Main pages

Surah Those who drag forth [An-Naziat] in Chewa

Surah Those who drag forth [An-Naziat] Ayah 46 Location Makkah Number 79

وَٱلنَّٰزِعَٰتِ غَرْقًۭا ﴿1﴾

Ndikulumbilira (angelo) amene amazula mwamphamvu (mizimu ya osakhulupirira).[379]

وَٱلنَّٰشِطَٰتِ نَشْطًۭا ﴿2﴾

Ndikulumbiliranso (angelo) amene amachotsa moleza (mizimu ya okhulupirira).

وَٱلسَّٰبِحَٰتِ سَبْحًۭا ﴿3﴾

Ndi omwe amasambira (nayo mizimuyo) mu mlengalenga (ponka nayo ku malo ake oyembekezera).

فَٱلسَّٰبِقَٰتِ سَبْقًۭا ﴿4﴾

Ndi iwo amene akupikisana pokwaniritsa malamulo a Allah.

فَٱلْمُدَبِّرَٰتِ أَمْرًۭا ﴿5﴾

Ndi iwo (angelo) amene akulongosola malamulo (Ake). (Ndithudi inu anthu mudzauka kwa akufa).

يَوْمَ تَرْجُفُ ٱلرَّاجِفَةُ ﴿6﴾

Patsiku lomwe (lipenga loyamba lidzaimbidwa), dziko lapansi ndi mapiri ake zidzagwedezeka (ndipo aliyense adzafa).

تَتْبَعُهَا ٱلرَّادِفَةُ ﴿7﴾

Ndipo kudzatsatira kuyimba kwa lipenga lachiwiri (kumene kudzaukitsa akufa onse).

قُلُوبٌۭ يَوْمَئِذٍۢ وَاجِفَةٌ ﴿8﴾

Tsiku limenelo mitima idzanjenjemera ndi kuopa.

أَبْصَٰرُهَا خَٰشِعَةٌۭ ﴿9﴾

Maso a eni mitimayo adzakhala ozyolika (chifukwa chamadandaulo);

يَقُولُونَ أَءِنَّا لَمَرْدُودُونَ فِى ٱلْحَافِرَةِ ﴿10﴾

(Osakhulupirira) akunena: “Kodi nzoona tidzabwezedwa pambuyo pa imfa monga tidalili kale?”

أَءِذَا كُنَّا عِظَٰمًۭا نَّخِرَةًۭ ﴿11﴾

“Pomwe ife titakhala mafupa ofumbwa (tingabwezedwe ndi kuukitsidwa mwa tsopano)?”

قَالُوا۟ تِلْكَ إِذًۭا كَرَّةٌ خَاسِرَةٌۭ ﴿12﴾

Adanena (mokanira ndi mwachipongwe): “Choncho kubwerera kumeneko ngati kudzakhalepodi kudzakhala kotaika (ndi kopanda phindu kwa ife. Pomwe ife sindife oyenera kutaika).”

فَإِنَّمَا هِىَ زَجْرَةٌۭ وَٰحِدَةٌۭ ﴿13﴾

(Musaganize kubwererako nchinthu chovuta). Ndithundithu Kiyamayo ndi nkuwo umodzi.

فَإِذَا هُم بِٱلسَّاهِرَةِ ﴿14﴾

Mwadzidzidzi (zolengedwa zonse) zidzangoona zili pa dziko latsopano (zili zamoyo).

هَلْ أَتَىٰكَ حَدِيثُ مُوسَىٰٓ ﴿15﴾

Kodi yakufika (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Mûsa?[380]

إِذْ نَادَىٰهُ رَبُّهُۥ بِٱلْوَادِ ٱلْمُقَدَّسِ طُوًى ﴿16﴾

Pamene Mbuye wake adamuitana pa chigwa choyera (chotchedwa) Tuwaa.

ٱذْهَبْ إِلَىٰ فِرْعَوْنَ إِنَّهُۥ طَغَىٰ ﴿17﴾

(Adamuuza kuti) pita kwa Farawo ndithu iye wapyola malire, (mkudzitukumula kwake ndikupondereza anthu).

فَقُلْ هَل لَّكَ إِلَىٰٓ أَن تَزَكَّىٰ ﴿18﴾

Choncho ukamuuze kuti: “Kodi ukufuna kudziyeretsa?”

وَأَهْدِيَكَ إِلَىٰ رَبِّكَ فَتَخْشَىٰ ﴿19﴾

“Ndikuti ndikuongolere kwa Mbuye wako kuti uzimuopa?”

فَأَرَىٰهُ ٱلْءَايَةَ ٱلْكُبْرَىٰ ﴿20﴾

(Basi Mûsa) adamuonetsa (Farawo) chozizwitsa chachikulu.

فَكَذَّبَ وَعَصَىٰ ﴿21﴾

Koma (Farawo) adatsutsa (Mûsa pazimene adadza nazo zija) ndi kunyoza.

ثُمَّ أَدْبَرَ يَسْعَىٰ ﴿22﴾

Kenaka adabwerera uku akulimbika kutsutsana naye (Allah),

فَحَشَرَ فَنَادَىٰ ﴿23﴾

Adawasonkhanitsa (afiti) uku akuitana anthu;

فَقَالَ أَنَا۠ رَبُّكُمُ ٱلْأَعْلَىٰ ﴿24﴾

Nanena: “Ine ndine mbuye wanu wapamwambamwamba!”

