Main pages

Surah Spoils of war, booty [Al-Anfal] in Chewa

Surah Spoils of war, booty [Al-Anfal] Ayah 75 Location Madinah Number 8

يَسْـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلْأَنفَالِ ۖ قُلِ ٱلْأَنفَالُ لِلَّهِ وَٱلرَّسُولِ ۖ فَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ وَأَصْلِحُوا۟ ذَاتَ بَيْنِكُمْ ۖ وَأَطِيعُوا۟ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥٓ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ ﴿1﴾

Akukufunsa za chuma cholandidwa pa nkhondo (mmene chingagawidwire). Nena: “Chuma cholanda pa nkhondo ndi cha Allah ndi Mtumiki (ndiamene ali olamula kagawidwe kake); choncho, muopeni Allah ndipo yanjanani mwachibale pakati panu. Mverani Allah ndi Mtumiki Wake, ngati mulidi okhulupirira.”[189]

إِنَّمَا ٱلْمُؤْمِنُونَ ٱلَّذِينَ إِذَا ذُكِرَ ٱللَّهُ وَجِلَتْ قُلُوبُهُمْ وَإِذَا تُلِيَتْ عَلَيْهِمْ ءَايَٰتُهُۥ زَادَتْهُمْ إِيمَٰنًۭا وَعَلَىٰ رَبِّهِمْ يَتَوَكَّلُونَ ﴿2﴾

Ndithu okhulupirira, enieni ndi amene akuti Allah akatchulidwa mitima yawo imadzadzidwa ndi mantha; pamenenso Ayah Zake zikuwerengedwa kwa iwo zimawaonjezera chikhulupiliro, ndipo amayadzamira kwa Mbuye wawo Yekha basi; (sakhulupirira nyanga ndi mizimu ya anthu akufa).[190]

ٱلَّذِينَ يُقِيمُونَ ٱلصَّلَوٰةَ وَمِمَّا رَزَقْنَٰهُمْ يُنفِقُونَ ﴿3﴾

Amene amaimilira kupemphera napereka chimene tawapatsa, (pa njira ya Allah, ndikuthandiza ovutika).

أُو۟لَٰٓئِكَ هُمُ ٱلْمُؤْمِنُونَ حَقًّۭا ۚ لَّهُمْ دَرَجَٰتٌ عِندَ رَبِّهِمْ وَمَغْفِرَةٌۭ وَرِزْقٌۭ كَرِيمٌۭ ﴿4﴾

Awa (okhala ndi makhalidwe otere) ndi amene ali okhulupirira mwachoonadi. Iwo adzapeza ulemelero (wapamwamba) kwa Mbuye wawo, ndi chikhululuko ndi zopatsidwa zaulemu.

كَمَآ أَخْرَجَكَ رَبُّكَ مِنۢ بَيْتِكَ بِٱلْحَقِّ وَإِنَّ فَرِيقًۭا مِّنَ ٱلْمُؤْمِنِينَ لَكَٰرِهُونَ ﴿5﴾

Monga mmene Mbuye wako adakulamulira kutuluka m’nyumba yako (kupita ku Badr kukachita nkhondo ndi osakhulupirira) mwachoonadi, ndithu gulu lina la okhulipirira silidafune (kuchoka kukakumana ndi adani).[191]

يُجَٰدِلُونَكَ فِى ٱلْحَقِّ بَعْدَمَا تَبَيَّنَ كَأَنَّمَا يُسَاقُونَ إِلَى ٱلْمَوْتِ وَهُمْ يَنظُرُونَ ﴿6﴾

Akutsutsana nawe (pa chinthu) choona pambuyo pakuti chaonekera poyera. (Kukuwaipira kukumana ndi adani) ngati kuti akubusidwa kunka ku imfa akuona.

وَإِذْ يَعِدُكُمُ ٱللَّهُ إِحْدَى ٱلطَّآئِفَتَيْنِ أَنَّهَا لَكُمْ وَتَوَدُّونَ أَنَّ غَيْرَ ذَاتِ ٱلشَّوْكَةِ تَكُونُ لَكُمْ وَيُرِيدُ ٱللَّهُ أَن يُحِقَّ ٱلْحَقَّ بِكَلِمَٰتِهِۦ وَيَقْطَعَ دَابِرَ ٱلْكَٰفِرِينَ ﴿7﴾

(Kumbukirani, E inu okhulupirira!) Pamene Allah anakulonjezani gulu limodzi mwa magulu awiri kuti likhale lanu (kuti mumenyane nalo). Koma inu mukufuna lopanda mphamvu kuti likhale lanu (kuti ndilo mumenyane nalo). Koma Allah akufuna kuchitsimikiza choonadi ndi mawu Ake ndi kudula mizu ya osakhulupirira, (pomenyana ndi gulu lamphamvulo, omwe ndi ankhondo a Chikuraishi).

لِيُحِقَّ ٱلْحَقَّ وَيُبْطِلَ ٱلْبَٰطِلَ وَلَوْ كَرِهَ ٱلْمُجْرِمُونَ ﴿8﴾

Kuti achitsimikizire choonadi ndi kulichotsa bodza; ngakhale zikuwaipira anthu oipa.

إِذْ تَسْتَغِيثُونَ رَبَّكُمْ فَٱسْتَجَابَ لَكُمْ أَنِّى مُمِدُّكُم بِأَلْفٍۢ مِّنَ ٱلْمَلَٰٓئِكَةِ مُرْدِفِينَ ﴿9﴾

(Kumbukirani) pamene mudali kupempha Mbuye wanu chithandizo, ndipo anakuyankhani kuti: “Ndithudi, Ine ndikuthandizani ndi chikwi cha angelo otsatizana potsika, (omenya nkhondo).”

وَمَا جَعَلَهُ ٱللَّهُ إِلَّا بُشْرَىٰ وَلِتَطْمَئِنَّ بِهِۦ قُلُوبُكُمْ ۚ وَمَا ٱلنَّصْرُ إِلَّا مِنْ عِندِ ٱللَّهِ ۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَزِيزٌ حَكِيمٌ ﴿10﴾

Ndipo Allah sadachite ichi koma kuti chikhale nkhani yabwino (yosangalatsa), ndi kuti mitima yanu ikhazikike ndi chimenecho. Ndipo palibe chipulumutso (chothandiza) koma chimene chachokera kwa Allah. Ndithu Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.[192]

إِذْ يُغَشِّيكُمُ ٱلنُّعَاسَ أَمَنَةًۭ مِّنْهُ وَيُنَزِّلُ عَلَيْكُم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءًۭ لِّيُطَهِّرَكُم بِهِۦ وَيُذْهِبَ عَنكُمْ رِجْزَ ٱلشَّيْطَٰنِ وَلِيَرْبِطَ عَلَىٰ قُلُوبِكُمْ وَيُثَبِّتَ بِهِ ٱلْأَقْدَامَ ﴿11﴾

(Kumbukirani) pamene anakugonetsani tulo tomwe tidali mtendere wochokera kwa Iye, ndipo anavumbwitsa mvula pa inu yochokera ku mitambo kuti akuyeretseni nayo (matupi anu) ndikukuchotserani manong’onong’o a satana, ndi kuipatsa mphamvu mitima yanu ndiponso ndi kulimbikitsa mapazi anu (pamchenga).

