Settings
Surah The family of Imran [Aal-e-Imran] in Chewa
الٓمٓ ﴿1﴾
Alif-Lâm-Mîm.
ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ٱلْحَىُّ ٱلْقَيُّومُ ﴿2﴾
Allah (ndimmodzi), palibe winanso wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye Yekha, Wamoyo wamuyaya, Woimira ndi kuteteza chilichonse.[60]
نَزَّلَ عَلَيْكَ ٱلْكِتَٰبَ بِٱلْحَقِّ مُصَدِّقًۭا لِّمَا بَيْنَ يَدَيْهِ وَأَنزَلَ ٱلتَّوْرَىٰةَ وَٱلْإِنجِيلَ ﴿3﴾
Wakuvumbulutsira buku mwachoonadi, lomwe likutsimikizira zomwe zidalipo patsogolo pake. Ndipo adavumbulutsa Taurat ndi Injil.
مِن قَبْلُ هُدًۭى لِّلنَّاسِ وَأَنزَلَ ٱلْفُرْقَانَ ۗ إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ لَهُمْ عَذَابٌۭ شَدِيدٌۭ ۗ وَٱللَّهُ عَزِيزٌۭ ذُو ٱنتِقَامٍ ﴿4﴾
Kale, kuti (mabukuwo) akhale chotsogolera anthu. Ndipo adavumbulutsa (Qur’an) yolekanitsa pakati pa choonadi ndi chonama.[61] Ndithudi, aja amene sadakhulupirire zizindikiro za Allah, adzakhala ndi chilango chaukali. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wobwezera (chilango mwaukali).
إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَخْفَىٰ عَلَيْهِ شَىْءٌۭ فِى ٱلْأَرْضِ وَلَا فِى ٱلسَّمَآءِ ﴿5﴾
Ndithudi, kwa Allah sikungabisike chilichonse cha pansi ngakhale cha kumwamba.
هُوَ ٱلَّذِى يُصَوِّرُكُمْ فِى ٱلْأَرْحَامِ كَيْفَ يَشَآءُ ۚ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ٱلْعَزِيزُ ٱلْحَكِيمُ ﴿6﴾
Iye ndi Yemwe amakulinganizani muli m’mimba mmaonekedwe anu mmene akufunira. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye; Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
هُوَ ٱلَّذِىٓ أَنزَلَ عَلَيْكَ ٱلْكِتَٰبَ مِنْهُ ءَايَٰتٌۭ مُّحْكَمَٰتٌ هُنَّ أُمُّ ٱلْكِتَٰبِ وَأُخَرُ مُتَشَٰبِهَٰتٌۭ ۖ فَأَمَّا ٱلَّذِينَ فِى قُلُوبِهِمْ زَيْغٌۭ فَيَتَّبِعُونَ مَا تَشَٰبَهَ مِنْهُ ٱبْتِغَآءَ ٱلْفِتْنَةِ وَٱبْتِغَآءَ تَأْوِيلِهِۦ ۗ وَمَا يَعْلَمُ تَأْوِيلَهُۥٓ إِلَّا ٱللَّهُ ۗ وَٱلرَّٰسِخُونَ فِى ٱلْعِلْمِ يَقُولُونَ ءَامَنَّا بِهِۦ كُلٌّۭ مِّنْ عِندِ رَبِّنَا ۗ وَمَا يَذَّكَّرُ إِلَّآ أُو۟لُوا۟ ٱلْأَلْبَٰبِ ﴿7﴾
Iye ndi Yemwe wakuvumbulutsira buku (ili la Qur’an), lomwe mkati mwake muli ndime zomveka zomwe ndimaziko a bukuli. Ndipo zilipo zina zokuluwika. Koma amene m’mitima mwawo muli kusokera, akutsata zomwe zili zokuluwika ndi cholinga chofuna kusokoneza anthu, ndi kufuna kudziwa tanthauzo lake lenileni. Palibe amene akudziwa tanthauzo lake lenileni koma Allah basi. Koma amene azama pa maphunziro, amanena: “Tawakhulupirira (ma Ayah amenewa). Onse ngochokera kwa Mbuye wathu.” Ndipo palibe angakumbukire koma eni nzeru basi.
رَبَّنَا لَا تُزِغْ قُلُوبَنَا بَعْدَ إِذْ هَدَيْتَنَا وَهَبْ لَنَا مِن لَّدُنكَ رَحْمَةً ۚ إِنَّكَ أَنتَ ٱلْوَهَّابُ ﴿8﴾
(Anzeruwo amanena): “ E Mbuye wathu! Musaikhotetse mitima yathu pambuyo potiongola. Tipatseni chifundo chochokera kwa Inu. Ndithudi, Inu Ndinu wopatsa kwambiri.
رَبَّنَآ إِنَّكَ جَامِعُ ٱلنَّاسِ لِيَوْمٍۢ لَّا رَيْبَ فِيهِ ۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُخْلِفُ ٱلْمِيعَادَ ﴿9﴾
E Mbuye wathu! Inu ndinu Wosonkhanitsa anthu patsiku lopanda chikaiko, ndithudi, Allah saswa lonjezo.
إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ لَن تُغْنِىَ عَنْهُمْ أَمْوَٰلُهُمْ وَلَآ أَوْلَٰدُهُم مِّنَ ٱللَّهِ شَيْـًۭٔا ۖ وَأُو۟لَٰٓئِكَ هُمْ وَقُودُ ٱلنَّارِ ﴿10﴾
Ndithu amene sadakhulupirire, chuma chawo sichidzawathandiza chilichonse ngakhalenso ana awo, ku chilango cha Allah. Ndipo iwo ndi nkhuni za ku Moto.
كَدَأْبِ ءَالِ فِرْعَوْنَ وَٱلَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۚ كَذَّبُوا۟ بِـَٔايَٰتِنَا فَأَخَذَهُمُ ٱللَّهُ بِذُنُوبِهِمْ ۗ وَٱللَّهُ شَدِيدُ ٱلْعِقَابِ ﴿11﴾
(Khalidwe la awa osakhulupiira, amumbadwo wako iwe mneneri Muhammad {s.a.w}, liri) ngati khalidwe la anthu a Farawo ndi amene adalipo pambuyo pawo. (Iwo) adatsutsa zisonyezo Zathu. Choncho, Allah adawakhaulitsa chifukwa cha machimo awo. Ndipo Allah Ngolanga mwaukali.
قُل لِّلَّذِينَ كَفَرُوا۟ سَتُغْلَبُونَ وَتُحْشَرُونَ إِلَىٰ جَهَنَّمَ ۚ وَبِئْسَ ٱلْمِهَادُ ﴿12﴾
Auze amene sadakhulupirire: “Posachedwapa mugonjetsedwa ndi kusonkhanitsidwa ndi kuponyedwa ku Moto. Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!”[62]
قَدْ كَانَ لَكُمْ ءَايَةٌۭ فِى فِئَتَيْنِ ٱلْتَقَتَا ۖ فِئَةٌۭ تُقَٰتِلُ فِى سَبِيلِ ٱللَّهِ وَأُخْرَىٰ كَافِرَةٌۭ يَرَوْنَهُم مِّثْلَيْهِمْ رَأْىَ ٱلْعَيْنِ ۚ وَٱللَّهُ يُؤَيِّدُ بِنَصْرِهِۦ مَن يَشَآءُ ۗ إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَعِبْرَةًۭ لِّأُو۟لِى ٱلْأَبْصَٰرِ ﴿13﴾
“Ndithudi, padapezeka chisonyezo chachikulu kwa inu m’magulu awiri omwe adakumana (tsiku la nkhondo ya Badri), pomwe gulu limodzi limamenya (nkhondo) pa njira ya Allah, pamene linalo lokanira, (ndipo gululo) linkawaona (Asilamu) kukhala ochuluka kawiri kuposa ilo, poona ndi maso awo. Ndipo Allah amamlimbikitsira mphamvu ndi chipulumutso chake amene wamfuna. Ndithudi, m’zimenezo muli malingaliro (akulu) kwa eni kupenyetsetsa mwanzeru.”
زُيِّنَ لِلنَّاسِ حُبُّ ٱلشَّهَوَٰتِ مِنَ ٱلنِّسَآءِ وَٱلْبَنِينَ وَٱلْقَنَٰطِيرِ ٱلْمُقَنطَرَةِ مِنَ ٱلذَّهَبِ وَٱلْفِضَّةِ وَٱلْخَيْلِ ٱلْمُسَوَّمَةِ وَٱلْأَنْعَٰمِ وَٱلْحَرْثِ ۗ ذَٰلِكَ مَتَٰعُ ٱلْحَيَوٰةِ ٱلدُّنْيَا ۖ وَٱللَّهُ عِندَهُۥ حُسْنُ ٱلْمَـَٔابِ ﴿14﴾
Kwakometsedwa kwa anthu kukonda zilakolako (za moyo wawo) monga akazi, ana, milumilu ya chuma cha golide ndi siliva, ndi mahachi oyang’aniridwa bwino, ziweto ndi mbewu. Izo ndi zosangalatsa za moyo wa dziko lapansi (zomwe sizili kanthu). Koma kwa Allah ndiko kuli mabwelero abwino.
۞ قُلْ أَؤُنَبِّئُكُم بِخَيْرٍۢ مِّن ذَٰلِكُمْ ۚ لِلَّذِينَ ٱتَّقَوْا۟ عِندَ رَبِّهِمْ جَنَّٰتٌۭ تَجْرِى مِن تَحْتِهَا ٱلْأَنْهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَا وَأَزْوَٰجٌۭ مُّطَهَّرَةٌۭ وَرِضْوَٰنٌۭ مِّنَ ٱللَّهِ ۗ وَٱللَّهُ بَصِيرٌۢ بِٱلْعِبَادِ ﴿15﴾
Nena: “Kodi ndikuuzeni zomwe zili zabwino kuposa zimenezo? Kwa omwe ali olungama, akapeza kwa Mbuye wawo Minda yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) mitsinje ikuyenda; adzakhala mmenemo nthawi yaitali ndikulandira akazi oyeretsedwa ndi chiyanjo chochokera kwa Allah. Ndipo Allah akuona akapolo ake onse.
ٱلَّذِينَ يَقُولُونَ رَبَّنَآ إِنَّنَآ ءَامَنَّا فَٱغْفِرْ لَنَا ذُنُوبَنَا وَقِنَا عَذَابَ ٱلنَّارِ ﴿16﴾
Omwe akunena: “Mbuye wathu! Ndithudi, ife takhulupirira. Choncho tikhululukireni machimo athu ndi kutipewetsa ku chilango cha Moto.”
ٱلصَّٰبِرِينَ وَٱلصَّٰدِقِينَ وَٱلْقَٰنِتِينَ وَٱلْمُنفِقِينَ وَٱلْمُسْتَغْفِرِينَ بِٱلْأَسْحَارِ ﴿17﴾
Opirira, onena zoona, omvera, opereka chaulere ndi opempha chikhululuko nthawi yam‘bandakucha.
شَهِدَ ٱللَّهُ أَنَّهُۥ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ وَٱلْمَلَٰٓئِكَةُ وَأُو۟لُوا۟ ٱلْعِلْمِ قَآئِمًۢا بِٱلْقِسْطِ ۚ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ٱلْعَزِيزُ ٱلْحَكِيمُ ﴿18﴾
Allah (Mwini) akuikira umboni kuti: “Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye basi.” Ndipo akuikiranso umboni (zomwezi) angelo ndi eni nzeru (kuti Iye) Ngokhazikitsa chilungamo. Palibe wina wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye. Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
إِنَّ ٱلدِّينَ عِندَ ٱللَّهِ ٱلْإِسْلَٰمُ ۗ وَمَا ٱخْتَلَفَ ٱلَّذِينَ أُوتُوا۟ ٱلْكِتَٰبَ إِلَّا مِنۢ بَعْدِ مَا جَآءَهُمُ ٱلْعِلْمُ بَغْيًۢا بَيْنَهُمْ ۗ وَمَن يَكْفُرْ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ فَإِنَّ ٱللَّهَ سَرِيعُ ٱلْحِسَابِ ﴿19﴾
Ndithudi, chipembedzo (choona) kwa Allah ndi Chisilamu. Ndipo amene adapatsidwa buku (Ayuda ndi Akhrisitu) sadatsutsane koma pambuyo powabwerera kuzindikira. (Adatsutsana) chifukwa cha dumbo lomwe lidali pakati pawo. Ndipo amene akukana zisonyezo za Allah, (Allah akamulanga pa tsiku la chiweruziro). Ndithu Allah Ngwachangu powerengera.
فَإِنْ حَآجُّوكَ فَقُلْ أَسْلَمْتُ وَجْهِىَ لِلَّهِ وَمَنِ ٱتَّبَعَنِ ۗ وَقُل لِّلَّذِينَ أُوتُوا۟ ٱلْكِتَٰبَ وَٱلْأُمِّيِّۦنَ ءَأَسْلَمْتُمْ ۚ فَإِنْ أَسْلَمُوا۟ فَقَدِ ٱهْتَدَوا۟ ۖ وَّإِن تَوَلَّوْا۟ فَإِنَّمَا عَلَيْكَ ٱلْبَلَٰغُ ۗ وَٱللَّهُ بَصِيرٌۢ بِٱلْعِبَادِ ﴿20﴾
Ngati (osakhulupirira) atsutsana nawe, nena: “Ndayang’anitsa nkhope yanga kwa Allah (ndadzipereka kwa Iye) pamodzi ndi amene anditsata.” Ndipo nena kwa onse adapatsidwa buku (Ayuda Ndi Akhrisitu) ndi osadziwa kulemba ndi kuwerenga (Arabu): “Kodi mwagonjera (kwa Allah)?” Ngati agonjera ndiye kuti aongoka. Koma ngati atembenukira kumbali, udindo wako ndikufikitsa uthenga basi. Ndipo Allah akuona akapolo Ake onse.
إِنَّ ٱلَّذِينَ يَكْفُرُونَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَيَقْتُلُونَ ٱلنَّبِيِّۦنَ بِغَيْرِ حَقٍّۢ وَيَقْتُلُونَ ٱلَّذِينَ يَأْمُرُونَ بِٱلْقِسْطِ مِنَ ٱلنَّاسِ فَبَشِّرْهُم بِعَذَابٍ أَلِيمٍ ﴿21﴾
Ndithudi, amene akutsutsa zizindikiro za Allah ndi kupha aneneri popanda choonadi, ndikuphanso anthu omwe akulamula (kuchita) zolungama, auze nkhani ya chilango chopweteka.
أُو۟لَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ حَبِطَتْ أَعْمَٰلُهُمْ فِى ٱلدُّنْيَا وَٱلْءَاخِرَةِ وَمَا لَهُم مِّن نَّٰصِرِينَ ﴿22﴾
Iwowo ndi omwe zochita zawo zaonongeka pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro. Ndipo iwo sadzapeza athandizi.
أَلَمْ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ أُوتُوا۟ نَصِيبًۭا مِّنَ ٱلْكِتَٰبِ يُدْعَوْنَ إِلَىٰ كِتَٰبِ ٱللَّهِ لِيَحْكُمَ بَيْنَهُمْ ثُمَّ يَتَوَلَّىٰ فَرِيقٌۭ مِّنْهُمْ وَهُم مُّعْرِضُونَ ﴿23﴾
Kodi sukuwaona omwe apatsidwa gawo la buku (la Allah)? Akuitanidwa ku buku la Allah kuti liwaweruze pakati pawo; kenako gulu lina la iwo likutembenukira kumbali iwo ali onyoza.[63]
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ قَالُوا۟ لَن تَمَسَّنَا ٱلنَّارُ إِلَّآ أَيَّامًۭا مَّعْدُودَٰتٍۢ ۖ وَغَرَّهُمْ فِى دِينِهِم مَّا كَانُوا۟ يَفْتَرُونَ ﴿24﴾
Zimenezo (kusalabadira malamulo a Allah) nchifukwa chakuti amanena: “Sudzatikhudza Moto koma masiku ochepa basi.” Ndipo zawanyenga pa chipembedzo chawo zomwe adali kupeka (kuti adzakhululukidwa kapena kulangidwa masiku ochepa okha).
فَكَيْفَ إِذَا جَمَعْنَٰهُمْ لِيَوْمٍۢ لَّا رَيْبَ فِيهِ وَوُفِّيَتْ كُلُّ نَفْسٍۢ مَّا كَسَبَتْ وَهُمْ لَا يُظْلَمُونَ ﴿25﴾
Kodi zidzakhala zotani pamene tidzawasonkhanitsa tsiku lopanda chikaiko? Ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa mokwanira pa zomwe udachita. Ndipo iwo sadzaponderezedwa.
قُلِ ٱللَّهُمَّ مَٰلِكَ ٱلْمُلْكِ تُؤْتِى ٱلْمُلْكَ مَن تَشَآءُ وَتَنزِعُ ٱلْمُلْكَ مِمَّن تَشَآءُ وَتُعِزُّ مَن تَشَآءُ وَتُذِلُّ مَن تَشَآءُ ۖ بِيَدِكَ ٱلْخَيْرُ ۖ إِنَّكَ عَلَىٰ كُلِّ شَىْءٍۢ قَدِيرٌۭ ﴿26﴾
Nena “E Mbuye wanga! Mwini ufumu wonse. Mumapereka ufumu kwa yemwe mwamfuna. Ndipo mumachotsa ufumu kwa yemwe mwamfuna. Mumapereka ulemelero kwa yemwe mwamfuna, ndipo mumamsambula yemwenso mwamfuna. Ubwino wonse uli m’manja Mwanu. Ndithudi, Inu ndinu Wokhonza chilichonse.”