فَأَخَذَهُ ٱللَّهُ نَكَالَ ٱلْءَاخِرَةِ وَٱلْأُولَىٰٓ ﴿25﴾

Pamenepo Allah adamulanga chifukwa cha mawu ake omaliza ndi oyamba.

إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَعِبْرَةًۭ لِّمَن يَخْشَىٰٓ ﴿26﴾

Ndithu pa zimenezi pali phunziro (lalikulu) kwa yemwe akuopa Allah.

ءَأَنتُمْ أَشَدُّ خَلْقًا أَمِ ٱلسَّمَآءُ ۚ بَنَىٰهَا ﴿27﴾

Kodi kulengedwa kwanu, (inu osakhulupirira kuti muuke) nkovuta kapena thambo limene adalimanga (posonkhanitsa mbali zake zosiyanasiyana ndikukhala chinthu chimodzi)?[381]

رَفَعَ سَمْكَهَا فَسَوَّىٰهَا ﴿28﴾

Adatukula nsinkhu wake ndikulikonza bwino (popanda pena pong’ambika kapena posiyana ndi pena).

وَأَغْطَشَ لَيْلَهَا وَأَخْرَجَ ضُحَىٰهَا ﴿29﴾

Ndipo amauvindikira usiku wake ndi mdima ndipo amatulutsa kuwala wake.

وَٱلْأَرْضَ بَعْدَ ذَٰلِكَ دَحَىٰهَآ ﴿30﴾

Ndipo pambuyo pazimenezo, nthaka adaiyala (kuti ikhale yoyenera kuikhala).

أَخْرَجَ مِنْهَا مَآءَهَا وَمَرْعَىٰهَا ﴿31﴾

Adatulutsa m’menemo madzi ake (potulutsa akasupe) ndikumeretsa msipu wake;

وَٱلْجِبَالَ أَرْسَىٰهَا ﴿32﴾

Ndipo mapiri adawakhazikitsa (ndikuwalimbika);

مَتَٰعًۭا لَّكُمْ وَلِأَنْعَٰمِكُمْ ﴿33﴾

(Adachita zonsezi) chifukwa chokusangalatsani inu ndi ziweto zanu.[382]

فَإِذَا جَآءَتِ ٱلطَّآمَّةُ ٱلْكُبْرَىٰ ﴿34﴾

Choncho likadzafika tsoka lalikulu (tsiku la Qiyâma).

يَوْمَ يَتَذَكَّرُ ٱلْإِنسَٰنُ مَا سَعَىٰ ﴿35﴾

Tsiku limenelo munthu adzakumbukira zimene adachita, (zabwino ndi zoipa).

وَبُرِّزَتِ ٱلْجَحِيمُ لِمَن يَرَىٰ ﴿36﴾

Ndipo Moto waukali udzawonetsedwa kwa yense openya.

فَأَمَّا مَن طَغَىٰ ﴿37﴾

Tsono amene adapyola malire (pochita machimo),

وَءَاثَرَ ٱلْحَيَوٰةَ ٱلدُّنْيَا ﴿38﴾

Ndikudzisankhira (yekha) moyo wa pa dziko lapansi,

فَإِنَّ ٱلْجَحِيمَ هِىَ ٱلْمَأْوَىٰ ﴿39﴾

Ndithu Jahannam ndiwo malo ake.

وَأَمَّا مَنْ خَافَ مَقَامَ رَبِّهِۦ وَنَهَى ٱلنَّفْسَ عَنِ ٱلْهَوَىٰ ﴿40﴾

Tsono amene akuopa kuti adzaimilira pamaso pa Mbuye wake, nauletsa mtima wake ku zilakolako zoipa,

فَإِنَّ ٱلْجَنَّةَ هِىَ ٱلْمَأْوَىٰ ﴿41﴾

Ndithu Munda wamtendere ndiwo adzakhale malo ake.

يَسْـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلسَّاعَةِ أَيَّانَ مُرْسَىٰهَا ﴿42﴾

Akukufunsa (iwe Mtumiki) (s.a.w) za nthawi (ya tsiku lachimaliziro kuti): “Idzakhala liti?”

فِيمَ أَنتَ مِن ذِكْرَىٰهَآ ﴿43﴾

Uli ndi mphamvu yanji iwe yofotokozera za tsikulo? (Iwe ulibe kuzindikira za nthawiyo kotero kuti ungaitchule kwa iwo).

إِلَىٰ رَبِّكَ مُنتَهَىٰهَآ ﴿44﴾

Kwa Mbuye wako ndiko kuli mathero ake.

إِنَّمَآ أَنتَ مُنذِرُ مَن يَخْشَىٰهَا ﴿45﴾

Iwe (ntchito yako) ndikuwachenjeza amene akuiopa; (osati kulengeza zanthawi yake).

كَأَنَّهُمْ يَوْمَ يَرَوْنَهَا لَمْ يَلْبَثُوٓا۟ إِلَّا عَشِيَّةً أَوْ ضُحَىٰهَا ﴿46﴾

Tsiku limene adzaiona adzakhala ngati sadakhale (pa dziko nthawi yayitali), koma ngati madzulo amodzi kapena masana ake (nthawi ya m’mawa).[383]