إِذْ يُوحِى رَبُّكَ إِلَى ٱلْمَلَٰٓئِكَةِ أَنِّى مَعَكُمْ فَثَبِّتُوا۟ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ ۚ سَأُلْقِى فِى قُلُوبِ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ ٱلرُّعْبَ فَٱضْرِبُوا۟ فَوْقَ ٱلْأَعْنَاقِ وَٱضْرِبُوا۟ مِنْهُمْ كُلَّ بَنَانٍۢ ﴿12﴾

(Kumbukira) pamene Mbuye wako anawauza angelo kuti: “Ine ndili pamodzi nanu (pokulimbikitsani ndi chithandizo Changa). Alimbikitseni amene akhulupirira, ndipo ndidzathira mantha mmitima mwa amene sadakhulupirire. Choncho amenyeni mmwamba mwa makosi awo, ndi kuwadula nsonga za zala zawo (zimene akugwilira zida).

ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ شَآقُّوا۟ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ ۚ وَمَن يُشَاقِقِ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ فَإِنَّ ٱللَّهَ شَدِيدُ ٱلْعِقَابِ ﴿13﴾

Izi ndi chifukwa chakuti iwo anatsutsana ndi Allah ndi Mtumiki wake (iwo podziika mbali ina kusiya komwe kudali Allah). Amene anatsutsana ndi Allah ndi Mtumiki Wake, ndithu Allah ndi wolanga kwambiri (amalanga ndi chilango choopsa).

ذَٰلِكُمْ فَذُوقُوهُ وَأَنَّ لِلْكَٰفِرِينَ عَذَابَ ٱلنَّارِ ﴿14﴾

Chimenecho ndi chilango (cha Allah E inu Maquraish)! Choncho chilaweni. Ndithu osakhulupirira adzapeza chilango cha Moto.

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓا۟ إِذَا لَقِيتُمُ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ زَحْفًۭا فَلَا تُوَلُّوهُمُ ٱلْأَدْبَارَ ﴿15﴾

E inu amene mwakhulupirira! Pamene mukumana nawo (pa nkhondo) amene sadakhulupirire alikudza kwa inu mwa unyinji musawatembenuzire misana kuthawa.

وَمَن يُوَلِّهِمْ يَوْمَئِذٍۢ دُبُرَهُۥٓ إِلَّا مُتَحَرِّفًۭا لِّقِتَالٍ أَوْ مُتَحَيِّزًا إِلَىٰ فِئَةٍۢ فَقَدْ بَآءَ بِغَضَبٍۢ مِّنَ ٱللَّهِ وَمَأْوَىٰهُ جَهَنَّمُ ۖ وَبِئْسَ ٱلْمَصِيرُ ﴿16﴾

Ndipo amene adzawatembenuzire msana kuthawa pa tsikulo - osati kutembenuka (kwa ndale) kofuna kumenyana kapena kukalowa m’gulu (la Asilamu ena) - ndiye kuti adziitanira mkwiyo wochokera kwa Allah; ndipo malo ake ndi ku Jahannam, kumeneko ndi ku malo koipa kubwererapo.

فَلَمْ تَقْتُلُوهُمْ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ قَتَلَهُمْ ۚ وَمَا رَمَيْتَ إِذْ رَمَيْتَ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ رَمَىٰ ۚ وَلِيُبْلِىَ ٱلْمُؤْمِنِينَ مِنْهُ بَلَآءً حَسَنًا ۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٌۭ ﴿17﴾

Inu simudawaphe (ndi mphamvu zanu) koma Allah ndi Yemwe anawapha; siudawagende pamene udagenda koma Allah ndi amene anawagenda (pofikitsa mchenga m’maso mwawo, wachita zimenezi) kuti awachitire zabwino Asilamu powapatsa dalitso labwino lochokera kwa Iye. Ndithu Allah Ngwakumva, Ngodziwa.[193]

ذَٰلِكُمْ وَأَنَّ ٱللَّهَ مُوهِنُ كَيْدِ ٱلْكَٰفِرِينَ ﴿18﴾

Izi akuchitirani (pakalipano), ndithudi Allah afooketsa ndale za osakhulupirira.

إِن تَسْتَفْتِحُوا۟ فَقَدْ جَآءَكُمُ ٱلْفَتْحُ ۖ وَإِن تَنتَهُوا۟ فَهُوَ خَيْرٌۭ لَّكُمْ ۖ وَإِن تَعُودُوا۟ نَعُدْ وَلَن تُغْنِىَ عَنكُمْ فِئَتُكُمْ شَيْـًۭٔا وَلَوْ كَثُرَتْ وَأَنَّ ٱللَّهَ مَعَ ٱلْمُؤْمِنِينَ ﴿19﴾

Ngati mwakhala mukufuna chiweruzo (pogwilira nsalu yovindikira Ka’aba kuti mupambane pa nkhondo), chiweruzo chakudzerani (chokomera Asilamu). Ndipo ngati musiya (kuwazunza okhulupirira kapena kusiya kunyoza Allah) chikhala chinthu chabwino kwa inu. Koma ngati mubwereza (kuwaputa) nafenso tidzabwereza (kukulangani). Gulu lanu lankhondo silikuthandizani kanthu ngakhale lichuluke chotani. Ndipo Allah ali pamodzi ndi okhulupirira.

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓا۟ أَطِيعُوا۟ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ وَلَا تَوَلَّوْا۟ عَنْهُ وَأَنتُمْ تَسْمَعُونَ ﴿20﴾

E inu amene mwakhulupirira! Mverani Allah ndi Mtumiki Wake, ndipo musamtembenukire kumbali pamene inu mukumva.[194]

وَلَا تَكُونُوا۟ كَٱلَّذِينَ قَالُوا۟ سَمِعْنَا وَهُمْ لَا يَسْمَعُونَ ﴿21﴾

Ndipo musakhale monga aja achinyengo omwe akunena: “Tamva (choonadi ndipo tachisunga),” pomwe iwo sakumva (kumva kochigonjera).