تُولِجُ ٱلَّيْلَ فِى ٱلنَّهَارِ وَتُولِجُ ٱلنَّهَارَ فِى ٱلَّيْلِ ۖ وَتُخْرِجُ ٱلْحَىَّ مِنَ ٱلْمَيِّتِ وَتُخْرِجُ ٱلْمَيِّتَ مِنَ ٱلْحَىِّ ۖ وَتَرْزُقُ مَن تَشَآءُ بِغَيْرِ حِسَابٍۢ ﴿27﴾
(Inu) mumalowetsa usiku mu usana (ndikukhala usana wautali monga m’nyengo yotentha). Ndipo mumalowetsa usana mu usiku (nkukhala usiku wautali monga m’nyengo yachisanu). Mumatulutsa cha moyo m’chakufa; ndipo mumatulutsa chakufa m’chamoyo. Ndipo mumapatsa rizq (chakudya) amene mwamfuna mopanda chiwerengero.”
لَّا يَتَّخِذِ ٱلْمُؤْمِنُونَ ٱلْكَٰفِرِينَ أَوْلِيَآءَ مِن دُونِ ٱلْمُؤْمِنِينَ ۖ وَمَن يَفْعَلْ ذَٰلِكَ فَلَيْسَ مِنَ ٱللَّهِ فِى شَىْءٍ إِلَّآ أَن تَتَّقُوا۟ مِنْهُمْ تُقَىٰةًۭ ۗ وَيُحَذِّرُكُمُ ٱللَّهُ نَفْسَهُۥ ۗ وَإِلَى ٱللَّهِ ٱلْمَصِيرُ ﴿28﴾
Asilamu asapale ubwenzi osakhulupirira kusiya Asilamu anzawo. Amene achite zimenezo, sadzakhala ndi chilichonse pachipembedzo cha Allah, kupatula (kupalana nawo ubwenzi mwachiphamaso) chifukwa cha kudzitchinjiriza kwa iwo. Ndipo Allah Iye Mwini akukuchenjezani (za chilango Chake). Ndipo kobwerera ndi kwa Allah (basi).
قُلْ إِن تُخْفُوا۟ مَا فِى صُدُورِكُمْ أَوْ تُبْدُوهُ يَعْلَمْهُ ٱللَّهُ ۗ وَيَعْلَمُ مَا فِى ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِى ٱلْأَرْضِ ۗ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَىْءٍۢ قَدِيرٌۭ ﴿29﴾
Nena: “Ngati mubisa zomwe zili m’zifuwa zanu, kapena kuzionetsa (poyera), Allah akuzidziwa. Iye akudziwa zonse zakumwamba ndi zapansi. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.”
يَوْمَ تَجِدُ كُلُّ نَفْسٍۢ مَّا عَمِلَتْ مِنْ خَيْرٍۢ مُّحْضَرًۭا وَمَا عَمِلَتْ مِن سُوٓءٍۢ تَوَدُّ لَوْ أَنَّ بَيْنَهَا وَبَيْنَهُۥٓ أَمَدًۢا بَعِيدًۭا ۗ وَيُحَذِّرُكُمُ ٱللَّهُ نَفْسَهُۥ ۗ وَٱللَّهُ رَءُوفٌۢ بِٱلْعِبَادِ ﴿30﴾
Tsiku lomwe mzimu uliwonse udzapeza zabwino zomwe udachita zitabweretsedwa, ndiponso zoipa zomwe udachita; udzalakalaka kuti pakadakhala ntunda wautali pakati pa machimo ake ndi iye. Ndipo Allah Mwini akukuchenjezani za chilango Chake. Ndipo Allah Ngoleza kwa akapolo Ake.[64]
قُلْ إِن كُنتُمْ تُحِبُّونَ ٱللَّهَ فَٱتَّبِعُونِى يُحْبِبْكُمُ ٱللَّهُ وَيَغْفِرْ لَكُمْ ذُنُوبَكُمْ ۗ وَٱللَّهُ غَفُورٌۭ رَّحِيمٌۭ ﴿31﴾
Nena: (Iwe Mtumiki) “Ngati inu mukumkonda Allah, tsatani ine; Allah akukondani ndikukukhululukirani machimo anu. Ndipo Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.”[65]
قُلْ أَطِيعُوا۟ ٱللَّهَ وَٱلرَّسُولَ ۖ فَإِن تَوَلَّوْا۟ فَإِنَّ ٱللَّهَ لَا يُحِبُّ ٱلْكَٰفِرِينَ ﴿32﴾
Nena: “Mvereni Allah ndi Mtumiki (wake).” Koma ngati akana, (Allah awakhaulitsa). Ndithudi, Allah sakonda anthu osakhulupirira.
۞ إِنَّ ٱللَّهَ ٱصْطَفَىٰٓ ءَادَمَ وَنُوحًۭا وَءَالَ إِبْرَٰهِيمَ وَءَالَ عِمْرَٰنَ عَلَى ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿33﴾
Ndithudi Allah adasankha Adam ndi Nuh ndi banja la Ibrahim ndi banja la Imran pa zolengedwa zonse.
ذُرِّيَّةًۢ بَعْضُهَا مِنۢ بَعْضٍۢ ۗ وَٱللَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٌ ﴿34﴾
Ana ena kuchokera mwa ena pakati pawo. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa.[66]
إِذْ قَالَتِ ٱمْرَأَتُ عِمْرَٰنَ رَبِّ إِنِّى نَذَرْتُ لَكَ مَا فِى بَطْنِى مُحَرَّرًۭا فَتَقَبَّلْ مِنِّىٓ ۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلسَّمِيعُ ٱلْعَلِيمُ ﴿35﴾
(Kumbukirani) pamene adanena mkazi wa Imran (mayi wa Mariya), m’mapemphero ake): “Mbuye wanga! Ndapereka kwa Inu chimene chili m’mimba mwanga monga “waqf” (wotumikira m’kachisi Wanu). Tero landirani ichi kwa ine. Ndithudi, Inu ndinu Akumva, Wodziwa.”[67]
فَلَمَّا وَضَعَتْهَا قَالَتْ رَبِّ إِنِّى وَضَعْتُهَآ أُنثَىٰ وَٱللَّهُ أَعْلَمُ بِمَا وَضَعَتْ وَلَيْسَ ٱلذَّكَرُ كَٱلْأُنثَىٰ ۖ وَإِنِّى سَمَّيْتُهَا مَرْيَمَ وَإِنِّىٓ أُعِيذُهَا بِكَ وَذُرِّيَّتَهَا مِنَ ٱلشَّيْطَٰنِ ٱلرَّجِيمِ ﴿36﴾
Choncho pamene adam’bala adati: “Mbuye wanga! Ndabala wamkazi!” Ndipo Allah akudziwa kwambiri chimene wabereka - “Ndipo wamwamuna (yemwe ndimayembekezera kubala) sali ngati wamkazi (amene ndamubala. Sangathe kutumikira moyenera mkachisi Wanu). Ndipo ine ndamutcha Mariya (wotumikira Allah). Ndipo ndikupempha Chitetezo Chanu pa iye ndi ana ake kwa satana wothamangitsidwayo.”
فَتَقَبَّلَهَا رَبُّهَا بِقَبُولٍ حَسَنٍۢ وَأَنۢبَتَهَا نَبَاتًا حَسَنًۭا وَكَفَّلَهَا زَكَرِيَّا ۖ كُلَّمَا دَخَلَ عَلَيْهَا زَكَرِيَّا ٱلْمِحْرَابَ وَجَدَ عِندَهَا رِزْقًۭا ۖ قَالَ يَٰمَرْيَمُ أَنَّىٰ لَكِ هَٰذَا ۖ قَالَتْ هُوَ مِنْ عِندِ ٱللَّهِ ۖ إِنَّ ٱللَّهَ يَرْزُقُ مَن يَشَآءُ بِغَيْرِ حِسَابٍ ﴿37﴾
Choncho Mbuye wake adamulandira, kulandira kwabwino; namkulitsa, kukulitsa kwabwino. Adampatsa Zakariya kuti amulere. Nthawi iliyonse Zakariya akamulowera mchipinda mwake (mwa Mariya) m’kachisimo, amampeza ali ndi chakudya. Amati: “Iwe Mariya! Ukuzipeza kuti izi?” (Iye) amati: “Izi zikuchokera kwa Allah. Ndipo Allah amampatsa yemwe wamfuna popanda chiyembekezo (mwini wakeyo).”[68]
هُنَالِكَ دَعَا زَكَرِيَّا رَبَّهُۥ ۖ قَالَ رَبِّ هَبْ لِى مِن لَّدُنكَ ذُرِّيَّةًۭ طَيِّبَةً ۖ إِنَّكَ سَمِيعُ ٱلدُّعَآءِ ﴿38﴾
Pompo Zakariya adapempha Mbuye wake nati: “Mbuye wanga! Ndipatseni kuchokera kwa Inu mwana wabwino. Ndithudi, Inu ndinu Akumva pempho!”[69]
فَنَادَتْهُ ٱلْمَلَٰٓئِكَةُ وَهُوَ قَآئِمٌۭ يُصَلِّى فِى ٱلْمِحْرَابِ أَنَّ ٱللَّهَ يُبَشِّرُكَ بِيَحْيَىٰ مُصَدِّقًۢا بِكَلِمَةٍۢ مِّنَ ٱللَّهِ وَسَيِّدًۭا وَحَصُورًۭا وَنَبِيًّۭا مِّنَ ٱلصَّٰلِحِينَ ﴿39﴾
Mwadzidzidzi, mngelo adamuitana uku iye ataimilira akupemphera mchipinda cha m’kachisi: “Allah akukuuza nkhani yabwino (yakuti ubereka mwana; dzina lake) Yahya yemwe adzakhala wotsimikizira (mneneri yemwe adzabadwa) ndi liwu lochokera kwa Allah, (yemwe ndi mneneri Isa (Yesu) amene adzakhalanso wolemekezeka ndi wolungama ndi mneneri wa mwa anthu abwino.”
قَالَ رَبِّ أَنَّىٰ يَكُونُ لِى غُلَٰمٌۭ وَقَدْ بَلَغَنِىَ ٱلْكِبَرُ وَٱمْرَأَتِى عَاقِرٌۭ ۖ قَالَ كَذَٰلِكَ ٱللَّهُ يَفْعَلُ مَا يَشَآءُ ﴿40﴾
(Zakariya) adati: “Mbuye wanga! Ndidzakhala bwanji ndi mwana pomwe ukalamba wandifikira, nayenso mkazi wanga ndichumba.” (Mngelo adati): “Ndimomwemo; Allah amachita chimene wafuna.”
قَالَ رَبِّ ٱجْعَل لِّىٓ ءَايَةًۭ ۖ قَالَ ءَايَتُكَ أَلَّا تُكَلِّمَ ٱلنَّاسَ ثَلَٰثَةَ أَيَّامٍ إِلَّا رَمْزًۭا ۗ وَٱذْكُر رَّبَّكَ كَثِيرًۭا وَسَبِّحْ بِٱلْعَشِىِّ وَٱلْإِبْكَٰرِ ﴿41﴾
(Iye) adati: “Mbuye wanga! Ndipatseni chizindikiro!” Adati: “Chizindikiro chako ndikuti sudzatha kuyankhula ndi anthu mpaka masiku atatu koma momangolozera (ndi chala) basi. Ndipo tamanda Mbuye wako, kutamanda kwambiri ndiponso umlemekeze (popemphera) madzulo ndi m’mawa.”
وَإِذْ قَالَتِ ٱلْمَلَٰٓئِكَةُ يَٰمَرْيَمُ إِنَّ ٱللَّهَ ٱصْطَفَىٰكِ وَطَهَّرَكِ وَٱصْطَفَىٰكِ عَلَىٰ نِسَآءِ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿42﴾
Ndipo (kumbukira) pamene angelo adati: “E Iwe Mariya! Ndithudi, Allah wakusankha, wakuyeretsa ndipo wakulemekeza, mwa akazi onse amitundu ya anthu.”[70]
يَٰمَرْيَمُ ٱقْنُتِى لِرَبِّكِ وَٱسْجُدِى وَٱرْكَعِى مَعَ ٱلرَّٰكِعِينَ ﴿43﴾
“E iwe Mariya, dzichepetse kwa Mbuye wako ndi kumlambira powerama pamodzi ndi owerama.”
ذَٰلِكَ مِنْ أَنۢبَآءِ ٱلْغَيْبِ نُوحِيهِ إِلَيْكَ ۚ وَمَا كُنتَ لَدَيْهِمْ إِذْ يُلْقُونَ أَقْلَٰمَهُمْ أَيُّهُمْ يَكْفُلُ مَرْيَمَ وَمَا كُنتَ لَدَيْهِمْ إِذْ يَخْتَصِمُونَ ﴿44﴾
Izi ndizina mwa nkhani zobisika zomwe tikukuvumbulutsira. Sudali nawo pamene amaponya zolembera zawo (m’madzi m’njira ya mayere) kuti aone ndani mwa iwo alere Mariya. Komanso sudali nawo pamene adali kutsutsana.
إِذْ قَالَتِ ٱلْمَلَٰٓئِكَةُ يَٰمَرْيَمُ إِنَّ ٱللَّهَ يُبَشِّرُكِ بِكَلِمَةٍۢ مِّنْهُ ٱسْمُهُ ٱلْمَسِيحُ عِيسَى ٱبْنُ مَرْيَمَ وَجِيهًۭا فِى ٱلدُّنْيَا وَٱلْءَاخِرَةِ وَمِنَ ٱلْمُقَرَّبِينَ ﴿45﴾
(Kumbukira) pamene angelo adati: “E iwe Mariya! Ndithu Allah akukuuza nkhani yabwino (kuti ubereka mwana popanda mwamuna koma kupyolera mu) liwu lochokera kwa Iye (Allah, lakuti: “Bereka,” ndipo nkubereka popanda kupezana ndi mwamuna). Dzina lake ndi Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, adzakhala wolemekezeka pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro; ndiponso ndi mmodzi wa oyandikitsidwa kwa Allah.
وَيُكَلِّمُ ٱلنَّاسَ فِى ٱلْمَهْدِ وَكَهْلًۭا وَمِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ ﴿46﴾
Iye adzayankhula ndi anthu ali mchikuta ndi kuukulu (wake). Ndipo adzakhala mmodzi wa anthu abwino.”
قَالَتْ رَبِّ أَنَّىٰ يَكُونُ لِى وَلَدٌۭ وَلَمْ يَمْسَسْنِى بَشَرٌۭ ۖ قَالَ كَذَٰلِكِ ٱللَّهُ يَخْلُقُ مَا يَشَآءُ ۚ إِذَا قَضَىٰٓ أَمْرًۭا فَإِنَّمَا يَقُولُ لَهُۥ كُن فَيَكُونُ ﴿47﴾
(Mariya) adati: “Mbuye wanga! Ndingakhale ndi mwana bwanji pomwe sadandikhudze munthu aliyense (wamwamuna)?” (Mngelo) adati: “Ndi momwemo. Allah amalenga chimene wafuna. Akafuna chinthu amanena kwa icho: ‘Chitika,’ ndipo chimachitikadi.”
وَيُعَلِّمُهُ ٱلْكِتَٰبَ وَٱلْحِكْمَةَ وَٱلتَّوْرَىٰةَ وَٱلْإِنجِيلَ ﴿48﴾
“Ndipo Allah adzamphunzitsa kulemba, nzeru, Taurat ndi Injili.”
وَرَسُولًا إِلَىٰ بَنِىٓ إِسْرَٰٓءِيلَ أَنِّى قَدْ جِئْتُكُم بِـَٔايَةٍۢ مِّن رَّبِّكُمْ ۖ أَنِّىٓ أَخْلُقُ لَكُم مِّنَ ٱلطِّينِ كَهَيْـَٔةِ ٱلطَّيْرِ فَأَنفُخُ فِيهِ فَيَكُونُ طَيْرًۢا بِإِذْنِ ٱللَّهِ ۖ وَأُبْرِئُ ٱلْأَكْمَهَ وَٱلْأَبْرَصَ وَأُحْىِ ٱلْمَوْتَىٰ بِإِذْنِ ٱللَّهِ ۖ وَأُنَبِّئُكُم بِمَا تَأْكُلُونَ وَمَا تَدَّخِرُونَ فِى بُيُوتِكُمْ ۚ إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَءَايَةًۭ لَّكُمْ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ ﴿49﴾
“Ndipo (adzamchita kukhala) mneneri kwa ana a Israyeli (adzakhala akuwauza kuti): “Ine ndakudzerani ndi zizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu kuti ndikuumbireni dongo ngati chithunzi chambalame, nkuuzira m’menemo nkukhaladi mbalame mwa chilolezo cha Allah. Ndipo ndichiritsa osapenya chibadwire, ndiwamaangamaanga (chinawa), ndi kuukitsa akufa mwa chilolezo cha Allah. Ndipo ndikuuzani zomwe mudye ndi zimene musunge m’nyumba zanu. Ndithudi, m’zimenezi muli zizindikiro kwa inu ngati mulidi okhulupirira.”[71]
وَمُصَدِّقًۭا لِّمَا بَيْنَ يَدَىَّ مِنَ ٱلتَّوْرَىٰةِ وَلِأُحِلَّ لَكُم بَعْضَ ٱلَّذِى حُرِّمَ عَلَيْكُمْ ۚ وَجِئْتُكُم بِـَٔايَةٍۢ مِّن رَّبِّكُمْ فَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ﴿50﴾
“Ndipo (ndikhala) wotsimikizira zomwe zidalipo patsogolo panga (rn’buku la) Taurat. Ndipo ndadza kuti ndikulolezeni zina mwa zomwe zidaletsedwa kwa inu. Ndipo ndakudzerani ndi zizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu (zotsimikizira uthenga wanga). Choncho, opani Allah ndi kundimvera (ine).”
