Main pages

Surah Luqman [Luqman] in Chewa

Surah Luqman [Luqman] Ayah 34 Location Makkah Number 31

الٓمٓ ﴿1﴾

Alif-Lâm-Mîm.[310]

تِلْكَ ءَايَٰتُ ٱلْكِتَٰبِ ٱلْحَكِيمِ ﴿2﴾

Izi ndi Ayah za buku lodzadza ndi nzeru.

هُدًۭى وَرَحْمَةًۭ لِّلْمُحْسِنِينَ ﴿3﴾

(Lomwe ndi) chiongoko ndi chifundo kwa ochita zabwino,

ٱلَّذِينَ يُقِيمُونَ ٱلصَّلَوٰةَ وَيُؤْتُونَ ٱلزَّكَوٰةَ وَهُم بِٱلْءَاخِرَةِ هُمْ يُوقِنُونَ ﴿4﴾

Amene akupemphera Swala moyenera ndi kupereka chopereka (Zakaat) omwenso akutsimikiza za tsiku lachimaliziro.

أُو۟لَٰٓئِكَ عَلَىٰ هُدًۭى مِّن رَّبِّهِمْ ۖ وَأُو۟لَٰٓئِكَ هُمُ ٱلْمُفْلِحُونَ ﴿5﴾

Iwowo ali pa chiongoko chochokera kwa Mbuye wawo; ndipo iwowo ndiwo opambana.

وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يَشْتَرِى لَهْوَ ٱلْحَدِيثِ لِيُضِلَّ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ بِغَيْرِ عِلْمٍۢ وَيَتَّخِذَهَا هُزُوًا ۚ أُو۟لَٰٓئِكَ لَهُمْ عَذَابٌۭ مُّهِينٌۭ ﴿6﴾

Koma alipo ena mwa anthu amene akusankha nkhani ya bodza (ndi kumaifotokoza kwa anthu) ndi cholinga choti awasokeretse ku njira ya Allah popanda kuzindikira. Ndipo akuichitira zachipongwe (njira ya Allah yi). Iwo adzapeza chilango chowasambula.

وَإِذَا تُتْلَىٰ عَلَيْهِ ءَايَٰتُنَا وَلَّىٰ مُسْتَكْبِرًۭا كَأَن لَّمْ يَسْمَعْهَا كَأَنَّ فِىٓ أُذُنَيْهِ وَقْرًۭا ۖ فَبَشِّرْهُ بِعَذَابٍ أَلِيمٍ ﴿7﴾

Ndipo pamene Ayah Zathu zilakatulidwa kwa iye, akuzitembenuzira msana modzikuza ngati kuti sanazimve, ngati kutinso m’makutu mwake muli ugonthi. Choncho muuze nkhani ya chilango chopweteka.

إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ وَعَمِلُوا۟ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُمْ جَنَّٰتُ ٱلنَّعِيمِ ﴿8﴾

Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzakhala ndi Minda yamtendere.

خَٰلِدِينَ فِيهَا ۖ وَعْدَ ٱللَّهِ حَقًّۭا ۚ وَهُوَ ٱلْعَزِيزُ ٱلْحَكِيمُ ﴿9﴾

Adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Ili nlonjezo la Allah lomwe lili loona. Ndipo Iye Ngwamphamvu, Ngwanzeru zakuya.

خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ بِغَيْرِ عَمَدٍۢ تَرَوْنَهَا ۖ وَأَلْقَىٰ فِى ٱلْأَرْضِ رَوَٰسِىَ أَن تَمِيدَ بِكُمْ وَبَثَّ فِيهَا مِن كُلِّ دَآبَّةٍۢ ۚ وَأَنزَلْنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءًۭ فَأَنۢبَتْنَا فِيهَا مِن كُلِّ زَوْجٍۢ كَرِيمٍ ﴿10﴾

Adalenga thambo popanda mizati yomwe mukuiona. Ndipo adaika mapiri m’nthaka kuti isakugwedezeni. Ndipo (Iye) adafalitsa nyama m’menemo zamitundu yosiyanasiyana. Ndipo tidatsitsa madzi kuchokera ku mitambo, choncho tidameretsa m’menemo (m’nthaka) mmera wokongola wamitundu yosiyanasiyana.[311]

هَٰذَا خَلْقُ ٱللَّهِ فَأَرُونِى مَاذَا خَلَقَ ٱلَّذِينَ مِن دُونِهِۦ ۚ بَلِ ٱلظَّٰلِمُونَ فِى ضَلَٰلٍۢ مُّبِينٍۢ ﴿11﴾

Izi (zonse) nzolengedwa za Allah. Choncho, tandisonyezani, nchiyani adalenga amene sali Allah. Koma odzichitira okha zoipa ali mkusokera koonekera.

