Settings
Surah The Hypocrites [Al-Munafiqoon] in Chewa
إِذَا جَاۤءَكَ ٱلۡمُنَـٰفِقُونَ قَالُوا۟ نَشۡهَدُ إِنَّكَ لَرَسُولُ ٱللَّهِۗ وَٱللَّهُ یَعۡلَمُ إِنَّكَ لَرَسُولُهُۥ وَٱللَّهُ یَشۡهَدُ إِنَّ ٱلۡمُنَـٰفِقِینَ لَكَـٰذِبُونَ ﴿1﴾
Akakudzera achiphamaso akunena kuti: “Tikuikira umboni kuti ndithu iwe ndiwe Mtumiki wa Allah, ndipo Allah akudziwa kuti iwe ndiwe mtumiki Wake. Ndipo Allah akuikira umboni kuti achiphamaso ngabodza (pa zomwe akunena).
ٱتَّخَذُوۤا۟ أَیۡمَـٰنَهُمۡ جُنَّةࣰ فَصَدُّوا۟ عَن سَبِیلِ ٱللَّهِۚ إِنَّهُمۡ سَاۤءَ مَا كَانُوا۟ یَعۡمَلُونَ ﴿2﴾
Kulumbira kwawo (kwa bodza) akuchita kukhala chotetezera (chuma chawo ndi matupi awo). Tero atsekereza (anthu kuyenda) panjira ya Allah. Ndithu nzoipa zedi zimene amachita.
ذَ ٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ ءَامَنُوا۟ ثُمَّ كَفَرُوا۟ فَطُبِعَ عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ فَهُمۡ لَا یَفۡقَهُونَ ﴿3﴾
Zimenezo nchifukwa chakuti iwo adakhulupirira (modzionetsera), kenako adakana (mobisa). Choncho mitima yawo idatsekedwa kotero kuti iwo sangathe kuzindikira (chimene chingawapulumutse ku chilango cha Allah.)
۞ وَإِذَا رَأَیۡتَهُمۡ تُعۡجِبُكَ أَجۡسَامُهُمۡۖ وَإِن یَقُولُوا۟ تَسۡمَعۡ لِقَوۡلِهِمۡۖ كَأَنَّهُمۡ خُشُبࣱ مُّسَنَّدَةࣱۖ یَحۡسَبُونَ كُلَّ صَیۡحَةٍ عَلَیۡهِمۡۚ هُمُ ٱلۡعَدُوُّ فَٱحۡذَرۡهُمۡۚ قَـٰتَلَهُمُ ٱللَّهُۖ أَنَّىٰ یُؤۡفَكُونَ ﴿4﴾
Ndipo ukawaona, akukondweretsa matupi awo; ndipo akayankhula umvetsera zoyankhula zawo (chifukwa chakuthwa kwa malirime awo, pomwe mkati mwawo ndiming’oma yopanda kanthu); iwo ali ngati matsinde a mitengo yomwe yayadzamiritsidwa (ku chipupa); (mwa iwo mulibe moyo). Mkuwe uliwonse (umene akuumva) akuganiza kuti ukulinga iwo, (chifukwa cha kuzindikira chinyengo chawo); iwowa ndiadani; chenjerani nawo. Allah awatembelere! Mwanjira yanji akuchotsedwa (ku choonadi)!
وَإِذَا قِیلَ لَهُمۡ تَعَالَوۡا۟ یَسۡتَغۡفِرۡ لَكُمۡ رَسُولُ ٱللَّهِ لَوَّوۡا۟ رُءُوسَهُمۡ وَرَأَیۡتَهُمۡ یَصُدُّونَ وَهُم مُّسۡتَكۡبِرُونَ ﴿5﴾
Kukanenedwa kwa iwo kuti: “Bwerani, akupemphereni chikhululuko mthenga wa Allah, akutembenuza mitu yawo (monyoza ndi modzitukumula), ndipo uwaona akunyoza uku akudzikweza (osatsatira langizo).”
سَوَاۤءٌ عَلَیۡهِمۡ أَسۡتَغۡفَرۡتَ لَهُمۡ أَمۡ لَمۡ تَسۡتَغۡفِرۡ لَهُمۡ لَن یَغۡفِرَ ٱللَّهُ لَهُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا یَهۡدِی ٱلۡقَوۡمَ ٱلۡفَـٰسِقِینَ ﴿6﴾
Kwa iwowa nchimodzimodzi kuwapemphera kwako chikhululuko, kapena kusawapemphera. Allah sangawakhululukire (chifukwa cha kuzama kwawo m’kusakhulupirira). Ndithu Allah saongola anthu otuluka m’chilamulo (Chake).