إِنَّ ٱللَّهَ رَبِّى وَرَبُّكُمْ فَٱعْبُدُوهُ ۗ هَٰذَا صِرَٰطٌۭ مُّسْتَقِيمٌۭ ﴿51﴾
“Ndithu Allah ndiye Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu; choncho mupembedzeni. Iyi ndiyo njira yoongoka.”
۞ فَلَمَّآ أَحَسَّ عِيسَىٰ مِنْهُمُ ٱلْكُفْرَ قَالَ مَنْ أَنصَارِىٓ إِلَى ٱللَّهِ ۖ قَالَ ٱلْحَوَارِيُّونَ نَحْنُ أَنصَارُ ٱللَّهِ ءَامَنَّا بِٱللَّهِ وَٱشْهَدْ بِأَنَّا مُسْلِمُونَ ﴿52﴾
Koma pamene Isa (Yesu) adazindikira mwa iwo kusakhulupirira adati: “Ndani akhale athandizi anga kwa Allah (popitiriza kufalitsa Chipembedzo Chake)?” Ophunzira ake adati: “Ife ndife athandizi a Allah (pofalitsa Chipembedzo Chake). Takhulupirira Allah; ndipo ikira umboni kuti ife ndithu ndi odzipereka kwa Allah (Asilamu).”
رَبَّنَآ ءَامَنَّا بِمَآ أَنزَلْتَ وَٱتَّبَعْنَا ٱلرَّسُولَ فَٱكْتُبْنَا مَعَ ٱلشَّٰهِدِينَ ﴿53﴾
“Mbuye wathu! Tazikhulupirira zimene mwavumbulutsa, ndipo tamtsata Mtumikiyo. Choncho tilembeni pamodzi ndi oikira umboniwo.”
وَمَكَرُوا۟ وَمَكَرَ ٱللَّهُ ۖ وَٱللَّهُ خَيْرُ ٱلْمَٰكِرِينَ ﴿54﴾
Ndipo (Ayuda) adakonza chiwembu (chofuna kupha Isa (Yesu), koma Allah adachiwononga chiwembu chawocho. Allah Ngokhoza bwino zedi poononga ziwembu za anthu a chiwembu.
إِذْ قَالَ ٱللَّهُ يَٰعِيسَىٰٓ إِنِّى مُتَوَفِّيكَ وَرَافِعُكَ إِلَىَّ وَمُطَهِّرُكَ مِنَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ وَجَاعِلُ ٱلَّذِينَ ٱتَّبَعُوكَ فَوْقَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓا۟ إِلَىٰ يَوْمِ ٱلْقِيَٰمَةِ ۖ ثُمَّ إِلَىَّ مَرْجِعُكُمْ فَأَحْكُمُ بَيْنَكُمْ فِيمَا كُنتُمْ فِيهِ تَخْتَلِفُونَ ﴿55﴾
(Kumbukirani) pamene Allah adati: “Iwe Isa (Yesu)! Ine ndikukwaniritsira nyengo yako yokhala ndi moyo (Ayuda sachita kanthu kwa iwe). Ndipo ndikunyamulira kwa Ine ndiponso ndikuyeretsa kwa anthu osakhulupirira (omwe ndi adani ako). Ndipo amene akutsata (iwe) ndiwasankha kukhala apamwamba pa amene sadakhulupirire kufikira tsiku lachimaliziro. Kenako kobwerera kwanu nkwa Ine, ndipo ndidzaweruza pakati panu pa zomwe mudali kusiyana.
فَأَمَّا ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ فَأُعَذِّبُهُمْ عَذَابًۭا شَدِيدًۭا فِى ٱلدُّنْيَا وَٱلْءَاخِرَةِ وَمَا لَهُم مِّن نَّٰصِرِينَ ﴿56﴾
Tsono amene sadakhulupirire, ndiwakhaulitsa ndi chilango chaukali pa dziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro, ndipo sadzapeza athandizi.
وَأَمَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ وَعَمِلُوا۟ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَيُوَفِّيهِمْ أُجُورَهُمْ ۗ وَٱللَّهُ لَا يُحِبُّ ٱلظَّٰلِمِينَ ﴿57﴾
Koma amene akhulupirira nachita zabwino, (Allah) adzawalipira malipiro awo (mokwanira). Ndipo Allah sakonda anthu ochita zoipa.
ذَٰلِكَ نَتْلُوهُ عَلَيْكَ مِنَ ٱلْءَايَٰتِ وَٱلذِّكْرِ ٱلْحَكِيمِ ﴿58﴾
Izi tikukuwerengera iwezi ndi zivumbulutso ndi ulaliki waluntha.
إِنَّ مَثَلَ عِيسَىٰ عِندَ ٱللَّهِ كَمَثَلِ ءَادَمَ ۖ خَلَقَهُۥ مِن تُرَابٍۢ ثُمَّ قَالَ لَهُۥ كُن فَيَكُونُ ﴿59﴾
Ndithudi, fanizo la Isa (Yesu) kwa Allah lili ngati fanizo la Adam; adamulenga ndi dothi namuuza kuti: “Khala munthu.” Ndipo adakhaladi.[72]
ٱلْحَقُّ مِن رَّبِّكَ فَلَا تَكُن مِّنَ ٱلْمُمْتَرِينَ ﴿60﴾
(Ichi ndi) choona chochokera kwa Mbuye wako; choncho usakhale mwa okaikira.
فَمَنْ حَآجَّكَ فِيهِ مِنۢ بَعْدِ مَا جَآءَكَ مِنَ ٱلْعِلْمِ فَقُلْ تَعَالَوْا۟ نَدْعُ أَبْنَآءَنَا وَأَبْنَآءَكُمْ وَنِسَآءَنَا وَنِسَآءَكُمْ وَأَنفُسَنَا وَأَنفُسَكُمْ ثُمَّ نَبْتَهِلْ فَنَجْعَل لَّعْنَتَ ٱللَّهِ عَلَى ٱلْكَٰذِبِينَ ﴿61﴾
Tsopano amene akutsutsana nawe (iwe Mtumiki s.a.w) pa ichi pambuyo pokudzera kuzindikira, auze: “Bwerani tiitane ana athu ndi ana anu, akazi athu ndi akazi anu, ife ndi inu; kenako modzichepetsa tipemphe tembelero la Allah kuti likhale pa amene ali abodza (mwa ife).”
إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ ٱلْقَصَصُ ٱلْحَقُّ ۚ وَمَا مِنْ إِلَٰهٍ إِلَّا ٱللَّهُ ۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَهُوَ ٱلْعَزِيزُ ٱلْحَكِيمُ ﴿62﴾
Ndithu iyi ndinkhani yoona; ndipo palibe woyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Allah. Ndithudi, Iye Allah Ngwamphamvu Zoposa, Ngwanzeru Zakuya.
فَإِن تَوَلَّوْا۟ فَإِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمٌۢ بِٱلْمُفْسِدِينَ ﴿63﴾
Ngati atembenuka (monyoza, Allah awalanga); ndithudi Allah Ngodziwa za oononga.
قُلْ يَٰٓأَهْلَ ٱلْكِتَٰبِ تَعَالَوْا۟ إِلَىٰ كَلِمَةٍۢ سَوَآءٍۭ بَيْنَنَا وَبَيْنَكُمْ أَلَّا نَعْبُدَ إِلَّا ٱللَّهَ وَلَا نُشْرِكَ بِهِۦ شَيْـًۭٔا وَلَا يَتَّخِذَ بَعْضُنَا بَعْضًا أَرْبَابًۭا مِّن دُونِ ٱللَّهِ ۚ فَإِن تَوَلَّوْا۟ فَقُولُوا۟ ٱشْهَدُوا۟ بِأَنَّا مُسْلِمُونَ ﴿64﴾
Nena: “Inu eni buku (la Allah, Ayuda ndi Akhrisitu!) Idzani ku liwu lolingana pakati pathu ndi inu (lakuti) tisapembedze aliyense koma Allah (Mmodzi Yekha), ndiponso tisamphatikize ndi chilichonse ndipo ena mwa ife asawasandutse anzawo kukhala milungu m’malo mwa Allah.” Ngati atembenuka ndi kunyoza, nenani: “Ikirani umboni kuti ife ndife Asilamu (ogonjera malamulo a Allah).”
يَٰٓأَهْلَ ٱلْكِتَٰبِ لِمَ تُحَآجُّونَ فِىٓ إِبْرَٰهِيمَ وَمَآ أُنزِلَتِ ٱلتَّوْرَىٰةُ وَٱلْإِنجِيلُ إِلَّا مِنۢ بَعْدِهِۦٓ ۚ أَفَلَا تَعْقِلُونَ ﴿65﴾
E inu amene mwapatsidwa buku! Bwanji mukutsutsana za Ibrahim pomwe Taurat ndi Injili sizidavumbulutsidwe koma pambuyo pake. Kodi simuzindikira?
هَٰٓأَنتُمْ هَٰٓؤُلَآءِ حَٰجَجْتُمْ فِيمَا لَكُم بِهِۦ عِلْمٌۭ فَلِمَ تُحَآجُّونَ فِيمَا لَيْسَ لَكُم بِهِۦ عِلْمٌۭ ۚ وَٱللَّهُ يَعْلَمُ وَأَنتُمْ لَا تَعْلَمُونَ ﴿66﴾
Taonani! Inu mudatsutsana pa zomwe mudazidziwa, nanga bwanji mukutsutsana pa zomwe simuzidziwa? Allah ndi Yemwe akudziwa. Pomwe inu simudziwa.
مَا كَانَ إِبْرَٰهِيمُ يَهُودِيًّۭا وَلَا نَصْرَانِيًّۭا وَلَٰكِن كَانَ حَنِيفًۭا مُّسْلِمًۭا وَمَا كَانَ مِنَ ٱلْمُشْرِكِينَ ﴿67﴾
Ibrahim sadali Myuda ndipo sadali Mkhrisitu, koma adali wolungama Msilamu (wodzipereka); ndipo sadali mwa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina).
إِنَّ أَوْلَى ٱلنَّاسِ بِإِبْرَٰهِيمَ لَلَّذِينَ ٱتَّبَعُوهُ وَهَٰذَا ٱلنَّبِىُّ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ ۗ وَٱللَّهُ وَلِىُّ ٱلْمُؤْمِنِينَ ﴿68﴾
Ndithu anthu omwe ali oyenera kudzilumikiza ndi Ibrahim ndi amene adamutsata (m’nyengo yake) ndi Mtumiki uyu (Muhammad {s.a.w}) ndi amene amkhulupirira (Mtumikiyu). Ndipo Allah ndi Mtetezi wa okhulupirira.
وَدَّت طَّآئِفَةٌۭ مِّنْ أَهْلِ ٱلْكِتَٰبِ لَوْ يُضِلُّونَكُمْ وَمَا يُضِلُّونَ إِلَّآ أَنفُسَهُمْ وَمَا يَشْعُرُونَ ﴿69﴾
Gulu lina la anthu amene adapatsidwa buku likufuna kukusokeretsani; ndipo sasokeretsa aliyense koma iwo wokha, pomwe (iwo eni) sakuzindikira.
يَٰٓأَهْلَ ٱلْكِتَٰبِ لِمَ تَكْفُرُونَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَأَنتُمْ تَشْهَدُونَ ﴿70﴾
E inu amene mwapatsidwa buku! Bwanji mukuzikana zizindikiro za Allah (Qur’an) pomwe mukudziwa?
يَٰٓأَهْلَ ٱلْكِتَٰبِ لِمَ تَلْبِسُونَ ٱلْحَقَّ بِٱلْبَٰطِلِ وَتَكْتُمُونَ ٱلْحَقَّ وَأَنتُمْ تَعْلَمُونَ ﴿71﴾
E inu amene mwapatsidwa buku! Bwanji mukusakaniza choona ndi chabodza, ndipo mukubisa choona uku mukudziwa?
وَقَالَت طَّآئِفَةٌۭ مِّنْ أَهْلِ ٱلْكِتَٰبِ ءَامِنُوا۟ بِٱلَّذِىٓ أُنزِلَ عَلَى ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ وَجْهَ ٱلنَّهَارِ وَٱكْفُرُوٓا۟ ءَاخِرَهُۥ لَعَلَّهُمْ يَرْجِعُونَ ﴿72﴾
Ndipo gulu lina la amene adapatsidwa buku lidati (kwa anzawo): “Khulupirirani chomwe chavumbulutsidwa kwa Asilamu kumayambiliro kwa usana, ndipo chikaneni kumalekezero kwake (kwa usana) mwina angabwelere (kusiya Chisilamu).[73]
وَلَا تُؤْمِنُوٓا۟ إِلَّا لِمَن تَبِعَ دِينَكُمْ قُلْ إِنَّ ٱلْهُدَىٰ هُدَى ٱللَّهِ أَن يُؤْتَىٰٓ أَحَدٌۭ مِّثْلَ مَآ أُوتِيتُمْ أَوْ يُحَآجُّوكُمْ عِندَ رَبِّكُمْ ۗ قُلْ إِنَّ ٱلْفَضْلَ بِيَدِ ٱللَّهِ يُؤْتِيهِ مَن يَشَآءُ ۗ وَٱللَّهُ وَٰسِعٌ عَلِيمٌۭ ﴿73﴾
Ndipo musakhulupirire aliyense kupatula yekhayo yemwe watsata chipembedzo chanu. (Allah adauza Mtumiki {s.a.w}), nena: “Ndithudi, chiongoko chenicheni ndi chiongoko cha Allah basi.” (Amene adapatsidwa buku Adanena kwa anzawo: “Musakhulupirire) kuti angapatsidwe aliyense zofanana ndi zomwe mwapatsidwa inu (Ayuda ndi Akhrisitu), kapena kuti angakutsutseni kwa Mbuye wanu.” (Allah adati kwa mtumiki{s.a.w}), nena: “Ndithu zabwino zonse zili m’manja mwa Allah; amazipereka kwa yemwe wamfuna. Allah ndi Mataya, Ngodziwa.”
يَخْتَصُّ بِرَحْمَتِهِۦ مَن يَشَآءُ ۗ وَٱللَّهُ ذُو ٱلْفَضْلِ ٱلْعَظِيمِ ﴿74﴾
Amamsankhira chifundo Chake amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino wawukulu.
۞ وَمِنْ أَهْلِ ٱلْكِتَٰبِ مَنْ إِن تَأْمَنْهُ بِقِنطَارٍۢ يُؤَدِّهِۦٓ إِلَيْكَ وَمِنْهُم مَّنْ إِن تَأْمَنْهُ بِدِينَارٍۢ لَّا يُؤَدِّهِۦٓ إِلَيْكَ إِلَّا مَا دُمْتَ عَلَيْهِ قَآئِمًۭا ۗ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ قَالُوا۟ لَيْسَ عَلَيْنَا فِى ٱلْأُمِّيِّۦنَ سَبِيلٌۭ وَيَقُولُونَ عَلَى ٱللَّهِ ٱلْكَذِبَ وَهُمْ يَعْلَمُونَ ﴿75﴾
Ndipo mwa iwo muli anthu ena oti ukawasungitsa milumilu ya chuma, akubwezera. Ndipo mwa iwo muli ena oti ukawasungitsa “dinar” (ndalama imodzi) sangakubwezere pokhapokha upitirize kwa iye kuimilira (kulonjelera). Izi nchifukwa chakuti amanena: “Palibe njira pa ife (yotidzudzulira) chifukwa chozibera mbulizi.” Koma akumnamizira Allah uku iwo akudziwa.
بَلَىٰ مَنْ أَوْفَىٰ بِعَهْدِهِۦ وَٱتَّقَىٰ فَإِنَّ ٱللَّهَ يُحِبُّ ٱلْمُتَّقِينَ ﴿76﴾
Sichoncho (monga momwe akunenera)! Koma amene akukwaniritsa lonjezo lake napewa machimo (ndiyemwe ayenera kukhala wokondedwa kwa Allah). Ndithudi, Allah amakonda opewa machimo.
إِنَّ ٱلَّذِينَ يَشْتَرُونَ بِعَهْدِ ٱللَّهِ وَأَيْمَٰنِهِمْ ثَمَنًۭا قَلِيلًا أُو۟لَٰٓئِكَ لَا خَلَٰقَ لَهُمْ فِى ٱلْءَاخِرَةِ وَلَا يُكَلِّمُهُمُ ٱللَّهُ وَلَا يَنظُرُ إِلَيْهِمْ يَوْمَ ٱلْقِيَٰمَةِ وَلَا يُزَكِّيهِمْ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌۭ ﴿77﴾
Ndithu anthu amene akusinthanitsa chipangano cha Allah ndi malumbiliro awo, (ndi zinthu za) mtengo wochepa, iwo alibe gawo labwino pa tsiku lachimaliziro. Ndipo Allah sadzawayankhula (ndi mawu abwino); ndipo sadzawayang’ana (ndi diso la chifundo) pa tsiku lachimaliziro. Ndiponso sadzawayeretsa (kumachimo awo); ndipo iwo adzapeza chilango chopweteka.