۞ إِنَّ شَرَّ ٱلدَّوَآبِّ عِندَ ٱللَّهِ ٱلصُّمُّ ٱلْبُكْمُ ٱلَّذِينَ لَا يَعْقِلُونَ ﴿22﴾

Ndithu nyama zoipitsitsa pamaso pa Allah ndi agonthi, abubu amene alibe nzeru, (omwe ndi aphatikizi ndi anthu achinyengo).

وَلَوْ عَلِمَ ٱللَّهُ فِيهِمْ خَيْرًۭا لَّأَسْمَعَهُمْ ۖ وَلَوْ أَسْمَعَهُمْ لَتَوَلَّوا۟ وَّهُم مُّعْرِضُونَ ﴿23﴾

Ndipo Allah akadadziwa mwa iwo (ndi kudziwa kwake kopanda chiyambi); kuti muli ubwino (pakuwamveretsa Qur’an ndi kuwazindikiritsa) akadawamveretsa. (Koma chikhalidwe chawo chili cha mtundu umenewo) ndipo ngakhale akadawamveretsa (Qur’an ndikuwazindikiritsa) akadatembenuka m’mbuyo uku akunyoza (chifukwa cha kugonjera zilakolako zawo).

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ ٱسْتَجِيبُوا۟ لِلَّهِ وَلِلرَّسُولِ إِذَا دَعَاكُمْ لِمَا يُحْيِيكُمْ ۖ وَٱعْلَمُوٓا۟ أَنَّ ٱللَّهَ يَحُولُ بَيْنَ ٱلْمَرْءِ وَقَلْبِهِۦ وَأَنَّهُۥٓ إِلَيْهِ تُحْشَرُونَ ﴿24﴾

E inu amene mwakhulupirira muvomereni Allah (pa zimene akukulamulani) ndiponso muvomereni Mtumiki Wake pamene akukuitanirani ku chimene chingakupatseni moyo (wabwino wa pa dziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro). Ndipo dziwani kuti Allah amatchinga pakati pa munthu ndi mtima wake (amautembenula mmene akufunira). Ndipo dziwani kuti kwa Iye mudzasonkhanitsidwa.[195]

وَٱتَّقُوا۟ فِتْنَةًۭ لَّا تُصِيبَنَّ ٱلَّذِينَ ظَلَمُوا۟ مِنكُمْ خَآصَّةًۭ ۖ وَٱعْلَمُوٓا۟ أَنَّ ٱللَّهَ شَدِيدُ ٱلْعِقَابِ ﴿25﴾

Ndipo muope mazunzo (a Allah a pano pa dziko lapansi) omwe sangagwere okhawo amene adzichitira zoipa mwa inu (koma adzawagweranso amene akusiya kuletsa zoipa) ndipo dziwani kuti Allah Ngolanga kwambiri.[196]

وَٱذْكُرُوٓا۟ إِذْ أَنتُمْ قَلِيلٌۭ مُّسْتَضْعَفُونَ فِى ٱلْأَرْضِ تَخَافُونَ أَن يَتَخَطَّفَكُمُ ٱلنَّاسُ فَـَٔاوَىٰكُمْ وَأَيَّدَكُم بِنَصْرِهِۦ وَرَزَقَكُم مِّنَ ٱلطَّيِّبَٰتِ لَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ ﴿26﴾

Ndipo kumbukirani (inu Asilamu) pamene mudali owerengeka, ochepa, onyozeka m’dziko. Mumakhala moopa anthu kuti angakufwambeni, koma anakupatsani pamalo pabwino pokhala, nakulimbikitsani ndi chipulumutso Chake, nakuninkhani zinthu zabwino kuti muyamike (Allah).[197]

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ لَا تَخُونُوا۟ ٱللَّهَ وَٱلرَّسُولَ وَتَخُونُوٓا۟ أَمَٰنَٰتِكُمْ وَأَنتُمْ تَعْلَمُونَ ﴿27﴾

E inu amene mwakhulupirira! Musachitire Allah ndi Mtumiki (Wake) chinyengo (pa kutsata zimene mwaletsedwa). Ndipo musazichitire chinyengo zimene mwakhulupirika nazo uku mukudziwa (kuti kutero ndikulakwa).

وَٱعْلَمُوٓا۟ أَنَّمَآ أَمْوَٰلُكُمْ وَأَوْلَٰدُكُمْ فِتْنَةٌۭ وَأَنَّ ٱللَّهَ عِندَهُۥٓ أَجْرٌ عَظِيمٌۭ ﴿28﴾

Ndipo dziwani kuti chuma chanu ndi ana anu ndimayesero (oyesedwa ndi Allah kuti aone mmene mungagwiritsire nazo ntchito). Ndi kuti kwa Allah kuli malipiro aakulu.

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓا۟ إِن تَتَّقُوا۟ ٱللَّهَ يَجْعَل لَّكُمْ فُرْقَانًۭا وَيُكَفِّرْ عَنكُمْ سَيِّـَٔاتِكُمْ وَيَغْفِرْ لَكُمْ ۗ وَٱللَّهُ ذُو ٱلْفَضْلِ ٱلْعَظِيمِ ﴿29﴾

E inu amene mwakhulupirira! Ngati muopa Allah, adzakupatsani chilekanitso (cholekanitsa pakati pa choonadi ndi chachabe), ndiponso akufafanizirani zoipa zanu ndi kukukhululukirani. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino waukulu.[198]

وَإِذْ يَمْكُرُ بِكَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ لِيُثْبِتُوكَ أَوْ يَقْتُلُوكَ أَوْ يُخْرِجُوكَ ۚ وَيَمْكُرُونَ وَيَمْكُرُ ٱللَّهُ ۖ وَٱللَّهُ خَيْرُ ٱلْمَٰكِرِينَ ﴿30﴾

Ndipo (kumbukira) pamene omwe sadakhulupirire amakuchitira chiwembu kuti akunjate, kapena akuphe, kapena akutulutse (m’dziko lawo la Makka mwachipongwe). Ndipo amachita chiwembu, naye Allah anawononga chiwembu chawocho. Ndipo Allah ndiwokhoza koposa poononga ziwembu (za anthu oipa).[199]

وَإِذَا تُتْلَىٰ عَلَيْهِمْ ءَايَٰتُنَا قَالُوا۟ قَدْ سَمِعْنَا لَوْ نَشَآءُ لَقُلْنَا مِثْلَ هَٰذَآ ۙ إِنْ هَٰذَآ إِلَّآ أَسَٰطِيرُ ٱلْأَوَّلِينَ ﴿31﴾

Ndipo (Aquraish) zikawerengedwa Ayah (ndime) Zathu kwa iwo amanena: “Tidazimva (izi kale). Tikadafuna tikadanena zonga izi. Izi sikanthu koma ndinthano za anthu akale.”