هُمُ ٱلَّذِینَ یَقُولُونَ لَا تُنفِقُوا۟ عَلَىٰ مَنۡ عِندَ رَسُولِ ٱللَّهِ حَتَّىٰ یَنفَضُّوا۟ۗ وَلِلَّهِ خَزَاۤىِٕنُ ٱلسَّمَـٰوَ ٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَلَـٰكِنَّ ٱلۡمُنَـٰفِقِینَ لَا یَفۡقَهُونَ ﴿7﴾
Amenewa ndiwo omwe akunena kwa Answari; (Asilamu aku Madina, kuti): “Musawapatse chuma (chanu) amene ali ndi Mtumiki wa Allah kuti abalalikane.” Pomwe nkhokwe zonse (zachuma) za kumwamba ndi dziko lapansi zili m’manja mwa Allah (ndipo amachipereka kwa amene wamfuna); koma achiphamaso sakuzindikira (zimenezo).[364]
یَقُولُونَ لَىِٕن رَّجَعۡنَاۤ إِلَى ٱلۡمَدِینَةِ لَیُخۡرِجَنَّ ٱلۡأَعَزُّ مِنۡهَا ٱلۡأَذَلَّۚ وَلِلَّهِ ٱلۡعِزَّةُ وَلِرَسُولِهِۦ وَلِلۡمُؤۡمِنِینَ وَلَـٰكِنَّ ٱلۡمُنَـٰفِقِینَ لَا یَعۡلَمُونَ ﴿8﴾
Akunena kuti: “Ngati tibwerera ku Madina wolemekezeka adzatulutsa wonyozeka m’menemo. “Pomwe ulemelero ngwa Allah ndi Mthenga Wake ndi okhulupirira; koma achinyengo sakudziwa (zimenezo).”
یَـٰۤأَیُّهَا ٱلَّذِینَ ءَامَنُوا۟ لَا تُلۡهِكُمۡ أَمۡوَ ٰلُكُمۡ وَلَاۤ أَوۡلَـٰدُكُمۡ عَن ذِكۡرِ ٱللَّهِۚ وَمَن یَفۡعَلۡ ذَ ٰلِكَ فَأُو۟لَـٰۤىِٕكَ هُمُ ٱلۡخَـٰسِرُونَ ﴿9﴾
E inu amene mwakhulupirira! Chuma chanu ngakhalenso ana anu zisakutangwanitseni ndi kusiya kukumbukira Allah (ndi kukwaniritsa zimene wakulamulani). Ndipo amene achite zimenezo iwo ndi otaika.
وَأَنفِقُوا۟ مِن مَّا رَزَقۡنَـٰكُم مِّن قَبۡلِ أَن یَأۡتِیَ أَحَدَكُمُ ٱلۡمَوۡتُ فَیَقُولَ رَبِّ لَوۡلَاۤ أَخَّرۡتَنِیۤ إِلَىٰۤ أَجَلࣲ قَرِیبࣲ فَأَصَّدَّقَ وَأَكُن مِّنَ ٱلصَّـٰلِحِینَ ﴿10﴾
Perekani (mwachangu pa njira ya Allah) zina mwa zomwe takupatsani, isanamfikire mmodzi wa inu imfa (mwadzidzidzi) ndi kuyamba kunena (modandaula): “Mbuye wanga! Bwanji osandichedwetsa nthawi pang’ono kuti ndipereke sadaka (ndi kuti ndikonze zina zimene sindinazikwaniritse) ndi kutinso ndikhale mwa anthu anu abwino.”
وَلَن یُؤَخِّرَ ٱللَّهُ نَفۡسًا إِذَا جَاۤءَ أَجَلُهَاۚ وَٱللَّهُ خَبِیرُۢ بِمَا تَعۡمَلُونَ ﴿11﴾
Ndipo Allah sangauchedwetse mzimu (ngakhale ndi mphindi imodzi) ukaidzera nthawi yake ya imfa; ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene mukuchita, (ndipo adzakulipirani pa zimenezo).