وَإِنَّ مِنْهُمْ لَفَرِيقًۭا يَلْوُۥنَ أَلْسِنَتَهُم بِٱلْكِتَٰبِ لِتَحْسَبُوهُ مِنَ ٱلْكِتَٰبِ وَمَا هُوَ مِنَ ٱلْكِتَٰبِ وَيَقُولُونَ هُوَ مِنْ عِندِ ٱللَّهِ وَمَا هُوَ مِنْ عِندِ ٱللَّهِ وَيَقُولُونَ عَلَى ٱللَّهِ ٱلْكَذِبَ وَهُمْ يَعْلَمُونَ ﴿78﴾
Ndipo ndithu mwa iwo muli gulu lomwe likukhotetsa malirime awo (powerenga) buku kuti muwaganizire (mawu awowo) kuti ndi a m’buku la Allah); pomwe si a m’buku (la Allah). Ndipo akunena: “Izi zachokera kwa Allah.” Pomwe zimenezo sizinachokere kwa Allah; ndipo akumnamizira Allah uku akudziwa.
مَا كَانَ لِبَشَرٍ أَن يُؤْتِيَهُ ٱللَّهُ ٱلْكِتَٰبَ وَٱلْحُكْمَ وَٱلنُّبُوَّةَ ثُمَّ يَقُولَ لِلنَّاسِ كُونُوا۟ عِبَادًۭا لِّى مِن دُونِ ٱللَّهِ وَلَٰكِن كُونُوا۟ رَبَّٰنِيِّۦنَ بِمَا كُنتُمْ تُعَلِّمُونَ ٱلْكِتَٰبَ وَبِمَا كُنتُمْ تَدْرُسُونَ ﴿79﴾
Sikoyenera kwa munthu yemwe Allah wampatsa buku ndi chiweruzo ndi uneneri, kenako nanena kwa anthu: “Khalani opembedza ine, mmalo mwa Allah.” Koma (awauze): “Khalani opembedza Allah, anzeru, aluntha chifukwa choti mukuphunzitsa buku ndi chifukwanso cha zomwe mukaphunzira.”
وَلَا يَأْمُرَكُمْ أَن تَتَّخِذُوا۟ ٱلْمَلَٰٓئِكَةَ وَٱلنَّبِيِّۦنَ أَرْبَابًا ۗ أَيَأْمُرُكُم بِٱلْكُفْرِ بَعْدَ إِذْ أَنتُم مُّسْلِمُونَ ﴿80﴾
Ndipo sangakulamulireni kuwasandutsa angelo ndi aneneri kukhala milungu. Kodi angakulamulireni kusakhulupirira pambuyo poti muli Asilamu (ogonjera)?
وَإِذْ أَخَذَ ٱللَّهُ مِيثَٰقَ ٱلنَّبِيِّۦنَ لَمَآ ءَاتَيْتُكُم مِّن كِتَٰبٍۢ وَحِكْمَةٍۢ ثُمَّ جَآءَكُمْ رَسُولٌۭ مُّصَدِّقٌۭ لِّمَا مَعَكُمْ لَتُؤْمِنُنَّ بِهِۦ وَلَتَنصُرُنَّهُۥ ۚ قَالَ ءَأَقْرَرْتُمْ وَأَخَذْتُمْ عَلَىٰ ذَٰلِكُمْ إِصْرِى ۖ قَالُوٓا۟ أَقْرَرْنَا ۚ قَالَ فَٱشْهَدُوا۟ وَأَنَا۠ مَعَكُم مِّنَ ٱلشَّٰهِدِينَ ﴿81﴾
Ndipo (kumbukirani) pamene Allah adatenga lonjezo kwa aneneri, (n’kuwauza): “Ndikakupatsani buku ndi nzeru, nakudzerani Mtumiki wotsimikizira zomwe zili pamodzi ndi inu, mudzamkhulupirire ndi kumthangata.” (Allah) adatinso: “Kodi mwavomereza ndi kulandira pa zimenezi pangano langali?” (Iwo) adati: “Tavomereza.” (Iye) adati: “Tsono chitirani umboni, ine ndili pamodzi nanu mwa oikira umboni.”
فَمَن تَوَلَّىٰ بَعْدَ ذَٰلِكَ فَأُو۟لَٰٓئِكَ هُمُ ٱلْفَٰسِقُونَ ﴿82﴾
Ndipo amene adzatembenuke pambuyo pa lonjezoli, (Allah adzawalanga chifukwa chakuti) iwo ngopandukiradi chilamulo cha Allah.
أَفَغَيْرَ دِينِ ٱللَّهِ يَبْغُونَ وَلَهُۥٓ أَسْلَمَ مَن فِى ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلْأَرْضِ طَوْعًۭا وَكَرْهًۭا وَإِلَيْهِ يُرْجَعُونَ ﴿83﴾
Kodi akufuna chipembedzo chomwe si cha Allah pomwe chinthu chilichonse chili kumwamba ndi pansi chikugonjera Iye, mofuna kapena mosafuna? Ndipo onse adzabwezedwa kwa Iye.
قُلْ ءَامَنَّا بِٱللَّهِ وَمَآ أُنزِلَ عَلَيْنَا وَمَآ أُنزِلَ عَلَىٰٓ إِبْرَٰهِيمَ وَإِسْمَٰعِيلَ وَإِسْحَٰقَ وَيَعْقُوبَ وَٱلْأَسْبَاطِ وَمَآ أُوتِىَ مُوسَىٰ وَعِيسَىٰ وَٱلنَّبِيُّونَ مِن رَّبِّهِمْ لَا نُفَرِّقُ بَيْنَ أَحَدٍۢ مِّنْهُمْ وَنَحْنُ لَهُۥ مُسْلِمُونَ ﴿84﴾
Nena: “Takhulupirira Allah ndi zomwe zavumbulutsidwa pa ife, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kwa Ibrahim, ndi Ismail, Ishâq ndi Yaqub ndi zidzukulu (zake), ndi zimene adapatsidwa Mûsa ndi Isa (Yesu), ndi aneneri (ena) zochokera kwa Mbuye wawo. Sitisiyanitsa aliyense pakati pawo, ndipo ife kwa Iye ndi Asilamu (odzipereka kwathunthu).”
وَمَن يَبْتَغِ غَيْرَ ٱلْإِسْلَٰمِ دِينًۭا فَلَن يُقْبَلَ مِنْهُ وَهُوَ فِى ٱلْءَاخِرَةِ مِنَ ٱلْخَٰسِرِينَ ﴿85﴾
Ndipo amene angafune chipembedzo chosakhala Chisilamu, sichidzalandiridwa kwa iye. Ndipo iye tsiku lachimaliziro adzakhala mmodzi mwa (anthu) otaika.
كَيْفَ يَهْدِى ٱللَّهُ قَوْمًۭا كَفَرُوا۟ بَعْدَ إِيمَٰنِهِمْ وَشَهِدُوٓا۟ أَنَّ ٱلرَّسُولَ حَقٌّۭ وَجَآءَهُمُ ٱلْبَيِّنَٰتُ ۚ وَٱللَّهُ لَا يَهْدِى ٱلْقَوْمَ ٱلظَّٰلِمِينَ ﴿86﴾
Kodi Allah angawaongole bwanji anthu omwe atuluka m’chikhulupiliro pambuyo pakukhulupirira natsimikiza kuti Mtumiki (uyu Muhammad{s.a.w}) ngoona, nkuwafikiranso zisonyezo zoonekera? Koma Allah saongola anthu ochita zoipa.
أُو۟لَٰٓئِكَ جَزَآؤُهُمْ أَنَّ عَلَيْهِمْ لَعْنَةَ ٱللَّهِ وَٱلْمَلَٰٓئِكَةِ وَٱلنَّاسِ أَجْمَعِينَ ﴿87﴾
Ndithu mphoto yawo ndiyakuti pa iwo pali matembelero a Allah, a angelo ndi anthu onse.
خَٰلِدِينَ فِيهَا لَا يُخَفَّفُ عَنْهُمُ ٱلْعَذَابُ وَلَا هُمْ يُنظَرُونَ ﴿88﴾
M’menemo adzakhala nthawi yaitali; ndipo sichidzapeputsidwa chilango kwa iwo, ndiponso sadzapatsidwa danga.
إِلَّا ٱلَّذِينَ تَابُوا۟ مِنۢ بَعْدِ ذَٰلِكَ وَأَصْلَحُوا۟ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٌۭ رَّحِيمٌ ﴿89﴾
Kupatula anthu amene alapa, pambuyo pa zimenezo nachita zabwino. ndithudi, Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.
إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ بَعْدَ إِيمَٰنِهِمْ ثُمَّ ٱزْدَادُوا۟ كُفْرًۭا لَّن تُقْبَلَ تَوْبَتُهُمْ وَأُو۟لَٰٓئِكَ هُمُ ٱلضَّآلُّونَ ﴿90﴾
Ndithudi, amene atuluka m’chikhulupiliro pambuyo pokhulupirira, kenako naonjezera kusakhulupirira, kulapa kwawo sikudzavomerezedwa konse. Ndipo iwo ndiosekera.
إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ وَمَاتُوا۟ وَهُمْ كُفَّارٌۭ فَلَن يُقْبَلَ مِنْ أَحَدِهِم مِّلْءُ ٱلْأَرْضِ ذَهَبًۭا وَلَوِ ٱفْتَدَىٰ بِهِۦٓ ۗ أُو۟لَٰٓئِكَ لَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌۭ وَمَا لَهُم مِّن نَّٰصِرِينَ ﴿91﴾
Ndithudi amene sadakhulupirire, nkumwalira pamene ali osakhulupirira, sikudzalandiridwa kwa aliyense wa iwo ngakhale atapereka dipo la golide lodzadza dziko lonse. Iwo ndi omwe adzalandire chilango chopweteka, ndipo sadzakhala ndi athandizi.
لَن تَنَالُوا۟ ٱلْبِرَّ حَتَّىٰ تُنفِقُوا۟ مِمَّا تُحِبُّونَ ۚ وَمَا تُنفِقُوا۟ مِن شَىْءٍۢ فَإِنَّ ٱللَّهَ بِهِۦ عَلِيمٌۭ ﴿92﴾
۞ Simudzapeza ubwino (weniweni) kufikira mutapereka m’zimene mukuzikonda. Ndipo chilichonse chimene mupereka, ndithudi, Allah akuchidziwa.
۞ كُلُّ ٱلطَّعَامِ كَانَ حِلًّۭا لِّبَنِىٓ إِسْرَٰٓءِيلَ إِلَّا مَا حَرَّمَ إِسْرَٰٓءِيلُ عَلَىٰ نَفْسِهِۦ مِن قَبْلِ أَن تُنَزَّلَ ٱلتَّوْرَىٰةُ ۗ قُلْ فَأْتُوا۟ بِٱلتَّوْرَىٰةِ فَٱتْلُوهَآ إِن كُنتُمْ صَٰدِقِينَ ﴿93﴾
Zakudya zonse zidali zololedwa kwa ana a Israyeli kupatula chimene adadziretsa Israyeli mwini wake Taurat isadavumbulutsidwe. Nena: “Bwerani ndi Tauratiyo ndipo iwerengeni ngati mukunena zoona.”[74]
فَمَنِ ٱفْتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ ٱلْكَذِبَ مِنۢ بَعْدِ ذَٰلِكَ فَأُو۟لَٰٓئِكَ هُمُ ٱلظَّٰلِمُونَ ﴿94﴾
Choncho aliyense amene adzapekera bodza Allah pambuyo pa izi iwo ndiwochita zoipa.
قُلْ صَدَقَ ٱللَّهُ ۗ فَٱتَّبِعُوا۟ مِلَّةَ إِبْرَٰهِيمَ حَنِيفًۭا وَمَا كَانَ مِنَ ٱلْمُشْرِكِينَ ﴿95﴾
Nena: “Allah wanena zoona. Choncho tsatirani chipembedzo cha Ibrahim yemwe adali wolungama; sadali mwa ophatikiza Allah ndi mafano.”
إِنَّ أَوَّلَ بَيْتٍۢ وُضِعَ لِلنَّاسِ لَلَّذِى بِبَكَّةَ مُبَارَكًۭا وَهُدًۭى لِّلْعَٰلَمِينَ ﴿96﴾
Ndithudi, nyumba yoyamba yomwe idakhazikitsidwa chifukwa cha anthu (kuti azipempheramo) ndiyomwe ili pa Bakka (ku Makka); yodalitsidwa ndiponso ndichiongolo kwa anthu onse.[75]
فِيهِ ءَايَٰتٌۢ بَيِّنَٰتٌۭ مَّقَامُ إِبْرَٰهِيمَ ۖ وَمَن دَخَلَهُۥ كَانَ ءَامِنًۭا ۗ وَلِلَّهِ عَلَى ٱلنَّاسِ حِجُّ ٱلْبَيْتِ مَنِ ٱسْتَطَاعَ إِلَيْهِ سَبِيلًۭا ۚ وَمَن كَفَرَ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَنِىٌّ عَنِ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿97﴾
M’menemo muli zizindikiro zoonekera (zozindikiritsa kupatulika kwake ndi ukale wake); ndi pamalo pomwe Ibrahim adali kuimilira; ndipo amene akulowamo amakhala m’chitetezo; ndipo Allah walamula anthu kuti akachite Hajj ku nyumbayo amene angathe kukonzekera ulendo wonka kumeneko. Ndipo yemwe angakane, (osapitako pomwe ali nazo zomuyenereza), ndithudi, Allah Ngwachikwanekwane pa zolengedwa Zake.
قُلْ يَٰٓأَهْلَ ٱلْكِتَٰبِ لِمَ تَكْفُرُونَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَٱللَّهُ شَهِيدٌ عَلَىٰ مَا تَعْمَلُونَ ﴿98﴾
Nena: “E inu amene mudapatsidwa buku! chifukwa chiyani mukuzikana zizindikiro za Allah pomwe Allah ndi Mboni wa zonse zimene mukuchita?”
قُلْ يَٰٓأَهْلَ ٱلْكِتَٰبِ لِمَ تَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ مَنْ ءَامَنَ تَبْغُونَهَا عِوَجًۭا وَأَنتُمْ شُهَدَآءُ ۗ وَمَا ٱللَّهُ بِغَٰفِلٍ عَمَّا تَعْمَلُونَ ﴿99﴾
Nena: “ E inu amene mudapatsidwa buku! Chifukwa chani mukutsekereza anthu amene akhulupirira kuyenda pa njira ya Allah? Mukufuna kuti ikhote pomwe inu ndinu mboni (kuti ndi njira ya Allah yopanda choipa)? Komatu Allah sanyalanyaza zomwe mukuchita.”
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓا۟ إِن تُطِيعُوا۟ فَرِيقًۭا مِّنَ ٱلَّذِينَ أُوتُوا۟ ٱلْكِتَٰبَ يَرُدُّوكُم بَعْدَ إِيمَٰنِكُمْ كَٰفِرِينَ ﴿100﴾
E inu amene mwakhulupirira! Ngati muwamvera ena mwa amene apatsidwa buku, akubwezani kuti mukhale osakhulupirira pambuyo pa chikhulupiliro chanu.
وَكَيْفَ تَكْفُرُونَ وَأَنتُمْ تُتْلَىٰ عَلَيْكُمْ ءَايَٰتُ ٱللَّهِ وَفِيكُمْ رَسُولُهُۥ ۗ وَمَن يَعْتَصِم بِٱللَّهِ فَقَدْ هُدِىَ إِلَىٰ صِرَٰطٍۢ مُّسْتَقِيمٍۢ ﴿101﴾
Kodi mukukanira bwanji pomwe ndime za Allah zikuwerengedwa kwa inu, pomwenso Mtumiki Wake ali pamodzi nanu? Ndipo amene agwiritse mwa Allah (bwinobwino), ndithudi iye wawongoleredwa kunjira yoongoka.
