Main pages

Surah The Mansions of the stars [Al-Burooj] in Chewa

Surah The Mansions of the stars [Al-Burooj] Ayah 22 Location Makkah Number 85

وَٱلسَّمَآءِ ذَاتِ ٱلْبُرُوجِ ﴿1﴾

Ndikulumbilira thambo lomwe liri ndi Buruj (Nyenyezi zikuluzikulu).[411]

وَٱلْيَوْمِ ٱلْمَوْعُودِ ﴿2﴾

Ndi tsiku lolonjezedwa (kuwerengedwa ndi kulipidwa),

وَشَاهِدٍۢ وَمَشْهُودٍۢ ﴿3﴾

Ndi woikira umboni, ndi woikiridwa umboni.[412]

قُتِلَ أَصْحَٰبُ ٱلْأُخْدُودِ ﴿4﴾

Atembeleredwa eni ngalande zamoto (zomwe adali kuwazunzira okhulupirira Allah, achimuna ndi achikazi).[413]

ٱلنَّارِ ذَاتِ ٱلْوَقُودِ ﴿5﴾

(Ngalande) za moto wankhuni (zambiri zomwe adali kuzikoleza ndikuotchera okhulupirira),

إِذْ هُمْ عَلَيْهَا قُعُودٌۭ ﴿6﴾

Pamene iwo adali chikhalire m’mphepete mwa ngalandezo.

وَهُمْ عَلَىٰ مَا يَفْعَلُونَ بِٱلْمُؤْمِنِينَ شُهُودٌۭ ﴿7﴾

Uku iwo akuyang’ana zomwe amawachitira okhulupirira, (pootchedwa ndi moto).

وَمَا نَقَمُوا۟ مِنْهُمْ إِلَّآ أَن يُؤْمِنُوا۟ بِٱللَّهِ ٱلْعَزِيزِ ٱلْحَمِيدِ ﴿8﴾

Sadaone choipa chilichonse mwa iwo koma chifukwa choti adakhulupirira Allah mwini mphamvu zonse ndiponso mwini kuyamikidwa,

ٱلَّذِى لَهُۥ مُلْكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلْأَرْضِ ۚ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَىْءٍۢ شَهِيدٌ ﴿9﴾

Yemwe ufumu wakumwamba ndi pansi ndiWake; ndipo Allah ndi mboni pachilichonse.

إِنَّ ٱلَّذِينَ فَتَنُوا۟ ٱلْمُؤْمِنِينَ وَٱلْمُؤْمِنَٰتِ ثُمَّ لَمْ يَتُوبُوا۟ فَلَهُمْ عَذَابُ جَهَنَّمَ وَلَهُمْ عَذَابُ ٱلْحَرِيقِ ﴿10﴾

Ndithu amene ayesa mayeso okhulupirira achimuna ndi achikazi (pa chipembedzo chawo ndi mazunzo ndi chilango cha moto), pambuyo pake osalapa (pa zimenezi), adzalandira chilango cha Jahena ndiponso chilango cha moto wopsereza,[414]

إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ وَعَمِلُوا۟ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُمْ جَنَّٰتٌۭ تَجْرِى مِن تَحْتِهَا ٱلْأَنْهَٰرُ ۚ ذَٰلِكَ ٱلْفَوْزُ ٱلْكَبِيرُ ﴿11﴾

Ndithudi amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, adzakhala ndi Minda yamtendere (momwe) mitsinje ikuyenda pansi pake; kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.

إِنَّ بَطْشَ رَبِّكَ لَشَدِيدٌ ﴿12﴾

Ndithu kulanga kwa Mbuye wako (kwa anthu achinyengo), ndi kwaukali kwambiri.[415]

إِنَّهُۥ هُوَ يُبْدِئُ وَيُعِيدُ ﴿13﴾

Iye, (Mmodzi yekha) ndi amene adayambitsa zolengedwa ndiponso ndi Yemwe adzazibweze (pambuyo poonongeka);

وَهُوَ ٱلْغَفُورُ ٱلْوَدُودُ ﴿14﴾

Iye, ndi Wokhululuka (kwa amene walapa kwa Iye), ndiponso Wokonda kwambiri (amene akumkonda ndi kumumvera),

ذُو ٱلْعَرْشِ ٱلْمَجِيدُ ﴿15﴾

Mwini Arsh (Mpando wachifumu), (ndiponso) Wolemekezeka (mmene alili ndi mbiri Zake),

فَعَّالٌۭ لِّمَا يُرِيدُ ﴿16﴾

Wochita zimene wafuna, (ndipo chimene wafuna sichikanika).

هَلْ أَتَىٰكَ حَدِيثُ ٱلْجُنُودِ ﴿17﴾

Kodi yakufika nkhani ya magulu a nkhondo,

فِرْعَوْنَ وَثَمُودَ ﴿18﴾

Firiaun (Farawo) ndi Samudu, (ndi chilango chimene chidawapeza chifukwa chakulimbikira kwawo pa zinthu zopanda pake)?

بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ فِى تَكْذِيبٍۢ ﴿19﴾

Koma amene sadakhulupirire ali mkati motsutsa basi.

وَٱللَّهُ مِن وَرَآئِهِم مُّحِيطٌۢ ﴿20﴾

Koma Allah awazinga mbali zonse.

بَلْ هُوَ قُرْءَانٌۭ مَّجِيدٌۭ ﴿21﴾

Koma iyi ndi Qur’an yolemekezeka.

فِى لَوْحٍۢ مَّحْفُوظٍۭ ﴿22﴾

Yomwe idachokera mu ubawo (chisileti chachikulu) wotetezedwa (ndi manja alionse, osintha kanthu kapena kuonjezerapo).