وَإِذْ قَالُوا۟ ٱللَّهُمَّ إِن كَانَ هَٰذَا هُوَ ٱلْحَقَّ مِنْ عِندِكَ فَأَمْطِرْ عَلَيْنَا حِجَارَةًۭ مِّنَ ٱلسَّمَآءِ أَوِ ٱئْتِنَا بِعَذَابٍ أَلِيمٍۢ ﴿32﴾

Ndipo (kumbukira) pamene adati: “E Inu Allah! Ngati ichi (chimene wadza nacho Muhammad {s.a.w}) chili choonadi chochokera kwa Inu, tivumbwitsireni mvula ya miyala yochokera kumwamba, kapena mutibweretsere chilango chowawa kwambiri.”[200]

وَمَا كَانَ ٱللَّهُ لِيُعَذِّبَهُمْ وَأَنتَ فِيهِمْ ۚ وَمَا كَانَ ٱللَّهُ مُعَذِّبَهُمْ وَهُمْ يَسْتَغْفِرُونَ ﴿33﴾

Koma Allah sangawalange pomwe iwe uli nawo. Ndipo Allah sakadawalanga pomwe (ena mwa iwo) akupempha chikhululuko.

وَمَا لَهُمْ أَلَّا يُعَذِّبَهُمُ ٱللَّهُ وَهُمْ يَصُدُّونَ عَنِ ٱلْمَسْجِدِ ٱلْحَرَامِ وَمَا كَانُوٓا۟ أَوْلِيَآءَهُۥٓ ۚ إِنْ أَوْلِيَآؤُهُۥٓ إِلَّا ٱلْمُتَّقُونَ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ لَا يَعْلَمُونَ ﴿34﴾

(Kodi iwo Aquraish) ali ndi chinthu chanji (chabwino chimene) chingamuletse Allah kuwalanga? Pomwe iwo akuwatsekereza anthu kulowa mu Msikiti Wopatulika. Iwo sanayenere kukhala ouyang’anira (Msikitiwo). Palibe angauyang’anire koma olungama, koma anthu ambiri sadziwa.[201]

وَمَا كَانَ صَلَاتُهُمْ عِندَ ٱلْبَيْتِ إِلَّا مُكَآءًۭ وَتَصْدِيَةًۭ ۚ فَذُوقُوا۟ ٱلْعَذَابَ بِمَا كُنتُمْ تَكْفُرُونَ ﴿35﴾

Ndipo mapemphero awo pa nyumba yopatulikayo sadali kanthu, koma kuyimba miluzi ndi kuomba m’manja. Choncho (adzauzidwa): “Lawani chilango chifukwa chakusakhulupirira kwanu.”

إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ يُنفِقُونَ أَمْوَٰلَهُمْ لِيَصُدُّوا۟ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ ۚ فَسَيُنفِقُونَهَا ثُمَّ تَكُونُ عَلَيْهِمْ حَسْرَةًۭ ثُمَّ يُغْلَبُونَ ۗ وَٱلَّذِينَ كَفَرُوٓا۟ إِلَىٰ جَهَنَّمَ يُحْشَرُونَ ﴿36﴾

Ndithu osakhulupirira akupereka chuma chawo (pa nkhondo yolimbana ndi Asilamu) ndi cholinga choti awatsekeleze anthu kuyenda pa njira ya Allah. Choncho adzapitiriza kupereka chumacho kenako chidzakhala chowadandaulitsa, ndipo adzagonjetsedwa. Ndipo omwe sanakhulupirire adzasonkhanitsidwa ku Jahannam.

لِيَمِيزَ ٱللَّهُ ٱلْخَبِيثَ مِنَ ٱلطَّيِّبِ وَيَجْعَلَ ٱلْخَبِيثَ بَعْضَهُۥ عَلَىٰ بَعْضٍۢ فَيَرْكُمَهُۥ جَمِيعًۭا فَيَجْعَلَهُۥ فِى جَهَنَّمَ ۚ أُو۟لَٰٓئِكَ هُمُ ٱلْخَٰسِرُونَ ﴿37﴾

Kuti Allah alekanitse oipa ndi abwino, ndi kuti awayike ena mwa oipawo pamwamba pa anzawo, potero nkuwaunjika oipawo mulu umodzi, kenako nawaponya ku Jahannam. Iwowa ndi anthu otaika.

قُل لِّلَّذِينَ كَفَرُوٓا۟ إِن يَنتَهُوا۟ يُغْفَرْ لَهُم مَّا قَدْ سَلَفَ وَإِن يَعُودُوا۟ فَقَدْ مَضَتْ سُنَّتُ ٱلْأَوَّلِينَ ﴿38﴾

Nena kwa osakhulupirira kuti: “Ngati asiya (zochita zawo zoipa), adzakhululukidwa zimene zidatsogola. Koma ngati abwereza (kuwazunza Asilamu, tiwalanga) ndithudi njira ya Allah yomwe idachitika kwa anthu akale inadutsa (powalanga akasiya kutsata malamulo a Allah).

وَقَٰتِلُوهُمْ حَتَّىٰ لَا تَكُونَ فِتْنَةٌۭ وَيَكُونَ ٱلدِّينُ كُلُّهُۥ لِلَّهِ ۚ فَإِنِ ٱنتَهَوْا۟ فَإِنَّ ٱللَّهَ بِمَا يَعْمَلُونَ بَصِيرٌۭ ﴿39﴾

Ndipo menyanani nawo osakhulupirira kufikira shirik itatha ndipo chipembedzo chonse chikhale cha Allah. Ndipo ngati asiya, ndithu Allah Ngoona zomwe akuchita.

وَإِن تَوَلَّوْا۟ فَٱعْلَمُوٓا۟ أَنَّ ٱللَّهَ مَوْلَىٰكُمْ ۚ نِعْمَ ٱلْمَوْلَىٰ وَنِعْمَ ٱلنَّصِيرُ ﴿40﴾

Koma ngati apitiriza kunyoza kwawo, dziwani kuti Allah ndi Mtetezi wanu, Mtetezi wokoma mtima koposa, ndi Mthandizi wabwino.