وَلَقَدْ ءَاتَيْنَا لُقْمَٰنَ ٱلْحِكْمَةَ أَنِ ٱشْكُرْ لِلَّهِ ۚ وَمَن يَشْكُرْ فَإِنَّمَا يَشْكُرُ لِنَفْسِهِۦ ۖ وَمَن كَفَرَ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَنِىٌّ حَمِيدٌۭ ﴿12﴾

Ndipo ndithu tidampatsa Luqmân nzeru (ndipo tidati kwa iye): “Thokoza Allah (pazimene wakupatsa).” Ndipo, amene athokoze, ndithu kuthokozako kumthandiza yekha, ndiponso amene akana (mtendere wa Allah pakusiya kuthokoza), ndithu Allah Ngwachikwanekwane, Ngotamandidwa.

وَإِذْ قَالَ لُقْمَٰنُ لِٱبْنِهِۦ وَهُوَ يَعِظُهُۥ يَٰبُنَىَّ لَا تُشْرِكْ بِٱللَّهِ ۖ إِنَّ ٱلشِّرْكَ لَظُلْمٌ عَظِيمٌۭ ﴿13﴾

Ndipo (akumbutse) pamene Luqmân adauza mwana wake akumulangiza: “E iwe mwana wanga! Usaphatikize Allah ndi mafano. Ndithu kumuphatikiza (Allah), ndi kuipitsa kwakukulu.”

وَوَصَّيْنَا ٱلْإِنسَٰنَ بِوَٰلِدَيْهِ حَمَلَتْهُ أُمُّهُۥ وَهْنًا عَلَىٰ وَهْنٍۢ وَفِصَٰلُهُۥ فِى عَامَيْنِ أَنِ ٱشْكُرْ لِى وَلِوَٰلِدَيْكَ إِلَىَّ ٱلْمَصِيرُ ﴿14﴾

Ndipo tamulangiza munthu kwa makolo ake (kuwachitira zabwino), mayi wake adatenga pathupi pake mofooka pamwamba pakufooka. (Adamuyamwitsa) ndi kumusiyitsa patapita zaka ziwiri, kuti: “Ndithokoze Ine ndi makolo ako, kwa Ine nkobwerera.” [312]

وَإِن جَٰهَدَاكَ عَلَىٰٓ أَن تُشْرِكَ بِى مَا لَيْسَ لَكَ بِهِۦ عِلْمٌۭ فَلَا تُطِعْهُمَا ۖ وَصَاحِبْهُمَا فِى ٱلدُّنْيَا مَعْرُوفًۭا ۖ وَٱتَّبِعْ سَبِيلَ مَنْ أَنَابَ إِلَىَّ ۚ ثُمَّ إِلَىَّ مَرْجِعُكُمْ فَأُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ ﴿15﴾

Ndipo (makolo ako) ngati atakukakamiza kuti undiphatikize Ine ndi zomwe iwe sukuzidziwa, usawamvere; koma khala nawo pa dziko mwaubwino; ndipo tsatira njira ya amene atembenukira kwa Ine. Ndipo kenako kobwerera kwanu nkwa Ine. Choncho ndidzakuuzani zimene mudali kuchita.

