Settings
Surah The Overthrowing [At-Takwir] in Chewa
إِذَا ٱلشَّمْسُ كُوِّرَتْ ﴿1﴾
Pamene dzuwa lidzakulungidwe (ndikuchotsedwa kuwala kwake),[388]
وَإِذَا ٱلنُّجُومُ ٱنكَدَرَتْ ﴿2﴾
Ndi pamene nyenyezi zidzathothoke (ndi kuchoka dangalira lake),
وَإِذَا ٱلْجِبَالُ سُيِّرَتْ ﴿3﴾
Ndi pamene mapiri adzayendetsedwe (kuchoka mmalo mwake),[389]
وَإِذَا ٱلْعِشَارُ عُطِّلَتْ ﴿4﴾
Ndi pamene ngamira zabere lamiyezi khumi zidzasiidwe (zopanda oziyang’anira),[390]
وَإِذَا ٱلْوُحُوشُ حُشِرَتْ ﴿5﴾
Ndi pamene nyama za mtchire zidzasonkhanitsidwe pamodzi (kuchokera mmalo osiyanasiyana chifukwa chakuopsa kwakukulu kwa tsikulo),[391]
وَإِذَا ٱلْبِحَارُ سُجِّرَتْ ﴿6﴾
Ndi pamene nyanja zidzayatsidwe moto,
وَإِذَا ٱلنُّفُوسُ زُوِّجَتْ ﴿7﴾
Ndi pamene mizimu idzalumikizidwe (ndi matupi ake),
وَإِذَا ٱلْمَوْءُۥدَةُ سُئِلَتْ ﴿8﴾
Ndi pamene mwana wamkazi yemwe adaikidwa m’manda wamoyo adzafunsidwe,[392]
بِأَىِّ ذَنۢبٍۢ قُتِلَتْ ﴿9﴾
Ndi tchimo lanji adaphedwera?
وَإِذَا ٱلصُّحُفُ نُشِرَتْ ﴿10﴾
Ndi pamene makalata (momwe mudalembedwa zochita za aliyense) adzatambasulidwe ndi kugawidwa (kuti awerengedwe),[393]
وَإِذَا ٱلسَّمَآءُ كُشِطَتْ ﴿11﴾
Ndi pamene thambo lidzayalulidwe (kuchoka mmalo mwake),
وَإِذَا ٱلْجَحِيمُ سُعِّرَتْ ﴿12﴾
Ndi pamene Jahena idzasonkhezeredwe mwamphamvu,[394]
وَإِذَا ٱلْجَنَّةُ أُزْلِفَتْ ﴿13﴾
Ndi pamene Jannah idzayandikitsidwe,
عَلِمَتْ نَفْسٌۭ مَّآ أَحْضَرَتْ ﴿14﴾
(Zikadzachitika zimenezi) mzimu uliwonse udzadziwa zimene wabweretsa (zabwino ndi zoipa).
فَلَآ أُقْسِمُ بِٱلْخُنَّسِ ﴿15﴾
Ndikulumbilira nyenyezi zimene zimabwerera masana ndi kutulukanso usiku.
ٱلْجَوَارِ ٱلْكُنَّسِ ﴿16﴾
Zomwe zimayenda kenako nkubisika,
وَٱلَّيْلِ إِذَا عَسْعَسَ ﴿17﴾
Ndi usiku pamene ukulowa.
وَٱلصُّبْحِ إِذَا تَنَفَّسَ ﴿18﴾
Ndi m’mawa kukamacha;
إِنَّهُۥ لَقَوْلُ رَسُولٍۢ كَرِيمٍۢ ﴿19﴾
Ndithu iyi (Qur’an) ndi liwu la mthenga wa Allah (Jibril) wolemekezeka,[395]
ذِى قُوَّةٍ عِندَ ذِى ٱلْعَرْشِ مَكِينٍۢ ﴿20﴾
Mwini mphamvu ndi mwini ulemelero kwa Mwini Arsh (Mpando wa chifumu),
مُّطَاعٍۢ ثَمَّ أَمِينٍۢ ﴿21﴾
Womveredwa kumeneko ndiponso wokhulupirika (pachivumbulutso).
وَمَا صَاحِبُكُم بِمَجْنُونٍۢ ﴿22﴾
Ndipo m’bale wanuyu siwamisala ayi.[396]
وَلَقَدْ رَءَاهُ بِٱلْأُفُقِ ٱلْمُبِينِ ﴿23﴾
Ndithu ndikulumbira kuti (iye Mtumiki) (s.a.w) adamuona (Jibril) mchizimezime (chakum’mawa) chooneka bwino.
وَمَا هُوَ عَلَى ٱلْغَيْبِ بِضَنِينٍۢ ﴿24﴾
Ndipo sali iye (Mtumiki) waumbombo ndi chivumbulutso (koma amafikitsa zonse ndi kuziphunzitsa kwa anthu).
وَمَا هُوَ بِقَوْلِ شَيْطَٰنٍۢ رَّجِيمٍۢ ﴿25﴾
(Chivumbulutso chomwe chavumbulutsidwachi kwa iye) si mawu a satana wothamangitsidwa (mchifundo cha Allah);
فَأَيْنَ تَذْهَبُونَ ﴿26﴾
Nanga mukupita kuti?
إِنْ هُوَ إِلَّا ذِكْرٌۭ لِّلْعَٰلَمِينَ ﴿27﴾
(Qur’ani) iyi sichina koma ndi chikumbutso cha zolengedwa zonse.
لِمَن شَآءَ مِنكُمْ أَن يَسْتَقِيمَ ﴿28﴾
Kwa yemwe mwa inu akufuna kuyenda mu njira yoongoka.
وَمَا تَشَآءُونَ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُ رَبُّ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿29﴾
Ndipo simungafune chinthu mwa inu nokha pokhapokha atafuna Allah Mbuye wa zolengedwa zonse.