۞ وَٱعْلَمُوٓا۟ أَنَّمَا غَنِمْتُم مِّن شَىْءٍۢ فَأَنَّ لِلَّهِ خُمُسَهُۥ وَلِلرَّسُولِ وَلِذِى ٱلْقُرْبَىٰ وَٱلْيَتَٰمَىٰ وَٱلْمَسَٰكِينِ وَٱبْنِ ٱلسَّبِيلِ إِن كُنتُمْ ءَامَنتُم بِٱللَّهِ وَمَآ أَنزَلْنَا عَلَىٰ عَبْدِنَا يَوْمَ ٱلْفُرْقَانِ يَوْمَ ٱلْتَقَى ٱلْجَمْعَانِ ۗ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَىْءٍۢ قَدِيرٌ ﴿41﴾

۞ Ndipo dziwani kuti chilichonse chimene mwapeza monga chuma cholanda ku nkhondo, gawo limodzi mwa magawo asanu ndi cha Allah ndi Mtumiki, ndi a chibale (a Mtumiki), amasiye, masikini ndi munthu wa pa ulendo (amene asowedwa choyendera pa ulendo. Tsatilani malamulowa) ngatidi mwakhulupirira Allah ndi chimene tachivumbulutsa kwa kapolo Wathu pa tsiku lachilekanitso (lolekanitsa pakati pa choona ndi chabodza), tsiku limene magulu awiri adakumana (tsiku la nkhondo ya Badr, gulu la nkhondo la Asilamu ndi gulu la nkhondo la osakhulupirira). Ndipo Allah Ngokhoza kuchita chilichonse.

إِذْ أَنتُم بِٱلْعُدْوَةِ ٱلدُّنْيَا وَهُم بِٱلْعُدْوَةِ ٱلْقُصْوَىٰ وَٱلرَّكْبُ أَسْفَلَ مِنكُمْ ۚ وَلَوْ تَوَاعَدتُّمْ لَٱخْتَلَفْتُمْ فِى ٱلْمِيعَٰدِ ۙ وَلَٰكِن لِّيَقْضِىَ ٱللَّهُ أَمْرًۭا كَانَ مَفْعُولًۭا لِّيَهْلِكَ مَنْ هَلَكَ عَنۢ بَيِّنَةٍۢ وَيَحْيَىٰ مَنْ حَىَّ عَنۢ بَيِّنَةٍۢ ۗ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَسَمِيعٌ عَلِيمٌ ﴿42﴾

(Kumbukirani) pamene mudali mbali ya chigwa yoyandikira (mzinda wa Madina) pomwe iwo (ankhondo a Chikuraishi) adali mbali ya kutali ya tsidya lina (la chigwacho) pomwe aulendo amalonda adali cha kumunsi kwanu. Ngati mukadapangana nthawi yokumanirana (kuti mukumane nthawi yakutiyakuti), mukadasiyana posunga chipangano (chifukwa cha kuopa kuchuluka kwa adani anuwo). Koma (mwakumana mosayembekezera ndi ankhondo a adaniwo) kuti Allah akwaniritse chinthu chomwe nchofunika kuti chichitike, kuti awonongeke amene waonongeka (posankha kusakhulupirira) ndi umboni woonekera (umene adaukana kuutsata), ndi kuti akhale ndi moyo amene wakhala ndi moyo (amene watsata njira ya Chisilamu) ndi umboninso woonekera. Ndithudi Allah Ngwakumva zonse, Ngodziwa kwambiri.[202]

إِذْ يُرِيكَهُمُ ٱللَّهُ فِى مَنَامِكَ قَلِيلًۭا ۖ وَلَوْ أَرَىٰكَهُمْ كَثِيرًۭا لَّفَشِلْتُمْ وَلَتَنَٰزَعْتُمْ فِى ٱلْأَمْرِ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ سَلَّمَ ۗ إِنَّهُۥ عَلِيمٌۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ ﴿43﴾

(Kumbukira) pamene Allah adakuonetsa iwo ku maloto kwako kuti ngochepa (pachiwerengero chawo potero udalimba mtima za kukumana nawo), akanakuonetsa iwo kuti ngambiri pa chiwerengero chawo; inu (Asilamu) mukadalephera (mukanataya mtima) ndipo mukanakangana pa chinthucho. (Ena akanafuna kumenyana nawo pamene ena akanakana), koma Allah anakutetezani (ku zimenezo). Ndithu Iye Ngodziwa kwambiri za m’mitima.

وَإِذْ يُرِيكُمُوهُمْ إِذِ ٱلْتَقَيْتُمْ فِىٓ أَعْيُنِكُمْ قَلِيلًۭا وَيُقَلِّلُكُمْ فِىٓ أَعْيُنِهِمْ لِيَقْضِىَ ٱللَّهُ أَمْرًۭا كَانَ مَفْعُولًۭا ۗ وَإِلَى ٱللَّهِ تُرْجَعُ ٱلْأُمُورُ ﴿44﴾

Ndipo (kumbukirani) pamene anakuonetsani iwo m’maso mwanu, pamene munakumana nawo kuti iwo ndi ochepa, (owerengeka, kuti mukhale ndi chidwi chomenyana nawo), ndiponso anakuchepetsani kwambiri m’maso mwawo (kuti iwo aone kuti nkosafunika kukonzekera kwambiri chifukwa chakuchepa kwa omenyana nawowo), kuti Allah akwaniritse chimene adalamula kuchitika. Kwa Allah Yekha ndiko kobwerera zinthu zonse.

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓا۟ إِذَا لَقِيتُمْ فِئَةًۭ فَٱثْبُتُوا۟ وَٱذْكُرُوا۟ ٱللَّهَ كَثِيرًۭا لَّعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ ﴿45﴾

E inu amene mwakhulupirira! Pamene mukumana ndi gulu (la osakhulupirira) mulimbe mtima, ndipo tamandani Allah kwambiri kuti mupambane.

وَأَطِيعُوا۟ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ وَلَا تَنَٰزَعُوا۟ فَتَفْشَلُوا۟ وَتَذْهَبَ رِيحُكُمْ ۖ وَٱصْبِرُوٓا۟ ۚ إِنَّ ٱللَّهَ مَعَ ٱلصَّٰبِرِينَ ﴿46﴾

Ndipo mumvereni Allah ndi Mtumiki Wake, musakangane (kuopera kuti) mungakhale olephera (ndi kutaya mtima), ndikuchoka mphamvu zanu. Koma pitirizani kupirira. Ndithudi, Allah ali pamodzi ndi anthu opirira.

وَلَا تَكُونُوا۟ كَٱلَّذِينَ خَرَجُوا۟ مِن دِيَٰرِهِم بَطَرًۭا وَرِئَآءَ ٱلنَّاسِ وَيَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ ۚ وَٱللَّهُ بِمَا يَعْمَلُونَ مُحِيطٌۭ ﴿47﴾

Ndipo musakhale ngati anthu amene anatuluka m’nyumba zawo modzikweza ndi modzionetsera kwa anthu, ndikuwasekereza anthu kuyenda pa njira ya Allah. Koma Allah ndi Wodziwa kwambiri zimene akuchita.

