Settings
Surah The Cleaving [AL-Infitar] in Chewa
إِذَا ٱلسَّمَآءُ ٱنفَطَرَتْ ﴿1﴾
Pamene thambo lidzasweke,[397]
وَإِذَا ٱلْكَوَاكِبُ ٱنتَثَرَتْ ﴿2﴾
Ndi pamene nyenyezi zidzayoyoke (ndi kumwazikana),
وَإِذَا ٱلْبِحَارُ فُجِّرَتْ ﴿3﴾
Pamenenso nyanja zikuluzikulu zidzaphwasulidwe.
وَإِذَا ٱلْقُبُورُ بُعْثِرَتْ ﴿4﴾
Ndiponso pamene manda adzafukulidwe (ndikutuluka akufa omwe adali mmenemo),
عَلِمَتْ نَفْسٌۭ مَّا قَدَّمَتْ وَأَخَّرَتْ ﴿5﴾
(Panthawiyo) mzimu uliwonse udzadziwa zimene udatsogoza (zabwino ndi zoipa) ndi zimene udasiya m’mbuyo.[398]
يَٰٓأَيُّهَا ٱلْإِنسَٰنُ مَا غَرَّكَ بِرَبِّكَ ٱلْكَرِيمِ ﴿6﴾
E iwe munthu! Nchiani chakunyenga kumsiya Mbuye wako wa ufulu (kufikira pomnyoza)?
ٱلَّذِى خَلَقَكَ فَسَوَّىٰكَ فَعَدَلَكَ ﴿7﴾
Amene adalenga iwe nakulinganiza (ziwalo zako) ndi kukulongosola (moyenera);
فِىٓ أَىِّ صُورَةٍۢ مَّا شَآءَ رَكَّبَكَ ﴿8﴾
Ndipo maonekedwe amtundu uliwonse omwe adawafuna adakuveka (popanda chifuniro chako).
كَلَّا بَلْ تُكَذِّبُونَ بِٱلدِّينِ ﴿9﴾
Ayi, sichoncho! Koma inu mukutsutsa za (tsiku) lamalipiro.
وَإِنَّ عَلَيْكُمْ لَحَٰفِظِينَ ﴿10﴾
Ndithu pa inu alipo okuyang’ anirani,[399]
كِرَامًۭا كَٰتِبِينَ ﴿11﴾
Olemekezeka, olemba (zochita zanu.)
يَعْلَمُونَ مَا تَفْعَلُونَ ﴿12﴾
Akudziwa (zonse) zimene mukuchita (zabwino ndi zoipa).
إِنَّ ٱلْأَبْرَارَ لَفِى نَعِيمٍۢ ﴿13﴾
Ndithudi ochita zabwino adzakhala mu mtendere.
وَإِنَّ ٱلْفُجَّارَ لَفِى جَحِيمٍۢ ﴿14﴾
Ndipo ndithu amene ali olakwira malamulo a Allah adzakhala ku Moto wopsereza.
يَصْلَوْنَهَا يَوْمَ ٱلدِّينِ ﴿15﴾
Adzaulowa tsiku la malipiro.
وَمَا هُمْ عَنْهَا بِغَآئِبِينَ ﴿16﴾
Ndipo iwo kumeneko sadzachokako.
وَمَآ أَدْرَىٰكَ مَا يَوْمُ ٱلدِّينِ ﴿17﴾
Kodi nchiyani chingakudziwitse za tsiku la malipiro?
ثُمَّ مَآ أَدْرَىٰكَ مَا يَوْمُ ٱلدِّينِ ﴿18﴾
Ndipo nchiyani chingakudziwitse za tsiku lamalipiro?
يَوْمَ لَا تَمْلِكُ نَفْسٌۭ لِّنَفْسٍۢ شَيْـًۭٔا ۖ وَٱلْأَمْرُ يَوْمَئِذٍۢ لِّلَّهِ ﴿19﴾
Limeneli ndi tsiku limene mzimu uliwonse sudzakhala ndi mphamvu (yodzetsa mtendere kapena yochotsa chovuta) pa mzimu wina. Ndipo lamulo pa tsiku limeneli ndi la Allah yekha.[400]