Settings
Surah The morning star [At-Tariq] in Chewa
وَٱلسَّمَآءِ وَٱلطَّارِقِ ﴿1﴾
Ndikulumbilira ku mwamba ndi Nyenyezi imene imadza usiku,
وَمَآ أَدْرَىٰكَ مَا ٱلطَّارِقُ ﴿2﴾
Chitakudziwitse nchiyani za Nyenyezi yodza usikuyo?
ٱلنَّجْمُ ٱلثَّاقِبُ ﴿3﴾
Imeneyo ndi nyenyezi yowala kwambiri (mu mdima).
إِن كُلُّ نَفْسٍۢ لَّمَّا عَلَيْهَا حَافِظٌۭ ﴿4﴾
Ndithudi palibe mzimu uliwonse koma uli ndi msungi wake (amene akuuyang’anira ndikulemba zonse zochita zake).
فَلْيَنظُرِ ٱلْإِنسَٰنُ مِمَّ خُلِقَ ﴿5﴾
Aganizire munthu, kodi adalengedwa kuchokera kuchiyani?
خُلِقَ مِن مَّآءٍۢ دَافِقٍۢ ﴿6﴾
Adalengedwa kuchokera ku madzi ofwamphuka.
يَخْرُجُ مِنۢ بَيْنِ ٱلصُّلْبِ وَٱلتَّرَآئِبِ ﴿7﴾
Amatuluka kuchokera pakati pa mafupa a msana (wa mwamuna) ndi chifuwa (cha mkazi).
إِنَّهُۥ عَلَىٰ رَجْعِهِۦ لَقَادِرٌۭ ﴿8﴾
Ndithu Iye ndiwakutha, kumbwezeranso (ku moyo pa mbuyo pa imfa).
يَوْمَ تُبْلَى ٱلسَّرَآئِرُ ﴿9﴾
Tsiku limene zobisika zonse zidzaonekera poyera.
فَمَا لَهُۥ مِن قُوَّةٍۢ وَلَا نَاصِرٍۢ ﴿10﴾
Munthu sadzakhala ndi mphamvu (tsiku limenelo zodzitetezera iye mwini) ndiponso sadzakhala ndi mtetezi.
وَٱلسَّمَآءِ ذَاتِ ٱلرَّجْعِ ﴿11﴾
Ndikulumbiliranso mitambo yobweretsabweretsa mvula.
وَٱلْأَرْضِ ذَاتِ ٱلصَّدْعِ ﴿12﴾
Ndi nthaka imene imang’ambika (potulutsa m’mera),
إِنَّهُۥ لَقَوْلٌۭ فَصْلٌۭ ﴿13﴾
Ndithudi iyi (Qur’an) ndi mawu olekanitsa (Haqq ndi Bâtwil - choona ndi chonama).
وَمَا هُوَ بِٱلْهَزْلِ ﴿14﴾
Imeneyi sinkhambakamwa.
إِنَّهُمْ يَكِيدُونَ كَيْدًۭا ﴿15﴾
Ndithudi iwo akukonza chiwembu.[416]
وَأَكِيدُ كَيْدًۭا ﴿16﴾
Nanenso ndikuwakonzera chiwembu (champhamvu kwambiri chimene sangathe kuchipewa).
فَمَهِّلِ ٱلْكَٰفِرِينَ أَمْهِلْهُمْ رُوَيْدًۢا ﴿17﴾
Basi, apatse nthawi osakhulupirira apatse nthawi pang’ono, (aona posachedwa).