyaya ndi (wopatsa) ufumu wosatha?”[286]
فَأَكَلَا مِنْهَا فَبَدَتْ لَهُمَا سَوْءَٰتُهُمَا وَطَفِقَا يَخْصِفَانِ عَلَيْهِمَا مِن وَرَقِ ٱلْجَنَّةِ ۚ وَعَصَىٰٓ ءَادَمُ رَبَّهُۥ فَغَوَىٰ ﴿121﴾
Ndipo (onse awiri) adaudya, ndipo umaliseche wawo awiriwo udaonekera poyera; ndipo adayamba kudziphatika masamba a m’mundamo; ndipo Adam adalakwira Mbuye wake, choncho adasokera.
ثُمَّ ٱجْتَبَٰهُ رَبُّهُۥ فَتَابَ عَلَيْهِ وَهَدَىٰ ﴿122﴾
Kenako Mbuye wake adamsankha pomulandira kulapa kwake ndikumuongola.
قَالَ ٱهْبِطَا مِنْهَا جَمِيعًۢا ۖ بَعْضُكُمْ لِبَعْضٍ عَدُوٌّۭ ۖ فَإِمَّا يَأْتِيَنَّكُم مِّنِّى هُدًۭى فَمَنِ ٱتَّبَعَ هُدَاىَ فَلَا يَضِلُّ وَلَا يَشْقَىٰ ﴿123﴾
(Allah) adati: “Chokani nonsenu m’menemo, uku pali chidani pakati pa wina ndi mnzake, (padzakhala chidani pakati pa ana anu); koma chikadzakudzerani chiongoko kuchokera kwa Ine, tero amene adzachitsate chiongoko changacho, sadzasokera ndiponso sadzavutika.”
وَمَنْ أَعْرَضَ عَن ذِكْرِى فَإِنَّ لَهُۥ مَعِيشَةًۭ ضَنكًۭا وَنَحْشُرُهُۥ يَوْمَ ٱلْقِيَٰمَةِ أَعْمَىٰ ﴿124﴾
Ndipo amene anyozere ulaliki wanga, ndithu moyo wamavuto udzakhala pa iye ndipo tidzamuukitsa m’manda tsiku la chimaliziro ali wakhungu.”
قَالَ رَبِّ لِمَ حَشَرْتَنِىٓ أَعْمَىٰ وَقَدْ كُنتُ بَصِيرًۭا ﴿125﴾
Adzanena: “Mbuye wanga! Chifukwa ninji mwandiukitsa ndili wakhungu, pomwe ndidali wopenya?”
قَالَ كَذَٰلِكَ أَتَتْكَ ءَايَٰتُنَا فَنَسِيتَهَا ۖ وَكَذَٰلِكَ ٱلْيَوْمَ تُنسَىٰ ﴿126﴾
(Allah) adzanena: “Zimenezo nchifukwa chakuti zidakudzera Ayah zathu koma udaziiwala (chifukwa chosalabadira), momwemo lero uiwalidwa, (salabadilidwa).”
وَكَذَٰلِكَ نَجْزِى مَنْ أَسْرَفَ وَلَمْ يُؤْمِنۢ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِۦ ۚ وَلَعَذَابُ ٱلْءَاخِرَةِ أَشَدُّ وَأَبْقَىٰٓ ﴿127﴾
Ndipo umo ndimomwe tidzamulipirire aliyense wopyola malire, wosakhulupirira Ayah za Mbuye wake. Ndipo chilango cha tsiku la chimaliziro nchaukali, ndiponso chamuyaya.
أَفَلَمْ يَهْدِ لَهُمْ كَمْ أَهْلَكْنَا قَبْلَهُم مِّنَ ٱلْقُرُونِ يَمْشُونَ فِى مَسَٰكِنِهِمْ ۗ إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَءَايَٰتٍۢ لِّأُو۟لِى ٱلنُّهَىٰ ﴿128﴾
Kodi sizidadziwikebe kwa iwo kuti ndi mibadwo ingati tidaiononga patsogolo pawo? Ndipo awa (osakhulupirira atsopano) akuyenda m’malo awo, (kodi saona zizindikiro zakuonongeka kwawo)? Ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa eni nzeru.
وَلَوْلَا كَلِمَةٌۭ سَبَقَتْ مِن رَّبِّكَ لَكَانَ لِزَامًۭا وَأَجَلٌۭ مُّسَمًّۭى ﴿129﴾
Ndipo pakadapanda liwu lomwe lidatsogola kuchokera kwa Mbuye wako (lochedwetsera chilango) ndi nthawi yomwe idaikidwa, ndithu (chilango) chikadawafika (tsopano lomwe lino.)