وَإِذْ زَيَّنَ لَهُمُ ٱلشَّيْطَٰنُ أَعْمَٰلَهُمْ وَقَالَ لَا غَالِبَ لَكُمُ ٱلْيَوْمَ مِنَ ٱلنَّاسِ وَإِنِّى جَارٌۭ لَّكُمْ ۖ فَلَمَّا تَرَآءَتِ ٱلْفِئَتَانِ نَكَصَ عَلَىٰ عَقِبَيْهِ وَقَالَ إِنِّى بَرِىٓءٌۭ مِّنكُمْ إِنِّىٓ أَرَىٰ مَا لَا تَرَوْنَ إِنِّىٓ أَخَافُ ٱللَّهَ ۚ وَٱللَّهُ شَدِيدُ ٱلْعِقَابِ ﴿48﴾

Ndipo (kumbukira) pamene satana adawakometsera zochita zawo zoipa (aja osakhulupirira) nati: “Lero palibe aliyense mwa anthu amene angakugonjetseni, ndipo ine ndine mtetezi wanu.” Koma pamene magulu awiri ankhondo anaonana (anakumana pamaso ndi pamaso) satana anabwerera pambuyo (kuthawa) nati: “Ine ndikudzipatula mwa inu. Ndithu ine ndikuona zimene inu simukuziona. Ndithu ine ndikuopa Allah.” Ndipo Allah Ngwaukali polanga.

إِذْ يَقُولُ ٱلْمُنَٰفِقُونَ وَٱلَّذِينَ فِى قُلُوبِهِم مَّرَضٌ غَرَّ هَٰٓؤُلَآءِ دِينُهُمْ ۗ وَمَن يَتَوَكَّلْ عَلَى ٱللَّهِ فَإِنَّ ٱللَّهَ عَزِيزٌ حَكِيمٌۭ ﴿49﴾

(Kumbukirani) pamene achiphamaso ndi amene ali ndi matenda m’mitima mwawo amanena: “Anthu awa chipembedzo chawo (cha Chisilamu) chawanyenga.” Komatu amene akuyadzamira kwa Allah ndithudi Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.

وَلَوْ تَرَىٰٓ إِذْ يَتَوَفَّى ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ ۙ ٱلْمَلَٰٓئِكَةُ يَضْرِبُونَ وُجُوهَهُمْ وَأَدْبَٰرَهُمْ وَذُوقُوا۟ عَذَابَ ٱلْحَرِيقِ ﴿50﴾

Ndipo ukadaona angelo pamene akuchotsa miyoyo ya anthu amene sadakhulupirire (pa imfa yawo) uku akumenya kunkhope zawo ndi kumisana yawo (uku akunena): “Lawani chilango cha Moto woocha. (Ukadaziona zoopsa kwabasi).”

ذَٰلِكَ بِمَا قَدَّمَتْ أَيْدِيكُمْ وَأَنَّ ٱللَّهَ لَيْسَ بِظَلَّٰمٍۢ لِّلْعَبِيدِ ﴿51﴾

“Izo ndi chifukwa cha (machimo) amene manja anu anawatsogoza, ndipo Allah sali opondereza akapolo (Ake).”[203]

كَدَأْبِ ءَالِ فِرْعَوْنَ ۙ وَٱلَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۚ كَفَرُوا۟ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ فَأَخَذَهُمُ ٱللَّهُ بِذُنُوبِهِمْ ۗ إِنَّ ٱللَّهَ قَوِىٌّۭ شَدِيدُ ٱلْعِقَابِ ﴿52﴾

(Khalidwe lawo awa lili ) ngati khalidwe la anthu a Farawo ndi omwe adalipo patsogolo pawo. Anazikana zizindikiro za Allah, choncho Allah anawalanga chifukwa cha machimo awo. Ndithudi Allah Ngwamphamvu, Wolanga moopsa.

ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ لَمْ يَكُ مُغَيِّرًۭا نِّعْمَةً أَنْعَمَهَا عَلَىٰ قَوْمٍ حَتَّىٰ يُغَيِّرُوا۟ مَا بِأَنفُسِهِمْ ۙ وَأَنَّ ٱللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٌۭ ﴿53﴾

Izo, (posawadzera miliri yotere) nchifukwa chakuti Allah sasintha chisomo (Chake) chimene wachipereka kwa anthu mpaka anthuwo asinthe okha zomwe zili m’mitima mwawo, (posiya kuthokoza Allah nayamba kuyenda m’njira zolakwira Allah). Ndithu Allah Ngwakumva Ngodziwa chilichonse.

كَدَأْبِ ءَالِ فِرْعَوْنَ ۙ وَٱلَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۚ كَذَّبُوا۟ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِمْ فَأَهْلَكْنَٰهُم بِذُنُوبِهِمْ وَأَغْرَقْنَآ ءَالَ فِرْعَوْنَ ۚ وَكُلٌّۭ كَانُوا۟ ظَٰلِمِينَ ﴿54﴾

(Khalidwe lawo lili) ngati khalidwe la anthu a Farawo ndi omwe adalipo patsogolo pawo. Adatsutsa zizindikiro za Mbuye wawo. Choncho, tidawaononga chifukwa cha machimo awo, ndipo tidawamiza anthu a Farawo. Ndipo onse adali ochita zoipa.

إِنَّ شَرَّ ٱلدَّوَآبِّ عِندَ ٱللَّهِ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ فَهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ ﴿55﴾

Ndithu nyama zoipitsitsa kwa Allah ndi amene sakhulupirira. (amamkana Allah ngakhale choonadi akuchidziwa bwinobwino), choncho iwo sakhulupirira

ٱلَّذِينَ عَٰهَدتَّ مِنْهُمْ ثُمَّ يَنقُضُونَ عَهْدَهُمْ فِى كُلِّ مَرَّةٍۢ وَهُمْ لَا يَتَّقُونَ ﴿56﴾

Omwe unapangana nawo chipangano kenako naaswa chipangano chawo panthawi iliyonse (imene mwapangana), ndiponso iwo saopa Allah.

فَإِمَّا تَثْقَفَنَّهُمْ فِى ٱلْحَرْبِ فَشَرِّدْ بِهِم مَّنْ خَلْفَهُمْ لَعَلَّهُمْ يَذَّكَّرُونَ ﴿57﴾

Choncho, ngati uwapeza ku nkhondo, (menyana nawo), uwabalalitse (kuti likhale phunziro kwa) amene ali pambuyo pawo kuti iwo azindikire.

وَإِمَّا تَخَافَنَّ مِن قَوْمٍ خِيَانَةًۭ فَٱنۢبِذْ إِلَيْهِمْ عَلَىٰ سَوَآءٍ ۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُحِبُّ ٱلْخَآئِنِينَ ﴿58﴾

Ngati uopa kusakhulupirika kwa anthu (omwe unapangana nawo chipangano), atayire (chipangano chawocho), mwachilungamo; ndithu Allah sakonda (anthu) osakhulupirika.

