Settings
Surah The City [Al-Balad] in Chewa
لَآ أُقْسِمُ بِهَٰذَا ٱلْبَلَدِ ﴿1﴾
Ndikulumbilira mzinda uwu (wa Makka).
وَأَنتَ حِلٌّۢ بِهَٰذَا ٱلْبَلَدِ ﴿2﴾
Ndipo iwe udzatsikira mu mzindawu mwa ufulu (ndi kuuonjezera ulemelero).
وَوَالِدٍۢ وَمَا وَلَدَ ﴿3﴾
Ndiponso ndikulumbilira chobereka ndi choberekedwa, (kudzera mwa iwo mtundu wa anthu udasungidwa).
لَقَدْ خَلَقْنَا ٱلْإِنسَٰنَ فِى كَبَدٍ ﴿4﴾
Ndithudi tamulenga munthu mmavuto (kuyambira chiyambi chake mpaka malekezero a moyo wake).[439]
أَيَحْسَبُ أَن لَّن يَقْدِرَ عَلَيْهِ أَحَدٌۭ ﴿5﴾
Kodi (munthu wolengedwa ndi mavutoyu) akuganiza kuti palibe amene angamuthe? [440]
يَقُولُ أَهْلَكْتُ مَالًۭا لُّبَدًا ﴿6﴾
Akunena (monyadira kuti): “Ndaononga chuma chambiri (chifukwa choletsa Chisilamu kufala).”[441]
أَيَحْسَبُ أَن لَّمْ يَرَهُۥٓ أَحَدٌ ﴿7﴾
Kodi akuganiza kuti palibe akumuona?
أَلَمْ نَجْعَل لَّهُۥ عَيْنَيْنِ ﴿8﴾
Kodi sitidampangire maso awiri (amene akuyang’anira)?
وَلِسَانًۭا وَشَفَتَيْنِ ﴿9﴾
Ndilirime ndi milomo iwiri (zimene akulankhulira)?
وَهَدَيْنَٰهُ ٱلنَّجْدَيْنِ ﴿10﴾
Ndipo tamlongosolera njira ziwiri: (yabwino ndi yoipa, ndipo tampatsa mphamvu yosankhira njira imene akufuna).
فَلَا ٱقْتَحَمَ ٱلْعَقَبَةَ ﴿11﴾
Kodi walikwera phiri lovutalo (lomwe lingakamfikitse ku Jannah)?[442]
وَمَآ أَدْرَىٰكَ مَا ٱلْعَقَبَةُ ﴿12﴾
Nanga nchiyani chakudziwitsa za kukwera phiri lovutalo?
فَكُّ رَقَبَةٍ ﴿13﴾
(Kutero ndiko) kupereka ufulu kwa kapolo,
أَوْ إِطْعَٰمٌۭ فِى يَوْمٍۢ ذِى مَسْغَبَةٍۢ ﴿14﴾
Kapena kuwadyetsa (osowa) pa tsiku la njala,
يَتِيمًۭا ذَا مَقْرَبَةٍ ﴿15﴾
Amasiye achibale,
أَوْ مِسْكِينًۭا ذَا مَتْرَبَةٍۢ ﴿16﴾
Kapena wosauka wa fumbi lokhalokha (chifukwa cha kuvutika kwambiri),
ثُمَّ كَانَ مِنَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ وَتَوَاصَوْا۟ بِٱلصَّبْرِ وَتَوَاصَوْا۟ بِٱلْمَرْحَمَةِ ﴿17﴾
Komanso nakhala mmodzi mwa okhulupirira ndikumalangizana za kupirira, ndi kumalangizananso za chifundo.
أُو۟لَٰٓئِكَ أَصْحَٰبُ ٱلْمَيْمَنَةِ ﴿18﴾
Otero ndiwo (anthu abwino) a ku dzanja lamanja.
وَٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ بِـَٔايَٰتِنَا هُمْ أَصْحَٰبُ ٱلْمَشْـَٔمَةِ ﴿19﴾
Koma amene sanakhulupirire Ayah Zathu, ndi anthu a kudzanja lamanzere (oipa).
عَلَيْهِمْ نَارٌۭ مُّؤْصَدَةٌۢ ﴿20﴾
Moto wozungulira mbali zonse udzakhala pa iwo (ndikuwatsekera makomo).