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ ٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ حَقَّ تُقَاتِهِۦ وَلَا تَمُوتُنَّ إِلَّا وَأَنتُم مُّسْلِمُونَ ﴿102﴾
E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah; kuopa kwenikweni. Ndipo musafe pokhapokha mutakhala Asilamu (ogonjera).[76]
وَٱعْتَصِمُوا۟ بِحَبْلِ ٱللَّهِ جَمِيعًۭا وَلَا تَفَرَّقُوا۟ ۚ وَٱذْكُرُوا۟ نِعْمَتَ ٱللَّهِ عَلَيْكُمْ إِذْ كُنتُمْ أَعْدَآءًۭ فَأَلَّفَ بَيْنَ قُلُوبِكُمْ فَأَصْبَحْتُم بِنِعْمَتِهِۦٓ إِخْوَٰنًۭا وَكُنتُمْ عَلَىٰ شَفَا حُفْرَةٍۢ مِّنَ ٱلنَّارِ فَأَنقَذَكُم مِّنْهَا ۗ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ ٱللَّهُ لَكُمْ ءَايَٰتِهِۦ لَعَلَّكُمْ تَهْتَدُونَ ﴿103﴾
Ndipo gwiritsani chingwe (chipembedzo) cha Allah nonsenu, ndipo musagawikane. Kumbukirani mtendere wa Allah womwe uli pa inu; pamene mudali odana ndipo Iye adalunzanitsa pakati pa mitima yanu, tero mwa mtendere Wake mudakhala abale; ndipo mudali m’mphepete mwa dzenje la moto (wa Jahanama), ndipo Iye adakupulumutsanimo. Umo ndi momwe Allah akukufotokozerani ma Ayah Ake (ndime Zake) kuti muongoke.[77]
وَلْتَكُن مِّنكُمْ أُمَّةٌۭ يَدْعُونَ إِلَى ٱلْخَيْرِ وَيَأْمُرُونَ بِٱلْمَعْرُوفِ وَيَنْهَوْنَ عَنِ ٱلْمُنكَرِ ۚ وَأُو۟لَٰٓئِكَ هُمُ ٱلْمُفْلِحُونَ ﴿104﴾
Ndipo mwa inu lipezeke gulu la anthu oitanira ku zabwino (Chisilamu) ndipo alamule (kuchita) zabwino ndikuletsa zoipa. Iwo ndiwo opambana.
وَلَا تَكُونُوا۟ كَٱلَّذِينَ تَفَرَّقُوا۟ وَٱخْتَلَفُوا۟ مِنۢ بَعْدِ مَا جَآءَهُمُ ٱلْبَيِّنَٰتُ ۚ وَأُو۟لَٰٓئِكَ لَهُمْ عَذَابٌ عَظِيمٌۭ ﴿105﴾
Ndipo musakhale monga aja amene adagawikana nasiyana pambuyo powadzera zisonyezo zoonekera poyera (zowaletsa kutero). Ndipo iwo adzakhala ndichilango chachikulu.
يَوْمَ تَبْيَضُّ وُجُوهٌۭ وَتَسْوَدُّ وُجُوهٌۭ ۚ فَأَمَّا ٱلَّذِينَ ٱسْوَدَّتْ وُجُوهُهُمْ أَكَفَرْتُم بَعْدَ إِيمَٰنِكُمْ فَذُوقُوا۟ ٱلْعَذَابَ بِمَا كُنتُمْ تَكْفُرُونَ ﴿106﴾
Patsikulo nkhope zina zidzakhala zowala pomwe nkhope zina zidzakhala zakuda. Tsono amene nkhope zawo zidzakhala zakuda, (adzauzidwa): “Kodi mudakana ( Allah) pambuyo pa chikhulupiliro chanu? Choncho, lawani chilango (chopweteka) chifukwa cha zomwe mudali kuzikana.”
وَأَمَّا ٱلَّذِينَ ٱبْيَضَّتْ وُجُوهُهُمْ فَفِى رَحْمَةِ ٱللَّهِ هُمْ فِيهَا خَٰلِدُونَ ﴿107﴾
Tsono (anthu odala) omwe nkhope zawo zidzawale, adzakhala m’chifundo cha Allah. Iwo mmenemo adzakhala nthawi yaitali.
تِلْكَ ءَايَٰتُ ٱللَّهِ نَتْلُوهَا عَلَيْكَ بِٱلْحَقِّ ۗ وَمَا ٱللَّهُ يُرِيدُ ظُلْمًۭا لِّلْعَٰلَمِينَ ﴿108﴾
Awo ndi ma Ayah (ndime) a Allah; tikukuwerengera mwa choonadi. Ndipo Allah safuna kupondereza zolengedwa (Zake).
وَلِلَّهِ مَا فِى ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِى ٱلْأَرْضِ ۚ وَإِلَى ٱللَّهِ تُرْجَعُ ٱلْأُمُورُ ﴿109﴾
Chilichonse cha kumwamba ndipansi ncha Allah. ndipo zinthu zonse zidzabwezedwa kwa Allah.
كُنتُمْ خَيْرَ أُمَّةٍ أُخْرِجَتْ لِلنَّاسِ تَأْمُرُونَ بِٱلْمَعْرُوفِ وَتَنْهَوْنَ عَنِ ٱلْمُنكَرِ وَتُؤْمِنُونَ بِٱللَّهِ ۗ وَلَوْ ءَامَنَ أَهْلُ ٱلْكِتَٰبِ لَكَانَ خَيْرًۭا لَّهُم ۚ مِّنْهُمُ ٱلْمُؤْمِنُونَ وَأَكْثَرُهُمُ ٱلْفَٰسِقُونَ ﴿110﴾
Inu (Asilamu) ndinu gulu labwino limene lasankhidwa kwa anthu. Mukulamula (kuchita) zabwino ndi kuletsa zoipa, ndipo mukukhulupirira mwa Allah. Ndipo aja adapatsidwa buku akadakhulupirira monga momwe (adawalamulira) kukadakhala kwabwino kwa iwo. (Koma) mwa iwo alipo okhulupirira pomwe ambiri mwa iwo ngopandukira (chilamulo cha Allah).[78]
لَن يَضُرُّوكُمْ إِلَّآ أَذًۭى ۖ وَإِن يُقَٰتِلُوكُمْ يُوَلُّوكُمُ ٱلْأَدْبَارَ ثُمَّ لَا يُنصَرُونَ ﴿111﴾
Sangakuvutitseni (adani anuwo, makamaka Ayuda) koma ndi timasautso (tochepa); ngati (atayesera) kukuthirani nkhondo, akufulatirani (kuthawa); ndipo kenako sangapulumutsidwe.
ضُرِبَتْ عَلَيْهِمُ ٱلذِّلَّةُ أَيْنَ مَا ثُقِفُوٓا۟ إِلَّا بِحَبْلٍۢ مِّنَ ٱللَّهِ وَحَبْلٍۢ مِّنَ ٱلنَّاسِ وَبَآءُو بِغَضَبٍۢ مِّنَ ٱللَّهِ وَضُرِبَتْ عَلَيْهِمُ ٱلْمَسْكَنَةُ ۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ كَانُوا۟ يَكْفُرُونَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَيَقْتُلُونَ ٱلْأَنۢبِيَآءَ بِغَيْرِ حَقٍّۢ ۚ ذَٰلِكَ بِمَا عَصَوا۟ وَّكَانُوا۟ يَعْتَدُونَ ﴿112﴾
Adindidwa chidindo chakunyozeka paliponse pamene angapezeke kupatula (akagwira) chingwe (cha chipembedzo) cha Allah, kapena chingwe cha anthu (pothandizidwa ndi anthu ena. Koma paokha sangakhale ndi nyonga). Abwerera ndi mkwiyo wa Allah; ndipo chidindo chaumphawi chadindidwa pa iwo. Izi nchifukwa chakuti iwo sadali kukhulupirira mawu a Allah, ndipo amapha aneneri popanda choonadi. Izi nchifukwa chakutinso adanyoza ndi kulumpha malire.
۞ لَيْسُوا۟ سَوَآءًۭ ۗ مِّنْ أَهْلِ ٱلْكِتَٰبِ أُمَّةٌۭ قَآئِمَةٌۭ يَتْلُونَ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ ءَانَآءَ ٱلَّيْلِ وَهُمْ يَسْجُدُونَ ﴿113﴾
Iwo amene adapatsidwa buku sali ofanana. Mwa iwo muli anthu olungama omwe akuwerenga ma Ayah (ndime) a Allah nthawi za usiku uku akumulambira.
يُؤْمِنُونَ بِٱللَّهِ وَٱلْيَوْمِ ٱلْءَاخِرِ وَيَأْمُرُونَ بِٱلْمَعْرُوفِ وَيَنْهَوْنَ عَنِ ٱلْمُنكَرِ وَيُسَٰرِعُونَ فِى ٱلْخَيْرَٰتِ وَأُو۟لَٰٓئِكَ مِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ ﴿114﴾
Amakhulupirira Allah ndi lsiku lomaliza; ndipo amalamulira (kuchita) zabwino ndikuletsa zoipa; ndipo amachita changu pa zinthu zabwino. Ndipo iwo ndi omwe ali mwa anthu abwino.
وَمَا يَفْعَلُوا۟ مِنْ خَيْرٍۢ فَلَن يُكْفَرُوهُ ۗ وَٱللَّهُ عَلِيمٌۢ بِٱلْمُتَّقِينَ ﴿115﴾
Ndipo chabwino chilichonse chimene angachite sadzakanidwa nacho, (koma adzawalipira malipiro abwino). Ndipo Allah Ngodziwa za amene akuopa Iye.[79]
إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ لَن تُغْنِىَ عَنْهُمْ أَمْوَٰلُهُمْ وَلَآ أَوْلَٰدُهُم مِّنَ ٱللَّهِ شَيْـًۭٔا ۖ وَأُو۟لَٰٓئِكَ أَصْحَٰبُ ٱلنَّارِ ۚ هُمْ فِيهَا خَٰلِدُونَ ﴿116﴾
Ndithudi, amene sakhulupirira, chuma chawo ngakhale ana awo, sizidzawathandiza chilichonse kwa Allah. Ndipo iwo ndi anthu a ku Moto basi; adzakhala mmenemo nthawi yaitali.
مَثَلُ مَا يُنفِقُونَ فِى هَٰذِهِ ٱلْحَيَوٰةِ ٱلدُّنْيَا كَمَثَلِ رِيحٍۢ فِيهَا صِرٌّ أَصَابَتْ حَرْثَ قَوْمٍۢ ظَلَمُوٓا۟ أَنفُسَهُمْ فَأَهْلَكَتْهُ ۚ وَمَا ظَلَمَهُمُ ٱللَّهُ وَلَٰكِنْ أَنفُسَهُمْ يَظْلِمُونَ ﴿117﴾
Fanizo la chimene akupereka mwaulere pa moyo uwu wa dziko lapansi, chili ngati mphepo yomwe mkati mwake muli chisanu chaukali, chagwera pa munda wa anthu omwe adadzichitira okha zoipa, n’kuuonongeratu. Si Allah amene adawachitira zoipa, koma iwo okha adadzichitira zoipa.[80]
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ لَا تَتَّخِذُوا۟ بِطَانَةًۭ مِّن دُونِكُمْ لَا يَأْلُونَكُمْ خَبَالًۭا وَدُّوا۟ مَا عَنِتُّمْ قَدْ بَدَتِ ٱلْبَغْضَآءُ مِنْ أَفْوَٰهِهِمْ وَمَا تُخْفِى صُدُورُهُمْ أَكْبَرُ ۚ قَدْ بَيَّنَّا لَكُمُ ٱلْءَايَٰتِ ۖ إِن كُنتُمْ تَعْقِلُونَ ﴿118﴾
E inu amene mwakhulupirira! Musawachite omwe sali mwa inu kukhala abwenzi; owauza chinsinsi, iwo sasiya kukuchitirani choipa. Amakonda zimene zikukuvutitsani. Chidani chawo (pa inu) chaonekera m’milomo yawo. Ndipo zimene zikubisa zifuwa zawo, nzazikulu zedi. Ndithudi, takufotokozerani zizindikiro zonse ngati inu muli anthu ozindikira.[81]
هَٰٓأَنتُمْ أُو۟لَآءِ تُحِبُّونَهُمْ وَلَا يُحِبُّونَكُمْ وَتُؤْمِنُونَ بِٱلْكِتَٰبِ كُلِّهِۦ وَإِذَا لَقُوكُمْ قَالُوٓا۟ ءَامَنَّا وَإِذَا خَلَوْا۟ عَضُّوا۟ عَلَيْكُمُ ٱلْأَنَامِلَ مِنَ ٱلْغَيْظِ ۚ قُلْ مُوتُوا۟ بِغَيْظِكُمْ ۗ إِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمٌۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ ﴿119﴾
Ha! Inu ndinu amene muwakonda (adani anu) pomwe iwo sakukondani ngakhale inu mukukhulupirira mabuku onse! Akakumana nanu amanena (mwachiphamaso): “Takhulupirira.” Koma akakhala kwa okha, amakulumirani nsonga za zala chifukwa chaukali. Nena: “Mwalirani ndiukali wanuwo ndithudi, Allah akudziwa za m’zifuwa (mwanu).”
إِن تَمْسَسْكُمْ حَسَنَةٌۭ تَسُؤْهُمْ وَإِن تُصِبْكُمْ سَيِّئَةٌۭ يَفْرَحُوا۟ بِهَا ۖ وَإِن تَصْبِرُوا۟ وَتَتَّقُوا۟ لَا يَضُرُّكُمْ كَيْدُهُمْ شَيْـًٔا ۗ إِنَّ ٱللَّهَ بِمَا يَعْمَلُونَ مُحِيطٌۭ ﴿120﴾
Ngati chabwino chikakufikirani, amaipidwa nacho; koma choipa chikakugwerani amachikondwelera. Koma ngati inu mupirira ndi kuopa Allah, ndale zawo sizingakuvutitseni chilichonse. Ndithu Allah akudziwa bwino zonse zimene iwo akuchita.[82]
وَإِذْ غَدَوْتَ مِنْ أَهْلِكَ تُبَوِّئُ ٱلْمُؤْمِنِينَ مَقَٰعِدَ لِلْقِتَالِ ۗ وَٱللَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٌ ﴿121﴾
(Kumbukira) pamene unachoka m’mawa kusiya banja lako kuti uwakonzere Asilamu malo omenyanira (nkhondo). Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa.[83]
إِذْ هَمَّت طَّآئِفَتَانِ مِنكُمْ أَن تَفْشَلَا وَٱللَّهُ وَلِيُّهُمَا ۗ وَعَلَى ٱللَّهِ فَلْيَتَوَكَّلِ ٱلْمُؤْمِنُونَ ﴿122﴾
(Kumbukira) pamene magulu awiri mwa inu anafunitsitsa kuti athawe (chifukwa cha mantha monga momwe adathawira achinyengo). Koma Allah adali Mtetezi wa magulu awiriwo. (Choncho adawasunga kuti asathawe). Ndipo okhulupirira ayadzamire kwa Allah Yekha basi.
وَلَقَدْ نَصَرَكُمُ ٱللَّهُ بِبَدْرٍۢ وَأَنتُمْ أَذِلَّةٌۭ ۖ فَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ لَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ ﴿123﴾
Allah adakupulumutsani pa (nkhondo) ya Badri pomwe inu munali ofooka (chifukwa chakuchepa ndi kusakhala ndi zida zokwanira). Choncho opani Allah kuti mumthokoze (nthawi zonse pa zomwe akukuchitirani).
إِذْ تَقُولُ لِلْمُؤْمِنِينَ أَلَن يَكْفِيَكُمْ أَن يُمِدَّكُمْ رَبُّكُم بِثَلَٰثَةِ ءَالَٰفٍۢ مِّنَ ٱلْمَلَٰٓئِكَةِ مُنزَلِينَ ﴿124﴾
(Kumbukira) pamene umauza okhulupirira: “Kodi sizikukukwanirani pokuonjezerani Mbuye wanu zikwi zitatu za angelo otsitsidwa?[84]
بَلَىٰٓ ۚ إِن تَصْبِرُوا۟ وَتَتَّقُوا۟ وَيَأْتُوكُم مِّن فَوْرِهِمْ هَٰذَا يُمْدِدْكُمْ رَبُّكُم بِخَمْسَةِ ءَالَٰفٍۢ مِّنَ ٱلْمَلَٰٓئِكَةِ مُسَوِّمِينَ ﴿125﴾
Inde, ngati mupirira ndi kudziteteza ku machimo, ndipo (adani anu) nakudzerani mwachangu chawo chimenechi, pamenepo Mbuye wanu adzakuonjezerani ndi zikwi zisanu za angelo odziwa kumenya nkhondo.”
وَمَا جَعَلَهُ ٱللَّهُ إِلَّا بُشْرَىٰ لَكُمْ وَلِتَطْمَئِنَّ قُلُوبُكُم بِهِۦ ۗ وَمَا ٱلنَّصْرُ إِلَّا مِنْ عِندِ ٱللَّهِ ٱلْعَزِيزِ ٱلْحَكِيمِ ﴿126﴾
Ndipo Allah sadachite izi (potumiza angelo) koma kuti ukhale uthenga wabwino kwa inu ndi kuti pakutero mitima yanu ikhazikike ndi zimenezo. Ndipo chithandizo sichichokera (kwa wina aliyense) koma kwa Allah basi, Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.
لِيَقْطَعَ طَرَفًۭا مِّنَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓا۟ أَوْ يَكْبِتَهُمْ فَيَنقَلِبُوا۟ خَآئِبِينَ ﴿127﴾
(Kuchita izi) nkuti adule gawo la osakhulupirira (kuti ena a iwo aphedwe) kapena awasambule ndi kuti abwelere ali olephera.[85]
لَيْسَ لَكَ مِنَ ٱلْأَمْرِ شَىْءٌ أَوْ يَتُوبَ عَلَيْهِمْ أَوْ يُعَذِّبَهُمْ فَإِنَّهُمْ ظَٰلِمُونَ ﴿128﴾
Iwe ulibe chako pa izi. Mwina (Allah) angalandire kulapa kwawo kapena kuwalanga pakuti ndithu iwo ndi anthu oipa.