وَلَا يَحْسَبَنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ سَبَقُوٓا۟ ۚ إِنَّهُمْ لَا يُعْجِزُونَ ﴿59﴾

Ndipo (anthu) amene sadakhulupirire asaganize kuti ampitilira (Allah kotero kuti sachita kanthu ndi iwo), iwo sangamulepheretse Allah (chimene akufuna kuchita pa iwo).

وَأَعِدُّوا۟ لَهُم مَّا ٱسْتَطَعْتُم مِّن قُوَّةٍۢ وَمِن رِّبَاطِ ٱلْخَيْلِ تُرْهِبُونَ بِهِۦ عَدُوَّ ٱللَّهِ وَعَدُوَّكُمْ وَءَاخَرِينَ مِن دُونِهِمْ لَا تَعْلَمُونَهُمُ ٱللَّهُ يَعْلَمُهُمْ ۚ وَمَا تُنفِقُوا۟ مِن شَىْءٍۢ فِى سَبِيلِ ٱللَّهِ يُوَفَّ إِلَيْكُمْ وَأَنتُمْ لَا تُظْلَمُونَ ﴿60﴾

Ndipo akonzekereni mmene mungathere ndi mphamvu zanu (zonse zomenyera nkhondo), ndiponso poikiratu mahatchi odikira nkhondo kuti muwaopseze nazo adani a Allah ndi adani anu (amene mukuwadziwa) ndiponso (ndi) ena omwe (inu) simukuwadziwa. Koma Allah akuwadziwa. Ndipo chilichonse mungapereke pa njira ya Allah chidzalipidwa kwa inu modzadza ndipo simuzaponderezedwa.

۞ وَإِن جَنَحُوا۟ لِلسَّلْمِ فَٱجْنَحْ لَهَا وَتَوَكَّلْ عَلَى ٱللَّهِ ۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلْعَلِيمُ ﴿61﴾

Ndipo ngati (awo adani) apendekera kumbali yokhalirana mwa mtendere, nawenso pendekera (ku mbaliyo) ukatero yadzamira kwa Allah. Ndithudi Iye Ngwakumva, Ngodziwa.

وَإِن يُرِيدُوٓا۟ أَن يَخْدَعُوكَ فَإِنَّ حَسْبَكَ ٱللَّهُ ۚ هُوَ ٱلَّذِىٓ أَيَّدَكَ بِنَصْرِهِۦ وَبِٱلْمُؤْمِنِينَ ﴿62﴾

Ngati afuna kukunyenga pa chimvanochi, ndithudi, Allah akukwanira kwa iwe (kukuteteza). Iye ndi Yemwe anakuthangata ndi chipulumutso chake ndi okhulupirira.

وَأَلَّفَ بَيْنَ قُلُوبِهِمْ ۚ لَوْ أَنفَقْتَ مَا فِى ٱلْأَرْضِ جَمِيعًۭا مَّآ أَلَّفْتَ بَيْنَ قُلُوبِهِمْ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ أَلَّفَ بَيْنَهُمْ ۚ إِنَّهُۥ عَزِيزٌ حَكِيمٌۭ ﴿63﴾

Ndipo (Allah) analuzanitsa pakati pa mitima yawo (poika chikondi pakati pawo). Ngati ukanapereka zonse za m’dziko lapansi (ncholinga choti uwaluzanitse mitima yawo mwa iwe wekha) sukadatha kuluzanitsa pakati pa mitima yawo. Koma Allah adaluzanitsa pakati pawo. Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya.

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِىُّ حَسْبُكَ ٱللَّهُ وَمَنِ ٱتَّبَعَكَ مِنَ ٱلْمُؤْمِنِينَ ﴿64﴾

E iwe Mneneri! Allah akukwanira kwa iwe kukuteteza pamodzi ndi amene akutsata (iwe) mwa okhulupirira.

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِىُّ حَرِّضِ ٱلْمُؤْمِنِينَ عَلَى ٱلْقِتَالِ ۚ إِن يَكُن مِّنكُمْ عِشْرُونَ صَٰبِرُونَ يَغْلِبُوا۟ مِا۟ئَتَيْنِ ۚ وَإِن يَكُن مِّنكُم مِّا۟ئَةٌۭ يَغْلِبُوٓا۟ أَلْفًۭا مِّنَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ بِأَنَّهُمْ قَوْمٌۭ لَّا يَفْقَهُونَ ﴿65﴾

E iwe Mneneri! Alimbikitse okhulupirira kupita ku nkhondo. Ngati mwa inu muli anthu makumi awiri olimba mtima (ndiye kuti) adzawagonjetsa mazana awiri (200) (a mwa anthu osakhulupirira). Ngati mwa inu muli anthu zana limodzi (100) (olimba mtima ndiye kuti) adzagonjetsa chikwi chimodzi (1,000) cha anthu omwe sadakhulupirire, chifukwa chakuti iwo ndi anthu osazindikira.

ٱلْـَٰٔنَ خَفَّفَ ٱللَّهُ عَنكُمْ وَعَلِمَ أَنَّ فِيكُمْ ضَعْفًۭا ۚ فَإِن يَكُن مِّنكُم مِّا۟ئَةٌۭ صَابِرَةٌۭ يَغْلِبُوا۟ مِا۟ئَتَيْنِ ۚ وَإِن يَكُن مِّنكُمْ أَلْفٌۭ يَغْلِبُوٓا۟ أَلْفَيْنِ بِإِذْنِ ٱللَّهِ ۗ وَٱللَّهُ مَعَ ٱلصَّٰبِرِينَ ﴿66﴾

Tsopano Allah wakupeputsirani (lamulo lovutali), ndipo wadziwa kuti muli kufooka mwa inu. Choncho ngati mwa inu muli anthu zana limodzi olimba mtima adzagonjetsa mazana awiri. Ngati alipo mwa inu chikwi chimodzi, adzagonjetsa zikwi ziwiri, mwachilolezo cha Allah. Allah ali pamodzi ndi opirira.

مَا كَانَ لِنَبِىٍّ أَن يَكُونَ لَهُۥٓ أَسْرَىٰ حَتَّىٰ يُثْخِنَ فِى ٱلْأَرْضِ ۚ تُرِيدُونَ عَرَضَ ٱلدُّنْيَا وَٱللَّهُ يُرِيدُ ٱلْءَاخِرَةَ ۗ وَٱللَّهُ عَزِيزٌ حَكِيمٌۭ ﴿67﴾

Sichoyenera kwa Mneneri kukhala ndi akayidi mpaka amenye nkhondo (kwambiri) ndi kugonjetseratu maiko molimba (ndi pamene atha kukhala ndi akayidi). Mukufuna zinthu za m’dziko pomwe Allah akufuna (mupeze mphoto ya) tsiku lachimaliziro! Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya.

