Settings
Surah The Clear proof [Al-Bayyina] in Chewa
لَمْ يَكُنِ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ مِنْ أَهْلِ ٱلْكِتَٰبِ وَٱلْمُشْرِكِينَ مُنفَكِّينَ حَتَّىٰ تَأْتِيَهُمُ ٱلْبَيِّنَةُ ﴿1﴾
Amene adakanira (Allah ndi Mthenga Wake) mwa omwe adapatsidwa buku ndi opembedza mafano sadali olekana (ndi umbuli wawo ndi kusalabadira kwawo choona) mpaka pomwe chidawadzera chisonyezo choonekera poyera.[466]
رَسُولٌۭ مِّنَ ٱللَّهِ يَتْلُوا۟ صُحُفًۭا مُّطَهَّرَةًۭ ﴿2﴾
(Yemwe ndi) Mtumiki wochokera kwa Allah akuwawerengera makalata oyeretsedwa (ku zonama).[467]
فِيهَا كُتُبٌۭ قَيِّمَةٌۭ ﴿3﴾
Omwe mkati mwake muli malamulo oongoka (ofotokoza za choona).[468]
وَمَا تَفَرَّقَ ٱلَّذِينَ أُوتُوا۟ ٱلْكِتَٰبَ إِلَّا مِنۢ بَعْدِ مَا جَآءَتْهُمُ ٱلْبَيِّنَةُ ﴿4﴾
Sadalekane omwe adapatsidwa mabuku mpaka pomwe chidawafikira chisonyezo (chosonyeza kuti Muhammad (s.a.w) ndi mthenga wa Allah yemwe adalonjezedwa mmabuku awo).
وَمَآ أُمِرُوٓا۟ إِلَّا لِيَعْبُدُوا۟ ٱللَّهَ مُخْلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ حُنَفَآءَ وَيُقِيمُوا۟ ٱلصَّلَوٰةَ وَيُؤْتُوا۟ ٱلزَّكَوٰةَ ۚ وَذَٰلِكَ دِينُ ٱلْقَيِّمَةِ ﴿5﴾
Ndipo sadalamulidwe (china) koma kuti ampembedze Allah (Mmodzi yekha) ndikuyeretsa chipembedzo chake popendekera ku choona (ndi kusiya njira zonama) ndi kuti asunge Swala ndiponso apereke chopereka (cha pachuma chawo); chimenecho (ndicho) chipembedzo choongoka.[469]
إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوا۟ مِنْ أَهْلِ ٱلْكِتَٰبِ وَٱلْمُشْرِكِينَ فِى نَارِ جَهَنَّمَ خَٰلِدِينَ فِيهَآ ۚ أُو۟لَٰٓئِكَ هُمْ شَرُّ ٱلْبَرِيَّةِ ﴿6﴾
Ndithu amene sadakhulupirire (Mneneri) (s.a.w) pakati pa anthu a mabuku ndi opembedza mafano adzalowetsedwa ku Jahannam ndikukhala m’menemo nthawi yaitali; iwowo ndiwo zolengedwa zoipa.
إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ وَعَمِلُوا۟ ٱلصَّٰلِحَٰتِ أُو۟لَٰٓئِكَ هُمْ خَيْرُ ٱلْبَرِيَّةِ ﴿7﴾
Ndithu amene akhulupirira (mwa Allah ndi Mthenga Wake) ndikumachita zabwino, iwo ndiwo zolengedwa zabwino.
جَزَآؤُهُمْ عِندَ رَبِّهِمْ جَنَّٰتُ عَدْنٍۢ تَجْرِى مِن تَحْتِهَا ٱلْأَنْهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدًۭا ۖ رَّضِىَ ٱللَّهُ عَنْهُمْ وَرَضُوا۟ عَنْهُ ۚ ذَٰلِكَ لِمَنْ خَشِىَ رَبَّهُۥ ﴿8﴾
Malipiro awo kwa Mbuye wawo, ndi minda yamuyaya momwe ikuyenda pansi pake mitsinje; adzakhala m’menemo muyaya. Allah adzawayanja nawonso adzamuyanja (chifukwa cha zomwe adzawapatse); zimenezo ndi za yemwe awope Mbuye wake (Allah).