يَٰبُنَىَّ إِنَّهَآ إِن تَكُ مِثْقَالَ حَبَّةٍۢ مِّنْ خَرْدَلٍۢ فَتَكُن فِى صَخْرَةٍ أَوْ فِى ٱلسَّمَٰوَٰتِ أَوْ فِى ٱلْأَرْضِ يَأْتِ بِهَا ٱللَّهُ ۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَطِيفٌ خَبِيرٌۭ ﴿16﴾

“E iwe mwana wanga! Ndithu icho (chabwino ndi choipa cha munthu) ngakhale chitakhala cholemera ngati njere ya mpiru ndi kukhala mkati mwa thanthwe kapena m’kati mwa thambo, kapena mkati mwa nthaka, Allah adzachibweretsa (ndi kumulipira amene adachita). Ndithu Allah Ngodziwa zinthu zobisika, (ndiponso) Ngodziwa zinthu zoonekera.”

يَٰبُنَىَّ أَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ وَأْمُرْ بِٱلْمَعْرُوفِ وَٱنْهَ عَنِ ٱلْمُنكَرِ وَٱصْبِرْ عَلَىٰ مَآ أَصَابَكَ ۖ إِنَّ ذَٰلِكَ مِنْ عَزْمِ ٱلْأُمُورِ ﴿17﴾

“E iwe mwana wanga! Pemphera Swala moyenera, lamula zabwino, letsa zoipa, ndipo pirira ndi masautso amene akukhudza. Ndithu zimenezo ndizinthu zofunika kuziikirapo mtima (munthu aliyense).”

وَلَا تُصَعِّرْ خَدَّكَ لِلنَّاسِ وَلَا تَمْشِ فِى ٱلْأَرْضِ مَرَحًا ۖ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُحِبُّ كُلَّ مُخْتَالٍۢ فَخُورٍۢ ﴿18﴾

“Ndipo usatembenuze tsaya lako kwa anthu monyogodola, ndipo usayende pa dziko monyada. Ndithu Allah sakonda yense wodzitukumula, wonyada.”

وَٱقْصِدْ فِى مَشْيِكَ وَٱغْضُضْ مِن صَوْتِكَ ۚ إِنَّ أَنكَرَ ٱلْأَصْوَٰتِ لَصَوْتُ ٱلْحَمِيرِ ﴿19﴾

“Ndipo lingana m’kuyenda kwako (popanda kufulumira kwambiri kapena kuyenda pang’onopang’ono); ndipo tsitsa mawu ako, ndithu mawu oyipitsitsa ndi mawu a bulu.”

أَلَمْ تَرَوْا۟ أَنَّ ٱللَّهَ سَخَّرَ لَكُم مَّا فِى ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِى ٱلْأَرْضِ وَأَسْبَغَ عَلَيْكُمْ نِعَمَهُۥ ظَٰهِرَةًۭ وَبَاطِنَةًۭ ۗ وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يُجَٰدِلُ فِى ٱللَّهِ بِغَيْرِ عِلْمٍۢ وَلَا هُدًۭى وَلَا كِتَٰبٍۢ مُّنِيرٍۢ ﴿20﴾

Kodi simuona kuti Allah adakugonjetserani zakumwamba ndi zapansi ndi kukukwaniritsirani chisomo Chake, choonekera ndi chobisika? Ndipo alipo ena mwa anthu amene akukangana pa za Allah popanda kuzindikira ngakhale chiongoko, ngakhalenso buku lounika.[313]

وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ٱتَّبِعُوا۟ مَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ قَالُوا۟ بَلْ نَتَّبِعُ مَا وَجَدْنَا عَلَيْهِ ءَابَآءَنَآ ۚ أَوَلَوْ كَانَ ٱلشَّيْطَٰنُ يَدْعُوهُمْ إِلَىٰ عَذَابِ ٱلسَّعِيرِ ﴿21﴾

Ndipo akauzidwa kuti: “Tsatani zimene Allah watsitsa.” Akunena: “Koma tikutsata zimene tidawapeza nazo makolo athu.” Kodi ngakhale kuti satana akuwaitanira ku chilango cha Moto (woyaka, adzatsatirabe)?

۞ وَمَن يُسْلِمْ وَجْهَهُۥٓ إِلَى ٱللَّهِ وَهُوَ مُحْسِنٌۭ فَقَدِ ٱسْتَمْسَكَ بِٱلْعُرْوَةِ ٱلْوُثْقَىٰ ۗ وَإِلَى ٱللَّهِ عَٰقِبَةُ ٱلْأُمُورِ ﴿22﴾

Ndipo amene akupereka nkhope yake kwa Allah (amene akugonjera Allah kwatunthu) ali ochita zabwino, ndiye kuti wagwira chogwilira cholimba. Ndipo mapeto a zinthu zonse nkwa Allah basi.