لَّوْلَا كِتَٰبٌۭ مِّنَ ٱللَّهِ سَبَقَ لَمَسَّكُمْ فِيمَآ أَخَذْتُمْ عَذَابٌ عَظِيمٌۭ ﴿68﴾

Pakadapanda lamulo la Allah limene linatsogolera kale (lokulolezani chuma chopeza ku nkhondo), chilango chachikulu chikanakugwerani, chifukwa cha zimene munatenga (ku-nkhondo ya Badri).

فَكُلُوا۟ مِمَّا غَنِمْتُمْ حَلَٰلًۭا طَيِّبًۭا ۚ وَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ ۚ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٌۭ رَّحِيمٌۭ ﴿69﴾

Tsopano idyani chuma chimene mwalanda pa nkhondo (chomwe chili) chololedwa, chabwino, ndipo pitirizani kuopa Allah. Ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِىُّ قُل لِّمَن فِىٓ أَيْدِيكُم مِّنَ ٱلْأَسْرَىٰٓ إِن يَعْلَمِ ٱللَّهُ فِى قُلُوبِكُمْ خَيْرًۭا يُؤْتِكُمْ خَيْرًۭا مِّمَّآ أُخِذَ مِنكُمْ وَيَغْفِرْ لَكُمْ ۗ وَٱللَّهُ غَفُورٌۭ رَّحِيمٌۭ ﴿70﴾

E iwe Mneneri! Uza akaidi a pankhondo amene ali m’manja mwanu kuti ngati Allah aona chabwino chilichonse m’mitima mwanu, adzakupatsani zoposa zimene mwalandidwa ndipo adzakukhululukirani; Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.

وَإِن يُرِيدُوا۟ خِيَانَتَكَ فَقَدْ خَانُوا۟ ٱللَّهَ مِن قَبْلُ فَأَمْكَنَ مِنْهُمْ ۗ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ ﴿71﴾

Ngati akufuna kukuchitirani chinyengo (chinyengo chawo sichiphula kanthu pa iwe), ndithu anamuchitirapo kale Allah chinyengo (chifukwa cha kusakhulupirira kwawo). Choncho anakupatsa mphamvu zowagonjetsera iwo. Ndipo Allah Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya.

إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ وَهَاجَرُوا۟ وَجَٰهَدُوا۟ بِأَمْوَٰلِهِمْ وَأَنفُسِهِمْ فِى سَبِيلِ ٱللَّهِ وَٱلَّذِينَ ءَاوَوا۟ وَّنَصَرُوٓا۟ أُو۟لَٰٓئِكَ بَعْضُهُمْ أَوْلِيَآءُ بَعْضٍۢ ۚ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ وَلَمْ يُهَاجِرُوا۟ مَا لَكُم مِّن وَلَٰيَتِهِم مِّن شَىْءٍ حَتَّىٰ يُهَاجِرُوا۟ ۚ وَإِنِ ٱسْتَنصَرُوكُمْ فِى ٱلدِّينِ فَعَلَيْكُمُ ٱلنَّصْرُ إِلَّا عَلَىٰ قَوْمٍۭ بَيْنَكُمْ وَبَيْنَهُم مِّيثَٰقٌۭ ۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌۭ ﴿72﴾

Ndithu anthu amene anakhulupirira nasamuka kwawo ndi kumenyana pa njira ya Allah ndi chuma chawo ndi moyo wawo; ndiponso amene anawalandira (iwo) ndi kuwapatsa malo ndi kuwathandiza, awa ndiabale otchinjirizana wina ndi mnzake. Ndipo anthu amene akhulupirira koma nasiya kusamuka (kudza ku Madina), palibe udindo pa inu wa kuwateteza kufikira nawonso atasamuka (kudza ku Madina). Ngati atakupemphani chithandizo cha chipembedzo athandizeni, kupatula (akaputana ndi anthu) amene pakati panu ndi iwo pali chipangano, (pamenepo musawathandize pomenyana ndi osakhulupirirawo omwe muli nawo chipangano). Ndipo Allah Ngowoona zomwe muchita.

وَٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ بَعْضُهُمْ أَوْلِيَآءُ بَعْضٍ ۚ إِلَّا تَفْعَلُوهُ تَكُن فِتْنَةٌۭ فِى ٱلْأَرْضِ وَفَسَادٌۭ كَبِيرٌۭ ﴿73﴾

Ndipo (anthu) amene sadakhulupirire (Allah) amatetezana okha ndi kukhala abwenzi pakati pawo. Ngati nanunso simuchita izi, padzakhala chisokonezo m’dziko ndi chionongeko chachikulu.

وَٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ وَهَاجَرُوا۟ وَجَٰهَدُوا۟ فِى سَبِيلِ ٱللَّهِ وَٱلَّذِينَ ءَاوَوا۟ وَّنَصَرُوٓا۟ أُو۟لَٰٓئِكَ هُمُ ٱلْمُؤْمِنُونَ حَقًّۭا ۚ لَّهُم مَّغْفِرَةٌۭ وَرِزْقٌۭ كَرِيمٌۭ ﴿74﴾

Amene akhulupirira nasamuka, namenya nkhondo panjira ya Allah (pamodzi nanu), ndiponso amene anawalandira (osamukawo), nawapatsa malo ndi kuwathandiza, iwo ndi omwe ali okhulupirira mwa choonadi. Iwo adzapeza chikhululuko ndi zopatsidwa za ulemu.

وَٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ مِنۢ بَعْدُ وَهَاجَرُوا۟ وَجَٰهَدُوا۟ مَعَكُمْ فَأُو۟لَٰٓئِكَ مِنكُمْ ۚ وَأُو۟لُوا۟ ٱلْأَرْحَامِ بَعْضُهُمْ أَوْلَىٰ بِبَعْضٍۢ فِى كِتَٰبِ ٱللَّهِ ۗ إِنَّ ٱللَّهَ بِكُلِّ شَىْءٍ عَلِيمٌۢ ﴿75﴾

Ndipo aja akhulupirira pambuyo (pa Amuhajirina ndi Answari), nawonso nasamukira (ku Madina kukakhala pamodzi ndi Mtumiki ndi Asilamu anzawo), namenyanso nkhondo pamodzi nanu, iwo ndi amene ali mwa inu. Koma achibale chakubadwana, ndiamene ali oyenera (kulowerana mmalo pa chuma) ena ndi ena, mmene zilili) m’buku la Allah. Ndithudi, Allah Ngodziwa chilichonse.