فَٱصْبِرْ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَسَبِّحْ بِحَمْدِ رَبِّكَ قَبْلَ طُلُوعِ ٱلشَّمْسِ وَقَبْلَ غُرُوبِهَا ۖ وَمِنْ ءَانَآئِ ٱلَّيْلِ فَسَبِّحْ وَأَطْرَافَ ٱلنَّهَارِ لَعَلَّكَ تَرْضَىٰ ﴿130﴾
Choncho pirira pa zomwe akunenazo, ndipo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda, dzuwa lisanatuluke (popemphera swala ya Fajr), ndiponso lisanalowe (popemphera swala ya Asr); ndiponso nthawi za usiku umulemekeze (popemphera swala ya Magrib ndi Isha), ndi pansonga za masana (pakatikati pa usana popemphera swala ya Dhuhr); kuti udzakhale wokondwa (ndi malipilo amene azakupatse tsiku la Qiyâma).
وَلَا تَمُدَّنَّ عَيْنَيْكَ إِلَىٰ مَا مَتَّعْنَا بِهِۦٓ أَزْوَٰجًۭا مِّنْهُمْ زَهْرَةَ ٱلْحَيَوٰةِ ٱلدُّنْيَا لِنَفْتِنَهُمْ فِيهِ ۚ وَرِزْقُ رَبِّكَ خَيْرٌۭ وَأَبْقَىٰ ﴿131﴾
Ndipo usazitong’olere maso ako (mozidololokera zinthu) zimene tawasangalatsa nazo ena mwa anthu pakati pawo; zimenezo nzokongoletsa za moyo wa pa dziko basi, kuti tiwayese mayeso pazimenezo; koma chopatsa cha Mbuye wako (chomwe nchololedwa ngakhale chikhale chochepa) nchabwino kwambiri ndiponso chokhalitsa.
وَأْمُرْ أَهْلَكَ بِٱلصَّلَوٰةِ وَٱصْطَبِرْ عَلَيْهَا ۖ لَا نَسْـَٔلُكَ رِزْقًۭا ۖ نَّحْنُ نَرْزُقُكَ ۗ وَٱلْعَٰقِبَةُ لِلتَّقْوَىٰ ﴿132﴾
Ndipo lamula banja lako kupemphera Swala ndi kuipirira iwe mwini Swalayo. Sitikukupempha rizq, (chakudya) koma Ife ndi amene tikukudyetsa ndipo malekezero abwino ali mukuopa (Allah).
وَقَالُوا۟ لَوْلَا يَأْتِينَا بِـَٔايَةٍۢ مِّن رَّبِّهِۦٓ ۚ أَوَلَمْ تَأْتِهِم بَيِّنَةُ مَا فِى ٱلصُّحُفِ ٱلْأُولَىٰ ﴿133﴾
Ndipo (osakhulupirira) adanena: “Chifukwa ninji sakutibweretsera chizizwa kuchokera kwa Mbuye wake?” Kodi sudawafike umboni woonekera wa zomwe zili m’mabuku akale? (Kodi sadakhutitsidwe ndi Qur’an chomwe ndi chizizwa chachikulu).”
وَلَوْ أَنَّآ أَهْلَكْنَٰهُم بِعَذَابٍۢ مِّن قَبْلِهِۦ لَقَالُوا۟ رَبَّنَا لَوْلَآ أَرْسَلْتَ إِلَيْنَا رَسُولًۭا فَنَتَّبِعَ ءَايَٰتِكَ مِن قَبْلِ أَن نَّذِلَّ وَنَخْزَىٰ ﴿134﴾
Ndipo ngati tikadawaononga ndi chilango, asanadze uyo (Mtumiki), akadanena: “Mbuye wathu! Bwanji osatitumizira mtumiki kuti titsate Ayah Zanu tisanayaluke ndi kunyozeka?”
قُلْ كُلٌّۭ مُّتَرَبِّصٌۭ فَتَرَبَّصُوا۟ ۖ فَسَتَعْلَمُونَ مَنْ أَصْحَٰبُ ٱلصِّرَٰطِ ٱلسَّوِىِّ وَمَنِ ٱهْتَدَىٰ ﴿135﴾
Nena: “Aliyense (wa ife) akuyembekezera (mphoto yake); choncho yembekezerani. Posachedwapa mudziwa kuti kodi ndani mwini njira yolingana, ndipo ndani amene waongoka.”