وَلِلَّهِ مَا فِى ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِى ٱلْأَرْضِ ۚ يَغْفِرُ لِمَن يَشَآءُ وَيُعَذِّبُ مَن يَشَآءُ ۚ وَٱللَّهُ غَفُورٌۭ رَّحِيمٌۭ ﴿129﴾
Zonse zakumwamba ndi zapansi nza Allah; amamkhululukira amene wamfuna, ndikumulanga amene wamfuna. Komatu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ لَا تَأْكُلُوا۟ ٱلرِّبَوٰٓا۟ أَضْعَٰفًۭا مُّضَٰعَفَةًۭ ۖ وَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ لَعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ ﴿130﴾
E inu amene mwakhulupirira! Musadye Riba (chuma cha katapira), kumangoonjezeraonjezera. Ndipo opani Allah kuti mupambane.[86]
وَٱتَّقُوا۟ ٱلنَّارَ ٱلَّتِىٓ أُعِدَّتْ لِلْكَٰفِرِينَ ﴿131﴾
Ndipo opani Moto umene wakonzedwa kwa (anthu) osakhulupirira.
وَأَطِيعُوا۟ ٱللَّهَ وَٱلرَّسُولَ لَعَلَّكُمْ تُرْحَمُونَ ﴿132﴾
Ndipo mverani Allah ndi Mtumiki kuti mumveredwe chisoni.
۞ وَسَارِعُوٓا۟ إِلَىٰ مَغْفِرَةٍۢ مِّن رَّبِّكُمْ وَجَنَّةٍ عَرْضُهَا ٱلسَّمَٰوَٰتُ وَٱلْأَرْضُ أُعِدَّتْ لِلْمُتَّقِينَ ﴿133﴾
Ndipo chimkereni mwachangu chikhululuko cha Mbuye wanu (kupyolera m’zochita zanu zabwino), ndi Munda (Wake) umene Kutambasuka kwake (mulifupi) kuli ngati kumwamba ndi pansi, (womwe) wakonzedwa kuti ukhale wa oopa Allah.[87]
ٱلَّذِينَ يُنفِقُونَ فِى ٱلسَّرَّآءِ وَٱلضَّرَّآءِ وَٱلْكَٰظِمِينَ ٱلْغَيْظَ وَٱلْعَافِينَ عَنِ ٱلنَّاسِ ۗ وَٱللَّهُ يُحِبُّ ٱلْمُحْسِنِينَ ﴿134﴾
Omwe amapereka (zopereka zawo mwaulere) pamene akupeza bwino ngakhale pamene akuvutika; amenenso amabisa ukali wawo ndi okhululukira anthu. Ndipo Allah amakonda ochita zabwino.[88]
وَٱلَّذِينَ إِذَا فَعَلُوا۟ فَٰحِشَةً أَوْ ظَلَمُوٓا۟ أَنفُسَهُمْ ذَكَرُوا۟ ٱللَّهَ فَٱسْتَغْفَرُوا۟ لِذُنُوبِهِمْ وَمَن يَغْفِرُ ٱلذُّنُوبَ إِلَّا ٱللَّهُ وَلَمْ يُصِرُّوا۟ عَلَىٰ مَا فَعَلُوا۟ وَهُمْ يَعْلَمُونَ ﴿135﴾
Ndi amene amati akachita uve (wamachimo), kapena kudzichitira okha zoipa, amakumbukira Allah nampempha chikhululuko pa machimo awo. Kodi ndindani angakhululuke machimo kupatula Allah; ndipo napanda kupitiriza machimo omwe achita uku akudziwa.
أُو۟لَٰٓئِكَ جَزَآؤُهُم مَّغْفِرَةٌۭ مِّن رَّبِّهِمْ وَجَنَّٰتٌۭ تَجْرِى مِن تَحْتِهَا ٱلْأَنْهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَا ۚ وَنِعْمَ أَجْرُ ٱلْعَٰمِلِينَ ﴿136﴾
Iwowo mphoto yawo ndi chikhululuko chochokera kwa Mbuye wawo, ndi minda yoyenda mitsinje pansi pake (ndi patsogolo pake), momwe akakhalamo nthawi yaitali. Taonani kukoma malipiro a ochita zabwino.
قَدْ خَلَتْ مِن قَبْلِكُمْ سُنَنٌۭ فَسِيرُوا۟ فِى ٱلْأَرْضِ فَٱنظُرُوا۟ كَيْفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلْمُكَذِّبِينَ ﴿137﴾
Zidapita njira za zilango zambiri zosiyanasiyana zomwe adapatsidwa amene adalipo patsogolo panu. Tero tayendani pa dziko ndi kuona momwe adalili mapeto a anthu otsutsa.
هَٰذَا بَيَانٌۭ لِّلنَّاسِ وَهُدًۭى وَمَوْعِظَةٌۭ لِّلْمُتَّقِينَ ﴿138﴾
Uku ndi kulengeza poyera kwa anthu (onse); komanso chiongoko ndi ulaliki kwa (anthu) oopa Allah!
وَلَا تَهِنُوا۟ وَلَا تَحْزَنُوا۟ وَأَنتُمُ ٱلْأَعْلَوْنَ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ ﴿139﴾
Ndipo musafooke (pomenya nkhondo), ndiponso musadandaule (ndi mavuto amene akupezani) pakuti ndinu apamwamba, ngati mulidi okhulupirira.
إِن يَمْسَسْكُمْ قَرْحٌۭ فَقَدْ مَسَّ ٱلْقَوْمَ قَرْحٌۭ مِّثْلُهُۥ ۚ وَتِلْكَ ٱلْأَيَّامُ نُدَاوِلُهَا بَيْنَ ٱلنَّاسِ وَلِيَعْلَمَ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ وَيَتَّخِذَ مِنكُمْ شُهَدَآءَ ۗ وَٱللَّهُ لَا يُحِبُّ ٱلظَّٰلِمِينَ ﴿140﴾
Ngati mwavulazidwa, naonso anthuwo avulazidwanso molingana. Ndipo amenewo ndimasiku, timawapatsa anthu mosinthanasinthana. (Ichi chachitika) kuti Allah aonetse poyera amene akhulupirira (moona; choncho sadathawe konse); ndi kuti awachite ena mwa inu kukhala Shuhadaa (ofera pankhondo yoyera). Komatu Allah sakonda anthu ochita zoipa.[89]
وَلِيُمَحِّصَ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ وَيَمْحَقَ ٱلْكَٰفِرِينَ ﴿141﴾
(Izi) nkuti Allah awayeretse amene akhulupirira ndikuwathetseratu osakhulupirira.
أَمْ حَسِبْتُمْ أَن تَدْخُلُوا۟ ٱلْجَنَّةَ وَلَمَّا يَعْلَمِ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ جَٰهَدُوا۟ مِنكُمْ وَيَعْلَمَ ٱلصَّٰبِرِينَ ﴿142﴾
Kodi mukuganiza kuti mukalowa ku Munda wamtendere pomwe Allah asadawaonetsere poyera amene amenyera chipembedzo cha Allah mwa inu ndi kuwaonetseranso poyera opirira (pa nkhondo ya Allah)?
وَلَقَدْ كُنتُمْ تَمَنَّوْنَ ٱلْمَوْتَ مِن قَبْلِ أَن تَلْقَوْهُ فَقَدْ رَأَيْتُمُوهُ وَأَنتُمْ تَنظُرُونَ ﴿143﴾
Ndithudi, mudali kuilakalaka imfa musanakumane nayo. Ndithudi tsopano mwaiona (ndikuphedwa kwa abale anu) inu mukupenya. [90]
وَمَا مُحَمَّدٌ إِلَّا رَسُولٌۭ قَدْ خَلَتْ مِن قَبْلِهِ ٱلرُّسُلُ ۚ أَفَإِي۟ن مَّاتَ أَوْ قُتِلَ ٱنقَلَبْتُمْ عَلَىٰٓ أَعْقَٰبِكُمْ ۚ وَمَن يَنقَلِبْ عَلَىٰ عَقِبَيْهِ فَلَن يَضُرَّ ٱللَّهَ شَيْـًۭٔا ۗ وَسَيَجْزِى ٱللَّهُ ٱلشَّٰكِرِينَ ﴿144﴾
Muhammad (s.a.w) sali chinthu china koma Mtumiki chabe. Patsogolo pake adamuka atumiki ambiri. Kodi ngati atamwalira kapena kuphedwa, mungabwelerenso m’mbuyo? Ndipo amene abwelere m’mbuyo mwake savutitsa Allah ndi chilichonse; koma Allah adzalipira othokoza.[91]
وَمَا كَانَ لِنَفْسٍ أَن تَمُوتَ إِلَّا بِإِذْنِ ٱللَّهِ كِتَٰبًۭا مُّؤَجَّلًۭا ۗ وَمَن يُرِدْ ثَوَابَ ٱلدُّنْيَا نُؤْتِهِۦ مِنْهَا وَمَن يُرِدْ ثَوَابَ ٱلْءَاخِرَةِ نُؤْتِهِۦ مِنْهَا ۚ وَسَنَجْزِى ٱلشَّٰكِرِينَ ﴿145﴾
Munthu aliyense sangafe pokhapokha mwa chilolezo cha Allah, (ndi kukwanira) nthawi yake yolembedwa. Ndipo amene akufuna mphoto ya pa dziko la pansi, timpatsa pompo; ndipo amene akufuna Mphoto ya tsiku lachimaliziro tidzampatsa konko. Ndipo, tidzawalipira (zabwino) othokoza.[92]
وَكَأَيِّن مِّن نَّبِىٍّۢ قَٰتَلَ مَعَهُۥ رِبِّيُّونَ كَثِيرٌۭ فَمَا وَهَنُوا۟ لِمَآ أَصَابَهُمْ فِى سَبِيلِ ٱللَّهِ وَمَا ضَعُفُوا۟ وَمَا ٱسْتَكَانُوا۟ ۗ وَٱللَّهُ يُحِبُّ ٱلصَّٰبِرِينَ ﴿146﴾
Ndi Aneneri angati adamenyana (ndi adani) pamodzi ndi anthu olungama ambiri, komatu sadataye mtima pa mavuto omwe adawagwera pa njira ya Allah; sadafooke ndipo sadagonjere (adani awo), ndipo Allah amakonda opirira.[93]
وَمَا كَانَ قَوْلَهُمْ إِلَّآ أَن قَالُوا۟ رَبَّنَا ٱغْفِرْ لَنَا ذُنُوبَنَا وَإِسْرَافَنَا فِىٓ أَمْرِنَا وَثَبِّتْ أَقْدَامَنَا وَٱنصُرْنَا عَلَى ٱلْقَوْمِ ٱلْكَٰفِرِينَ ﴿147﴾
(Anthu olungamawa) kunena kwawo sikudali kwina koma ankati: “Mbuye wathu! Tikhululukireni machimo athu ndi kupyola malire kwathu m’zinthu zathu. Ndipo limbikitsani mapazi athu (panjira Yanu) ndipo tithandizeni ku anthu osakhulupirira.”
فَـَٔاتَىٰهُمُ ٱللَّهُ ثَوَابَ ٱلدُّنْيَا وَحُسْنَ ثَوَابِ ٱلْءَاخِرَةِ ۗ وَٱللَّهُ يُحِبُّ ٱلْمُحْسِنِينَ ﴿148﴾
Choncho Allah adawapatsa mphoto ya pa dziko lapansi ndi mphoto yabwino ya tsiku lachimaliziro. Allah amakonda ochita zabwino.
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓا۟ إِن تُطِيعُوا۟ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ يَرُدُّوكُمْ عَلَىٰٓ أَعْقَٰبِكُمْ فَتَنقَلِبُوا۟ خَٰسِرِينَ ﴿149﴾
E inu amene mwakhulupirira! Ngati muwamvere amene sadakhulupirire, akubwezerani kumbuyo kwanu (kumachitidwe achikunja) tero mudzakhala otaika.
بَلِ ٱللَّهُ مَوْلَىٰكُمْ ۖ وَهُوَ خَيْرُ ٱلنَّٰصِرِينَ ﴿150﴾
Komatu Allah ndiye Mbuye wanu. Iye Ngwabwino kwabasi kuposa athandizi (ena onse).
سَنُلْقِى فِى قُلُوبِ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ ٱلرُّعْبَ بِمَآ أَشْرَكُوا۟ بِٱللَّهِ مَا لَمْ يُنَزِّلْ بِهِۦ سُلْطَٰنًۭا ۖ وَمَأْوَىٰهُمُ ٱلنَّارُ ۚ وَبِئْسَ مَثْوَى ٱلظَّٰلِمِينَ ﴿151﴾
Tiponya mantha m’mitima mwa amene sadakhulupirire chifukwa chakumphatikiza Allah (ndi mafano) omwe Allah sadatsitsire umboni (wosonyeza umulungu wawo) ndipo malo awo adzakhala ku Moto. Taonani kuipitsitsa malo a anthu ochita zoipa.
وَلَقَدْ صَدَقَكُمُ ٱللَّهُ وَعْدَهُۥٓ إِذْ تَحُسُّونَهُم بِإِذْنِهِۦ ۖ حَتَّىٰٓ إِذَا فَشِلْتُمْ وَتَنَٰزَعْتُمْ فِى ٱلْأَمْرِ وَعَصَيْتُم مِّنۢ بَعْدِ مَآ أَرَىٰكُم مَّا تُحِبُّونَ ۚ مِنكُم مَّن يُرِيدُ ٱلدُّنْيَا وَمِنكُم مَّن يُرِيدُ ٱلْءَاخِرَةَ ۚ ثُمَّ صَرَفَكُمْ عَنْهُمْ لِيَبْتَلِيَكُمْ ۖ وَلَقَدْ عَفَا عَنكُمْ ۗ وَٱللَّهُ ذُو فَضْلٍ عَلَى ٱلْمُؤْمِنِينَ ﴿152﴾
Ndithudi, Allah adakutsimikizirani lonjezo lake (lakuti muwagonjetsa adani). Choncho mudali kuwapha mwachilolezo Chake kufikira pamene mudafooka ndikuyamba kukangana za lamulolo, tero mudalinyozera pambuyo pokuonetsani zimene mumazikonda; (pamenepo mpomwe adasiya kukuthangatani). Alipo ena mwa inu amene akukonda dziko lapansi (zamdziko), ndipo alipo ena mwa inu amene akukonda tsiku lachimaliziro. Kenako (Allah) adakuchotsani pa iwo (adakusiitsani kuwamenya osakhulupirirawo) kuti akuyeseni mayeso. Koma Iye tsopano wakukhululukirani. Ndipo Allah ndi mwini kuchita zabwino pa okhulupirira.[94]
۞ إِذْ تُصْعِدُونَ وَلَا تَلْوُۥنَ عَلَىٰٓ أَحَدٍۢ وَٱلرَّسُولُ يَدْعُوكُمْ فِىٓ أُخْرَىٰكُمْ فَأَثَٰبَكُمْ غَمًّۢا بِغَمٍّۢ لِّكَيْلَا تَحْزَنُوا۟ عَلَىٰ مَا فَاتَكُمْ وَلَا مَآ أَصَٰبَكُمْ ۗ وَٱللَّهُ خَبِيرٌۢ بِمَا تَعْمَلُونَ ﴿153﴾
Kumbukirani pamene mudali kuthawa mwa liwiro popanda kumvera aliyense; pomwe Mtumiki adali kukuitanani, ali pambuyo panu. Ndipo (Allah) Adakupatsani madandaulo pa madandaulo. (Motero wakukhululukirani) kuti musadandaule pa zomwe zakudutsani, ngakhalenso (pa masautso) omwe akupezani. Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene muchita.
ثُمَّ أَنزَلَ عَلَيْكُم مِّنۢ بَعْدِ ٱلْغَمِّ أَمَنَةًۭ نُّعَاسًۭا يَغْشَىٰ طَآئِفَةًۭ مِّنكُمْ ۖ وَطَآئِفَةٌۭ قَدْ أَهَمَّتْهُمْ أَنفُسُهُمْ يَظُنُّونَ بِٱللَّهِ غَيْرَ ٱلْحَقِّ ظَنَّ ٱلْجَٰهِلِيَّةِ ۖ يَقُولُونَ هَل لَّنَا مِنَ ٱلْأَمْرِ مِن شَىْءٍۢ ۗ قُلْ إِنَّ ٱلْأَمْرَ كُلَّهُۥ لِلَّهِ ۗ يُخْفُونَ فِىٓ أَنفُسِهِم مَّا لَا يُبْدُونَ لَكَ ۖ يَقُولُونَ لَوْ كَانَ لَنَا مِنَ ٱلْأَمْرِ شَىْءٌۭ مَّا قُتِلْنَا هَٰهُنَا ۗ قُل لَّوْ كُنتُمْ فِى بُيُوتِكُمْ لَبَرَزَ ٱلَّذِينَ كُتِبَ عَلَيْهِمُ ٱلْقَتْلُ إِلَىٰ مَضَاجِعِهِمْ ۖ وَلِيَبْتَلِىَ ٱللَّهُ مَا فِى صُدُورِكُمْ وَلِيُمَحِّصَ مَا فِى قُلُوبِكُمْ ۗ وَٱللَّهُ عَلِيمٌۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ ﴿154﴾
Kenako pambuyo pa kudandaula, adakutsitsirani mpumulo - tulo tomwe tidaphimba gulu lina mwa inu. Padali gulu lina lomwe maganizo awo adawatangwanitsa namuganizira Allah ndizoganizira zopanda choonadi, zoganizira zaumbuli; ankati: “Ha! Kodi tili ndi chiyani ife pa chinthu ichi?” Nena: “Zinthu zonse nza Allah.” Akubisa m’mitima mwawo zomwe sakuzionetsa kwa iwe. Akunena: “Tidakakhala ndi chilichonse pa chinthu ichi, sitikadaphedwa apa.” Nena: “Ngakhale mukadakhala m’nyumba zanu, ndithudi kwa iwo amene imfa idalembedwa (kuti amwalire) akadapita kumalo omwalilirawo, koma Allah (adachita izi) kuti awonetse poyera zomwe zili m’zifuwa zanu. Ndikuyeretsa zomwe zili m’mitima mwanu. Ndipo Allah Ngodziwa za mzifuwa.”[95]
إِنَّ ٱلَّذِينَ تَوَلَّوْا۟ مِنكُمْ يَوْمَ ٱلْتَقَى ٱلْجَمْعَانِ إِنَّمَا ٱسْتَزَلَّهُمُ ٱلشَّيْطَٰنُ بِبَعْضِ مَا كَسَبُوا۟ ۖ وَلَقَدْ عَفَا ٱللَّهُ عَنْهُمْ ۗ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٌ حَلِيمٌۭ ﴿155﴾
Ndithudi, mwa inu amene adabwerera m’mbuyo (kuthawa) tsiku lomwe magulu awiri a nkhondo adakumana (pa nkhondo ya Uhudi; gulu la osakhulupirira ndi gulu lankhondo la Asilamu), satana ndiyemwe adawaterezetsa chifukwa cha zina (zolakwa) zomwe adachita; ndipo Allah (tsopano) wawakhululukira. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngoleza koposa.
