Settings
Surah The Dawn [Al-Fajr] in Chewa
وَٱلْفَجْرِ ﴿1﴾
Ndikulumbilira kuyera kwa m’bandakucha; (pamene usiku uthawa).
وَلَيَالٍ عَشْرٍۢ ﴿2﴾
Ndi masiku khumi (a mwezi wa Dhul-Hijjah omwe ngopatulika kwa Allah).[430]
وَٱلشَّفْعِ وَٱلْوَتْرِ ﴿3﴾
Ndi Shaf’i ndi Witri: (nambala yogawika ndi yosagawika).[431]
وَٱلَّيْلِ إِذَا يَسْرِ ﴿4﴾
Ndi usiku pamene ukupita (chifukwa cha kuyenda kwa dziko kodabwitsa).
هَلْ فِى ذَٰلِكَ قَسَمٌۭ لِّذِى حِجْرٍ ﴿5﴾
Kodi m’zimene zatchulidwazi simuli kulumbira kokwanira, kwa munthu wa nzeru?
أَلَمْ تَرَ كَيْفَ فَعَلَ رَبُّكَ بِعَادٍ ﴿6﴾
Kodi sudadziwe momwe Mbuye wako adawalangira Âdi (anthu a mneneri Hûd).
إِرَمَ ذَاتِ ٱلْعِمَادِ ﴿7﴾
Aku Irama; ataliatali ngati zipilala.[432]
ٱلَّتِى لَمْ يُخْلَقْ مِثْلُهَا فِى ٱلْبِلَٰدِ ﴿8﴾
Omwe onga iwo sadalengedwe m’maiko ena?
وَثَمُودَ ٱلَّذِينَ جَابُوا۟ ٱلصَّخْرَ بِٱلْوَادِ ﴿9﴾
Ndi Asamudu, (anthu a mneneri Swaleh) amene adali kudula matanthwe ku chigwa (chotchedwa Wadi Qura ndi kumamanga nyumba zikuluzikulu)?
وَفِرْعَوْنَ ذِى ٱلْأَوْتَادِ ﴿10﴾
Komanso Firiauna (Farawo) mwini magulu ankhondo (omwe amalimbikitsa ufumu wake monga momwe zichiri zimalimbikitsira tenti)?
ٱلَّذِينَ طَغَوْا۟ فِى ٱلْبِلَٰدِ ﴿11﴾
Amene adaipitsa m’maiko mopyola malire?
فَأَكْثَرُوا۟ فِيهَا ٱلْفَسَادَ ﴿12﴾
Ndipo adachulukitsa m’menemo kuononga (pamwamba pa kuononga).[433]
فَصَبَّ عَلَيْهِمْ رَبُّكَ سَوْطَ عَذَابٍ ﴿13﴾
Choncho Mbuye wako adawathira ndi mitundu ya zilango (zoopsa).
إِنَّ رَبَّكَ لَبِٱلْمِرْصَادِ ﴿14﴾
Ndithu Mbuye wako ali tcheru (ndi zochita za anthu. Ndipo akuwasungira kuti adzawalipire).[434]
فَأَمَّا ٱلْإِنسَٰنُ إِذَا مَا ٱبْتَلَىٰهُ رَبُّهُۥ فَأَكْرَمَهُۥ وَنَعَّمَهُۥ فَيَقُولُ رَبِّىٓ أَكْرَمَنِ ﴿15﴾
Pamene munthu Mbuye wake akumuyesa (mayeso) ndikumulemekeza ndi kumpatsa mtendere (wachuma, ulemelero ndi mphamvu) amanena monyada: Mbuye wanga wandilemekeza (chifukwa zimenezi nzondiyenera ine).
وَأَمَّآ إِذَا مَا ٱبْتَلَىٰهُ فَقَدَرَ عَلَيْهِ رِزْقَهُۥ فَيَقُولُ رَبِّىٓ أَهَٰنَنِ ﴿16﴾
Koma akamuyesa mayeso ndi kumchepetsera rizq lake, (chuma) amanena (motaya rntima): Mbuye wanga wandinyoza!
كَلَّا ۖ بَل لَّا تُكْرِمُونَ ٱلْيَتِيمَ ﴿17﴾
Sichoncho ayi, (monga momwe mukuganizira) koma inu simuchitira za ufulu ana amasiye!
وَلَا تَحَٰٓضُّونَ عَلَىٰ طَعَامِ ٱلْمِسْكِينِ ﴿18﴾
Ndipo simulimbikitsana za kudyetsa osauka,
وَتَأْكُلُونَ ٱلتُّرَاثَ أَكْلًۭا لَّمًّۭا ﴿19﴾
Ndipo mukudya chuma cha masiye; kudya kosusuka.[435]
وَتُحِبُّونَ ٱلْمَالَ حُبًّۭا جَمًّۭا ﴿20﴾
Ndiponso mukukonda chuma; kukonda kopyola muyeso.
كَلَّآ إِذَا دُكَّتِ ٱلْأَرْضُ دَكًّۭا دَكًّۭا ﴿21﴾
Sichoncho! (Siyani machitidwe amenewa); nthaka ikadzapondedwa (ndikuifafaniza).
وَجَآءَ رَبُّكَ وَٱلْمَلَكُ صَفًّۭا صَفًّۭا ﴿22﴾
Ndikubwera Mbuye wako (mmabweredwe omwe akuwadziwa Iye Mwini) ndi angelo ali mmizeremizere.
وَجِا۟ىٓءَ يَوْمَئِذٍۭ بِجَهَنَّمَ ۚ يَوْمَئِذٍۢ يَتَذَكَّرُ ٱلْإِنسَٰنُ وَأَنَّىٰ لَهُ ٱلذِّكْرَىٰ ﴿23﴾
Ndi kubweretsedwa Jahannam pa tsikulo, basi tsiku limenelo munthu adzakumbukira, koma kukumbuka kumeneko kudzamthandiza chiyani?
يَقُولُ يَٰلَيْتَنِى قَدَّمْتُ لِحَيَاتِى ﴿24﴾
Adzanena: Kalanga ine! Ndikadatsogoza zabwino pa za moyo wanga uno!
فَيَوْمَئِذٍۢ لَّا يُعَذِّبُ عَذَابَهُۥٓ أَحَدٌۭ ﴿25﴾
Motero patsikuli, palibe wina amene adzalange monga momwe (Allah) adzalangire.[436]
وَلَا يُوثِقُ وَثَاقَهُۥٓ أَحَدٌۭ ﴿26﴾
Ndiponso sanganjate aliyense monga kunjata kwa iye (Allah).
يَٰٓأَيَّتُهَا ٱلنَّفْسُ ٱلْمُطْمَئِنَّةُ ﴿27﴾
E iwe mzimu wokhazikika (ndi choona)![437]
ٱرْجِعِىٓ إِلَىٰ رَبِّكِ رَاضِيَةًۭ مَّرْضِيَّةًۭ ﴿28﴾
Bwerera kwa Mbuye wako uli wokondwera (ndi zomwe wapatsidwa), ndipo uli woyanjidwa (ndi Allah pa zomwe udatsogoza).[438]
فَٱدْخُلِى فِى عِبَٰدِى ﴿29﴾
Lowa mgulu la akapolo anga abwino.
وَٱدْخُلِى جَنَّتِى ﴿30﴾
Ndipo lowa m’munda Wanga (mnyumba ya mtendere wa muyaya).