Settings
Surah The Sun [Ash-Shams] in Chewa
وَٱلشَّمْسِ وَضُحَىٰهَا ﴿1﴾
Ndikulumbilira dzuwa ndi dangalira lake.
وَٱلْقَمَرِ إِذَا تَلَىٰهَا ﴿2﴾
Ndi mwezi pamene ukulitsatira (dzuwalo ndikulowa mmalo mwake powalitsa dziko dzuwalo litalowa).
وَٱلنَّهَارِ إِذَا جَلَّىٰهَا ﴿3﴾
Ndi usana pamene ukulisonyeza poyera (kuti lisaphimbidwe).
وَٱلَّيْلِ إِذَا يَغْشَىٰهَا ﴿4﴾
Ndi usiku pamene ukuliphimba.
وَٱلسَّمَآءِ وَمَا بَنَىٰهَا ﴿5﴾
Ndi thambo ndi (Mwini mphamvu zonse Wamkulu) Yemwe adalimanga ndi kulitukula (mwaluso).
وَٱلْأَرْضِ وَمَا طَحَىٰهَا ﴿6﴾
Ndi nthaka ndi (Mwini mphamvu zonse Wamkulu), Yemwe adaiyala (mbali zonse ndi kuichita kukhala ngati choyala).
وَنَفْسٍۢ وَمَا سَوَّىٰهَا ﴿7﴾
Ndi mzimu ndi Yemwe adawulinganiza (powupatsa mphamvu).
فَأَلْهَمَهَا فُجُورَهَا وَتَقْوَىٰهَا ﴿8﴾
Ndipo adaudziwitsa zoipa zake ndi zabwino zake; (ndi kuwupatsa ufulu ndi mphamvu zochitira zimene ukufuna).
قَدْ أَفْلَحَ مَن زَكَّىٰهَا ﴿9﴾
Ndithu wapambana amene wauyeretsa.[443]
وَقَدْ خَابَ مَن دَسَّىٰهَا ﴿10﴾
Ndipo ndithu wataika amene wauononga.[444]
كَذَّبَتْ ثَمُودُ بِطَغْوَىٰهَآ ﴿11﴾
Thamud (Samudu) adakanira (Mneneri wawo) chifukwa cha kulumpha malire kwawo.[445]
إِذِ ٱنۢبَعَثَ أَشْقَىٰهَا ﴿12﴾
Pamene woipitsitsa wawo adadzipereka (kupha ngamira yozizwitsa).
فَقَالَ لَهُمْ رَسُولُ ٱللَّهِ نَاقَةَ ٱللَّهِ وَسُقْيَٰهَا ﴿13﴾
Pamenepo Mneneri wa Allah (Swaleh) adawauza: “Isiyeni ngamira ya Allah (idye mdziko la Allah). Musailetse kumwa madzi (pa tsiku lake).”
فَكَذَّبُوهُ فَعَقَرُوهَا فَدَمْدَمَ عَلَيْهِمْ رَبُّهُم بِذَنۢبِهِمْ فَسَوَّىٰهَا ﴿14﴾
Koma adamutsutsa ndikuipha; kwa chifukwa chimenecho Mbuye wawo (Allah) adawaononga chifukwa cha tchimo lawo; adangowafafaniza (onse mnthaka).
وَلَا يَخَافُ عُقْبَٰهَا ﴿15﴾
Iye saopa zotsatira za chilangochi (chifukwa amenewa ndi malipiro a chilungamo pa zomwe adachita).