Settings
Surah The Overwhelming [Al-Ghashiya] in Chewa
هَلْ أَتَىٰكَ حَدِيثُ ٱلْغَٰشِيَةِ ﴿1﴾
Kodi yakudzera, (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Qiyâma (imene idzaphimba anthu ndi zoopsa zake)?
وُجُوهٌۭ يَوْمَئِذٍ خَٰشِعَةٌ ﴿2﴾
Nkhope zina tsiku limenelo, zidzakhala zonyozeka,[425]
عَامِلَةٌۭ نَّاصِبَةٌۭ ﴿3﴾
Zogwira ntchito yotopetsa kwambiri.
تَصْلَىٰ نَارًا حَامِيَةًۭ ﴿4﴾
Zikalowa ku Moto wotentha kwambiri.
تُسْقَىٰ مِنْ عَيْنٍ ءَانِيَةٍۢ ﴿5﴾
Zikamwetsedwa mu kasupe wotentha kwabasi.
لَّيْسَ لَهُمْ طَعَامٌ إِلَّا مِن ضَرِيعٍۢ ﴿6﴾
Sadzakhala ndichakudya koma minga.
لَّا يُسْمِنُ وَلَا يُغْنِى مِن جُوعٍۢ ﴿7﴾
Yosanenepetsa (thupi) ndiponso yosathetsa njala.
وُجُوهٌۭ يَوْمَئِذٍۢ نَّاعِمَةٌۭ ﴿8﴾
Nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zosangalala.
لِّسَعْيِهَا رَاضِيَةٌۭ ﴿9﴾
Zidzakondwera ndi malipiro a zochita zake (za pa dziko lapansi).[426]
فِى جَنَّةٍ عَالِيَةٍۢ ﴿10﴾
M’minda ya pamwamba (Jannah).
لَّا تَسْمَعُ فِيهَا لَٰغِيَةًۭ ﴿11﴾
Sizikamva m’menemo mawu oipa, (otukwana ndi kulaula).
فِيهَا عَيْنٌۭ جَارِيَةٌۭ ﴿12﴾
Mmenemo muli kasupe woyenda (mokongola).[427]
فِيهَا سُرُرٌۭ مَّرْفُوعَةٌۭ ﴿13﴾
Mmenemo muli makama a pamwamba,
وَأَكْوَابٌۭ مَّوْضُوعَةٌۭ ﴿14﴾
Ndi zikho zoikidwa bwino (pamaso pawo),
وَنَمَارِقُ مَصْفُوفَةٌۭ ﴿15﴾
Ndi misamiro yoikidwa bwino m’mizeremizere
وَزَرَابِىُّ مَبْثُوثَةٌ ﴿16﴾
Ndi mphasa (zamtengo wapatali, carpet) zoyalidwa ponseponse.
أَفَلَا يَنظُرُونَ إِلَى ٱلْإِبِلِ كَيْفَ خُلِقَتْ ﴿17﴾
Kodi (akunyozera kulingalira zisonyezo za Allah), sakulingalira kungamira idalengedwa motani?[428]
وَإِلَى ٱلسَّمَآءِ كَيْفَ رُفِعَتْ ﴿18﴾
Ndi thambo (limene akuliona nthawi zonse) m’mene lidatukulidwira (kutali popanda mzati)?
وَإِلَى ٱلْجِبَالِ كَيْفَ نُصِبَتْ ﴿19﴾
Ndi mapiri momwe adakhazikitsidwira (molimba)?
وَإِلَى ٱلْأَرْضِ كَيْفَ سُطِحَتْ ﴿20﴾
Ndi nthaka momwe idayalidwira.
فَذَكِّرْ إِنَّمَآ أَنتَ مُذَكِّرٌۭ ﴿21﴾
Basi, kumbutsa (anthu) ndithu iwe, ndiwe mkumbutsi.
لَّسْتَ عَلَيْهِم بِمُصَيْطِرٍ ﴿22﴾
Sindiwe wokakamiza anthu (kuti akhulupirire).[429]
إِلَّا مَن تَوَلَّىٰ وَكَفَرَ ﴿23﴾
Koma amene anyoza ndi kukanira (ulaliki wako),
فَيُعَذِّبُهُ ٱللَّهُ ٱلْعَذَابَ ٱلْأَكْبَرَ ﴿24﴾
Allah amulanga chilango chachikulu zedi.
إِنَّ إِلَيْنَآ إِيَابَهُمْ ﴿25﴾
Ndithu kobwerera kwawo ndi kwa Ife basi.
ثُمَّ إِنَّ عَلَيْنَا حِسَابَهُم ﴿26﴾
Ndipo ndithu kuwerengedwa kwawo kuli kwa Ife.