Main pages

Surah The congregation, Friday [Al-Jumua] in Chewa

Surah The congregation, Friday [Al-Jumua] Ayah 11 Location Madinah Number 62

يُسَبِّحُ لِلَّهِ مَا فِى ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِى ٱلْأَرْضِ ٱلْمَلِكِ ٱلْقُدُّوسِ ٱلْعَزِيزِ ٱلْحَكِيمِ ﴿1﴾

Zonse zakumwamba ndi dziko lapansi zikulemekeza Allah; Mfumu, Woyera, Wamphamvu zopambana ndi nzeru zakuya (ndi kumyeretsa ku makhalidwe osayenerana ndi ulemelero Wake).

هُوَ ٱلَّذِى بَعَثَ فِى ٱلْأُمِّيِّۦنَ رَسُولًۭا مِّنْهُمْ يَتْلُوا۟ عَلَيْهِمْ ءَايَٰتِهِۦ وَيُزَكِّيهِمْ وَيُعَلِّمُهُمُ ٱلْكِتَٰبَ وَٱلْحِكْمَةَ وَإِن كَانُوا۟ مِن قَبْلُ لَفِى ضَلَٰلٍۢ مُّبِينٍۢ ﴿2﴾

Iye ndiAmene adatumiza kwa Ummiyyina (osadziwa kulemba ndi kuwerenga), Mtumiki wochokera mwa iwo kuti awawerengere ndime Zake ndi kuti awayeretse (ku uchimo ndi kumakhalidwe oipa) ndi kuwaphunzitsa Qur’an ndi mawu anzeru (a mtumiki) ndithu kale adali osokera kowonekera (Mtumiki {s.a.w} asadadze kwa iwo).[361]

وَءَاخَرِينَ مِنْهُمْ لَمَّا يَلْحَقُوا۟ بِهِمْ ۚ وَهُوَ ٱلْعَزِيزُ ٱلْحَكِيمُ ﴿3﴾

Ndipo (adamtumizanso) kwa ena mwa iwo, omwe sadakumane nawo, ndipo Iye (Allah) Ngopambana (pa chinthu chilichonse ndi Wamphamvu zoposa ndiponso) Ngwanzeru zakuya.

ذَٰلِكَ فَضْلُ ٱللَّهِ يُؤْتِيهِ مَن يَشَآءُ ۚ وَٱللَّهُ ذُو ٱلْفَضْلِ ٱلْعَظِيمِ ﴿4﴾

Umenewo ndiwo ubwino wa Allah akuupereka kwa amene wamfuna (mwa akapolo Ake); ndipo Allah yekha ndi Mwini ubwino waukulu.

مَثَلُ ٱلَّذِينَ حُمِّلُوا۟ ٱلتَّوْرَىٰةَ ثُمَّ لَمْ يَحْمِلُوهَا كَمَثَلِ ٱلْحِمَارِ يَحْمِلُ أَسْفَارًۢا ۚ بِئْسَ مَثَلُ ٱلْقَوْمِ ٱلَّذِينَ كَذَّبُوا۟ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ ۚ وَٱللَّهُ لَا يَهْدِى ٱلْقَوْمَ ٱلظَّٰلِمِينَ ﴿5﴾

Fanizo la (Ayuda) amene adawasenzetsa Taurat (pokakamizidwa kuti atsatire zophunzitsa za bukulo, koma osatsatira), ali ngati bulu amene akusenza mabuku akuluakulu anzeru, (koma osathandizika nawo). Taonani kuipa fanizo la anthu amene atsutsa zisonyezo za Allah. Ndipo Allah saongola anthu achinyengo.[362]

قُلْ يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ هَادُوٓا۟ إِن زَعَمْتُمْ أَنَّكُمْ أَوْلِيَآءُ لِلَّهِ مِن دُونِ ٱلنَّاسِ فَتَمَنَّوُا۟ ٱلْمَوْتَ إِن كُنتُمْ صَٰدِقِينَ ﴿6﴾

Nena: “E inu Ayuda! Ngati mwadziganizira kuti ndithu ndinu okondedwa a Allah kuposa (mitundu ina ya) anthu, ilakelakeni imfa (kuti mukalowe ku mtendere wa Allah) ngati mukunena zoona.

وَلَا يَتَمَنَّوْنَهُۥٓ أَبَدًۢا بِمَا قَدَّمَتْ أَيْدِيهِمْ ۚ وَٱللَّهُ عَلِيمٌۢ بِٱلظَّٰلِمِينَ ﴿7﴾

Ndipo sangailakelake mpang’ono pomwe chifukwa cha (zoipa) zimene manja awo atsogoza! Ndipo Allah akudziwa bwino za (anthu) osalungama.

قُلْ إِنَّ ٱلْمَوْتَ ٱلَّذِى تَفِرُّونَ مِنْهُ فَإِنَّهُۥ مُلَٰقِيكُمْ ۖ ثُمَّ تُرَدُّونَ إِلَىٰ عَٰلِمِ ٱلْغَيْبِ وَٱلشَّهَٰدَةِ فَيُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ ﴿8﴾

Nena (kuti): “Ndithu imfa imene mukuithawa (palibe chipeneko) ikumana nanu; kenako muzabwezedwa kwa wodziwa zobisika ndi zooneka; ndipo adzakuuzani zimene mudali kuchita.

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓا۟ إِذَا نُودِىَ لِلصَّلَوٰةِ مِن يَوْمِ ٱلْجُمُعَةِ فَٱسْعَوْا۟ إِلَىٰ ذِكْرِ ٱللَّهِ وَذَرُوا۟ ٱلْبَيْعَ ۚ ذَٰلِكُمْ خَيْرٌۭ لَّكُمْ إِن كُنتُمْ تَعْلَمُونَ ﴿9﴾

E inu amene mwakhulupirira! Kukaitanidwa ku Swala (pemphero la Ijuma) tsiku la Ijuma, pitani mwachangu kukamtamanda Allah. Ndipo siyani malonda; zimenezo (mwalamulidwazo) nzabwino kwa inu ngati mukudziwa.[363]

فَإِذَا قُضِيَتِ ٱلصَّلَوٰةُ فَٱنتَشِرُوا۟ فِى ٱلْأَرْضِ وَٱبْتَغُوا۟ مِن فَضْلِ ٱللَّهِ وَٱذْكُرُوا۟ ٱللَّهَ كَثِيرًۭا لَّعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ ﴿10﴾

Choncho Swala (ya Ijumayo) ikatha, balalikanani pa dziko, ndipo funani ubwino wa Allah; ndipo mtamandeni Allah kwambiri kuti mupambane (pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro).

وَإِذَا رَأَوْا۟ تِجَٰرَةً أَوْ لَهْوًا ٱنفَضُّوٓا۟ إِلَيْهَا وَتَرَكُوكَ قَآئِمًۭا ۚ قُلْ مَا عِندَ ٱللَّهِ خَيْرٌۭ مِّنَ ٱللَّهْوِ وَمِنَ ٱلتِّجَٰرَةِ ۚ وَٱللَّهُ خَيْرُ ٱلرَّٰزِقِينَ ﴿11﴾

Ndipo akaona malonda kapena masewero, akubalalika kunka ku zimenezo ndi kukusiya uli chiimire (ukuchita khutuba ndi anthu ochepa). Nena (kwa iwo): “Zimene zili kwa Allah nzabwino kwa inu kuposa masewero ndi malonda. Ndipo Allah Ngwabwino kwambiri kuposa opatsa onse.”