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ لَا تَكُونُوا۟ كَٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ وَقَالُوا۟ لِإِخْوَٰنِهِمْ إِذَا ضَرَبُوا۟ فِى ٱلْأَرْضِ أَوْ كَانُوا۟ غُزًّۭى لَّوْ كَانُوا۟ عِندَنَا مَا مَاتُوا۟ وَمَا قُتِلُوا۟ لِيَجْعَلَ ٱللَّهُ ذَٰلِكَ حَسْرَةًۭ فِى قُلُوبِهِمْ ۗ وَٱللَّهُ يُحْىِۦ وَيُمِيتُ ۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌۭ ﴿156﴾
E inu amene mwakhulupirira! Musakhale ngati amene sadakhulupirire, nanena za anzawo pamene akuyenda pa dziko kapena pomwe akumenyana nkhondo (ndikufera konko): “Akadakhala ndi ife sakadafa, ndiponso sakadaphedwa.” Allah (adawathira maganizo amenewa) kuti azipange zimenezo kukhala zodandaulitsa m’mitima mwawo. Komatu Allah ndi amene amapereka moyo ndi imfa. Ndipo Allah akuona zonse zomwe mukuchita.[96]
وَلَئِن قُتِلْتُمْ فِى سَبِيلِ ٱللَّهِ أَوْ مُتُّمْ لَمَغْفِرَةٌۭ مِّنَ ٱللَّهِ وَرَحْمَةٌ خَيْرٌۭ مِّمَّا يَجْمَعُونَ ﴿157﴾
Ndipo ngati mwaphedwa pa njira ya Allah, kapena kufa, (palibe chotaika kwa inu) pakuti chikhululuko ndi chisoni zochokera kwa Allah nzabwino kuposa zomwe akuzisonkhanitsa (pa moyo wa pa dziko lapansi).
وَلَئِن مُّتُّمْ أَوْ قُتِلْتُمْ لَإِلَى ٱللَّهِ تُحْشَرُونَ ﴿158﴾
Ndipo ngati mumwalira kapena kuphedwa (n’chimodzimodzi), ndithudi nonsenu mudzasonkhanitsidwa kwa Allah.
فَبِمَا رَحْمَةٍۢ مِّنَ ٱللَّهِ لِنتَ لَهُمْ ۖ وَلَوْ كُنتَ فَظًّا غَلِيظَ ٱلْقَلْبِ لَٱنفَضُّوا۟ مِنْ حَوْلِكَ ۖ فَٱعْفُ عَنْهُمْ وَٱسْتَغْفِرْ لَهُمْ وَشَاوِرْهُمْ فِى ٱلْأَمْرِ ۖ فَإِذَا عَزَمْتَ فَتَوَكَّلْ عَلَى ٱللَّهِ ۚ إِنَّ ٱللَّهَ يُحِبُّ ٱلْمُتَوَكِّلِينَ ﴿159﴾
Chifukwa cha chifundo chochokera kwa Allah, uli woleza mtima kwa iwo, (iwe Mtumiki Muhammad {s.a.w}). Ndipo ukadakhala waukali, wouma mtima, ndithudi, akadakuthawa pamaso pako. Choncho akhululukire ndi kuwapemphera chikhululuko (kwa Allah); ndipo chita nawo upo pa zinthu. Ndipo ngati watsimikiza, tsamira kwa Allah (basi, ndi kuchita chimene watsimikiza kuchichita). Ndithudi, Allah amakonda oyadzamira Kwake (odalira Iye).
إِن يَنصُرْكُمُ ٱللَّهُ فَلَا غَالِبَ لَكُمْ ۖ وَإِن يَخْذُلْكُمْ فَمَن ذَا ٱلَّذِى يَنصُرُكُم مِّنۢ بَعْدِهِۦ ۗ وَعَلَى ٱللَّهِ فَلْيَتَوَكَّلِ ٱلْمُؤْمِنُونَ ﴿160﴾
Ngati Allah akupulumutsani, palibe amene angathe kukugonjetsani. Ndipo ngati akulekani, ndaninso angakupulumutseni pambuyo pake. Choncho, okhulupirira ayadzamire kwa Allah basi.
وَمَا كَانَ لِنَبِىٍّ أَن يَغُلَّ ۚ وَمَن يَغْلُلْ يَأْتِ بِمَا غَلَّ يَوْمَ ٱلْقِيَٰمَةِ ۚ ثُمَّ تُوَفَّىٰ كُلُّ نَفْسٍۢ مَّا كَسَبَتْ وَهُمْ لَا يُظْلَمُونَ ﴿161﴾
Nkosatheka kwa Mtumiki kuchita chinyengo. Ndipo amene achite chinyengo adzadza pa tsiku lachimaliziro ndi zomwe adazichitira chinyengo. Kenako munthu aliyense adzalipidwa mokwanira pa zomwe adachita. Ndipo sadzaponderezedwa.
أَفَمَنِ ٱتَّبَعَ رِضْوَٰنَ ٱللَّهِ كَمَنۢ بَآءَ بِسَخَطٍۢ مِّنَ ٱللَّهِ وَمَأْوَىٰهُ جَهَنَّمُ ۚ وَبِئْسَ ٱلْمَصِيرُ ﴿162﴾
Kodi amene akutsata chokondweretsa Allah angalingane ndi yemwe wabwerera ndi mkwiyo wochokera kwa Allah, ndipo Jahannam nkukhala malo ake? Taonani kuipa kumalo obwerera!
هُمْ دَرَجَٰتٌ عِندَ ٱللَّهِ ۗ وَٱللَّهُ بَصِيرٌۢ بِمَا يَعْمَلُونَ ﴿163﴾
Iwo ali ndi maulemelero (osiyanasiyana) kwa Allah. Ndipo Allah akuona zonse zomwe akuchita.
لَقَدْ مَنَّ ٱللَّهُ عَلَى ٱلْمُؤْمِنِينَ إِذْ بَعَثَ فِيهِمْ رَسُولًۭا مِّنْ أَنفُسِهِمْ يَتْلُوا۟ عَلَيْهِمْ ءَايَٰتِهِۦ وَيُزَكِّيهِمْ وَيُعَلِّمُهُمُ ٱلْكِتَٰبَ وَٱلْحِكْمَةَ وَإِن كَانُوا۟ مِن قَبْلُ لَفِى ضَلَٰلٍۢ مُّبِينٍ ﴿164﴾
Ndithudi, Allah adawachitira ubwino waukulu okhulupirira powatumizira Mtumiki wochokera mwa iwo yemwe akuwawerengera ma Ayah ake (ndime zake) ndikuwayeretsa ndikuwaphunzitsa buku ndi (mawu a) nzeru. Ndithudi, kale adali mkusokera koonekera.[97]
أَوَلَمَّآ أَصَٰبَتْكُم مُّصِيبَةٌۭ قَدْ أَصَبْتُم مِّثْلَيْهَا قُلْتُمْ أَنَّىٰ هَٰذَا ۖ قُلْ هُوَ مِنْ عِندِ أَنفُسِكُمْ ۗ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَىْءٍۢ قَدِيرٌۭ ﴿165﴾
Pamene sautso lidakupezani lomwe inu mudawathira nalo (adani anu) lochulukirapo kawiri, mudanena: “Lachokera kuti (sautso) ili?” Nena: “Ilo lachokera kwa inu eni (chifukwa cha kunyoza lamulo lomwe adakuuzani). Ndithudi, Allah Ngokhoza chilichonse.”
وَمَآ أَصَٰبَكُمْ يَوْمَ ٱلْتَقَى ٱلْجَمْعَانِ فَبِإِذْنِ ٱللَّهِ وَلِيَعْلَمَ ٱلْمُؤْمِنِينَ ﴿166﴾
Ndipo sautso lomwe lidakupezani tsiku lomwe adakumana magulu awiri ankhondo, lidali mwa chilolezo cha Allah ndikutinso awaonetsere poyera okhulupirira.
وَلِيَعْلَمَ ٱلَّذِينَ نَافَقُوا۟ ۚ وَقِيلَ لَهُمْ تَعَالَوْا۟ قَٰتِلُوا۟ فِى سَبِيلِ ٱللَّهِ أَوِ ٱدْفَعُوا۟ ۖ قَالُوا۟ لَوْ نَعْلَمُ قِتَالًۭا لَّٱتَّبَعْنَٰكُمْ ۗ هُمْ لِلْكُفْرِ يَوْمَئِذٍ أَقْرَبُ مِنْهُمْ لِلْإِيمَٰنِ ۚ يَقُولُونَ بِأَفْوَٰهِهِم مَّا لَيْسَ فِى قُلُوبِهِمْ ۗ وَٱللَّهُ أَعْلَمُ بِمَا يَكْتُمُونَ ﴿167﴾
Ndi kuwadziwitsa amene adachita uchiphamaso. Iwo adauzidwa: “Bwerani, menyani (nkhondo) pa njira ya Allah kapena mwatsekereze (adani kwa ife).” Adati: “Tikadadziwa kuti pali kumenyana, ndithudi, tikadakutsatani (koma kumeneko kuli kuphedwa kokhakokha basi).” Iwo tsiku limenelo adali pafupi ndikusakhulupirira kuposa chikhulupiliro (ngakhale kuti masiku onse amasonyeza Chisilamu mwa chiphamaso). Akunena ndi milomo yawo zomwe sizili m’mitima mwawo. Koma Allah akudziwa bwinobwino (zonse) zomwe akubisa.
ٱلَّذِينَ قَالُوا۟ لِإِخْوَٰنِهِمْ وَقَعَدُوا۟ لَوْ أَطَاعُونَا مَا قُتِلُوا۟ ۗ قُلْ فَٱدْرَءُوا۟ عَنْ أَنفُسِكُمُ ٱلْمَوْتَ إِن كُنتُمْ صَٰدِقِينَ ﴿168﴾
Iwo ndi amene adanena za abale awo pomwe iwo adakhala osapita ku nkhondo: “Akadatimvera, sibwenzi ataphedwa.” Nena: “Dzichotsereni imfa nokha, (kuti musafe) ngati mukunenadi zoona.”
وَلَا تَحْسَبَنَّ ٱلَّذِينَ قُتِلُوا۟ فِى سَبِيلِ ٱللَّهِ أَمْوَٰتًۢا ۚ بَلْ أَحْيَآءٌ عِندَ رَبِّهِمْ يُرْزَقُونَ ﴿169﴾
Ndipo musawaganizire omwe adaphedwa pa njira ya Allah kuti ndi akufa, koma iwo ngamoyo, akudyetsedwa kwa Mbuye wawo;
فَرِحِينَ بِمَآ ءَاتَىٰهُمُ ٱللَّهُ مِن فَضْلِهِۦ وَيَسْتَبْشِرُونَ بِٱلَّذِينَ لَمْ يَلْحَقُوا۟ بِهِم مِّنْ خَلْفِهِمْ أَلَّا خَوْفٌ عَلَيْهِمْ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ ﴿170﴾
Akukondwera pa zimene wawapatsa Allah kuchokera m’zabwino Zake. Ndipo akufunira mafuno abwino amene sadakumane nawo omwe ali pambuyo pawo, (omwe alipobe pa dziko lapansi) ponena kuti pa iwo sipadzakhala mantha kapena kudandaula.
۞ يَسْتَبْشِرُونَ بِنِعْمَةٍۢ مِّنَ ٱللَّهِ وَفَضْلٍۢ وَأَنَّ ٱللَّهَ لَا يُضِيعُ أَجْرَ ٱلْمُؤْمِنِينَ ﴿171﴾
Akukondwelera chisomo ndi ubwino zochokera kwa Allah, ndi kuti Allah sasokoneza malipiro a okhulupirira.
ٱلَّذِينَ ٱسْتَجَابُوا۟ لِلَّهِ وَٱلرَّسُولِ مِنۢ بَعْدِ مَآ أَصَابَهُمُ ٱلْقَرْحُ ۚ لِلَّذِينَ أَحْسَنُوا۟ مِنْهُمْ وَٱتَّقَوْا۟ أَجْرٌ عَظِيمٌ ﴿172﴾
(Awa ndi) amene adavomera Allah ndi Mtumiki pambuyo povulazidwa; kwa amene achita zabwino mwa iwo ndi kuopa Allah, adzakhala ndi malipiro aakulu.[98]
ٱلَّذِينَ قَالَ لَهُمُ ٱلنَّاسُ إِنَّ ٱلنَّاسَ قَدْ جَمَعُوا۟ لَكُمْ فَٱخْشَوْهُمْ فَزَادَهُمْ إِيمَٰنًۭا وَقَالُوا۟ حَسْبُنَا ٱللَّهُ وَنِعْمَ ٱلْوَكِيلُ ﴿173﴾
Omwenso adauzidwa ndi anthu (olembedwa ganyu ndi Akafiri aku Makka) kuti: “Anthu Akusonkhanirani. Choncho aopeni.” Koma (zonenazo) zidawaonjezera chikhulupiliro (Asilamu). Ndipo adati: “Allah akutikwanira, ndipo Iye ndi Mtetezi wabwino koposa.”
فَٱنقَلَبُوا۟ بِنِعْمَةٍۢ مِّنَ ٱللَّهِ وَفَضْلٍۢ لَّمْ يَمْسَسْهُمْ سُوٓءٌۭ وَٱتَّبَعُوا۟ رِضْوَٰنَ ٱللَّهِ ۗ وَٱللَّهُ ذُو فَضْلٍ عَظِيمٍ ﴿174﴾
Choncho adabwerera ndi chisomo ndi ubwino zochokera kwa Allah. Sichidawakhudze choipa chilichonse; adatsatira zokondweretsa Allah. Ndipo Allah ndimwini ubwino waukulu.
إِنَّمَا ذَٰلِكُمُ ٱلشَّيْطَٰنُ يُخَوِّفُ أَوْلِيَآءَهُۥ فَلَا تَخَافُوهُمْ وَخَافُونِ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ ﴿175﴾
Ndithudi uyo (anakuopsezani) ndi satana yemwe amaopseza anzake. Choncho musawaope, ndiopeni Ine ngati inu mulidi okhulupirira.
وَلَا يَحْزُنكَ ٱلَّذِينَ يُسَٰرِعُونَ فِى ٱلْكُفْرِ ۚ إِنَّهُمْ لَن يَضُرُّوا۟ ٱللَّهَ شَيْـًۭٔا ۗ يُرِيدُ ٱللَّهُ أَلَّا يَجْعَلَ لَهُمْ حَظًّۭا فِى ٱلْءَاخِرَةِ ۖ وَلَهُمْ عَذَابٌ عَظِيمٌ ﴿176﴾
Ndipo asakudandaulitse omwe akuthamangira kuchita zinthu zachikunja. Ndithu iwo sangapereke sautso lililonse kwa Allah. Allah akufuna kuti asawaikire gawo lililonse la (zabwino) tsiku lachimaliziro, ndipo pa iwo padzakhala chilango chachikulu.
إِنَّ ٱلَّذِينَ ٱشْتَرَوُا۟ ٱلْكُفْرَ بِٱلْإِيمَٰنِ لَن يَضُرُّوا۟ ٱللَّهَ شَيْـًۭٔا وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌۭ ﴿177﴾
Ndithudi, amene asinthanitsa kusakhulupirira ndi chikhulupiliro, sangathe kumvutitsa Allah ndi chilichonse. Ndipo pa iwo padzakhala chilango chopweteka.
وَلَا يَحْسَبَنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓا۟ أَنَّمَا نُمْلِى لَهُمْ خَيْرٌۭ لِّأَنفُسِهِمْ ۚ إِنَّمَا نُمْلِى لَهُمْ لِيَزْدَادُوٓا۟ إِثْمًۭا ۚ وَلَهُمْ عَذَابٌۭ مُّهِينٌۭ ﴿178﴾
Ndipo amene sadakhulupirire asaganize kuti nthawi yaitali imene tikuwapatsayi njabwino kwa iwo. Ndithudi, tikuwapatsa nthawiyi kuti aonjezere kuchita uchimo. Ndipo pa iwo padzakhala chilango chosambula.