وَمَن كَفَرَ فَلَا يَحْزُنكَ كُفْرُهُۥٓ ۚ إِلَيْنَا مَرْجِعُهُمْ فَنُنَبِّئُهُم بِمَا عَمِلُوٓا۟ ۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمٌۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ ﴿23﴾

Koma amene sadakhulupirire (Allah ndi mtima wake) choncho kusakudandaulitse kusakhulupirira kwake. Kobwerera kwawo nkwa Ife basi. Kumeneko tidzawauza zimene adachita. Ndithu Allah Ngodziwa zonse zam’zifuwa.

نُمَتِّعُهُمْ قَلِيلًۭا ثُمَّ نَضْطَرُّهُمْ إِلَىٰ عَذَابٍ غَلِيظٍۢ ﴿24﴾

Tikuwasangalatsa pang’ono (apo pa dziko lapansi). Kenako tidzawakankhira ku chilango chokhwima.

وَلَئِن سَأَلْتَهُم مَّنْ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلْأَرْضَ لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُ ۚ قُلِ ٱلْحَمْدُ لِلَّهِ ۚ بَلْ أَكْثَرُهُمْ لَا يَعْلَمُونَ ﴿25﴾

Ndipo ukawafunsa: “Ndani adalenga thambo ndi nthaka?” Ndithu anena: “Ndi Allah.” Nena: “Kutamandidwa konse nkwa Allah.” Koma ambiri a iwo sadziwa.

لِلَّهِ مَا فِى ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلْأَرْضِ ۚ إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلْغَنِىُّ ٱلْحَمِيدُ ﴿26﴾

Zonse zakumwamba ndi za pansi, nza Allah. Ndithu Allah Ngwachikwanekwane, Ngotamandidwa.

وَلَوْ أَنَّمَا فِى ٱلْأَرْضِ مِن شَجَرَةٍ أَقْلَٰمٌۭ وَٱلْبَحْرُ يَمُدُّهُۥ مِنۢ بَعْدِهِۦ سَبْعَةُ أَبْحُرٍۢ مَّا نَفِدَتْ كَلِمَٰتُ ٱللَّهِ ۗ إِنَّ ٱللَّهَ عَزِيزٌ حَكِيمٌۭ ﴿27﴾

Ndipo ndithu ngakhale mitengo yonse ili m’nthaka ikadakhala zolembera, ndipo nyanja (nkukhala inki), ndipo pambuyo pake ndikuionjezeranso (madzi ake) ndi nyanja zisanu ndi ziwiri, mawu a Allah sakadatha. Ndithu Allah Ngwamphamvu, Wanzeru zakuya.[314]

مَّا خَلْقُكُمْ وَلَا بَعْثُكُمْ إِلَّا كَنَفْسٍۢ وَٰحِدَةٍ ۗ إِنَّ ٱللَّهَ سَمِيعٌۢ بَصِيرٌ ﴿28﴾

Kulengedwa kwanu, ngakhale kuukitsidwa kwanu m’manda sikuli kanthu koma kuli ngati (kulenga kapena kuukitsa kwa) munthu mmodzi. (Palibe chokanika kwa Allah). Ndithu Allah Ngwakumva, Ngopenya chilichonse.

أَلَمْ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ يُولِجُ ٱلَّيْلَ فِى ٱلنَّهَارِ وَيُولِجُ ٱلنَّهَارَ فِى ٱلَّيْلِ وَسَخَّرَ ٱلشَّمْسَ وَٱلْقَمَرَ كُلٌّۭ يَجْرِىٓ إِلَىٰٓ أَجَلٍۢ مُّسَمًّۭى وَأَنَّ ٱللَّهَ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرٌۭ ﴿29﴾

Kodi suona (kuona kolingalira) kuti Allah amalowetsa nthawi ya usiku mu usana, ndipo amalowetsa nthawi ya usana mu usiku; ndipo adagonjetsa dzuwa ndi mwezi. Chilichonse chikuyenda mwa nthawi imene idaikidwa? Ndithu Allah akudziwa zonse zimene mukuchita.

ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلْحَقُّ وَأَنَّ مَا يَدْعُونَ مِن دُونِهِ ٱلْبَٰطِلُ وَأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلْعَلِىُّ ٱلْكَبِيرُ ﴿30﴾

Izi nchifukwa chakuti Allah, Iye Ngoona; ndipo zomwe akuzipembedza kusiya Iye, nzachabe. Ndipo ndithu Allah ndiye Wotukuka, Wamkulu.

أَلَمْ تَرَ أَنَّ ٱلْفُلْكَ تَجْرِى فِى ٱلْبَحْرِ بِنِعْمَتِ ٱللَّهِ لِيُرِيَكُم مِّنْ ءَايَٰتِهِۦٓ ۚ إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَءَايَٰتٍۢ لِّكُلِّ صَبَّارٍۢ شَكُورٍۢ ﴿31﴾

Kodi suona kuti zombo zikuyenda pa nyanja mwachisomo cha Allah kuti akusonyezeni zisonyezo Zake (zamtendere Wake)? Ndithu M’zimenezo muli zisonyezo kwa yense wopirira, wothokoza.

وَإِذَا غَشِيَهُم مَّوْجٌۭ كَٱلظُّلَلِ دَعَوُا۟ ٱللَّهَ مُخْلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ فَلَمَّا نَجَّىٰهُمْ إِلَى ٱلْبَرِّ فَمِنْهُم مُّقْتَصِدٌۭ ۚ وَمَا يَجْحَدُ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَّا كُلُّ خَتَّارٍۢ كَفُورٍۢ ﴿32﴾

Ndipo mafunde onga mitambo akawavindikira, amampempha Allah modzipereka kwambiri. Koma akawapulumutsira ku ntunda, ena a iwo amachita zolungama (koma ena a iwo amakana mtendere wa Allah). Ndipo sangazikane zisonyezo zathu koma yense wachinyengo wosathokoza.

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ ٱتَّقُوا۟ رَبَّكُمْ وَٱخْشَوْا۟ يَوْمًۭا لَّا يَجْزِى وَالِدٌ عَن وَلَدِهِۦ وَلَا مَوْلُودٌ هُوَ جَازٍ عَن وَالِدِهِۦ شَيْـًٔا ۚ إِنَّ وَعْدَ ٱللَّهِ حَقٌّۭ ۖ فَلَا تَغُرَّنَّكُمُ ٱلْحَيَوٰةُ ٱلدُّنْيَا وَلَا يَغُرَّنَّكُم بِٱللَّهِ ٱلْغَرُورُ ﴿33﴾

E inu anthu! Muopeni Mbuye wanu (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa); ndipo liopeni tsiku limene kholo silidzathandiza mwana wake, ngakhalenso mwana sadzathandiza kholo lake chilichonse. Ndithu lonjezo la Allah ndiloona; choncho usakunyengeni moyo wa dziko lapansi, ndiponso asakunyengeni mdyerekezi pa za Allah.

إِنَّ ٱللَّهَ عِندَهُۥ عِلْمُ ٱلسَّاعَةِ وَيُنَزِّلُ ٱلْغَيْثَ وَيَعْلَمُ مَا فِى ٱلْأَرْحَامِ ۖ وَمَا تَدْرِى نَفْسٌۭ مَّاذَا تَكْسِبُ غَدًۭا ۖ وَمَا تَدْرِى نَفْسٌۢ بِأَىِّ أَرْضٍۢ تَمُوتُ ۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمٌ خَبِيرٌۢ ﴿34﴾

Ndithu kudziwa kwa nthawi (yakutha kwa dziko) kuli ndi Allah (Yekha). Iye ndiamene amavumbitsa mvula (nthawi imene wafuna); ndipo akudziwa zimene zili m’ziberekero. Ndipo aliyense sadziwa chomwe apeze mawa; (chabwino kapena choipa); ndiponso sadziwa aliyense kuti ndi dziko liti adzafera. Ndithu Allah Ngodziwa zedi, Ngozindikira kwambiri.