Settings
Surah The Fig [At-Tin] in Chewa
بِّسْمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحْمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ وَٱلتِّينِ وَٱلزَّيْتُونِ ﴿1﴾
Ndikulumbilira mitengo ya Mkuyu ndi Zitona (pansi pa mitengo imeneyi Ibrahim ndi Nuh (Nowa) adapeza uneneri),
وَطُورِ سِينِينَ ﴿2﴾
Ndi phiri la Sinai (pamene Allah adamulankhulira Mûsa),
وَهَٰذَا ٱلْبَلَدِ ٱلْأَمِينِ ﴿3﴾
Ndiponso mzinda uwu (wolemekezeka) wamtendere; (Makka, womwe adapatsiridwa uneneri Muhammad) (s.a.w).
لَقَدْ خَلَقْنَا ٱلْإِنسَٰنَ فِىٓ أَحْسَنِ تَقْوِيمٍۢ ﴿4﴾
Palibe chikaiko, tamulenga munthu mkalengedwe kabwino, kolingana (ndipo ali ndi mbiri zabwino).[457]
ثُمَّ رَدَدْنَٰهُ أَسْفَلَ سَٰفِلِينَ ﴿5﴾
Pambuyo pake tamubwezera pansi kumposa wa pansi.[458]
إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ وَعَمِلُوا۟ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَلَهُمْ أَجْرٌ غَيْرُ مَمْنُونٍۢ ﴿6﴾
Kupatula amene akhulupirira ndikumachita zabwino, adzakhala nawo iwo malipiro osatha.
فَمَا يُكَذِّبُكَ بَعْدُ بِٱلدِّينِ ﴿7﴾
Tsono nchiyani chakuchititsa kuti ukanire kuuka ndi malipiro pambuyo (poona mphamvu zathu pa chilichonse)?[459]
أَلَيْسَ ٱللَّهُ بِأَحْكَمِ ٱلْحَٰكِمِينَ ﴿8﴾
Kodi Allah si Muweruzi wa nzeru kuposa aweruzi onse?