مَّا كَانَ ٱللَّهُ لِيَذَرَ ٱلْمُؤْمِنِينَ عَلَىٰ مَآ أَنتُمْ عَلَيْهِ حَتَّىٰ يَمِيزَ ٱلْخَبِيثَ مِنَ ٱلطَّيِّبِ ۗ وَمَا كَانَ ٱللَّهُ لِيُطْلِعَكُمْ عَلَى ٱلْغَيْبِ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ يَجْتَبِى مِن رُّسُلِهِۦ مَن يَشَآءُ ۖ فَـَٔامِنُوا۟ بِٱللَّهِ وَرُسُلِهِۦ ۚ وَإِن تُؤْمِنُوا۟ وَتَتَّقُوا۟ فَلَكُمْ أَجْرٌ عَظِيمٌۭ ﴿179﴾
Nkosatheka kwa Allah kusiya okhulupirira momwe mulilimu, mpaka atalekanitsa (pakati pawo) oipa ndi abwino. Ndipo nkosatheka kwa Allah kukudziwitsani zinthu zamseri, koma Allah amasankha mwa atumiki ake amene wamfuna (nkumdziwitsa zina mwa zimenezo). Choncho khulupirirani Allah ndi atumiki ake. Ndipo ngati mukhulupirira ndi kuopa (Allah), pa inu padzakhala malipiro aakulu.[99]
وَلَا يَحْسَبَنَّ ٱلَّذِينَ يَبْخَلُونَ بِمَآ ءَاتَىٰهُمُ ٱللَّهُ مِن فَضْلِهِۦ هُوَ خَيْرًۭا لَّهُم ۖ بَلْ هُوَ شَرٌّۭ لَّهُمْ ۖ سَيُطَوَّقُونَ مَا بَخِلُوا۟ بِهِۦ يَوْمَ ٱلْقِيَٰمَةِ ۗ وَلِلَّهِ مِيرَٰثُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلْأَرْضِ ۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرٌۭ ﴿180﴾
Ndipo asaganize amene akuchitira umbombo zimene Allah wawapatsa kuchokera m’zabwino Zake kuti kutero ndibwino kwa iwo, koma kutero nkoipa kwa iwo. Adzanjatidwa magoli pa zomwe adazichitira umbombo pa tsiku lachimaliziro. Ndipo um’lowam’malo wa zakumwamba ndi pansi ngwa Allah. Ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita.[100]
لَّقَدْ سَمِعَ ٱللَّهُ قَوْلَ ٱلَّذِينَ قَالُوٓا۟ إِنَّ ٱللَّهَ فَقِيرٌۭ وَنَحْنُ أَغْنِيَآءُ ۘ سَنَكْتُبُ مَا قَالُوا۟ وَقَتْلَهُمُ ٱلْأَنۢبِيَآءَ بِغَيْرِ حَقٍّۢ وَنَقُولُ ذُوقُوا۟ عَذَابَ ٱلْحَرِيقِ ﴿181﴾
Ndithu Allah wamva liwu (lonyogodola) la omwe (Ayuda) anena kuti: “Allah ngosauka, ndipo ife ndife olemera.” Tazilemba zimene anena, ndipo (talembanso) kupha kwawo aneneri popanda choonadi. Ndipo tidzawauza (tsiku la chiweruziro): “Lawani chilango cha Moto owotcha.”[101]
ذَٰلِكَ بِمَا قَدَّمَتْ أَيْدِيكُمْ وَأَنَّ ٱللَّهَ لَيْسَ بِظَلَّامٍۢ لِّلْعَبِيدِ ﴿182﴾
“Izi nchifukwa cha zomwe manja anu adatsogoza. Ndithudi, Allah sali opondereza akapolo Ake.”[102]
ٱلَّذِينَ قَالُوٓا۟ إِنَّ ٱللَّهَ عَهِدَ إِلَيْنَآ أَلَّا نُؤْمِنَ لِرَسُولٍ حَتَّىٰ يَأْتِيَنَا بِقُرْبَانٍۢ تَأْكُلُهُ ٱلنَّارُ ۗ قُلْ قَدْ جَآءَكُمْ رُسُلٌۭ مِّن قَبْلِى بِٱلْبَيِّنَٰتِ وَبِٱلَّذِى قُلْتُمْ فَلِمَ قَتَلْتُمُوهُمْ إِن كُنتُمْ صَٰدِقِينَ ﴿183﴾
Amene anenanso: “Allah Adatilamula ife kuti tisakhulupirire mtumiki aliyense mpaka atabwera ndi nsembe yopserezedwa ndi moto.” Nena: “Adakudzerani atumiki ndisanadze ndi zisonyezo zooneka ndi chimene mukunenachi. Nanga bwanji mudawapha, ngati mukunenadi zoona?”[103]
فَإِن كَذَّبُوكَ فَقَدْ كُذِّبَ رُسُلٌۭ مِّن قَبْلِكَ جَآءُو بِٱلْبَيِّنَٰتِ وَٱلزُّبُرِ وَٱلْكِتَٰبِ ٱلْمُنِيرِ ﴿184﴾
Ndipo ngati akutsutsa iwe (Mtumiki Muhammad (s.a.w}, sichachilendo) adatsutsidwanso atumiki patsogolo pako omwe adadza ndi zisonyezo zoonekera ndi mabuku anzeru, ndi mabukunso ounika.
كُلُّ نَفْسٍۢ ذَآئِقَةُ ٱلْمَوْتِ ۗ وَإِنَّمَا تُوَفَّوْنَ أُجُورَكُمْ يَوْمَ ٱلْقِيَٰمَةِ ۖ فَمَن زُحْزِحَ عَنِ ٱلنَّارِ وَأُدْخِلَ ٱلْجَنَّةَ فَقَدْ فَازَ ۗ وَمَا ٱلْحَيَوٰةُ ٱلدُّنْيَآ إِلَّا مَتَٰعُ ٱلْغُرُورِ ﴿185﴾
Munthu aliyense adzalawa imfa. Ndithudi, mudzalipidwa malipiro anu mokwanira tsiku lachimaliziro. Ndipo amene adzatalikitsidwe ndi Moto nalowetsedwa ku Munda wamtendere, ndiye kuti wapambana, (kupambana kwakukulu), ndipo moyo wapadziko lapansi sulikanthu koma ndichisangalalo chonyenga basi.[104]
۞ لَتُبْلَوُنَّ فِىٓ أَمْوَٰلِكُمْ وَأَنفُسِكُمْ وَلَتَسْمَعُنَّ مِنَ ٱلَّذِينَ أُوتُوا۟ ٱلْكِتَٰبَ مِن قَبْلِكُمْ وَمِنَ ٱلَّذِينَ أَشْرَكُوٓا۟ أَذًۭى كَثِيرًۭا ۚ وَإِن تَصْبِرُوا۟ وَتَتَّقُوا۟ فَإِنَّ ذَٰلِكَ مِنْ عَزْمِ ٱلْأُمُورِ ﴿186﴾
Ndithu mudzayesedwa m’chuma chanu ndi miyoyo yanu; ndipo mudzamva masautso ambiri kuchokera kwa omwe adapatsidwa mabuku kale ndiponso kuchokera kwa omwe akuphatikiza Allah ndi zinthu zina (Arab), koma ngati mupirira ndi kudzisunga ku zomwe mwaletsedwa ndi Allah, (ndiye kuti mwachita chinthu chabwino kwambiri) pakuti zinthu izi (ndi zinthu zazikulu) zofunika munthu kuikirapo mtima.
وَإِذْ أَخَذَ ٱللَّهُ مِيثَٰقَ ٱلَّذِينَ أُوتُوا۟ ٱلْكِتَٰبَ لَتُبَيِّنُنَّهُۥ لِلنَّاسِ وَلَا تَكْتُمُونَهُۥ فَنَبَذُوهُ وَرَآءَ ظُهُورِهِمْ وَٱشْتَرَوْا۟ بِهِۦ ثَمَنًۭا قَلِيلًۭا ۖ فَبِئْسَ مَا يَشْتَرُونَ ﴿187﴾
Ndipo (akumbutse) pamene Allah adamanga chipangano ndi amene adapatsidwa buku (ndi kuwauza) kuti ndithudi mudzalifotokoze mwatsatanetsatane (bukulo) kwa anthu, ndipo musadzalibise. Koma Adaliponya kumbuyo kwa misana yawo naligulitsa ndi mtengo wochepa. Taonani kuipa chimene adagula (chimene adasankha)!
لَا تَحْسَبَنَّ ٱلَّذِينَ يَفْرَحُونَ بِمَآ أَتَوا۟ وَّيُحِبُّونَ أَن يُحْمَدُوا۟ بِمَا لَمْ يَفْعَلُوا۟ فَلَا تَحْسَبَنَّهُم بِمَفَازَةٍۢ مِّنَ ٱلْعَذَابِ ۖ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌۭ ﴿188﴾
Musaganize kuti amene akukondwera ndi zinthu (zoipa) zomwe achita nakonda kutamandidwa ndi zomwe sadachite, musawaganizire kuti akapulumuka. (Koma kuti) pa iwo padzakhala chilango chopweteka.
وَلِلَّهِ مُلْكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلْأَرْضِ ۗ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَىْءٍۢ قَدِيرٌ ﴿189﴾
Ndipo ufumu wa kumwamba ndi pansi ngwa Allah; ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.
إِنَّ فِى خَلْقِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلْأَرْضِ وَٱخْتِلَٰفِ ٱلَّيْلِ وَٱلنَّهَارِ لَءَايَٰتٍۢ لِّأُو۟لِى ٱلْأَلْبَٰبِ ﴿190﴾
Ndithudi, m’kulenga kwa kumwamba ndi dziko lapansi ndi kusinthana kwa usiku ndi usana, muli zisonyezo kwa eni nzeru,
ٱلَّذِينَ يَذْكُرُونَ ٱللَّهَ قِيَٰمًۭا وَقُعُودًۭا وَعَلَىٰ جُنُوبِهِمْ وَيَتَفَكَّرُونَ فِى خَلْقِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلْأَرْضِ رَبَّنَا مَا خَلَقْتَ هَٰذَا بَٰطِلًۭا سُبْحَٰنَكَ فَقِنَا عَذَابَ ٱلنَّارِ ﴿191﴾
Omwe amakumbukira Allah, ali chiimire, ali chikhalire, ndi ali chigonere chamnthiti mwawo; namalingalira kalengedwe ka thambo ndi nthaka (mmene Allah adazilengera, uku akuti): “E Mbuye wathu! simunalenge izi mwachabe. Ulemelero Ngwanu. Tichinjirizeni ku chilango cha Moto.”
رَبَّنَآ إِنَّكَ مَن تُدْخِلِ ٱلنَّارَ فَقَدْ أَخْزَيْتَهُۥ ۖ وَمَا لِلظَّٰلِمِينَ مِنْ أَنصَارٍۢ ﴿192﴾
“E Mbuye wathu! Ndithudi, yemwe mudzamulowetse ku Moto ndiye kuti mwamuyalutsa, ndipo sipadzakhala athandizi kwa ochita zoipa.”
رَّبَّنَآ إِنَّنَا سَمِعْنَا مُنَادِيًۭا يُنَادِى لِلْإِيمَٰنِ أَنْ ءَامِنُوا۟ بِرَبِّكُمْ فَـَٔامَنَّا ۚ رَبَّنَا فَٱغْفِرْ لَنَا ذُنُوبَنَا وَكَفِّرْ عَنَّا سَيِّـَٔاتِنَا وَتَوَفَّنَا مَعَ ٱلْأَبْرَارِ ﴿193﴾
“E Mbuye wathu! Ndithudi, ife tamva woitana akuitanira ku chikhulupiliro kuti: ‘Khulupirirani Mbuye wanu,’ ndipo takhulupirira. E Mbuye wathu! Tikhululukireni machimo athu ndi kutifafanizira zoipa zathu, ndipo mutenge mizimu yathu tili pamodzi ndi anthu abwino.”
رَبَّنَا وَءَاتِنَا مَا وَعَدتَّنَا عَلَىٰ رُسُلِكَ وَلَا تُخْزِنَا يَوْمَ ٱلْقِيَٰمَةِ ۗ إِنَّكَ لَا تُخْلِفُ ٱلْمِيعَادَ ﴿194﴾
“E, Mbuye wathu! Tipatseni zimene mudatilonjeza kupyolera mwa atumiki anu ndipo musadzatisambule tsiku lachimaliziro. Ndithudi, inu simuswa lonjezo.”
فَٱسْتَجَابَ لَهُمْ رَبُّهُمْ أَنِّى لَآ أُضِيعُ عَمَلَ عَٰمِلٍۢ مِّنكُم مِّن ذَكَرٍ أَوْ أُنثَىٰ ۖ بَعْضُكُم مِّنۢ بَعْضٍۢ ۖ فَٱلَّذِينَ هَاجَرُوا۟ وَأُخْرِجُوا۟ مِن دِيَٰرِهِمْ وَأُوذُوا۟ فِى سَبِيلِى وَقَٰتَلُوا۟ وَقُتِلُوا۟ لَأُكَفِّرَنَّ عَنْهُمْ سَيِّـَٔاتِهِمْ وَلَأُدْخِلَنَّهُمْ جَنَّٰتٍۢ تَجْرِى مِن تَحْتِهَا ٱلْأَنْهَٰرُ ثَوَابًۭا مِّنْ عِندِ ٱللَّهِ ۗ وَٱللَّهُ عِندَهُۥ حُسْنُ ٱلثَّوَابِ ﴿195﴾
Choncho Mbuye wawo adawavomereza (zopempha zawo ponena kuti): “Ndithudi, ine sindidzasokoneza (khama la) ntchito yabwino kwa ochita ntchito mwa inu, kaya atakhala mwamuna kapena mkazi, (pakuti) inu ndinu amodzi. Choncho amene asamuka (kumidzi yawo mwachifuniro chawo), naapirikitsidwa m’midzi yawo navutitsidwa pa njira Yanga, namenya nkhondo ndikuphedwa, ndithudi, ndiwafafanizira zolakwa zawo. Ndipo ndidzawalowetsa m’Minda yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) mitsinje ikuyenda. Amenewo ndimalipiro ochokera kwa Allah, ndipo kwa Allah kuli malipiro abwino.”
لَا يَغُرَّنَّكَ تَقَلُّبُ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ فِى ٱلْبِلَٰدِ ﴿196﴾
Ndithu kusakunyenge kuyendayenda pa dziko kwa amene sadakhulupirire.
مَتَٰعٌۭ قَلِيلٌۭ ثُمَّ مَأْوَىٰهُمْ جَهَنَّمُ ۚ وَبِئْسَ ٱلْمِهَادُ ﴿197﴾
Ndichisangalalo chochepa; kenako malo awo ndi kumoto wa Jahannam. Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!
لَٰكِنِ ٱلَّذِينَ ٱتَّقَوْا۟ رَبَّهُمْ لَهُمْ جَنَّٰتٌۭ تَجْرِى مِن تَحْتِهَا ٱلْأَنْهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَا نُزُلًۭا مِّنْ عِندِ ٱللَّهِ ۗ وَمَا عِندَ ٱللَّهِ خَيْرٌۭ لِّلْأَبْرَارِ ﴿198﴾
Koma amene aopa Mbuye wawo (potsatira zolamulidwa ndi kuleka zoletsedwa) adzapeza Minda yamtendere momwe mitsinje ikuyenda pansi (ndi patsogolo pake). Adzakhala m’menemo nthawi yaitali, ndi phwando lochokera kwa Allah. Ndipo zomwe zili kwa Allah nzabwino kwa anthu abwino (kuposa zosangalatsa za dziko lapansi).
وَإِنَّ مِنْ أَهْلِ ٱلْكِتَٰبِ لَمَن يُؤْمِنُ بِٱللَّهِ وَمَآ أُنزِلَ إِلَيْكُمْ وَمَآ أُنزِلَ إِلَيْهِمْ خَٰشِعِينَ لِلَّهِ لَا يَشْتَرُونَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ ثَمَنًۭا قَلِيلًا ۗ أُو۟لَٰٓئِكَ لَهُمْ أَجْرُهُمْ عِندَ رَبِّهِمْ ۗ إِنَّ ٱللَّهَ سَرِيعُ ٱلْحِسَابِ ﴿199﴾
Ndithudi mwa amene adapatsidwa buku, alipo amene akukhulupirira Allah ndi zimene zavumbulutsidwa kwa inu, ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa iwo, uku akudzichepetsa kwa Allah; sagulitsa ndime za Allah ndi mtengo wochepa (wa pa dziko lapansi). Iwo adzalandira malipiro awo kwa Mbuye wawo. Ndithudi, Allah Ngwachangu pakuwerengera.
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ ٱصْبِرُوا۟ وَصَابِرُوا۟ وَرَابِطُوا۟ وَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ لَعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ ﴿200﴾
E inu amene mwakhulupirira! Pirirani, ndipo agonjetseni adani anu ndikupirirako; ndipo tetezani malire anu ndipo muopeni Allah kuti mukhale opambana.